Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 3/15 tsamba 10-14
  • Taonani Okhulupirika!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Taonani Okhulupirika!
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhulupirika ndi Chinthu Chapadera
  • Yehova, Wokhulupirika Wamkulukulu
  • Yesu Kristu, Mwana Wokhulupirika
  • Anthu Opanda Ungwiro Amene Anali Okhulupirika
  • Okhulupirika m’Nthaŵi Zamakono
  • ‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’
    Yandikirani Yehova
  • Kupambana Chiyeso cha Kukhulupirika
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kukhulupirika—Pamtengo Wotani?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Muyenera Kukhala Okhulupirika kwa Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 3/15 tsamba 10-14

Taonani Okhulupirika!

“Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu [Yehova, NW]? Chifukwa inu nokha muli [wokhulupirika, NW].”​—CHIVUMBULUTSO 15:4.

1. Kodi ndi umboni wotani wokhudza kukhulupirika kwa C. T. Russell umene J. F. Rutherford wom’loŵa m’malo anapereka?

JOSEPH F. RUTHERFORD, amene anatenga malo a C. T. Russell kukhala pulezidenti wa Watch Tower Society mu 1917, anayamba kulankhula poika maliro a Russell mwa kunena kuti: “Charles Taze Russell anali wokhulupirika kwa Mulungu, wokhulupirika kwa Kristu Yesu, wokhulupirika pa chifuno cha ufumu wa Mesiya. Anali wokhulupirika ndi mtima wonse​—inde, wokhulupirika mpaka imfa.” Ndithudi, kunena mawu amenewo kunali kupereka thamo loyenera kwa mtumiki wodalirika wa Yehova Mulungu. Palibe thamo lokulirapo limene tingapereke kwa munthu aliyense kuposa kunena kuti anapambana chiyeso cha kukhulupirika, kuti anali wokhulupirika​—wokhulupirika ndi mtima wonse.

2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji kukhulupirika kuli kovuta? (b) Kodi ndani amene amatsutsa Akristu oona pakuyesayesa kwawo kukhala okhulupirika?

2 Kukhulupirika nkovuta. Chifukwa ninji? Chifukwa kukhulupirika kumawombana ndi kudzikonda. Pakati pa anthu osakhulupirika kwa Mulungu, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu ndiwo osakhulupirika koposa. Ndiyenonso, sipanayambe pakhala kusakhulupirika kofala konga komwe kuli mu ukwati lerolino. Chigololo chili ponseponse. Kusakhulupirika kulinso kowanda m’dziko la malonda. Za nkhaniyi, tikuuzidwa kuti: “Amanijala ambiri ndi akatswiri . . . amakhulupirira kuti ndi mbuli zokha ndi ogona amene amakhala okhulupirika ku makampani awo lerolino.” Anthu amene ali “okhulupirika konyanyitsa” amawanyoza. “Muyenera kukhala wokhulupirika kwa inu nokha osatinso kwa wina” anatero pulezidenti wa kampani yolangiza amanijala ndi kuwafunira antchito yoyang’anira. Kulankhula za kukhulupirika kulinga kwa munthu mwini ndiko kupotoza tanthauzo la liwulo. Kumatikumbutsa zimene Mika 7:2 amanena kuti: “Watha [wokhulupirika, NW] m’dziko.”

3 Pamlingo waukulu kwambiri, Satana ndi ziŵanda zake akutitsutsa, ali otsimikiza kutichititsa kukhala osakhulupirika kwa Mulungu. Nchifukwa chake pa Aefeso 6:12, NW, Akristu akuuzidwa kuti: “Tili nako kulimbana, osati ndi mwazi ndi thupi, koma ndi maboma, ndi maulamuliro, ndi olamulira a dzikoli a mdima uno, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” Inde, tifunika kulabadira chenjezo lakuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”​—1 Petro 5:8.

4. Kodi ndi zikhoterero ziti zimene zimapereka vuto pa kukhala wokhulupirika?

4 Chinanso chimene chimachititsa kukhulupirika kukhala kovuta ndicho zikhoterero zadyera zimene tinalandira kwa makolo athu, zimene zimatchulidwa pa Genesis 8:21 kuti: “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa”​—ndi yadyera​—“kuyambira pa unyamata wake.” Ife tonse tili ndi vuto limene mtumwi Paulo anati anali nalo: “Chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindifuna, chimenecho ndichichita.”​—Aroma 7:19.

Kukhulupirika ndi Chinthu Chapadera

5, 6. Kodi tinganenenji ponena za chimene chili kukhulupirika, ndipo kwamasuliridwa motani?

5 Liwu lakuti “kukhulupirika” nlapadera kwambiri. Chifukwa chake Insight on the Scriptures imati: “Zikuoneka ngati kuti kulibe mawu achingelezi amene amasonyeza ndendende tanthauzo lokwanira la mawu achihebri ndi achigiriki, koma ‘loyalty’ (kukhulupirika), limene limaphatikizapo lingaliro la kudzipereka ndi kudalirika, pamene ligwiritsiridwa ntchito kwa Mulungu ndi utumiki wake, limapereka tanthauzo lokwanira pang’ono.”a Ponena za “kukhulupirika,” Nsanja ya Olonda nthaŵi ina inati: “Kudalirika, ntchito, chikondi, thayo, kugonjera. Kodi mawuwa ali ndi chiyani chofanana? Iwo ali mbali zosiyanasiyana za kukhulupirika.” Inde, maubwino ambirimbiri angokhala mbali zosiyanasiyana za kukhulupirika. Ndipotu nthaŵi zimene Malemba amagwirizanitsa kukhulupirika ndi chilungamo zilidi zofunika kuzizindikira.

6 Othandizanso ndi matanthauzo otsatirawa: ‘Kukhulupirika kungasonyeze kudalirika ndi kugonjera kopitiriza ndi kothembeka, kuletsa kugwedera kapena kugonja pa chiyeso.’ ‘Kukhulupirika kumatanthauza kudalirika pamawu ako kapena kupitiriza kugonjera makonzedwe kapena mwambo umene wina aganiza kuti ali ndi thayo la kuutsatira malinga ndi chikhalidwe; liwulo silimangonena za kuumirira chinthu komanso za kukana kukopedwa ndi kunyengereredwa kusiya chinthu chimene waumirirapocho.’ Chotero, anthu amene amakhalabe odalirika ngakhale akuyesedwa, kutsutsidwa, ndi kuzunzidwa ayenerera kutchedwa “okhulupirika.”

7. Kodi tingasiyanitse motani kukhulupirika ndi kudalirika?

7 Komabe, pankhani imodzimodziyi, kungakhale bwino kufotokoza mwachitsanzo kusiyana kumene kungakhalepo pakati pa kukhulupirika ndi kudalirika. Kumadzulo kwa United States, kuli kasupe wa madzi otentha amene amatulutsa madzi pafupifupi ola lililonse. Amachita zimenezo nthaŵi zonse kwakuti watchedwa Old Faithful (Wodalirika Wakale). Baibulo limalankhula za zinthu zopanda moyo zotero monga mwezi kuti uli wodalirika, pakuti uli wothembeka. Salmo 89:37, NW, limati mwezi uli “mboni yodalirika m’thambo.” Mawu a Mulungu amanenedwa kukhala odalirika. Chivumbulutso 21:5 chimati: “Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali [odalirika, NW] ndi oona.” Zonsezi zili zodalirika, zothembeka, koma zilibe mtima woti nkukopeka ndi chinthu china kapena zilibe chikhalidwe, monga kukhulupirika.

Yehova, Wokhulupirika Wamkulukulu

8. Kodi ndi umboni wa m’Malemba uti umene ukudziŵikitsa chitsanzo chabwino koposa cha kukhulupirika?

8 Mosakayikira konse, Yehova Mulungu ali chitsanzo chabwino koposa cha kukhulupirika. Yehova wakhala wokhulupirika kwa fuko la anthu, kufika ndi pakupereka Mwana wake kuti anthu alandire moyo wosatha. (Yohane 3:16) Pa Yeremiya 3:12, timaŵerenga kuti: “Bwera iwe Israyeli wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang’anira iwe ndi kukwiya; pakuti ine ndili [wokhulupirika, NW].” Mawu enanso amene amachitira umboni kukhulupirika kwa Yehova ndi aja olembedwa pa Chivumbulutso 16:5 kuti: “Muli wolungama, amene muli, nimunali, [wokhulupirika, NW] Inu.” Ndiyenonso, pa Salmo 145:17, timauzidwa kuti: “Yehova ali wolungama m’njira zake zonse, ndi [wokhulupirika, NW] m’ntchito zake zonse.” Kwenikweni, Yehova ali wopambana kwambiri pa kukhulupirika kwake kwakuti Chivumbulutso 15:4 chimati: “Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu [Yehova]? Chifukwa inu nokha muli [wokhulupirika].” Yehova Mulungu ali wokhulupirika pamlingo woposa.

9, 10. Kodi ndi mbiri yotani ya kukhulupirika imene Yehova anapanga pochita ndi mtundu wa Israyeli?

9 Makamaka mbiri ya mtundu wa Israyeli ili ndi umboni wochuluka wa kukhulupirika kwa Yehova kulinga kwa anthu ake. M’masiku a Oweruza, Israyeli anapatuka pa kulambira koona nthaŵi ndi nthaŵi, koma Yehova mobwerezabwereza anachita naye chisoni nampulumutsa. (Oweruza 2:15-22) Pazaka zonse mazana asanu zimene Israyeli anali ndi mafumu, Yehova anasonyeza kukhulupirika kwake kulinga kwa mtunduwo.

10 Kukhulupirika kwa Yehova kunamchititsa kuleza nawo mtima anthu ake, malinga ndi kunena kwa 2 Mbiri 36:15, 16: “Yehova Mulungu wa makolo awo anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalaŵirira mamaŵa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake; koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.”

11. Kodi ndi chitsimikizo chotani kapena chitonthozo chimene kukhulupirika kwa Yehova kumatipatsa?

11 Chifukwa chakuti Yehova ali wokhulupirika koposa, mtumwi Paulo anatha kulemba zimene zili pa Aroma 8:38, 39 kuti: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Inde, Yehova akutilonjeza kuti: “Kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Ndithudi, nkotonthoza kudziŵa kuti Yehova Mulungu ali wokhulupirika nthaŵi zonse!

Yesu Kristu, Mwana Wokhulupirika

12, 13. Kodi tili ndi umboni wotani wonena za kukhulupirika kwa Mwana wa Mulungu?

12 Amene anatsanzira Yehova mwangwiro pakupambana chiyeso cha kukhulupirika anali ndipo akali Yesu Kristu. Moyenerera mtumwi Petro anatha kugwira mawu Salmo 16:10 naligwiritsira ntchito pa Yesu Kristu pa Machitidwe 2:27 kuti: “Simudzasiya moyo wanga ku Hade, kapena simudzapereka [wokhulupirika, NW] wanu aone chivund[i].” Yesu Kristu moyenerera akutchedwa “wokhulupirika.” Pazonse, iye ali wokhulupirika kwa Atate wake ndi ku Ufumu wolonjezedwa wa Mulungu. Poyamba Satana anayesa kuswa umphumphu wa Yesu mwa kugwiritsira ntchito ziyeso, zinthu zosonkhezera kudzikonda. Atalephera, Mdyerekezi anasintha nayamba kumzunza, potsirizira akumaphetsa Yesu pamtengo wopachikira. Yesu sanapatuke konse pa kukhulupirika kwake kwa Atate wake wakumwamba, Yehova Mulungu.​—Mateyu 4:1-11.

13 Yesu Kristu wakhala wokhulupirika kwa otsatira ake mwa kusunga lonjezo lolembedwa pa Mateyu 28:20 lakuti: “Onani, ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Kukwaniritsa lonjezo limenelo, iye wakhala akuchita utsogoleri mokhulupirika pa mpingo wake kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E. kufikira lero.

Anthu Opanda Ungwiro Amene Anali Okhulupirika

14. Kodi Yobu anapereka chitsanzo chotani cha kukhulupirika?

14 Nanga, bwanji za anthu opanda ungwiro? Kodi angakhale okhulupirika kwa Mulungu? Tili ndi chitsanzo chapadera cha Yobu. Satana anamveketsadi nkhaniyo ponena za iye. Kodi Yobu anali wokhulupirika kwa Yehova Mulungu, kapena anali kungomtumikira chifukwa cha kudzikonda kwake? Satana anadzimva kuti angathe kuchotsa Yobu kwa Yehova mwa kudzetsa mavuto pa Yobu. Yobu atataya chuma chake chonse, ana ake onse, ndipo ngakhale thanzi lake, mkazi wake anamlimbikitsa kuti: “Chitira Mulungu mwano, ufe.” Koma Yobu anali wokhulupirika, pakuti anati kwa iye: “Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwa ndi milomo yake.” (Yobu 2:9, 10) Kwenikweni, kwa omwe anafunikira kumtonthoza, Yobu anati: “Ngakhale ngati iye [Mulungu] andipha, ndidzamyembekezerabe.” (Yobu 13:15, New International Version) Nchifukwa chake Yobu anakhala ndi chiyanjo cha Yehova! Chifukwa chake, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani: “Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako aŵiri, pakuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.”​—Yobu 42:7, 10-16; Yakobo 5:11.

15. Kodi ndi umboni wotani wa m’Malemba umene tili nawo wonena za kukhulupirika kwa atumiki ambiri a Yehova Mulungu?

15 Amuna ndi akazi onse achikhulupiriro otchulidwa m’Ahebri chaputala 11 anganenedwe kuti anali okhulupirika. Sanali chabe odalirika komanso okhulupirika poyang’anizana ndi mavuto. Motero, timaŵerenga za iwo “amene mwa chikhulupiriro . . . anatseka pakamwa mikango, nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa . . . Ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m’ndende; anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osoŵa, osautsidwa, ochitidwa zoipa.”​—Ahebri 11:33-37.

16. Kodi ndi chitsanzo chotani cha kukhulupirika chimene mtumwi Paulo anapereka?

16 Malemba Achigiriki Achikristu amaperekanso chitsanzo chabwino cha mtumwi Paulo. Iye moyenerera anatha kunena kwa Akristu a ku Tesalonika za utumiki wake kuti: “Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala [okhulupirika, NW] ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira.” (1 Atesalonika 2:10) Tilinso ndi umboni wina wa kukhulupirika kwa Paulo wopezeka m’mawu ake olembedwa pa 2 Akorinto 6:4, 5, pamene timaŵerenga kuti: “M’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m’kupirira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja, m’mikwingwirima, m’ndende, m’mapokoso, m’mavutitso, m’madikiro, m’masalo a chakudya.” Zonsezi zimachitira umboni wakuti mtumwi Paulo anali ndi ulemu waumwini chifukwa anali wokhulupirika.

Okhulupirika m’Nthaŵi Zamakono

17. Kodi ndi mawu ati a J. F. Rutherford amene anasonyeza kuti anali wotsimikiza kukhala wokhulupirika?

17 M’nthaŵi zino zamakono, tili ndi chitsanzo chabwino chimene taona kale potsegulira nkhani ino. Tamverani zimene likunena buku lakuti Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere,” patsamba 146 pakamutu kakuti “Kukhulupirika Mkati mwa Nthaŵi ya Kuikidwa m’Ndende.” Pamenepo limati: “Kusonyeza kukhulupirika kugulu la Yehova mkati mwa nthaŵi ya kuikidwa kwake m’ndende, prezidenti wa Watch Tower Society, Joseph F. Rutherford, pa December 25, 1918, analemba zotsatirazi: ‘Chifukwa chakuti ndinakana kugonjera ku Babulo, koma ndinayesa mokhulupirika kutumikira Mbuye wanga, ndili m’ndende, chinthu chimene ndikuchiyamikira. . . . Ndithudi ndikasankha kuvomerezedwa ndi kuyanjidwa ndi Iye ndi kukhala m’ndende, kuposa kulolera molakwa kapena kugonjera ku Chirombo ndi kumasulidwa ndi kutamandidwa ndi dziko lonse.’”b

18, 19. Kodi ndi zitsanzo zabwino ziti za kukhulupirika m’nthaŵi zamakono zomwe tili nazo?

18 Tili ndi zitsanzo zabwino kwambiri za kukhulupirika za Akristu ena ambiri amene apirira chizunzo. Ena a anthu okhulupirika otero ndi Mboni za Yehova zachijeremani mu ulamuliro wa Nazi, monga momwe imasonyezera vidiyo yakuti Purple Triangles, yofalitsidwa kwambiri m’Chingelezi. Ndiponso zosaiŵalika ndi Mboni za Yehova zambiri zokhulupirika zachiafirika, monga zija za ku Malaŵi. Kumeneko, wosunga ndende wina anachitira umboni kukhulupirika kwa Mbonizo, kuti: “Samagonja konse. Amangowonjezeka.”

19 Munthu sangangoŵerenga ma Yearbook of Jehovah’s Witnesses aposachedwapa popanda kuchita chidwi ndi kukhulupirika kosonyezedwa ndi Akristu oona, monga aja a ku Greece, Mozambique, ndi Poland. Ambiri a iwo anazunzika koŵaŵa; ena anaphedwa. Patsamba 177 la 1992 Yearbook pali zithunzithunzi za amuna achikristu asanu ndi anayi a ku Ethiopia amene anapambana chiyeso cha kukhulupirika kufikira pakuphedwa. Monga Mboni za Yehova, kodi sitili okondwa kukhala ndi zitsanzo zabwino zambiri zotisonkhezera kupambana chiyeso cha kukhulupirika?

20. Kodi chidzatsatirapo nchiyani ngati tikhalabe okhulupirika?

20 Mwa kukaniza mokhulupirika ziyeso ndi zovuta, timakulitsa ulemu wathu waumwini. Chotero, kodi ndi kumbali yayani m’nkhani ya kukhulupirika kumene tifuna kupezekako? Mwa kupambana chiyeso cha kukhulupirika, timaima kumbali ya Yehova Mulungu m’nkhaniyo ndi kutsimikizira Satana Mdyerekezi kukhala wabodza woipa ndi wanjiru monga momwedi alili! Motero timapeza chiyanjo cha Mpangi wathu, Yehova Mulungu, ndi mphotho ya moyo wosatha wachimwemwe. (Salmo 37:29; 144:15b) Zimene zimafunika kuti munthu apambane chiyeso cha kukhulupirika zidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Insaikulopediya ya Baibulo ya mavoliyumu aŵiri yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji kukhala wokhulupirika kuli kovuta?

◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti liwu lakuti “kukhulupirika” lili lapadera kwambiri?

◻ Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Malemba zimene tili nazo za anthu opanda ungwiro omwe anali okhulupirika?

◻ Kodi ndi zitsanzo ziti zabwino zamakono za kukhulupirika zomwe tili nazo?

[Chithunzi patsamba 11]

Charles Taze Russell

[Chithunzi patsamba 12]

Yesu analidi “wokhulupirika” wa Yehova

[Chithunzi patsamba 13]

Yobu wopanda ungwiroyo, anakhulupirikabe kwa Mulungu

[Chithunzi patsamba 14]

Paulo anapereka chitsanzo chabwino cha kukhulupirika kwa Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena