OLENGEZA UFUMU AKUSIMBA
Mphamvu ya Kusintha ya Mawu a Mulungu
MWA kuvomereza kwa iye mwini, anali “wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe.” (1 Timoteo 1:13) Koma anasintha! Kusintha kwa mtumwi Paulo kunali kwakukuludi kwakuti pambuyo pake anakhoza kunena kuti: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.”—1 Akorinto 11:1.
Lerolino, olambira oona mtima zikwi mazana ambiri padziko lonse akupanga kusintha kofananako. Kodi nchiyani chimawatheketsa kutero? Iwo akukhala ndi chidziŵitso cha Mawu a Mulungu ndipo akuchigwiritsira ntchito m’moyo wawo. Chokumana nacho chotsatirapochi chikusonyeza mphamvu ya kusintha ya Mawu a Mulungu.
Ku Slovenia achikulire aŵiri okwatirana ankakhala okha kunja kwa mudzi. Mwamuna, Jože, anali ndi zaka pafupifupi 60 ndipo anali ndi vuto lalikulu la uchidakwa. Komabe, anasamalira mkazi wake wodwala, Ljudmila. Tsiku lina ofalitsa Ufumu aŵiri anafikira Jože. Iye anaitanira Mbonizo m’nyumba mwake, mmene anaonana ndi mkazi wake. Atamva uthenga wa Ufumu, Ljudmila anagwetsa misozi yachimwemwe. Nayenso Jože anasangalala ndi zimene anamva nafunsa mafunso ambiri. Atagaŵira mabuku ena ofotokoza Baibulo kwa okwatiranawa, Mbonizo zinapita.
Mwezi umodzi pambuyo pake Mbonizo zinabwererako, ndipo zinaona buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi pathebulo. Zitamfunsa kumene analichotsa, Jože anati: “Ndinaona akulisatsa patsamba la kumbuyo kwa amodzi a magazini amene munandisiyira. Motero ndinalembera ofesi yanu ku Zagreb kupempha bukulo.” Poona chikondwerero chake, zinamuitanira ku Chikumbutso cha imfa ya Kristu chimene chinali kudzachitidwa pa Nyumba ya Ufumu. Iye anabwera, ndipo Mbonizo zinakondwera!
Posapita nthaŵi anayamba phunziro la Baibulo, ndipo anapanga kupita patsogolo kwabwino. Mwachitsanzo, pamene Jože anasonyezedwa kuchokera m’Baibulo kuti “usadzipangire iwe wekha fano losema, . . . usazipembedzere izo, usazitumikire izo,” pomwepo anasonkhanitsa mafano achipembedzo onse amene anali m’nyumba, kuphatikizapo zithunzithunzi, nazitaya.—Eksodo 20:4, 5.
Ludzu la choonadi la Jože linali kukhutiritsidwa. Komabe, mwatsoka, anali adakali ndi ludzu lina. Kwa zaka 18, ankamwa malitala asanu ndi aŵiri a vinyo tsiku lililonse. Chifukwa cha vuto lake la kumwa, sankasamalira kwambiri za maonekedwe ake aumwini. Koma atadziŵa lingaliro la Mulungu pa kumwetsa zakumwa zaukali, anatsimikiza mtima za kusintha.
Anayesetsa kugonjetsa vuto lake lakumwa pang’onopang’ono, akumalemba unyinji wa vinyo amene ankamwa tsiku lililonse. Posapita nthaŵi sanalinso kapolo wa vinyo. Mkati mwa maphunziro ake a Baibulo, anaphunziranso kuti Akristu oona ayenera kukhala aukhondo. Motero, anapatsa Mbonizo ndalama nanena kuti: “Chabwino, mukandigulire zovala zilizonse zofunika kuti ndizioneka bwino pamisonkhano yachikristu ndi mu utumiki wakumunda!” Mbonizo zinabwera ndi zovala zamkati, masokosi, nsapato, mashati, masuti, mataye, ndi chikwama chamabuku.
Ataphunzira Baibulo kwa chaka chimodzi, Jože ndi Ljudmila anayeneretsedwa kupita m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba ndi Mboni. Miyezi itatu pambuyo pake anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Mosasamala kanthu za kukalamba ndi matenda, Jože anatenga mbali mokhazikika m’kulalikira uthenga wabwino ndipo pambuyo pake anatumikira mokhulupirika monga mtumiki wotumikira mumpingo kufikira imfa yake m’May 1995. Zipatso zabwino zotulutsidwa m’moyo wa mwamuna ndi mkazi wake odzichepetsawa zimapereka umboni wa mphamvu ya kusintha ya Mawu a Mulungu!