Kupereka Zake za Kaisara kwa Kaisara
“Perekani kwa anthu onse mangaŵa awo.”—AROMA 13:7.
1, 2. (a) Malinga ndi kunena kwa Yesu, kodi Akristu angalinganize motani mathayo awo a kwa Mulungu ndi a kwa Kaisara? (b) Kodi choyamba chimene Mboni za Yehova zimafuna nchiyani?
MALINGA ndi kunena kwa Yesu, tili ndi mangaŵa kwa Mulungu ndipo tilinso ndi mangaŵa kwa Kaisara, kapena Boma. Yesu anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” M’mawu ochepa ameneŵa, anazunguza adani ake ndipo anafotokoza bwinobwino mwachidule lingaliro loyenera limene tiyenera kukhala nalo pa unansi wathu ndi Mulungu ndi pa kuchita kwathu zinthu ndi Boma. Mposadabwitsa kuti omvetsera ake “anazizwa naye kwambiri.”—Marko 12:17.
2 Zoonadi, choyamba chimene atumiki a Yehova amafuna kuchita ndicho kupereka zake za Mulungu kwa Mulungu. (Salmo 116:12-14) Komabe, pochita zimenezo, samaiŵala kuti Yesu ananena kuti ayenera kupereka zinthu zina kwa Kaisara. Zikumbumtima zawo zophunzitsidwa Baibulo zimafuna kuti alingalire mwapemphero mlingo umene ayenera kuufikira popereka zimene Kaisara amafuna. (Aroma 13:7) M’nthaŵi zamakono, oweruza ambiri azindikira kuti mphamvu za boma zili ndi malire ndi kuti anthu ndi maboma kulikonse ali pansi pa lamulo lachibadwa.
3, 4. Kodi ndi ndemanga zokondweretsa zotani zimene zanenedwa ponena za lamulo lachibadwa, lamulo lovumbulidwa, ndi lamulo laumunthu?
3 Mtumwi Paulo anali kunena za lamulo lachibadwa limeneli pamene analemba za anthu a m’dziko kuti: “Chodziŵika cha Mulungu chaonekera mkati mwawo; pakuti Mulungu anachionetsera kwa iwo. Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu akuŵiringula.” Pamene alilabadira, lamulo lachibadwalo limasonkhezera osakhulupirira ameneŵa. Motero, Paulo anawonjezera kuti: “Pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo.”—Aroma 1:19, 20; 2:14, 15.
4 M’zaka za zana la 18, woweruza milandu wachingelezi wotchuka William Blackstone analemba kuti: “Lamulo lachibadwalo, pokhala ndi zaka zolingana ndi zimene munthu wakhalako ndiponso poperekedwa ndi Mulungu mwini, lilidi lamphamvu kuposa lina lililonse. Limalamulira padziko lonse, m’maiko onse, ndi panthaŵi zonse: malamulo alionse aumunthu amakhala osayenera, ngati awombana ndi limeneli.” Blackstone anapitiriza kunena za “lamulo lovumbulidwa,” lopezeka m’Baibulo, ndipo anati: “Pamalamulo aŵiri ameneŵa, lamulo lachibadwa ndi lamulo lovumbulidwa, pazikidwa malamulo onse a anthu; ndiko kuti, malamulo alionse a munthu sayenera kuloledwa kuwombana ndi ameneŵa.” Zimenezi nzogwirizana ndi zimene Yesu ananena ponena za Mulungu ndi Kaisara, monga momwe kwalembedwera pa Marko 12:17. Mwachionekere, pali mbali zimene Mulungu amaika malire pa zimene Kaisara angafune kwa Mkristu. Sanhedrin inadutsa malire amenewo pamene inalamula atumwi kuleka kulalikira za Yesu. Chifukwa chake, atumwiwo anayankha molondola kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:28, 29.
“Zake za Mulungu”
5, 6. Polingalira za kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu mu 1914, kodi Akristu ayenera kukumbukira kwambiri za chiyani? (b) Kodi Mkristu amapereka motani umboni wakuti iyeyo ndi mtumiki?
5 Makamaka kuyambira 1914, pamene Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, anayamba kulamulira monga mfumu kupyolera mu Ufumu Waumesiya wa Kristu, Akristu anafunikira kuonetsetsa kuti sakupereka zake za Mulungu kwa Kaisara. (Chivumbulutso 11:15, 17) Tsopano, kuposa ndi kalelonse, lamulo la Mulungu limafuna kuti Akristu ‘asakhale a dziko lapansi.’ (Yohane 17:16) Pokhala odzipatulira kwa Mulungu, Mpatsi wawo wa Moyo, ayenera kusonyeza bwino lomwe kuti sadzikhalira moyo iwo eni. (Salmo 100:2, 3) Paulo analemba kuti, “tikhala ake a [Yehova, NW].” (Aroma 14:8) Ndiponso, pa ubatizo wa Mkristu, iye amaikidwa kukhala mtumiki wa Mulungu, kuti athe kunena monga Paulo kuti: “Mulungu; . . . anatikwaniritsa ife tikhale atumiki.”—2 Akorinto 3:5, 6.
6 Mtumwi Paulo analembanso kuti: “Ndilemekeza utumiki wanga.” (Aroma 11:13) Ndithudi nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Kaya timakhala ndi phande mu utumiki wanthaŵi yonse kapena wapanthaŵi ndi nthaŵi, timakumbukira kuti Yehova mwiniyo anatipatsa utumiki. (2 Akorinto 2:17) Popeza kuti ena angakayikire za kaimidwe kathu, Mkristu aliyense wodzipatulira ndi wobatizidwa ayenera kukhala wokonzekera kupereka umboni womveka bwino ndi wotsimikizirika wakuti iye alidi mtumiki wa uthenga wabwino. (1 Petro 3:15) Utumiki wake uyeneranso kuonekera mwa khalidwe lake. Monga mtumiki wa Mulungu, Mkristu ayenera kuchirikiza ndi kusonyeza makhalidwe oyera, kuchirikiza umodzi wa banja, kukhala woona mtima, ndi kusasokoneza bata ndi mtendere. (Aroma 12:17, 18; 1 Atesalonika 5:15) Unansi wa Mkristu ndi Mulungu ndi utumiki wake wopatsidwa ndi Mulungu ndizo zinthu zofunika koposa m’moyo wake. Sayenera kulepa zimenezi chifukwa cholamulidwa ndi Kaisara. Mwachionekere, ziyenera kuŵerengeredwa kukhala pakati pa “zake za Mulungu.”
“Zake za Kaisara”
7. Kodi mbiri ya Mboni za Yehova njotani ponena za kukhoma misonkho?
7 Mboni za Yehova zimadziŵa kuti zili ndi mangaŵa a ‘kumvera maulamuliro aakulu,’ olamulira a maboma. (Aroma 13:1) Chifukwa chake, pamene Kaisara, Boma, lipereka mapempho oyenera, zikumbumtima zawo zophunzitsidwa Baibulo zimawalola kukwaniritsa mapempho ameneŵa. Mwachitsanzo, Akristu oona ali pakati pa anthu okhoma misonkho achitsanzo chabwino kwambiri padziko lapansi. Ku Germany nyuzipepala ya Münchner Merkur inati ponena za Mboni za Yehova: “Iwo ndiwo okhoma msonkho panthaŵi yake oona mtima koposa mu Federal Republic.” Ku Italy nyuzipepala ya La Stampa inati: “Iwo [Mboni za Yehova] ndiwo nzika zokhulupirika koposa zimene munthu angazifune: samazemba misonkho kapena kufuna kupeŵa malamulo ovuta kaamba ka phindu la iwo eni.” Atumiki a Yehova amachita zimenezi ‘chifukwa cha chikumbumtima chawo.’—Aroma 13:5, 6.
8. Kodi mangaŵa amene tili nawo kwa Kaisara ndi a ndalama za msonkho okha?
8 Kodi “zake za Kaisara” ndizo pa kukhoma misonkho chabe? Ayi. Paulo anandandalika zinthu zina, monga ngati kuwopa ndi ulemu. Mu Critical and Exegetical Hand-Book to the Gospel of Matthew yake, katswiri wachijeremani Heinrich Meyer analemba kuti: “Mwa kunena kuti [zake za Kaisara] . . . sitiyenera kungolingalira za msonkho wa boma, koma zonse zimene zili za Kaisara chifukwa cha ulamuliro wake wovomerezedwa.” Wolemba mbiri E. W. Barnes, m’buku lake lakuti The Rise of Christianity, ananena kuti Mkristu anali kukhoma msonkho pamene anafunikira kutero ndipo “mofananamo iye analandira mathayo ena onse a Boma, malinga ngati iye sanafunikire kupereka za Mulungu kwa Kaisara.”
9, 10. Kodi ndi chikayikiro chotani chimene Mkristu angakhale nacho ponena za kupereka zake za Kaisara, koma kodi ndi mfundo ziti zimene ayenera kukumbukira?
9 Kodi Boma lingafune zinthu zotani popanda kuloŵerera mu zinthu zimene zili za Mulungu? Ena alingalira kuti akhoza moyenerera kupatsa Kaisara ndalama monga misonkho ndipo osati kanthu kenanso. Iwo sangakhaledi omasuka kuti apereke kwa Kaisara kanthu kalikonse kamene kangadye nthaŵi imene angagwiritsire ntchito m’ntchito zateokrase. Komabe, pamene kuli kwakuti nzoona kuti tiyenera ‘kukonda [Yehova, NW] Mulungu wathu ndi mtima wathu wonse, ndi moyo wathu wonse, ndi nzeru zathu zonse, ndi mphamvu yathu yonse,’ Yehova amafuna kuti tipatule nthaŵi yochitanso zinthu zina m’malo mwa utumiki wathu chabe. (Marko 12:30; Afilipi 3:3) Mwachitsanzo, Mkristu amalangizidwa kupatula nthaŵi ya kukondweretsa mnzake wa muukwati. Ntchito zimenezo sizili zoipa, koma mtumwi Paulo akunena kuti izo zili “zinthu za dziko lapansi” osati “za Ambuye.”—1 Akorinto 7:32-34; yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:8.
10 Ndiponso, Kristu analamula otsatira ake ‘kupereka’ misonkho, ndipo ndithudi zimenezi zimaloŵetsamo kugwiritsira ntchito nthaŵi yopatuliridwa kwa Yehova—popeza kuti moyo wathu wonse uli wopatulidwa mwa njira imeneyi. Ngati avareji ya msonkho wa m’dziko ili 33 peresenti ya ndalama za munthu (njaikulu m’maiko ena), zimenezi zikutanthauza kuti chaka chilichonse wantchito wamba amapereka ku Thumba la Boma ndalama zokwanira malipiro ake a miyezi inayi. Mwa mawu ena, pamapeto a moyo wake wa kugwira ntchito, wantchito wamba amakhala atathera malipiro a zaka 15 pa ndalama za msonkho zimene “Kaisara” amafuna. Lingaliraninso nkhani ya maphunziro. M’maiko ochuluka lamulo limafuna kuti makolo apititse ana awo kusukulu kwa zaka zingapo. Chiŵerengero cha zaka za kuphunzira kusukulu chimasiyanasiyana m’maiko. M’malo ochuluka amafuna nthaŵi yaitali. Zoonadi, maphunziro amenewo kaŵirikaŵiri amakhala opindulitsa, koma Kaisara ndiye amene amasankha za mbali ya moyo wa mwana imene nthaŵi yake iyenera kutheredwa motere, ndipo makolo achikristu amachita mogwirizana ndi chosankha cha Kaisara.
Utumiki wa Nkhondo Woumiriza
11, 12. (a) Kodi Kaisara amafunanji m’maiko ambiri? (b) Kodi Akristu oyambirira anaona motani utumiki wa nkhondo?
11 China chimene Kaisara amafuna m’maiko ena ndicho kuchita utumiki wa nkhondo woumiriza. M’zaka za zana la 20, makonzedwe ameneŵa akhazikitsidwa m’maiko ochuluka m’nthaŵi ya nkhondo ndiponso ena m’nthaŵi za mtendere. Ku France thayo limeneli kwa zaka zambiri linatchedwa kuti msonkho wa mwazi, kutanthauza kuti mnyamata aliyense anafunikira kukonzekera kulepa moyo wake kaamba ka Boma. Kodi zimenezi ndizo zimene awo odzipatulira kwa Yehova angachite ndi chikumbumtima chabwino? Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anaona motani nkhaniyi?
12 Pamene kuli kwakuti Akristu oyambirira anayesayesa kukhala nzika zabwino, chikhulupiriro chawo chinawaletsa kupha munthu wina kapena kulepa moyo wawo kaamba ka Boma. The Encyclopedia of Religion ikuti: “Abambo a tchalitchi choyambirira, kuphatikizapo Tertullian ndi Origen, ananenetsa kuti Akristu analetsedwa kupha munthu, lamulo limene linawaletsa kukhala ndi phande m’gulu la nkhondo la Roma.” M’buku lake lakuti The Early Church and the World, Profesa C. J. Cadoux akulemba kuti: “Kufikira pa ulamuliro wa Marcus Aurelius pafupifupi [161-180 C.E.], panalibe Mkristu amene anakhala msilikali pambuyo pa ubatizo wake.”
13. Kodi nchifukwa ninji ochuluka m’Dziko Lachikristu samaona utumiki wa nkhondo monga momwe anachitira Akristu oyambirira?
13 Kodi nchifukwa ninji mamembala a matchalitchi a Dziko Lachikristu samaona zinthu mwanjira imeneyi lerolino? Chifukwa cha kusintha kwakukulu kumene kunachitika m’zaka za zana lachinayi. Buku lachikatolika lakuti A History of the Christian Councils likufotokoza kuti: “Akristu ambiri, . . . okhala pansi pa mafumu achikunja, anali ndi ziletso zachipembedzo kulinga ku utumiki wa nkhondo, ndipo anakana motsimikiza kunyamula zida, ndipo mwina anali kuthaŵa. Sinodi [ya Arles, imene inaliko mu 314 C.E.], pokambitsirana za masinthidwe amene Constantine anawayambitsa, inaika lamulo lakuti Akristu ayenera kutumikira mu nkhondo, . . . chifukwa chakuti Tchalitchi chili pamtendere (in pace) pansi pa kalonga waubwenzi kwa Akristu.” Monga chotulukapo cha kusiya ziphunzitso za Yesu kumeneku, kuyambira panthaŵi imeneyo kufikira tsopano, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu alimbikitsa magulu awo kutumikira m’magulu ankhondo a maiko, ngakhale kuti anthu ena akana chifukwa cha chikumbumtima.
14, 15. (a) Kodi Akristu a m’maiko ena amazika pati pempho la kukhuthulidwa kwawo pa utumiki wa nkhondo? (b) Kumene lamulo la kukhuthulidwa kulibe, kodi ndi mapulinsipulo a Malemba otani amene angathandize Mkristu kupanga chosankha cholondola pa nkhani ya utumiki wa nkhondo?
14 Kodi Akristu lerolino afunikira kutsata unyinji wa anthu pa nkhaniyi? Ayi. Ngati Mkristu wodzipatulira ndi wobatizidwa akukhala m’dziko limene atumiki achipembedzo amaloledwa kukhuthulidwa pa utumiki wa nkhondo, angagwiritsire ntchito makonzedwe ameneŵa, pakuti ndithudi iyeyo ndi mtumiki. (2 Timoteo 4:5) Maiko ambiri, kuphatikizapo United States ndi Australia, alola kukhuthula kumeneko ngakhale m’nthaŵi yankhondo. Ndipo m’nthaŵi yamtendere, m’maiko ambiri amene amachita utumiki wa nkhondo woumiriza, amalola kukhuthula Mboni za Yehova, monga atumiki a chipembedzo. Motero zimapitiriza kuthandiza anthu ndi utumiki wawo wapoyera.
15 Komabe, bwanji ngati Mkristu akukhala m’dziko limene atumiki achipembedzo samaloledwa kukhuthulidwako? Pamenepo iye afunikira kupanga chosankha chaumwini akumatsatira chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. (Agalatiya 6:5) Pamene akulingalira za ulamuliro wa Kaisara, afunikira kupenda mosamalitsa zimene zili zake za Yehova. (Salmo 36:9; 116:12-14; Machitidwe 17:28) Mkristuyo adzakumbukira kuti chizindikiro cha Mkristu woona ndicho kukonda okhulupirira anzake onse, ngakhale aja okhala m’maiko ena kapena aja amene ali a mafuko ena. (Yohane 13:34, 35; 1 Petro 2:17) Ndiponso, sadzaiŵala mapulinsipulo a Malemba opezeka m’mavesi onga Yesaya 2:2-4; Mateyu 26:52; Aroma 12:18; 14:19; 2 Akorinto 10:4; ndi Ahebri 12:14.
Utumiki wa m’Boma
16. M’maiko ena, kodi Kaisara amafuna utumiki wotani wosakhala wa nkhondo kwa awo amene amakana utumiki wa nkhondo?
16 Komabe, pali maiko aja mmene Boma, ngakhale kuti silimakhuthula atumiki achipembedzo pa zankhondo, limavomerezabe kuti anthu ena angakane utumiki wa nkhondo. Ambiri a maiko ameneŵa amapanga makonzedwe kaamba ka anthu okana amenewo kuti asaumirizidwe kuchita utumiki wa nkhondo. M’malo ena utumiki wa m’boma wofunika, monga ngati ntchito yothandiza m’chitaganya, simaonedwa kukhala utumiki wa nkhondo. Kodi Mkristu wodzipatulira angachite ntchito imeneyo? Pano kachiŵirinso, Mkristu wodzipatulira ndi wobatizidwa ayenera kupanga chosankha cha iye mwini pamaziko a chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo.
17. Kodi pali chitsanzo cha m’Baibulo cha kutumikira boma kosakhala kwa m’gulu la nkhondo?
17 Zichita ngati kuti utumiki woumiriza unachitidwa m’nthaŵi za Baibulo. Buku lina la mbiri likunena kuti: “Kuwonjezera pa misonkho ndi mangaŵa amene anafunidwa kwa nzika za Yudeya, panalinso thangata [ntchito yopanda malipiro imene boma linafuna]. Ameneŵa anali makonzedwe akale ku East, amene maboma a Ahelene ndi Aroma anapitiriza kutsata. . . . Chipangano Chatsopano, nachonso, chimatchula za thangata ku Yudeya, chikumasonyeza mmene linawandira. Chifukwa cha mwambo umenewu, asilikali anaumiriza Simoni wa ku Kurene kunyamula mtanda [mtengo wozunzirapo] wa Yesu (Mateyu 5:41; 27:32; Marko 15:21; Luka 23:26).”
18. Kodi Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimagwirizana nawo m’kuchita utumiki wotani wosakhala wa nkhondo, kapena wachipembedzo?
18 Mofananamo, m’maiko ena Boma kapena akuluakulu aboma kumaloko amafuna kuti nzika zikhale ndi phande m’mautumiki osiyanasiyana a m’chitaganya. Nthaŵi zina amafuna zimenezi kaamba ka ntchito ina yakutiyakuti, monga ngati kukumba zitsime kapena kumanga misewu; nthaŵi zina zimakhala zochitika zanthaŵi zonse, monga ngati kukhala ndi phande mlungu ndi mlungu m’kuyeretsa misewu, sukulu, kapena zipatala. Kumene mautumiki ameneŵa ali opindulitsa anthu ndipo saali ogwirizana ndi chipembedzo chonyenga kapena pamene saali otsutsidwa ndi chikumbumtima cha Mboni za Yehova m’njira ina, izo zawachita. (1 Petro 2:13-15) Kaŵirikaŵiri zimenezi zapereka umboni wabwino kwambiri ndipo nthaŵi zina zatontholetsa aja amene amanenera Mboni monama kuti nzotsutsa boma.—Yerekezerani ndi Mateyu 10:18.
19. Kodi Mkristu ayenera kuchita motani ngati Kaisara ampempha kuchita utumiki wa m’boma umene suli wa nkhondo kwa nyengo yakutiyakuti?
19 Komabe, bwanji ngati Boma lifuna kuti Mkristu achite utumiki wa m’boma kwa nyengo yakutiyakuti umene uli mbali ya utumiki wa m’boma pansi pa ofesi ya boma yosakhala ya gulu la nkhondo? Panonso Akristu ayenera kudzipangira chosankha chozikidwa pa chikumbumtima chozindikira bwino. “Ife tonse tidzaimirira ku mpando wakuweruza wa Mulungu.” (Aroma 14:10) Akristu amene akuyang’anizana ndi zofuna za Kaisara ayenera kupenda mwapemphero nkhaniyo ndi kuisinkhasinkha.a Kungakhale kwanzerunso kukambitsirana za nkhaniyo ndi Akristu aakulu msinkhu mumpingo. Zimenezi zitachitidwa munthu mwini ayenera kupanga chosankha.—Miyambo 2:1-5; Afilipi 4:5.
20. Kodi ndi mafunso otani ndi mapulinsipulo a Malemba amene amathandiza Mkristu kulingalira bwino nkhani ya utumiki wa m’boma umene suli wa nkhondo?
20 Pamene ali pakati pa kufufuza kumeneko, Akristu ayenera kulingalira za mapulinsipulo angapo a Baibulo. Paulo anati tiyenera ‘kugonjera kwa akulu, ndi aulamuliro, . . . okonzeka pantchito iliyonse yabwino; . . . kukhala aulere, ndi kuonetsa chifatso chonse pa anthu onse.’ (Tito 3:1, 2) Panthaŵi imodzimodziyo, Akristu angachite bwino kupenda utumiki wa m’boma wonenedwawo. Kodi iwo adzakhala okhoza kusunga uchete wawo wachikristu ngati awuvomereza? (Mika 4:3, 5; Yohane 17:16) Kodi udzawaloŵetsa m’chipembedzo china chonyenga? (Chivumbulutso 18:4, 20, 21) Kodi kuuchita kudzawaletsa kapena kuchepetsa kwambiri mwaŵi wa kukwaniritsa mathayo awo achikristu? (Mateyu 24:14; Ahebri 10:24, 25) Ndiponso, kodi adzatha kupitiriza kupanga kupita patsogolo kwauzimu, mwinamwake ngakhale kukhala ndi phande mu utumiki wanthaŵi yonse pamene akuchita ntchito yofunidwayo?—Ahebri 6:11, 12.
21. Mulimonse mmene angasankhire, kodi mpingo uyenera kuona motani mbale amene akukhudzidwa ndi nkhani ya utumiki wa m’boma umene suli wa nkhondo?
21 Bwanji ngati mayankho oona mtima a mafunso amenewo a Mkristu amchititsa kulingalira kuti utumiki wa m’bomawo ndi “ntchito yabwino” imene angaichite pomvera olamulira? Chimenecho nchosankha chake pamaso pa Yehova. Akulu oikidwa ndiponso ena ayenera kulemekeza kwambiri chikumbumtima cha mbaleyo ndi kupitiriza kumuona monga Mkristu wa kaimidwe kabwino. Komabe, ngati Mkristu wina alingalira kuti sangathe kuchita utumiki wa m’boma umenewu, kaimidwe kakeko kayeneranso kulemekezedwa. Nayenso ali ndi kaimidwe kabwino ndipo ayenera kuchirikizidwa mwachikondi.—1 Akorinto 10:29; 2 Akorinto 1:24; 1 Petro 3:16.
22. Kodi tidzapitiriza kuchitanji mu mkhalidwe uliwonse umene tingayang’anizane nawo?
22 Monga Akristu sitidzaleka kupereka “ulemu kwa eni ake a ulemu.” (Aroma 13:7) Sitidzasokoneza bata ndipo tidzafuna kukhala nzika zomvera lamulo, zamtendere. (Salmo 34:14) Tingapempherere ngakhale “mafumu ndi onse akuchita ulamuliro” pamene anthu ameneŵa afunikira kupanga zosankha zimene zimakhudza moyo ndi ntchito yathu yachikristu. Monga chotulukapo chake cha kupereka kwathu zake za Kaisara kwa Kaisara, tikukhulupirira kuti ‘m’moyo mwathu tingakhale odikha mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekezeka monse.’ (1 Timoteo 2:1, 2) Pa zonsezo, tidzapitiriza kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu monga chiyembekezo chokha cha anthu, tikumapereka zake za Mulungu kwa Mulungu ndi chikumbumtima chabwino.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 15, 1964, tsamba 308, ndime 21.
Kodi Mungalongosole?
◻ Polinganiza unansi wake pakati pa Kaisara ndi Yehova, kodi choyamba chimene Mkristu amafuna nchiyani?
◻ Kodi tili ndi mangaŵa otani kwa Yehova amene sitingapereke konse kwa Kaisara?
◻ Kodi ndi zinthu zina zotani zimene timapatsa moyenerera kwa Kaisara?
◻ Kodi ndi malemba ati amene amatithandiza kupanga chosankha cholondola pankhani ya utumiki wa nkhondo woumiriza?
◻ Kodi tiyenera kukumbukira mfundo zina ziti ngati tipemphedwa kuchita utumiki wa m’boma umene suli wa nkhondo?
◻ Kodi timapitiriza kuchitanji ponena za Yehova ndi Kaisara?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Atumwi anauza Sanhedrin kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu”