Olengeza Ufumu Akusimba
“Malamulo Anu Onse Ndiwo Choonadi”
KUTANGOTSALA pang’ono kuti afe, Mose analimbikitsa anthu a Israyeli kulabadira malamulo onse a Yehova. Iye anati: “Ikani mitima yanu pa mawu onse ndikuchitirani nawo mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mawu onse a chilamulo ichi. Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu.”—Deuteronomo 32:46, 47.
Zaka mazana ambiri pambuyo pake, wamasalmo anasonyeza kufunika kwa ziphunzitso zonse za Mulungu pamene anati: “Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi.” (Salmo 119:151) M’zaka za zana loyamba, Yesu iye mwini anatchula za “mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Ndipo motsogozedwa ndi Mulungu mtumwi Paulo analemba kuti “lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.”—2 Timoteo 3:16.
Mosakayikira, Yehova Mulungu amafuna kuti alambiri ake aone mwamphamvu uthenga wonse umene tapatsidwa m’masamba a Mawu ake kukhala wofunika. M’Baibulo mulibe mbali ngakhale imodzi yokha imene siili yofunika. Ndi mmene Mboni za Yehova zimaonera Mawu a Mulungu, monga momwe chochitika chotsatirapochi chochokera ku Mauritius chikusonyezera.
A D— ankakhala m’mudzi wina wakutali, kumene anali mlonda wausiku. Kwa nthaŵi yaitali, anakhala akufunafuna moona mtima njira yolondola yolambirira Mulungu. Usiku pamene anali kulonda, anayamba kuŵerenga Baibulo. M’kupita kwa nthaŵi anali ataliŵerenga kuchokera kuchikuto kufika kuchikuto. Iwo anaphunzira kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova—dzina limene limaonekera nthaŵi zambiri m’Baibulo lawo lachihindi. Anaona kuti buku la Chivumbulutso linali lokondweretsa mwapadera.
Ndiyeno anadzifunsa ngati panali chipembedzo chilichonse chimene chimatsatira Baibulo lonse lathunthu. Anaona kuti zipembedzo zimene ankadziŵa kwenikweni zinkangotsatira mbali zina za Baibulo. Zipembedzo zina zinalandira Malemba Achihebri ndi kukana Malemba Achigiriki Achikristu. Zipembedzo zina zinali kunyalanyaza Malemba Achihebri, zikumaona Malemba Achigiriki Achikristu okha kukhala ofunika kwambiri.
Tsiku lina a D— anaona okwatirana aŵiri akuvumbidwa ndi mvula nawaitana kudzabisala m’nyumba mwawo. Iwo anali Mboni za Yehova. Mkazi anali ndi buku la Revelation—Its Grand Climax At Hand!a Pomwepo a D— anawapempha bukulo. Mbonizo zinalingalira kuti nkhani za maulosi a Chivumbulutso zinali zakuya kwambiri kwa iwo, chotero anawagaŵira chofalitsa china m’malo mwake. Koma a D— analimbikira kuti akufuna buku la Revelation.
Pamene anapeza kopelo, anaŵerenga bukulo mofulumira. Ndiyeno anavomereza kumaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mosataya nthaŵi anakondwera ndi chenicheni chakuti Mboni zimalemekeza kwambiri Baibulo lonse lathunthu. Anayamba kufika pamisonkhano mokhazikika pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, kumene Malemba Achihebri ndi Malemba Achigiriki Achikristu omwe amaphunziridwa mosamalitsa. Tsopano iwo ali wolengeza Ufumu wobatizidwa wamumpingo wachikristu.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.