Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 6/1 tsamba 32
  • Simudzafuna Kuuphonya!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Simudzafuna Kuuphonya!
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mudzapezekako?
    Galamukani!—1996
  • Simungadzafune Kuuphonya!
    Galamukani!—2000
  • Tikukuitanani ku Msonkhano Wachigawo wa “Olengeza Ufumu Achangu”
    Galamukani!—2002
  • Kodi Mwakonzeka Kukapezekako?
    Galamukani!—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 6/1 tsamba 32

Simudzafuna Kuuphonya!

KUPHONYANJI? Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa Mboni za Yehova umene ukuyandikira mofulumira! M’malo ochuluka msonkhanowo udzayamba pa 9:30 Lachisanu mmaŵa ndi nyimbo zamalimba. Mutamvetsera ofunsidwa olimbitsa chikhulupiriro mu nkhani yakuti “Kumvetsera kwa Olengeza Mtendere Achangu,” mudzasangalala ndi nkhani yolimbikitsa yakuti “Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?”

Chinthu chapadera pa Lachisanu masana chidzakhala nkhani yaikulu yosonkhezera mtima yakuti “Mbali Yathu Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu.” Ndiyeno nkhani yakuti “Kuthandiza Ena Kudziŵa Zofuna za Mulungu” idzapereka malingaliro a mmene tingaphunzitsire atsopano. Zimenezi zidzatsatiridwa ndi nkhani yosiyirana yapanthaŵi yake yakuti “Chenjerani ndi Misampha Yobisika ya Zosangulutsa.” Programu ya Lachisanu idzamalizidwa ndi nkhani zakuti “Kanizani Mdyerekezi​—Chitani Nsanje” ndi “Kuchirikiza Mokhulupirika Kudalirika kwa Mawu a Mulungu.”

Programu ya pa Loŵeruka mmaŵa idzagogomezera kufunika kwa ntchito ya kupanga ophunzira m’nkhani ya mbali zitatu yosiyirana yakuti “Amithenga Obweretsa Uthenga Wabwino wa Mtendere.” Chigawocho chidzamalizidwa ndi nkhani zakuti “Kupereka Mokondwera m’Gulu la Yehova” ndi “Moyo ndi Mtendere mwa Kudzipatulira ndi Ubatizo,” imene pambuyo pake ophunzira atsopano adzakhala ndi mpata wa kubatizidwa.

Nkhani ya pa Loŵeruka masana yakuti “Lingalirani za Maganizo a Yehova pa Nkhani Zofunika” idzayankha mafunso onga akuti ‘Kodi Akristu ali ndi phande mu ntchito ya kulekanitsa lerolino?’ ndi ‘Kodi lingaliro la Baibulo pa chilango cha imfa nlotani?’ Mudzasangalalanso ndi nkhani ya mbali ziŵiri yosiyirana yakuti “Mulungu Wamtendere Amasamala za Inu” ndipo makamaka nkhani yomaliza yakuti “Londolani Mtendere Waumulungu m’Moyo wa Banja.”

Programu ya pa Lamlungu mmaŵa idzaphatikizapo nkhani ya mbali zitatu yosiyirana yakuti “Kudziŵa Mtundu Wabwino wa Amithenga” ndi nkhani yakuti “Mvetserani ndi Kumvera Mawu a Mulungu.” Programu ya mmaŵa idzamalizidwa ndi seŵero limene lidzapereka maphunziro ofunika m’nkhani ya Baibulo ya Woweruza Gideoni.

Gawo lomalizira la msonkhanowo pa Lamlungu masana lidzakhala ndi nkhani yapoyera, ya mutu wakuti “Mtendere Weniweni Potsirizira Pake!​—Kuchokera ku Magwero Ati?” Potsirizira pake, nkhani yosonkhezera mtima yakuti “Kupita Patsogolo Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu” idzatseka msonkhanowo.

Pangani makonzedwe tsopano kuti mudzakhalepo. Kuti mudziŵe za malo akufupi ndi kwanu, fikani pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kapena lemberani afalitsi a magazini ano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena