Kodi Mungathe Kumkondadi Mulungu?
“PALIBE munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo,” atero Mulungu. (Eksodo 33:20) Ndiponso, kuyambira m’nthaŵi za Baibulo kwakhala kulibe umboni wakuti munthu aliyense wakhala akulankhulana naye mwachindunji. Kodi sikumaoneka kukhala kovuta—ngakhale kosatheka—kukhala ndi chikondi chachikulu pa munthu wina amene simunaonepo kapena kumumva? Kodi kulidi kotheka kukhala ndi unansi wachikondi ndi Mlengi wa chilengedwe chonse?
Sitiyenera kukayikira konse kuti nkotheka kukhala ndi unansi wolimba waumwini ndi Mulungu. Pa Deuteronomo 6:5, timaŵerenga kuti mtundu wa Israyeli unalamulidwa kuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” Pambuyo pake Yesu Kristu anabwerezanso lamuloli kwa otsatira ake nawonjezera kuti: “Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba.” (Mateyu 22:37, 38) Kodi Baibulo likanatilimbikitsa kukonda Mulungu ngati unansi wotero unali wosatheka?
Koma kodi Yehova amayembekezera ife kumkonda chabe chifukwa chakuti iye amatilamula kutero? Iyayi. Mulungu analenga anthu aŵiri oyamba ndi mphamvu ya kumkonda. Adamu ndi Hava sanakakamizidwe kukhala ndi unansi wachikondi ndi Mlengi wawo. M’malo mwake, Mulungu anawaika m’malo abwino amene iwo akanakulitsiramo chikondi chachikulu pa iye. Iwo anayenera kusankha—kuyandikira kwa Mulungu kapena kuchoka kwa iye.
Adamu ndi Hava anasankha kupanduka. (Genesis 2:16, 17; 3:6, 7) Komabe, mbadwa zawo zikanatha kukulitsa unansi wachikondi ndi Mlengi.
Kuyenda ndi Mulungu Woona
Mwachitsanzo, m’Baibulo, Abrahamu amatchedwa “bwenzi” la Mulungu. (Yakobo 2:23) Komanso Abrahamu sindiye yekha amene anali ndi unansi wapafupi ndi Mulungu. Baibulo limatchula anthu ena ambiri opanda ungwiro amene anasonyeza chikondi chenicheni kwa Yehova ndipo “anayendabe ndi Mulungu.”—Genesis 5:24; 6:9; Yobu 29:4; Salmo 25:14; Miyambo 3:32.
Atumiki akale a Mulungu sanabadwe ali ndi chikondi pa Mulungu. Anachita kuchikulitsa. Motani? Mwa kumdziŵa iye ndi dzina lake, Yehova. (Eksodo 3:13-15; 6:2, 3) Mwa kuzindikira kukhalapo kwake ndi Umulungu wake. (Ahebri 11:6) Mwa kusinkhasinkha nthaŵi zonse pa zochita zake zachikondi. (Salmo 63:6) Mwa kumuuza Mulungu m’pemphero zolingilira za mtima wawo. (Salmo 39:12) Mwa kuphunzira za ukoma wake. (Zekariya 9:17) Mwa kukulitsa mantha oyenera a kusamkwiyitsa.—Miyambo 16:6.
Kodi mungakhale bwenzi la Mulungu ndi kuyenda naye? Zoona, simutha kuona Mulungu kapena kumva liwu lake. Chikhalirechobe, Yehova akukupemphani ‘[kukhala mlendo, NW] m’chihema chake,’ kukhala bwenzi lake. (Salmo 15:1-5) Chotero, nkotheka kwa inu kumkonda Mulungu. Koma kodi mungakhale naye motani paunansi wapafupi ndi wachikondi?