Kuuluka Pamwamba ndi Mapiko Monga Ziombankhanga
KODI munthu amamva bwanji pambuyo pa kupirira kwa zaka zisanu m’misasa yachibalo ya Nazi? Wotaya mtima? Waudani? Wofuna kubwezera?
Ngakhale kuti zingaoneke kukhala zachilendo, mwamuna wina wotere analemba kuti: “Moyo wanga unalemeretsedwa kuposa ndi mmene ndikanayembekezera ndi kale lonse.” Kodi nchifukwa ninji anamva motero? Anafotokoza kuti: “Ndinapeza pobisalira pansi pa mapiko a Wammwambamwamba, ndipo ndinaona kukwaniritsidwa kwa mawu a mneneri Yesaya, pamene anati: ‘Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; . . . adzayenda koma osalefuka.’”—Yesaya 40:31.
Mwamuna wachikristu ameneyu, amene anazunzika ndi nkhanza yoipa koposa, anali ndi mzimu umene unakwera kumka pamwamba mophiphiritsira, mzimu umene nkhanza za Nazi sizinagonjetse. Monga Davide iye anapeza pobisalira mumthunzi wa “mapiko” a Mulungu. (Salmo 57:1) Mkristu ameneyu anagwiritsira ntchito kuyerekezera kumene mneneri Yesaya anagwiritsira ntchito, akumayerekezera nyonga yake yauzimu ndi ija ya chiombankhanga chimene chimauluka kumkabe pamwamba mumlengalenga.
Kodi nthaŵi zina mumamva kukhala wolefulidwa ndi mavuto? Mosakayikira inunso mungafune kupeza pobisalira pansi pa mapiko a Wammwambamwamba, ‘kuuluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga.’ Kuti mumvetsetse mmene zimenezi zilili zotheka, kuli bwino kudziŵa zinthu zina ponena za chiombankhanga, chimene kaŵirikaŵiri m’Malemba chimagwiritsiridwa ntchito mophiphiritsira.
Pansi pa Mbendera Yachiombankhanga
Pakati pa mbalame zonse zimene anthu akale anapenyerera, mwinamwake chiombankhanga ndicho chimene ankakonda kwambiri chifukwa cha mphamvu yake ndi kuuluka kwake kochititsa chidwi. Magulu a nkhondo ambiri akale, kuphatikizapo aja a Babulo, Aperisi, ndi Roma, anayenda pansi pa mbendera yokhala ndi chiombankhanga. Gulu la nkhondo la Koresi Wamkulu linali limodzi la ameneŵa. Baibulo linalosera kuti mfumu ya Aperisi imeneyi idzakhala ngati mbalame yolusa yochokera kummaŵa kudzalikwira Ufumu wa Babulo. (Yesaya 45:1; 46:11) Zaka mazana aŵiri ulosiwu utalembedwa, asilikali a Koresi, amene anali ndi ziombankhanga pa mbendera zawo zankhondo, anakupa mzinda wa Babulo monga chiombankhanga chimene chikumbwandira nyama yake.
Chaposachedwapa, ankhondo monga Charlemagne ndi Napoleon ndi maiko monga United States ndi Germany nawonso asankha chiombankhanga kukhala chizindikiro chawo. Aisrayeli analamulidwa kusalambira mafano a ziombankhanga kapena a cholengedwa china chilichonse. (Exodus 20:4, 5) Komabe, olemba Baibulo anasonya ku makhalidwe a chiombankhanga pofotokoza uthenga wawo mwafanizo. Motero chiombankhanga, mbalame yotchulidwa koposa m’Malemba, ikugwiritsiridwa ntchito kuimira zinthu izi monga nzeru, chitetezo chaumulungu, ndi liŵiro.
Diso la Chiombankhanga
Maso akuthwa a chiombankhanga akhala odziŵika kwambiri nthaŵi zonse. Ngakhale kuti chiombankhanga chotchedwa golden eagle kaŵirikaŵiri sichimalemera makilogalamu asanu, diso lake kwenikweni nlalikulu kuposa la munthu, ndipo kapenyedwe kake nkakuthwa koposa. Yehova iye mwini, pofotokozera Yobu kukhoza kwa chiombankhanga kufunafuna chakudya chake, anati: “Maso ake achipenyetsetsa chili kutali.” (Yobu 39:27, 29) Alice Parmelee, m’buku lake lakuti All the Birds of the Bible, akunena kuti “nthaŵi ina chiombankhanga chinaona nsomba yakufa ili kuyandama panyanja makilomita asanu kuchokera kumene chinali ndipo chinacholima kupita pamalo enieniwo. Chiombankhangacho sichinangotha kuona kanthu kakang’ono pamtunda wautali kwambiri kuposa mmene munthu angachitire, koma mbalameyo inayang’anabe nsombayo mosalekeza pakuulukira pansi kwakeko pamtunda wa makilomita asanu.”
Chifukwa cha kuthwa kwa maso ake, chiombankhanga nchizindikiro choyenera cha nzeru, imodzi ya mikhalidwe yaikulu ya Yehova. (Yerekezerani ndi Ezekieli 1:10; Chivumbulutso 4:7.) Nchifukwa ninji zili choncho? Nzeru zimaloŵetsamo kuoneratu zotulukapo za chilichonse chimene tingachite. (Miyambo 22:3) Chiombankhanga, ndi kukhoza kwake kuona zimene zili pamtunda wautali, chingaone ngozi ikali kutali ndi kuchitapo kanthu kuti chidzitetezere, mongadi mwamuna wochenjera m’fanizo la Yesu, amene anadziŵiratu kuti mphepo zingaombe namanga nyumba yake pathanthwe. (Mateyu 7:24, 25) Chokondweretsa nchakuti m’Chispanya, kunena wina kuti ndi chiombankhanga kumatanthauza kuti ali ndi chidziŵitso kapena kuzindikira.
Ngati mudzakhalapo ndi mwaŵi wa kuona chiombankhanga pafupi kwambiri, mukapenyetsetse mmene chimagwiritsira ntchito maso ake. Sichimakuyang’anani kwa kanthaŵi; m’malo mwake, chimaoneka kuti chikusanthula maonekedwe anu mosamalitsa. Mofananamo, munthu wanzeru amasanthula nkhani iliyonse mosamalitsa asanapange chosankha m’malo mwa kudalira pa nzeru zake zachibadwa kapena malingaliro ake. (Miyambo 28:26) Pamene kuli kwakuti maso akuthwa a chiombankhanga amachipangitsa kukhala chizindikiro chabwino cha mkhalidwe wa Mulungu wa nzeru, olemba Baibulo anagwiritsiranso ntchito mophiphiritsira kuuluka kwake kochititsa chidwi.
“Njira ya Chiombankhanga m’Mlengalenga”
“Njira ya [chiombankhanga, NW] m’mlengalenga” njodabwitsa kaamba ka liŵiro lake ndi mmenenso chimaonekera kuti chikuuluka popanda kuyesayesa kwenikweni, chikumalondola njira yosaoneka ndi kusasiya zizindikiro zilizonse kumbuyo. (Miyambo 30:19) Liŵiro la chiombankhanga likutchulidwa pa Maliro 4:19, pamene asilikali a Babulo akufotokozedwa kuti: “Otilondola anaposa ziombankhanga za m’mlengalenga m’liŵiro lawo, anatithamangitsa pamapiri.” Pamene chiombankhanga chimene chikuuluka pamwamba chiona nyama yake, chimapinda mapiko ake ndi kuulukira pansi, ndipo chikamatero chingafike pa liŵiro la makilomita 130 pa ola limodzi, malinga ndi nkhani zina. Mosadabwitsa, Malemba amagwiritsira ntchito chiombankhanga monga chizindikiro cha liŵiro, makamaka ponena za gulu la asilikali.—2 Samueli 1:23; Yeremiya 4:13; 49:22.
Komabe, Yesaya akutchula za kuuluka kosavutika kwa chiombankhanga. “Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” (Yesaya 40:31) Kodi chinsinsi cha kuuluka koyandama kwa chiombankhanga nchiyani? Kuuluka sikumafuna mphamvu kwambiri popeza chiombankhanga chimagwiritsira ntchito mpweya wotentha womakwera kupita pamwamba. Mpweya umenewu sumaoneka, koma chiombankhanga chimadziŵa bwino kwambiri moupezera. Chitaupeza, chiombankhanga chimatambasula mapiko ake ndi chipsera chake nichimazungulira mumpweya wotentha umenewo, umene umapititsa chiombankhangacho pamwamba kwambiri. Pamene ufika polekezera pake, icho chimaulukira ku mpweya winanso wotentha, kumene chimachitanso chimodzimodzi. Mwa kuchita zimenezi chiombankhanga chingakhale m’mwamba kwa maola ambiri mosataya nyonga yochuluka.
Ku Israyeli, makamaka mu Rift Valley (Chigwa Chocholima) chimene chimachokera ku Ezion-geber ku gombe la Nyanja Yofiira kufika kumpoto ku Dan, ziombankhanga zimaonekaoneka. Izo zimachuluka kwambiri makamaka m’ngululu ndi posakasa pamene zimasamuka. M’zaka zina ziombankhanga pafupifupi 100,000 zaŵerengedwa. Mmaŵa pamene dzuŵa liyamba kufunda, mbalame zolusa zimenezi mazana zimaoneka zikuuluka pamwamba pa mapiri amene ali m’mbali mwa Rift Valley.
Kuuluka kosavutika kwa chiombankhanga kuli fanizo labwino kwambiri la mmene nyonga ya Yehova ingatitukulire mwauzimu ndi mwamaganizo kotero kuti tipitirize ndi ntchito yathu. Mongadi mmene chiombankhanga sichingauluke kufika pamwamba potero chikumagwiritsira ntchito nyonga yake, sitingalimbike ngati tidalira pa mphamvu zathu. “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo,” anafotokoza motero mtumwi Paulo. (Afilipi 4:13) Monga chiombankhanga chimene mosalekeza chimafunafuna mpweya wotentha wosaonekawo, ‘timapitirizabe kupempha’ mphamvu yogwira ntchito yosaonekayo ya Yehova mwa mapemphero athu ochokera pansi pa mtima.—Luka 11:9, 13.
Kaŵirikaŵiri ziombankhanga zimene zikusamuka zimapeza mpweya wotenthaŵo mwa kuyang’ana mbalame zina zolusa. Katswiri wa zinthu zachilengedwe D. R. Mackintosh ananena kuti panthaŵi ina ziombankhanga ndi miimba 250 zinaonedwa zikuzungulira kupita pamwamba mumpweya wotentha umodzimodzi. Mofananamo Akristu lerolino angaphunzire kudalira nyonga ya Yehova mwa kutsanzira zitsanzo zokhulupirika za atumiki ena owopa Mulungu.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 11:1.
Mumthunzi wa Mapiko a Chiombankhanga
Imodzi yanthaŵi zangozi kwambiri m’moyo wa chiombankhanga ndiyo pamene chikuphunzira kuuluka. Ziombankhanga zambiri zimafa poyesa kutero. Mtundu wa Israyeli wosakhwimawo unalinso pangozi pamene unachoka ku Igupto. Motero mawu a Yehova kwa Aisrayeli anali apanthaŵi yakedi pamene anati: “Inu munaona chimene ndinachitira Aaigupto; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a [chiombankhanga, NW], ndi kubwera nanu kwa ine ndekha.” (Eksodo 19:4) Pali nkhani zakuti ziombankhanga zabereka mbalame yochepayo kwa kanthaŵi kotero kuti isagwe pa kuyesa kwake kuuluka nthaŵi yoyamba. Pothirira ndemanga pankhani zotere mu Palestine Exploration Quarterly, G. R. Driver anati: “Motero chithunzicho [cha m’Baibulo] sindicho kuuluka kongopeka koma nchozikidwa pa zenizeni.”
Ziombankhanga ndi makolo achitsanzo chabwinonso m’zinthu zina. Sizimangopatsa ana awo zakudya nthaŵi zonse komanso mayi amanyenya nyama bwinobwino imene tate amabweretsa ku chisa kuti chiombankhanga chaching’onocho chidye. Popeza zisa zawo kaŵirikaŵiri zimamangidwa pamwamba penipeni pamapiri kapena m’mitengo yaitali, mbalame zazing’onozo zimayang’anizana ndi machedwe osiyanasiyana. (Yobu 39:27, 28) Dzuŵa lotentha, limene limakhala ku maiko a Baibulo, lingaphe mbalame yaing’onoyo ngati makolo ake saisamalira. Chiombankhanga chokhwima chimatambasula mapiko ake, nthaŵi zina kwa maola ambiri panthaŵi imodzi, kuti chichite mthunzi pa mwana wake wosakhwimayo.
Chifukwa cha zimenezi nkoyenerera kwambiri kuti m’Malemba mapiko a chiombankhanga amagwiritsiridwa ntchito monga chizindikiro cha chitetezo chaumulungu. Deuteronomo 32:9-12 amafotokoza mmene Yehova anatetezerera Aisrayeli pa ulendo wawo wa m’chipululu pamene amati: “Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa choloŵa chake. Anampeza m’dziko la mabwinja, ndi m’chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m’diso; monga [chiombankhanga, NW] [ch]ikasula chisa chake, ni[chi]kapakapa pa ana ake, [nichitambasula mapiko ake, nichiwatenga, ndi kuwanyamula, NW] pa mapiko ake; Yehova yekha anamtsogolera.” Yehova adzatipatsanso chitetezo chachikondi chimodzimodzicho ngati timdalira.
Njira Yothaŵiramo
Nthaŵi zina pamene tayang’anizana ndi mavuto, timalingalira kuti bwenzi tikanathaŵa mavuto athu onse. Davide analingaliranso motero. (Yerekezerani ndi Salmo 55:6, 7.) Koma ngakhale kuti Yehova walonjeza kutithandiza pamene tikuyang’anizana ndi ziyeso ndi kuvutika m’dongosolo lino, iye samathetseratu mavuto onse. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.”—1 Akorinto 10:13.
“Populumukira” kapena “njira yothaŵiramo” (King James Version) imaphatikizapo kuphunzira kudalira Yehova. Izi nzimene Max Liebster anapeza, amene ndemanga zake zagwidwa mawu pachiyambi pa nkhaniyi. Pazaka zake za m’misasa yachibalo, anadziŵa Yehova ndi kumdalira. Monga momwe Max anapezera, Yehova amatilimbitsa kupyolera mwa Mawu ake, mzimu wake, ndi gulu lake. Ngakhale m’misasayo, Mboni zinafunafuna okhulupirira anzawo ndi kuwapatsa thandizo lauzimu, kugaŵana nawo malingaliro a Malemba ndi mabuku alionse ofotokoza Baibulo amene analipo. Ndipo monga momwe opulumuka okhulupirika achitira umboni nthaŵi ndi nthaŵi, Yehova anawalimbitsadi. “Nthaŵi zonse ndinapempha Yehova kundithandiza,” akufotokoza motero Max, “ndipo mzimu wake unandichirikiza.”
Chiyeso chilichonse chimene tingakumane nacho, tingadalirenso mzimu woyera wa Mulungu, malinga ngati tipitirizabe kuupempha. (Mateyu 7:7-11) Titapatsidwa nyonga ndi “ukulu woposa wamphamvu” umenewu, tidzauluka pamwamba m’malo mothedwa mphamvu ndi mavuto athu. Tidzayendabe m’njira ya Yehova, ndipo sitidzalema. Tidzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga.—2 Akorinto 4:7; Yesaya 40:31.
[Mawu Otsindika patsamba 10]
Sichimakuyang’anani kwa kanthaŵi
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Chithunzithunzi: Cortesía de GREFA
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Chithunzithunzi: Cortesía de Zoo de Madrid