Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 8/1 tsamba 15-20
  • “Khalani Inunso Oyera Mtima m’Makhalidwe anu Onse”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Khalani Inunso Oyera Mtima m’Makhalidwe anu Onse”
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo Woyera, Mtengo Woyera
  • Khalidwe Loyera m’Banja
  • Chiyero ndi Apabanja Lathu Osakhulupirira
  • Kodi Tingakhale Motani Oyera Mumpingo?
  • Kodi Chiyero Chathu Chimaonekera Kumalo Kumene Timakhala?
  • Chiyero Kuntchito ndi Kusukulu
  • ‘Muyenera Kukhala Oyera Pakuti Ine Ndine Woyera’
    Nsanja ya Olonda—1996
  • “Woyera, Woyera, Woyera Ndi Yehova”
    Yandikirani Yehova
  • “Mukhale Oyera”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Khalani ‘Oyera Poopa Mulungu’
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 8/1 tsamba 15-20

“Khalani Inunso Oyera Mtima m’Makhalidwe anu Onse”

“Monga Iye wakuitana inu ali Woyera Mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.”​—1 PETRO 1:15, 16.

1. Kodi nchifukwa ninji Petro analimbikitsa Akristu kukhala oyera?

KODI nchifukwa ninji mtumwi Petro anapereka uphungu uli pamwambawu? Chifukwa anaona kufunika kwa Mkristu aliyense kutetezera malingaliro ake ndi zochita kuti zikhale zogwirizana ndi chiyero cha Yehova. Chifukwa chake, asanatchule mawu ali pamwambawo, anati: ‘Dzimangeni m’chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga . . . monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziŵa inu.’​—1 Petro 1:13, 14.

2. Kodi nchifukwa ninji zilakolako zathu zinali zopanda chiyero tisanaphunzire choonadi?

2 Zilakolako zathu zakale zinali zopanda chiyero. Chifukwa? Chifukwa ambiri a ife tinatsatira njira ya dziko yochitira zinthu tisanalandire choonadi chachikristu. Petro anadziŵa zimenezi pamene analemba momveka kuti: “Nthaŵi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka.” Inde, Petro sanatchule machitachita odetsa a m’dziko lathu lamakono, pakuti panthaŵiyo anali osadziŵika.​—1 Petro 4:3, 4.

3, 4. (a) Kodi tingalimbane nazo motani zilakolako zolakwa? (b) Kodi Akristu ayenera kupondereza mtima? Fotokozani.

3 Kodi mwaona kuti zilakolako zimenezi ndi zija zimene zimasangalatsa thupi, maganizo, ndi mtima? Pamene tizilola kutilamulira, pamenepo malingaliro athu ndi zochita zathu zimakhala zopanda chiyero mosavuta. Zimenezi zikusonyeza kufunika kwake kwakuti mphamvu ya kulingalira izilamulira zochita zathu. Paulo anafotokoza zimenezi motere: “Chifukwa chake ndikupemphani abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu ya kulingalira.”​—Aroma 12:1, 2, NW.

4 Kuti tipereke kwa Mulungu nsembe yoyera, tiyenera kulola mphamvu ya kulingalira kutilamulira m’malo mwa mtima. Ndi anthu ochuluka chotani nanga amene agwera m’chisembwere chifukwa chakuti analola zikhumbo zawo kulamulira khalidwe lawo! Zimenezi sizikutanthauza kuti tiyenera kupondereza mtima wathu; chifukwa ngati tatero, tingasonyeze bwanji chimwemwe mu utumiki wa Yehova? Komabe, ngati tifuna kutulutsa zipatso za mzimu m’malo mwa ntchito za thupi, pamenepo tisandulize maganizo athu kuti agwirizane ndi kalingaliridwe ka Kristu.​—Agalatiya 5:22, 23; Afilipi 2:5.

Moyo Woyera, Mtengo Woyera

5. Kodi nchifukwa ninji Petro anaona kufunika kwa chiyero?

5 Kodi nchifukwa ninji Petro anaona kufunika kwake kwa chiyero chachikristu? Chifukwa anali kuudziŵa bwino lomwe mtengo woyera umene unaperekedwa kuombola anthu omvera. Analemba kuti: “Podziŵa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golidi ndi siliva, kusiyana nawo makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu.” (1 Petro 1:18, 19) Inde, Magwero a chiyero, Yehova Mulungu, anatumiza Mwana wake wobadwa yekha, “Woyera,” ku dziko lapansi kupereka dipo limene lidzalola anthu kukhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu.​—Yohane 3:16; 6:69; Eksodo 28:36; Mateyu 20:28.

6. (a) Kodi nchifukwa ninji si kwapafupi kwa ife kulondola khalidwe loyera? (b) Kodi nchiyani chingatithandize kusunga khalidwe lathu loyera?

6 Komabe, tiyenera kudziŵa kuti kuli kovuta kukhala ndi moyo woyera pamene tili pakati pa dziko loipa la Satana. Iye amatchera misampha Akristu oona, amene akuyesa kupirira m’dongosolo lake la zinthu. (Aefeso 6:12; 1 Timoteo 6:9, 10) Zipsinjo za kuntchito, za chitsutso cha banja, za kusekedwa kusukulu, ndi za chisonkhezero cha mabwenzi zimafuna mkhalidwe wauzimu wolimba kuti tisunge chiyero chathu. Zimenezo zikusonyeza kufunika kwake kwa phunziro lathu laumwini ndi kupezeka kwathu pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse. Paulo analangiza Timoteo kuti: “Gwira chitsanzo cha mawu a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 1:13) Timamva mawu opatsa moyo amenewo ku Nyumba yathu ya Ufumu ndi paphunziro lathu laumwini la Baibulo. Angatithandize kukhala oyera m’khalidwe lathu tsiku ndi tsiku m’mikhalidwe yambiri yosiyanasiyana.

Khalidwe Loyera m’Banja

7. Kodi chiyero chiyenera kukhudza motani moyo wathu wa banja?

7 Pamene Petro anagwira mawu Levitiko 11:44, anagwiritsira ntchito liwu lachigiriki haʹgi·os, lotanthauza “cholekana ndi tchimo ndipo motero chopatuliridwa kwa Mulungu, chopatulika.” (An Expository Dictionary of New Testament Words, lolembedwa ndi W. E. Vine) Kodi zimenezi ziyenera kutikhudza motani m’moyo wathu wa banja monga Akristu? Kwenikweni zikutanthauza kuti moyo wathu wa banja uyenera kuzikidwa pa chikondi, pakuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Chikondi chodzimana ndicho mafuta amene amafeŵetsa maunansi pakati pa okwatirana ndi pakati pa makolo ndi ana.​—1 Akorinto 13:4-8; Aefeso 5:28, 29, 33; 6:4; Akolose 3:18, 21.

8, 9. (a) Kodi ndi mkhalidwe wotani umene nthaŵi zina umakhalapo m’banja lachikristu? (b) Kodi ndi uphungu wabwino wotani umene Baibulo limapereka pankhaniyi?

8 Tingaganize kuti kusonyeza chikondi chotero kumangochitika mwachibadwa m’banja lachikristu. Komabe, tiyenera kuvomereza kuti chikondi nthaŵi zina sichimafunga m’mabanja ena achikristu pamlingo wofunika. Kungaoneke kuti chimasonyezedwa pa Nyumba ya Ufumu, koma chiyero chathu chikhoza kuzimiririka mosavuta kunyumba. Pamenepo tingaiŵale mwamsanga kuti mkazi akali mlongo wathu wachikristu kapena kuti mwamuna akali mbale uja (ndipo mwinamwake mtumiki wotumikira kapena mkulu) amene ku Nyumba ya Ufumu anali kuoneka kuti timamlemekeza. Timapsa mtima, ndipo pangakhale kukangana kwaukali. Ndipo moyo wathu ungakhale wapaŵiri. Sitimakhalanso monga mwamuna wonga Kristu ndi mkazi wake koma monga mwamuna wamba ndi mkazi wina akukangana. Timaiŵala kuti panyumba payenera kukhala pamalo oyera. Mwinamwake timayamba kulankhula ngati anthu akudziko. Ndithudi, mawu oipa ndi amwano sangavute konse kutuluka pakamwa mumkhalidwe umenewo!​—Miyambo 12:18; yerekezerani ndi Machitidwe 15:37-39.

9 Komabe, Paulo analangiza kuti: “Nkhani yonse yovunda [Chigiriki, loʹgos sa·prosʹ, “mawu odetsa,” motero opanda chiyero] isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.” Ndipo zimenezo zikunena za onse omvetsera panyumba, kuphatikizapo ana.​—Aefeso 4:29; Yakobo 3:8-10.

10. Kodi uphungu wonena za chiyero umagwira ntchito motani kwa ana?

10 Ndiponso chitsogozo chimenechi cha chiyero chimagwiranso ntchito kwa ana m’banja lachikristu. Nkwapafupi chotani nanga kwa iwo kufika panyumba ataŵeruka kusukulu ndi kuyamba kutsanzira kalankhulidwe kachipanduko ndi kopanda ulemu ka anzawo akudziko! Ana inu, musatengeke ndi mzimu wosonyezedwa ndi anyamata opanda mwambo amene anatukwana mneneri wa Yehova ndi amene lerolino ali ndi anzawo oola pakamwa ndi amwano. (2 Mafumu 2:23, 24) Kalankhulidwe kanu kasadetsedwe ndi mawu onyoza a anthu aulesi kulankhula mawu abwino kapena osalingalira. Monga Akristu, mawu athu akhale oyera, abwino, omangirira, okoma mtima, ndi “okoleretsa.” Atisonyeze kuti ndife osiyana ndi anthu ena.​—Akolose 3:8-10; 4:6.

Chiyero ndi Apabanja Lathu Osakhulupirira

11. Kodi nchifukwa ninji kukhala oyera sikumatanthauza kudziyesa olungama?

11 Pamene tikuyesetsa kutsatira chiyero, tisaoneke kukhala odzikweza ndi kudziyesa olungama, makamaka pochita ndi apabanja osakhulupirira. Khalidwe lathu lachikristu la kukoma mtima liyenera kuwathandiza kuona kuti tili osiyana nawo m’lingaliro labwino, kuti timadziŵa kusonyeza chikondi ndi chifundo, monga momwedi anachitira Msamariya wachifundo wa m’fanizo la Yesu.​—Luka 10:30-37.

12. Kodi ndi motani mmene Mkristu wokwatira angapangire choonadi kukhala chokopa kwambiri kwa mnzake?

12 Petro anasonyeza kufunika kwakuti tikhale ndi maganizo abwino kulinga kwa apabanja lathu osakhulupirira pamene analembera akazi achikristu kuti: “Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuwopa kwanu.” Mkazi (kapenanso mwamuna) wachikristu angachititse choonadi kukhala chokopa kwambiri kwa mnzake wosakhulupirira ngati khalidwe lake lili loyera, loyenera, ndi laulemu. Zimenezi zikutanthauza kuti ayenera kusiya mpata m’zochita zake zateokrase kuti mnzake wosakhulupirirayo asanyalanyazidwe.a​—1 Petro 3:1, 2.

13. Kodi ndi motani mmene akulu ndi atumiki otumikira nthaŵi zina angathandizire amuna osakhulupirira kuyamikira choonadi?

13 Nthaŵi zina akulu ndi atumiki otumikira angathandize mwa kudziŵana ndi mwamuna wosakhulupirira mwa kucheza naye. Mwanjira imeneyi iye angaone kuti Mboni zili anthu abwino ndipo zimakonda zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo nkhani zina zosakhala za Baibulo. Panthaŵi ina, mkulu wina anali kuchita chidwi ndi kusodza kumene mwamuna wina anakonda kwambiri. Zimenezo zinawamasula. Mwamuna ameneyo anakhala mbale wobatizidwa m’kupita kwa nthaŵi. Panthaŵi inanso, mwamuna wosakhulupirira anali kukonda kwambiri mbalame za mtundu wa canary. Zimenezo sizinawalefule akulu. Mmodzi wa iwo anaŵerenga za nkhaniyo moti nthaŵi yotsatira imene anakumana ndi mwamunayo, anayambitsa makambitsirano pa nkhani imene mwamunayo anaikonda kwambiri! Chotero, kukhala oyera sikumatanthauza kukhala olimbirira kapena oumirira chinthu chimodzi.​—1 Akorinto 9:20-23.

Kodi Tingakhale Motani Oyera Mumpingo?

14. (a) Kodi njira imene Satana amagwiritsira ntchito kusokoneza mpingo njotani? (b) Kodi tingaupeŵe motani msampha wa Satana?

14 Satana Mdyerekezi ndi woneneza, pakuti dzina lachigiriki la Mdyerekezi, di·aʹbo·los, limatanthauza “wosinjirira” kapena “woneneza.” Kuneneza ndiko umodzi wa mikhalidwe yake yapadera, ndipo amayesa kuugwiritsira ntchito mumpingo. Njira imene amaikonda kwambiri ndiyo miseche. Kodi timamlola kutinyenga kutsatira khalidwe lopanda chiyero limeneli? Kodi zimenezo zitheka bwanji? Mwa kuyamba miseche, kuuzako ena, kapena kumvetsera. Mwambi wanzeru umati: “Munthu wokhota amautsa makani; kazitape afetsa ubwenzi.” (Miyambo 16:28) Kodi mankhwala othetsa miseche ndi kuneneza nchiyani? Tiyenera kutsimikizira kuti nthaŵi zonse tikulankhula zomangirira ndi zachikondi. Ngati timafunafuna ukoma m’malo mwa zoipa za abale athu, zokamba zathu zidzakhala zabwino ndi zauzimu nthaŵi zonse. Kumbukirani kuti kusuliza nkwapafupi. Ndipo munthu amene amadyera ena miseche kwa inu angakudyereninso miseche kwa ena!​—1 Timoteo 5:13; Tito 2:3.

15. Kodi ndi mikhalidwe iti ya Kristu imene idzatithandiza kusunga mpingo kukhala woyera?

15 Kuti mpingo ukhale woyera, ife tonse tifunikira kukhala ndi mtima wa Kristu, ndipo tikudziŵa kuti mkhalidwe wake waukulu ndiwo chikondi. Chifukwa chake, Paulo anauza Akolose kukhala achifundo monga Kristu: “Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima . . . kukhululukirana eni okha . . . Koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ndipo mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yanu.” Ndithudi, ndi mzimu umenewu wa kukhululukirana, tingasunge umodzi ndi chiyero cha mpingo.​—Akolose 3:12-15.

Kodi Chiyero Chathu Chimaonekera Kumalo Kumene Timakhala?

16. Kodi nchifukwa ninji kulambira kwathu koyera kuyenera kukhala kulambira kwa chimwemwe?

16 Bwanji ponena za anansi athu? Kodi amationa bwanji? Kodi timasonyeza chimwemwe cha choonadi, kapena kodi timachichititsa kuoneka ngati cholemetsa? Ngati ndife oyera monga momwedi Yehova alili, chiyero chathu chidzaonekera m’kalankhulidwe kathu ndi m’khalidwe lathu. Onse ayenera kuona kuti kulambira kwathu koyera kulinso kulambira kwa chimwemwe. Chifukwa ninji? Chifukwa Yehova Mulungu wathu ndi Mulungu wachimwemwe, ndipo amafuna olambira ake kukhala achimwemwe. Chifukwa chake, wamasalmo anati za anthu a Yehova m’nthaŵi zakale: “Odala [“achimwemwe ndi,” NW] anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” Kodi timasonyeza chimwemwe chimenecho? Kodi ana athunso amasonyeza chikhutiro cha kukhala pakati pa anthu a Yehova pa Nyumba ya Ufumu ndi pamisonkhano yaikulu?​—Salmo 89:15, 16; 144:15b.

17. Kodi tingachitenji mwanjira yoonekera kuti tisonyeze chiyero choyenera?

17 Tingasonyezenso chiyero chathu choyenera mwa mzimu wathu wa kugwirizana ndi kukomera mtima achinansi. Nthaŵi zina achinansi amafunikira kugwirizana, mwinamwake kuyeretsa malo awo kapena, monga m’maiko ena, kuthandiza kukonza misewu. Pambali imeneyi, chiyero chathu chingasonyezedwe mwa njira imene timasamalirira maluŵa athu, bwalo, kapena katundu wina. Ngati tisiya zinyalala ponseponse kapena tili ndi bwalo lauve kapena losakonzeka, mwinamwake ndi zimagalimoto zakale zakufa kuti onse aziona, kodi tinganene kuti tikulemekeza anansi athu?​—Chivumbulutso 11:18.

Chiyero Kuntchito ndi Kusukulu

18. (a) Kodi pali vuto lanji kwa Akristu lerolino? (b) Kodi ndi motani mmene tingakhalire osiyana ndi dziko?

18 Mtumwi Paulo analembera Akristu mumzinda wopanda chiyero wa Korinto kuti: “Ndinalembera inu m’kalata uja, kuti musayanjane ndi achigololo; si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m’dziko lapansi.” (1 Akorinto 5:9, 10) Limeneli ndi vuto kwa Akristu, amene amakumana masiku onse ndi anthu oipa kapena osadziŵa chabwino ndi choipa. Chimenechi ndi chiyeso chachikulu cha umphumphu, makamaka kumalo kumene amasonkhezera kuvuta akazi, chiphuphu, ndi kusaona mtima. M’mikhalidwe imeneyi sitiyenera kutaya miyezo yathu kuti tioneke “abwino” kwa otizinga. M’malo mwake, khalidwe lathu lachikristu la kukoma mtima komanso losiyana ndi lawo limatichititsa kuoneka apadera kwa anthu odziŵa, kwa ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu ndipo akufunafuna kanthu kena kabwino.​—Mateyu 5:3; 1 Petro 3:16, 17.

19. (a) Kodi inu ana mumakhala ndi ziyeso zotani kusukulu? (b) Kodi makolo angachitenji kuchirikiza ana awo limodzi ndi khalidwe lawo loyera?

19 Momwemonso, pali ziyeso zambiri zimene ana athu akuyang’anizana nazo kusukulu. Kodi inu makolo mumapita kusukulu kumene ana anu amaphunzira? Kodi mumaudziŵa mkhalidwe umene uliko? Kodi mumamvana ndi aphunzitsi? Nchifukwa ninji mafunso ameneŵa ali ofunika? Chifukwa m’mizinda yambiri ya dziko, sukulu zakhala nkhalango zochitiramo chiwawa, za anamgoneka, ndi kugonana. Kodi ana anu angasunge motani umphumphu wawo ndi khalidwe lawo loyera ngati inu makolo simukuwachirikiza mwachifundo? Nchifukwa chake Paulo anauza makolo kuti: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21) Njira ina yoputira ana ndiyo kulephera kuzindikira zothetsa nzeru zawo za tsiku ndi tsiku ndi ziyeso zawo. Kukonzekera ziyeso za kusukulu kumayamba ndi mkhalidwe wauzimu wa m’nyumba yachikristu.​—Deuteronomo 6:6-9; Miyambo 22:6.

20. Kodi nchifukwa ninji chiyero chikufunika kwa ife tonse?

20 Pomaliza, kodi nchifukwa ninji chiyero chikufunika kwa ife tonse? Chifukwa chimatitetezera ku dziko la Satana ndi kalingaliridwe kake. Chili dalitso tsopano ndi mtsogolo. Chimathandizira kutitsimikizira za moyo umene udzakhala moyo weniweni m’dziko latsopano lolungama. Chimatithandiza kukhala Akristu osamala, ofikirika, ndi okhoza kulankhulana ndi ena​—osati anthu otengeka maganizo osafuna kusintha. Mwachidule, chimatichititsa kukhala onga Kristu.​—1 Timoteo 6:19.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mufuna chidziŵitso chowonjezera ponena za mmene mungachitire mwanzeru ndi anzanu osakhulupirira, onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1990, “Musanyalanyaze Mnzanu!” masamba 20-2 ndi November 1, 1988, masamba 24-5, ndime 20-2.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nchifukwa ninji Petro anakuona kukhala kofunika kupatsa Akristu uphungu wa chiyero?

◻ Kodi nchifukwa ninji si kwapafupi kukhala ndi moyo woyera?

◻ Kodi ife tonse tingachitenji kuwongolera chiyero m’banja?

◻ Kuti mpingo ukhalebe woyera, kodi ndi khalidwe lodetsa liti limene tiyenera kupeŵa?

◻ Kodi tingakhalebe motani oyera kuntchito ndi kusukulu?

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Monga Mboni za Yehova, tiyenera kukhala achimwemwe potumikira Mulungu ndi m’zochita zina

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena