Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 8/15 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Tipita Nanu Limodzi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Kodi Mgonero wa Ambuye Uli ndi Phindu Lanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Tipita Nanu Limodzi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • ‘Mzimu Umachitira Umboni’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 8/15 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Malipoti a zaka zina amasonyeza kuti chiŵerengero cha amene amadya zizindikiro za pa Chikumbutso chinakwera pango’no. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ambiri atsopano akudzozedwa ndi mzimu woyera?

Pali chifukwa chabwino chokhulupirira kuti chiŵerengerochi cha 144,000 cha Akristu odzozedwa chinakwanira zaka makumi ambiri kumbuyoku.

Pa Machitidwe 2:1-4, timaŵerenga za oyambirira a gulu lochepa limenelo kuti: “Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi. Ndipo mwadzidzidzi anamveka mawu ochokera kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogaŵanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga mzimu anawalankhulitsa.”

Pambuyo pake, Yehova anasankha ena, ndipo anawadzoza ndi mzimu wake woyera. Zikwi zambiri anawonjezeredwa m’zaka zoyambirirazo za Chikristu. Paphwando la Chikumbutso m’nthaŵi yathu, wokamba nkhani kaŵirikaŵiri amafotokoza mawu a Paulo a pa Aroma 8:15-17, amene amanena kuti odzozedwa ‘amalandira mzimu wa umwana.’ Paulo anawonjezera kuti mzimu woyera umene amalandira ‘umachita umboni pamodzi ndi mzimu wawo kuti ali ana a Mulungu, oloŵa anzake a Kristu.’ Awo amene anadzozedwadi motero ndi mzimu amadziŵa motsimikizira. Sichimangokhala chikhumbo wamba kapena chotulukapo cha kutengeka maganizo ndi kudziyesa zimene iwo saali.

Tikudziŵa kuti chiitano chakumwamba chimenechi chinapitiriza m’zaka mazana ambiri, ngakhale kuti mkati mwa imene imatchedwa kuti Nyengo ya Mdima, pangakhale nthaŵi zina pamene chiŵerengero cha odzozedwa chinali chaching’ono kwambiri.a Ndi kukhazikitsidwanso kwa Chikristu choona chakumapeto kwa zaka za zana lapitali, ambiri anaitanidwa ndi kusankhidwa. Koma kukuoneka kuti chapakati pa ma 1930, chiŵerengero chonse cha 144,000 chinakwanira. Chotero panayamba kuonekera gulu la Akristu okhulupirika okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. Yesu anatcha ameneŵa “nkhosa zina,” amene amagwirizana pa kulambira ndi odzozedwa monga gulu limodzi la nkhosa.​—Yonane 10:14-16.

Zochitika mkati mwa zaka makumi ambiri zimasonyeza kutha kwa kuitanidwa kwa odzozedwa ndi dalitso la Yehova pa “khamu lalikulu” lomawonjezerekalo, amene ali ndi chiyembekezo cha kupulumuka “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:9, 14) Mwachitsanzo, paphwando la Chikumbutso mu 1935, pamene panapezeka anthu 63,146, awo amene anadya zizindikiro posonyeza kudzinenera kwawo kuti ali odzozedwa anali 52,465. Zaka makumi atatu pambuyo pake, kapena kuti mu 1965, opezekapo anali 1,933,089, pamene kuli kwakuti akudya anachepa kukhala 11,550. Zaka 30 pambuyo pake kufikira pafupi posachedwapa mu 1995, opezekapo anawonjezereka kwambiri kukhala 13,147,201, koma 8,645 okha ndiwo amene anadya mkate ndi kumwa vinyo. (1 Akorinto 11:23-26) Mwachionekere, pamene zaka makumi ambiri zinali kupita, chiŵerengero cha awo odzinenera kukhala otsalira chinachepa kwambiri​—oposa 52,400 mu 1935; 11,500 mu 1965; 8,600 mu 1995. Komabe, awo okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi adalitsidwa, ndipo chiŵerengero chawo chawonjezereka kwambiri.

Lipoti latsopano kwambiri limene lafalitsidwa ndilo la chaka cha 1995, ndipo likusonyeza akudya owonjezereka 28 kuposa chaka chinacho ngakhale kuti kwenikweni chiŵerengero cha akudya chinatsika polinganiza ndi cha opezekapo. Zonse zitalingaliridwa, kusankha kudya zizindikiro kwa anthu angapo owonjezereka sikuyenera kutidetsa nkhaŵa. Pazaka zambiri ena, ngakhale obatizidwa chatsopano, mosayembekezereka ayamba kudya. Nthaŵi zingapo, iwo azindikira pambuyo pake kuti zimenezo zinali kulakwitsa. Ena azindikira kuti anadya potengeka maganizo mwinamwake chifukwa cha kupsinjika kuthupi kapena m’maganizo. Koma anadzazindikira kuti kwenikweni sanaitanidwe ku moyo wakumwamba. Iwo anapempha Mulungu kuti awachitire chifundo. Ndipo akupitirizabe kumtumikira monga Akristu abwino ndi okhulupirika, okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi.

Palibe chifukwa chimene aliyense wa ife ayenera kudera nkhaŵa ngati wina ayamba kudya zizindikiro kapena aleka kuchita motero. Ndithudi si thayo lathu kudziŵa kuti kaya winawake wadzozedwadi ndi mzimu woyera ndi kuitanidwa ku moyo wakumwamba kapena ayi. Kumbukirani chitsimikizo cholimba cha Yesu chakuti: “Ine ndine mbusa wabwino; ndipo ndizindikira [nkhosa, NW] zanga.” Ndi chitsimikizo chofananacho, Yehova amawadziŵa awo amene wawasankha monga ana auzimu. Pali zifukwa zabwino zokhulupiririra kuti chiŵerengero cha odzozedwa chidzapitirizabe kuchepa pamene ukalamba ndi zochitika zosadziŵika zithetsa moyo wawo wapadziko lapansi. Komabe, monga mmene odzozedwadi ameneŵa amakhala okhulupirika kufikira imfa, akumayembekezera kulandira korona wa moyo, nkhosa zina, amene ayeretsa zovala zawo m’mwazi wa Mwanawankhosa, angayembekezere kupulumuka chisautso chachikulu chimene chayandikiracho.​—2 Timoteo 4:6-8; Chivumbulutso 2:10.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 15, 1965, masamba 191-2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena