Kutumikira Yehova Monga Banja Logwirizana
YOSIMBIDWA NDI ANTONIO SANTOLERI
Atate anali ndi zaka 17 pamene anachoka ku Italy mu 1919. Anasamukira ku Brazil pofunafuna moyo wabwinopo. M’kupita kwa nthaŵi, anakhala ndi malo ometera m’tauni ina yaing’ono mkati mwa boma la São Paulo.
TSIKU lina mu 1938, pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, Atate anagula Baibulo la matembenuzidwe a Brasileira kwa munthu amene anadzera pamalo awo ometera. Patapita zaka ziŵiri Amayi anadwala kwambiri nakhala osatha kuchita kanthu kufikira imfa yawo. Nawonso Atate anadwala, chotero ife tonse—ine, Amayi, Atate, ndi mlongo wanga Ana—tinamka kukakhala ndi achibale mumzinda wa São Paulo.
Mkati mwa kuimba kwanga sukulu ku São Paulo, ndinakhala woŵerenga wakhama, makamaka mabuku a mbiri. Ndinachita chidwi kuti Baibulo linali kutchulidwamo nthaŵi ndi nthaŵi. Buku lina la nkhani zopeka, limene ndinabwereka ku laibulale ya boma ya São Paulo, linatchula za Ulaliki wa pa Phiri nthaŵi zingapo. Imeneyo ndiyo nthaŵi imene ndinasankha zopeza Baibulo kuti ndidziŵerengere ndekha ulaliki umenewo. Ndinafunafuna Baibulo limene Atate anagula zaka zapitazo ndipo pomalizira pake ndinalipeza pansi m’bokosi, mmene linali kwa zaka zisanu ndi ziŵiri.
Banja lathu linali lachikatolika, chotero sanandilimbikitsepo kuŵerenga Baibulo. Tsopano, ndinaphunzira kupeza machaputala ndi mavesi pandekha. Ndinaŵerenga mokondwera kwambiri osati Ulaliki wa pa Phiri wokha komanso buku lonse la Mateyu ndiponso mabuku ena a Baibulo. Chimene chinandichititsa chidwi kwambiri chinali kamvekedwe ka choonadi ka mmene ziphunzitso ndi zozizwitsa za Yesu zinasimbidwira.
Pozindikira mmene chipembedzo cha Katolika chinalili chosiyana ndi zimene ndinaŵerenga m’Baibulo, ndinayamba kupita ku tchalitchi cha Presbyterian, ndipo Ana anagwirizana nane. Komabe, ndinali ndi njala mumtima. Kwa zaka zambiri ndinali kufunafuna Mulungu mwakhama. (Machitidwe 17:27) Usiku wina wopanda mitambo, pamene ndinali kusinkhasinkha, ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji ndilipo? Kodi chifuno cha moyo nchiyani?’ Ndinafuna malo andekha kuseri kwa nyumba, ndinagwada, ndi kupemphera kuti, ‘Ambuye Mulungu! Kodi ndinu yani? Ndingakudziŵeni bwanji?’ Yankho lake linadza posakhalitsa.
Kuphunzira Choonadi cha Baibulo
Tsiku lina mu 1949, msungwana wina anafikira Atate pamene iwo anali kutsika m’galimoto la panjanji. Anawagaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi a Galamukani! Analembetsa Nsanja ya Olonda nampempha kuti adzafike kwathu, akumalongosola kuti anali ndi ana aŵiri amene anali kupita ku tchalitchi cha Presbyterian. Pa kucheza kwa mkaziyo, anasiyira Ana buku lakuti Children nayamba kuphunzira naye Baibulo. Pambuyo pake ndinagwirizana nawo m’phunzirolo.
Mu November 1950 tinafika pa msonkhano wathu wachigawo woyamba wa Mboni za Yehova. Buku lakuti “Mulungu Akhale Woona” linatulutsidwa pamenepo, ndipo tinapitiriza phunziro lathu la Baibulo tikumagwiritsira ntchito buku limenelo monga chitsogozo chathu. Mwamsanga pambuyo pake tinazindikira kuti tinali titapeza choonadi, ndipo mu April 1951 tinabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova. Atate anadzipatulira patapita zaka zina pambuyo pake ndipo anamwalira ali okhulupirika kwa Mulungu mu 1982.
Wachimwemwe mu Utumiki Wanthaŵi Zonse
Mu January 1954, pamene ndinali ndikali ndi zaka 22 zokha, anandivomereza kukatumikira ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, imene imatchedwa Beteli. Nditafika kumeneko, ndinadabwa kupeza kuti munthu amene anali wamkulu kwa ine ndi zaka ziŵiri zokha, Richard Mucha, ndiye amene anali woyang’anira nthambi. Mu 1955, pamene atumiki amadera anafunika, monga momwe oyang’anira oyendayenda tinali kuwatchera panthaŵiyo, ndinali mmodzi wa anthu asanu amene anapemphedwa kukachita nawo utumiki umenewu.
Gawo langa linali boma la Rio Grande do Sul. Panali mipingo isanu ndi itatu yokha ya Mboni za Yehova pamene ndinayamba, koma miyezi 18 isanathe mipingo ina iŵiri yatsopano ndi magulu akutali 20 anakhazikitsidwa. Lero dera limeneli lili ndi madera 15 a Mboni za Yehova, lililonse lokhala ndi mipingo pafupifupi 20! Kumapeto kwa 1956, ndinalangizidwa kuti dera langa lagaŵidwa kukhala madera anayi aang’ono amene adzatumikiridwa ndi atumiki amadera anayi. Panthaŵiyo ndinalangizidwa kubwerera ku Beteli kukapatsidwa gawo latsopano.
Mondidabwitsa ndiponso mondikondweretsa, anandipatsa gawo la kumpoto kwa Brazil monga mtumiki wachigawo, mtumiki woyendayenda amene amatumikira madera angapo. Panthaŵiyo Brazil anali ndi atumiki a Mboni za Yehova 12,000, ndipo dzikoli linali ndi zigawo ziŵiri. Richard Wuttke anatumikira kummwera, ndipo ine chigawo cha kumpoto. Pa Beteli tinaphunzitsidwa kugwiritsira ntchito pulojekitala kusonyeza mafilimu otulutsidwa ndi Mboni za Yehova akuti The New World Society in Action ndi The Happiness of the New World Society.
M’masiku amenewo kuyenda ulendo kunali kosiyana. Panalibe Mboni imene inali ndi galimoto, chotero ndinkayenda pabwato, paboti, pangolo ya ng’ombe, pakavalo, palole, ndipo kamodzi pandege. Kunali kokondweretsa kuuluka pamwamba pa nkhalango ya Amazon kukatera ku Santarém, mzinda wokhala pakati pa Belém pamathiriro pa Amazon ndi Manaus, malikulu a Amazonas State. Atumiki azigawo panthaŵiyo anali ndi misonkhano yadera yoŵerengeka yoti achititse, chotero ndinathera nthaŵi yanga yambiri ndikumaonetsa mafilimu a Sosaite. M’mizinda yokulirapo, panali kufika anthu mazana ambiri.
Chimene chinandichititsa chidwi kwambiri kumpoto kwa Brazil chinali chigawo cha Amazon. Pamene ndinali kutumikira kumeneko mu April 1957, madzi anasefukira mu mtsinje wa Amazon ndi mitsinje yake yaing’ono. Ndinali ndi mwaŵi wa kuonetsa imodzi ya mafilimuwo mu nkhalango, kufutukula poonetsera pake pakati pa mitengo iŵiri. Magetsi a pulojekitala anachokera m’boti lamakina lokochezedwa mu mtsinje umene unali pafupi. Kwa ochuluka inali filimu yoyamba kuiona m’moyo wawo.
Posakhalitsa ndinabwerera kukatumikira ku Beteli, ndipo chaka chotsatira, mu 1958, ndinali ndi mwaŵi wa kukafika pa Msonkhano wa Mitundu wa “Chifuniro cha Mulungu” wa Mboni za Yehova, ku New York City. Nthumwi zochokera m’maiko 123 zinali pakati pa anthu 253,922 amene anadzaza Yankee Stadium ndi Polo Grounds ya pafupi pake pa tsiku lomaliza la msonkhano wamasiku asanu ndi atatu umenewo.
Kusangalala ndi Masinthidwe m’Moyo Wanga
Posakhalitsa nditabwerera ku Beteli, ndinadziŵana ndi Clara Berndt, ndipo m’March 1959 tinakwatirana. Tinapatsidwa gawo la ntchito yadera m’boma la Bahia, mmene tinatumikiramo pafupifupi chaka chimodzi. Ine ndi Clara timakumbukirabe mwachimwemwe za kudzichepetsa, ufulu, changu, ndi chikondi cha abale kumeneko; iwo anali osauka mwakuthupi koma olemera pa zipatso za Ufumu. Ndiyeno anatisamutsira ku São Paulo State. Kunali kumeneko mu 1960, pamene mkazi wanga anakhala ndi pathupi, ndipo tinasiya utumiki wanthaŵi zonse.
Tinasankha kusamukira m’boma la Santa Catarina, kumene mkazi wanga anabadwirako. Mwana wathu wamwamuna, Gerson, anali woyamba wa ana athu asanu. Anatsatiridwa ndi Gilson mu 1962, Talita mu 1965, Tárcio mu 1969, ndi Janice mu 1974. Chifukwa cha Yehova ndi uphungu wake wabwino kwambiri umene amapereka, tinatha kuyang’anizana ndi chitokoso cha kuwalera “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].”—Aefeso 6:4.
Timaona mwana wathu aliyense kukhala wamtengo wapatali. Wamasalmo anafotokoza bwino kwambiri malingaliro ake kuti: “Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Ngakhale kuti panali mavuto, tasamalira ana athu monga momwe tikanachitira ndi ‘cholandira chilichonse cha kwa Yehova,’ tikumakumbukira malangizo opezeka m’Mawu ake. Mfupo zake zakhala zambiri. Zinatipatsa chimwemwe chosaneneka pamene asanu onsewo molondolana, aliyense payekha ndipo mwa kusankha kwawo anasonyeza chikhumbo cha kubatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova.—Mlaliki 12:1.
Zosankha za Ana Athu
Tinasangalala koposa pamene Gerson, atangomaliza kosi yake ya makompyuta, ananena kuti anafuna kukatumikira ku Beteli, motero akumasankha utumiki wanthaŵi zonse m’malo mwa ntchito ina yakuthupi. Komabe moyo wa ku Beteli unali wovuta poyamba kwa Gerson. Titakamuona pamene anali atakhala ku Beteli kwa miyezi inayi yokha, ndinagwidwa mtima kwambiri ndi chisoni chimene nkhope yake inasonyeza pamene tinali kuchoka. Ndinamuona pa galasi lathu la galimoto akutiyang’ana kufikira pamene tinapyola gulaye la msewu. Ndinali ndi misozi m’maso kwakuti ndinaima pambali pa msewu tisanapitirize ulendo wathu wakunyumba wa makilomita 700.
Gerson anafikiradi pakukonda Beteli. Atakhalako pafupifupi zaka zisanu ndi chimodzi, anakwatirana ndi Heidi Besser, ndipo anatumikira limodzi pa Beteli kwa zaka zina ziŵiri. Ndiyeno Heidi anakhala ndi pathupi, ndipo anachoka. Mwana wawo wamkazi, Cintia, amene tsopano ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi, amatsagana nawo m’ntchito zawo za Ufumu.
Pasanapite nthaŵi yaitali pamene tinakaona Gerson ku Beteli, Gilson, amene anali atangomaliza kumene chaka chake choyamba m’maphunziro azamalonda, ananena kuti nayenso anafuna kukatumikira kumeneko. Cholinga chake chinali chakuti adzapitirize kosi yake yazamalondayo atatumikira chaka chimodzi pa Beteli. Koma cholinga chakecho chinasintha, ndipo anapitiriza mu utumiki wa ku Beteli. Mu 1988 anakwatirana ndi Vivian Gonçalves, mpainiya, monga momwe timatchera atumiki anthaŵi zonse. Kuyambira pamenepo atumikira pamodzi ku Beteli.
Chimwemwe chathu chinapitiriza pamene mwana wathu wachitatu, Talita, anasankha kuloŵa utumiki waupainiya mu 1986 atachita kosi ya kujambula mapulani a nyumba. Zaka zitatu zitapita nayenso anamuitana ku Beteli. Mu 1991 anakwatirana ndi José Cozzi, amene anali atatumikira pa Beteli kwa zaka khumi. Iwo akupitiriza kukhala pamenepo monga okwatirana.
Ine ndi mkazi wanga tinasangalalanso pamene Tárcio, wotsatirapo mu mzerawo, anabwereza kunena mawu amodzimodziwo amene tinali titawamva kale katatu, “Atate, ndikufuna kupita ku Beteli.” Pempho lake linavomerezedwa, ndipo mu 1991 nayenso anayamba utumiki pa Beteli, kumene anakhala kufikira 1995. Tili achimwemwe kuti iyeyo anagwiritsira ntchito unyamata wake ndi nyonga kuchirikizira zinthu za Ufumu wa Yehova mwa m’njira imeneyi kwa zaka zoposa zitatu.
Mwana wathu wamng’ono pa onse, Janice, anasankha kutumikira Yehova ndipo anabatizidwa pa usinkhu wa zaka zakubadwa 13. Mkati mwa kuphunzira sukulu kwake, anatumikira kwa chaka chimodzi monga mpainiya wothandiza. Ndiyeno, pa September 1, 1993, anayamba upainiya wokhazikika mumpingo wathu muno mu mzinda wa Gaspar.
Njira Yachipambano
Kodi nchiyani chimene chili chinsinsi chochititsa banja kukhala logwirizana pa kulambira Yehova? Sindikhulupirira kuti pali njira imodzi yokha. Yehova wapereka uphungu m’Mawu ake kwa makolo achikristu kuti awatsatire, chotero thamo lonse liyenera kumka kwa iye chifukwa cha zotulukapo zabwino zimene talandira. Ife tangoyesa kutsatira zitsogozo zake. (Miyambo 22:6) Ana athu onse atengera malingaliro achilatini kwa ine ndi mzimu wothandiza wachijeremani kwa amawo. Koma chinthu chofunika koposa chimene iwo analandira kwa ife ndicho choloŵa chauzimu.
Moyo wathu wa banja unazikidwa pa zinthu za Ufumu. Kuika zinthu zimenezi poyamba kunali kovuta. Mwachitsanzo, tinali ndi vuto pa kuchita phunziro la Baibulo labanja mokhazikika, komabe sitinaleke. Kuyambira pa masiku awo oyamba a moyo, tinapititsa mwana aliyense ku misonkhano yachikristu ndiponso kumisonkhano yadera ndi yachigawo. Kudwala kokha kapena zina zamwadzidzidzi nzimene zinatiletsa kufika pamisonkhano. Ndiponso, pausinkhu waung’ono, anawo anatsagana nafe mu utumiki wachikristu.
Pamene anali pafupifupi zaka khumi, anawo anayamba kupereka nkhani m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Tinawathandiza kukonzekera nkhani zawo zoyamba, kuwalimbikitsa kugwiritsira ntchito autilaini m’malo mwa malembo oŵerenga. Pambuyo pake, aliyense ankakonzekera nkhani yake. Ndiponso, pamene anali ndi zaka za pakati pa 10 ndi 12, aliyense anayamba kukhala ndi phande mokhazikika mu utumiki. Uwu ndiwo moyo wokha umene anadziŵa.
Mkazi wanga, Clara, anachita zofunika kwambiri pa kulera ana athu. Usiku uliwonse, pamene anali aang’ono kwambiri—nthaŵi imene mwana amatsopa zonse zimene akuphunzitsidwa monga siponji—Clara anali kuwaŵerengera nkhani ya m’Baibulo ndi kupemphera ndi aliyense wa iwo. Anagwiritsira ntchito bwino mwaŵi wa mabuku akuti Kucokera ku Paradaiso Wotaika Kumka ku Paradaiso Wopezedwanso, Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.a Pamene zothandizira za makaseti a mawu ndi za zithunzi zogaŵiridwa ndi Mboni za Yehova zinayamba kupezeka tinazigwiritsiranso ntchito.
Zokumana nazo zathu monga makolo achikristu zimatsimikizira kuti ana amafunikira chisamaliro chamasiku onse. Chikondi chachikulu, chikondwerero chaumwini, ndi nthaŵi yochuluka zili pakati pa zinthu zazikulu zofunika kwa achichepere. Sitinalione chabe monga thayo lathu laukholo loti tikwaniritsire zofunika zimenezi monga momwe tingathere komanso tinapeza chikondwerero chachikulu mwa kuchita motero.
Zoonadi, nkokhutiritsa kwa makolo kuona kukwaniritsidwa kwa mawu a pa Salmo 127:3-5 akuti: “Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chimphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake.” Kutumikira Yehova monga banja logwirizana kwatibweretseradi chimwemwe!
[Mawu a M’munsi]
a Onsewo ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 26]
Antonio Santoleri ndi banja lake