Uthenga Wabwino Malinga ndi Akatswiri
“MAKAMUWO a anthu anena kuti Ine ndine yani?” (Luka 9:18) Yesu anafunsa ophunzira ake zimenezi pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo. Funsolo linali lochititsa anthu kukangana panthaŵiyo. Likuoneka kukhala lotero kwambiri tsopano, makamaka panyengo ya Krisimasi, imene amati njozikidwa pa Yesu. Ambiri amakhulupirira kuti Yesu anatumidwa kuchokera kumwamba kudzaombola mtundu wa munthu. Kodi ndi zimene mumaganiza zimenezo?
Akatswiri ena akupereka lingaliro lina. “Lingaliro lakuti Yesu anali munthu amene anaphunzitsa kuti anali Mwana wa Mulungu amene anali kudzafera machimo a dziko si loona malinga ndi mbiri,” akutero Marcus J. Borg, profesa wa chipembedzo ndi mwambo.
Akatswiri ena akunena kuti Yesu weniweni anali wosiyana ndi uja amene timamuŵerenga m’Baibulo. Ena amakhulupirira kuti Mauthenga Abwino onse analembedwa pambuyo pa imfa ya Yesu patapita zaka makumi anayi kapena oposapo ndi kuti mafotokozedwe odziŵikitsa Yesu panthaŵiyo anali okukumaza. Vuto silinali lakuti olemba Mauthenga Abwino sanali kukumbukira, akutero akatswiriwo, koma linali pa kumasulira kwawo. Pambuyo pa imfa ya Yesu ophunzira anayamba kumuona mosiyana—monga Mwana wa Mulungu, Mpulumutsi, ndi Mesiya. Ena monenetsa amati Yesu anali chabe munthu wanzeru woyenda peyupeyu, munthu wofuna kusintha makhalidwe a anthu. Chimenechi, akutero akatswiri, ndicho choonadi chonse.
Lingaliro “Laukatswiri” Ponena za Yesu
Kuti achirikize lingaliro lawo “laukatswiri,” ofufuza akuoneka kukhala ofunitsitsa kukana chilichonse chonena za Yesu chooneka chachilendo. Mwachitsanzo, ena amanena kuti kubadwa mwa namwali inali njira yobisira Yesu kuti asadziŵike kuti anali mwana wapathengo. Ena amakana maulosi a Yesu onena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu, akumalimbikira kunena kuti ameneŵa anaphatikizidwa m’Mauthenga Abwino pambuyo pa “kukwaniritsidwa” kwake. Ena amanena kuti kuchiritsa kwa Yesu kunali kongosintha maganizo a munthu. Kodi malingaliro ameneŵa mumawaona kukhala oona kapena opusa?
Akatswiri ena amanenadi kuti ophunzira a Yesu anapeka chiukiriro kuti chipani chawo chisagwe. Ndi iko komwe, akatswiriwo amatero, otsatira a Yesu analibe mphamvu popanda iye, choncho analemba zopeka ponena za Mbuye wawo. Ndiko kunena kuti, chinali Chikristu chimene chinaukitsidwa, osati Kristu. Ngati zimenezo zikuoneka ngati kuzemba choonadi kwaukatswiri, bwanji ponena za lingaliro la Barbara Thiering lakuti Yesu sanaphedwe nkomwe? Iyeyo amakhulupirira kuti Yesu anapulumuka kupachikidwa kwake ndipo anapitiriza kukhala ndi moyo nakwatira kaŵiri ndi kukhala ndi ana atatu.
Zonena zonsezi zimamtsitsa Yesu kumuika pamalo amodzi okha pamene akatswiri ochuluka angamlandire: aja a munthu wanzeru, Myuda wapansi, wosintha makhalidwe a anthu—chilichonse koma osati Mwana wa Mulungu, amene anadza ‘kudzapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’—Mateyu 20:28.
Mwinamwake chapanthaŵi ino ya chaka, mwaŵerenga mbali za Mauthenga Abwino, monga mbali ya kubadwa kwa Yesu modyera ziŵeto. Kapena mwina mwazimva m’tchalitchi. Kodi munalandira nkhani za m’Mauthenga Abwino kukhala zofunika ndi zokhulupiririka? Ndiyetu onani chochitikachi chodabwitsa kwambiri. Pa imene amatcha kuti Seminale ya Yesu, gulu la akatswiri lakumana kaŵiri pachaka chiyambire 1985 kuti adziŵe ngati mawu a Yesu ali odalirika. Kodi Yesu ananenadi zimene Baibulo limati anazinena? Mamembala a seminale imeneyi anaponya voti ndi mikanda ya maonekedwe osiyanasiyana pa mawu alionse. Mkanda wofiira unatanthauza kuti mawuwo ndithudi ananenedwa ndi Yesu; mkanda wa upofu unatanthauza kuti Yesu angakhale atawanena; mkanda wotumbuluka unasonyeza kukayikira; ndipo mkanda wakuda unatanthauza chinyengo.
Mungadabwe kwambiri kudziŵa kuti Seminale ya Yesu imeneyo yanena kuti 82 peresenti ya mawu amene amati ndi a Yesu akuoneka kuti sindiye anawanena. Mawu a mu Uthenga Wabwino wa Marko a pamalo amodzi okha ndi amene anaonedwa kukhala odalirika. Anati Uthenga Wabwino wa Luka ngwodzala ndi nkhani zosinjirira zokhazokha “zosatheka kuwongolera.” Mawu onse a Uthenga Wabwino wa Yohane kusiyapo mizere itatu analandira mkanda wakuda, kusonyeza kuti ndi chinyengo, ndipo ochepawo amene anatsala analandira mkanda wotumbuluka wosonyeza kukayikira.
Si Nkhani ya Maphunziro Chabe
Kodi mukuvomerezana ndi akatswiri? Kodi iwo akutipatsa chithunzi cholongosoka cha Yesu kuposa chija chopezeka m’Baibulo? Mafunso ameneŵa si nkhani yongofuna kukambitsirana kwa akatswiri. Panthaŵi ino ya chaka, mwinamwake mwakumbutsidwa kuti, malinga ndi kunena kwa Baibulo, Mulungu anatuma Yesu “kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Ngati Yesu anali chabe munthu wanzeru woyenda peyupeyu amene mwinamwake sitikumdziŵa bwinobwino, ‘kumkhulupirira’ kungakhale kopanda pake. Komabe, ngati mafotokozedwe a Baibulo a Yesu ngoona, chipulumutso chathu chosatha chikukhudzidwa. Chotero, tifunikira kudziŵa—kodi Baibulo lili ndi choonadi ponena za Yesu?