Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 12/15 tsamba 22-24
  • Akula ndi Priskila—Banja Lopereka Chitsanzo Chabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akula ndi Priskila—Banja Lopereka Chitsanzo Chabwino
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Osoka Mahema
  • Zitsanzo za Kuchereza Alendo
  • “Anapereka Khosi Lawo” Chifukwa cha Paulo
  • Banja Lokondana Kwambiri
  • Lalikirani ndi Cholinga Chopanga Ophunzira
    Nsanja ya Olonda—2003
  • ‘Pitiriza Kulankhula, Usakhale Chete’
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Akristu Amafunika Kuthandizana
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Mukukumbukira?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 12/15 tsamba 22-24

Akula ndi Priskila​—Banja Lopereka Chitsanzo Chabwino

“MULANKHULE Priska ndi Akula, antchito anzanga m’Kristu Yesu, amene anapereka khosi lawo chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu.”​—Aroma 16:3, 4.

Mawu ameneŵa a mtumwi Paulo ku mpingo wachikristu ku Roma akusonyeza ulemu ndi chikondi chachikulu chimene anali nacho pa banja limeneli. Iye anatsimikizira kuti sanawanyalanyaze polembera kalata mpingo wawo. Koma kodi ‘antchito anzake’ aŵiri a Paulo ameneŵa anali yani, ndipo nchifukwa ninji iye ndi mipingo anawakonda kwambiri?​—2 Timoteo 4:19.

Akula anali mmodzi wa Ayuda omwazikana ndipo wafuko la ku Ponto, dera lina la kumpoto kwa Asia Minor. Iye ndi mkazi wake Priskila (Priska) anakakhala mu Roma. Mumzinda umenewo munali Ayuda ambiri makamaka chiyambire pamene Pompey analanda Yerusalemu mu 63 B.C.E., pamene andende ambiri anapititsidwa ku Roma monga akapolo. Kwenikweni, zolemba za Aroma zimasonyeza kuti mumzindawo munali masunagoge khumi ndi aŵiri kapena kuposapo. Ayuda angapo ochokera ku Roma analipo pa Pentekoste ku Yerusalemu mu 33 C.E., pamene anamva uthenga wabwino. Mwinamwake ameneŵa ndiwo anafikitsa uthenga wachikristu ku likulu la Ufumu wa Roma.​—Machitidwe 2:10.

Komabe, Ayuda anali atathamangitsidwa m’Roma m’chaka cha 49 kapena kuchiyambi cha 50 C.E. mwa lamulo loperekedwa ndi Mfumu Klaudiyo. Choncho, mtumwi Paulo anakumana ndi Akula ndi Priskila mumzinda wa Korinto ku Greece. Pamene Paulo anafika mu Korinto, Akula ndi Priskila mwachifundo anamchereza ndi kumpatsa ntchito yochita, popeza kuti ankadziŵa ntchito imodzimodzi​—kusoka mahema.​—Machitidwe 18:2, 3.

Osoka Mahema

Imeneyi siinali ntchito yopepuka. Kuti apange mahema anali kudula ndi kusoka pamodzi zidutswa zolimba ndi zonyankhalala za nsalu kapena chikopa. Malinga ndi kunena kwa wolemba mbiri Fernando Bea, inali “ntchito yofuna luso ndi kusamala” kwa osoka mahema amene ankagwiritsira ntchito “nsalu zokhakhala ndi zolimba zogwiritsira ntchito kumangira misasa paulendo, kudzichinjiriza kudzuŵa ndi mvula, kapena kulongedza katundu m’munsi mwa zombo.”

Zimenezi zikudzutsa funso. Kodi Paulo sananene kuti ‘anaphunzitsidwa pamapazi a Gamaliyeli,’ motero nakhala wokonzeka kupeza ntchito yapamwamba m’zaka zotsatira? (Machitidwe 22:3, NW) Pamene kuli kwakuti zimenezi nzoona, Ayuda a m’zaka za zana loyamba ankaona kuphunzitsa mwana ntchito kukhala chinthu chodzetsa ulemu ngakhale ngati mwanayo anali kudzalandira maphunziro apamwamba. Chotero Akula ndi Paulo yemwe ayenera kuti anaphunzira luso lawo la kusoka mahema akali aang’ono. Chidziŵitso chimenecho chinadzakhala chantchito kwambiri pambuyo pake. Koma pokhala Akristu, iwo sanaone ntchito yakuthupi imeneyi kukhala chinthu chofunika koposa. Paulo anafotokoza kuti ntchito imene anachita ku Korinto limodzi ndi Akula ndi Priskila inali chabe njira yochirikizira ntchito yake yaikulu, ija yolengeza uthenga wabwino popanda ‘kulemetsa wina aliyense.’​—2 Atesalonika 3:8; 1 Akorinto 9:18; 2 Akorinto 11:7.

Mwachionekere, Akula ndi Priskila anakondwera kuchita zonse zothekera pochirikiza utumiki waumishonale wa Paulo. Sitingadziŵe, mwinamwake mabwenzi atatuwo ankalekeza ntchito yawo kangapo kuti achite umboni wamwamwaŵi kwa ochita nawo malonda kapena kwa odutsa pafupi! Ndipo ngakhale kuti ntchito yawo yosoka mahema inali yapansi ndipo yotopetsa, anakonda kuichita, nagwira ntchito ngakhale “usiku ndi usana” kuti achirikize zinthu za Mulungu​—monga momwe Akristu ambiri amakono amadzichirikizira ndi ntchito ya maola ochepa kapena yodalira panyengo kuti nthaŵi yawo yotsala yaikulu aipatulire pa kuthandiza anthu kumva uthenga wabwino.​—1 Atesalonika 2:9; Mateyu 24:14; 1 Timoteo 6:6.

Zitsanzo za Kuchereza Alendo

Paulo ayenera kuti ankakhala panyumba ya Akula pochita ntchito yake yaumishonale m’miyezi 18 imene anakhala m’Korinto. (Machitidwe 18:3, 11) Ndiye kuti mwinamwakenso, Akula ndi Priskila anali ndi mwaŵi wa kulandira Sila ndi Timoteo monga alendo awo atafika kuchokera ku Makedoniya. (Machitidwe 18:5) Makalata aŵiri a Paulo opita kwa Atesalonika, amene pambuyo pake anadzakhala mbali ya mabuku ovomerezedwa a Baibulo, ayenera kuti analembedwa pamene mtumwiyo anali kukhala ndi Akula ndi Priskila.

Tingalingalire kuti panthaŵiyi nyumba ya Priskila ndi Akula inalidi malo apakati a ntchito yateokrase. Kuyenera kuti mabwenzi okondedwa ambiri ankapitako kaŵirikaŵiri​—Stefana ndi banja lake, Akristu oyamba m’chigawo cha Akaya, obatizidwa ndi Paulo iyemwini; Tito Yusto, amene analola Paulo kugwiritsira ntchito nyumba yake kuti aperekeremo nkhani; ndi Krispo, mkulu wa sunagoge, amene analandira choonadi limodzi ndi banja lake lonse. (Machitidwe 18:7, 8; 1 Akorinto 1:16) Ndiyeno panali Fortunato ndi Akayiko; Gayo, amene mwinamwake misonkhano ya mpingo inkachitikira m’nyumba mwake; Erasto, woyang’anira mudzi; Tertio, mlembi amene Paulo anagwiritsira ntchito kulemba kalata yake kwa Aroma; ndi Febe, mlongo wokhulupirika wa mumpingo wapafupi wa Kenkreya, amene ayenera kuti ndiye ananyamula kalatayo kuchokera ku Korinto kupita ku Roma.​—Aroma 16:1, 22, 23; 1 Akorinto 16:17.

Atumiki a Yehova amakono amene akhala ndi mwaŵi wa kuchereza mtumiki woyendayenda akudziŵa mmene kuchita motero kumakhalira kolimbikitsa ndi kosaiŵalika. Nkhani zomangirira zimene zimasimbidwa panthaŵi zimenezi zimadzetsadi mpumulo wauzimu kwa onse. (Aroma 1:11, 12) Ndipo, monga mmene Akula ndi Priskila anachitira, awo amene amapereka nyumba zawo kuti achitiremo misonkhano, mwinamwake Phunziro la Buku la Mpingo, ali ndi chimwemwe ndi chikhutiro pokhoza kuthandiza mwa njira imeneyi kulambira koona.

Ubwenzi wawo ndi Paulo unali wapafupi kwambiri kwakuti Akula ndi Priskila ananyamuka naye pamene anachoka mu Korinto m’ngululu ya 52 C.E., kutsagana naye mpaka ku Efeso. (Machitidwe 18:18-21) Iwo anakhala mumzinda umenewo ndi kuyala maziko a ulendo wotsatira wa mtumwiyo. Kunali kuno kumene aphunzitsi aluso ameneŵa a uthenga wabwino ‘anatenga’ Apolo wolankhula mwanzeruyo nakhala ndi mwaŵi wa kumthandiza kumvetsa “njira ya Mulungu mosamalitsa.” (Machitidwe 18:24-26) Pamene Paulo anakachezanso ku Efeso paulendo wake wachitatu waumishonale, nthaŵi inayake m’chisanu cha mu 52/53 C.E., munda umene banja limeneli lamphamvu linali litalima unali wocha kale. Kwa zaka ngati zitatu, Paulo analalikira ndi kuphunzitsa kumeneko za “Njirayo,” pamene mpingo wa ku Efeso unkachitira misonkhano m’nyumba ya Akula.​—Machitidwe 19:1-20, 26; 20:31; 1 Akorinto 16:8, 19.

Pambuyo pake, atabwerera ku Roma, mabwenzi aŵiri a Paulo ameneŵa anapitirizabe ‘kuchereza alendo,’ akumapereka nyumba yawo kuti achitiremo misonkhano yachikristu.​—Aroma 12:13; 16:3-5.

“Anapereka Khosi Lawo” Chifukwa cha Paulo

Mwinamwake Paulo ankakhalanso ndi Akula ndi Priskila pamene anali ku Efeso. Kodi anali kukhala nawo panthaŵi ya chipolowe cha osula siliva? Malinga ndi nkhani ya pa Machitidwe 19:23-31, pamene amisiri opanga tiakachisi anaukira kulalikira kwa uthenga wabwino, abale anamletsa Paulo kuti asadziike pangozi mwa kukayang’anizana ndi gululo. Othirira ndemanga Baibulo ena anena kuti mwinamwake panalidi panthaŵi yachipolowe ngati imeneyi pamene Paulo ‘anada nkhaŵa ngakhale za moyo wake’ ndi kuti Akula ndi Priskila analoŵererapo mwa njira ina yake, ‘akumapereka khosi lawo’ chifukwa cha iye.​—2 Akorinto 1:8; Aroma 16:3, 4.

“Litaleka phokoso,” Paulo mwanzeru anachokamo mumzindamo. (Machitidwe 20:1) Mosakayikira Akula ndi Priskila nawonso anatsutsidwa ndi kunyodoledwa. Kodi zimenezi zinawatayitsa mtima? Ayi. M’malo mwake, Akula ndi Priskila anapitirizabe ndi zoyesayesa zawo zachikristu molimba mtima.

Banja Lokondana Kwambiri

Ulamuliro wa Klaudiyo utatha, Akula ndi Priskila anabwerera ku Roma. (Aroma 16:3-15) Komabe, nthaŵi yomaliza pamene akutchulidwanso m’Baibulo, tikuwapeza atabwerera ku Efeso. (2 Timoteo 4:19) Monga m’Malemba ena onse amene iwo akupezekamo, mwamuna ndi mkazi wake ameneŵa akutchulidwanso pamodzi. Linali banja lokondana ndi logwirizana chotani nanga! Paulo sanathe kulingalira za mbale wokondedwayo, Akula, popanda kukumbukira kuthangata kokhulupirika kwa mkazi wake. Ndipo ndi chitsanzo chabwino chotani nanga kwa mabanja achikristu lerolino, popeza thandizo lokhulupirika la mnzake wodzipereka limalola munthu kuchita zambiri mu “ntchito ya Ambuye” ndipo, nthaŵi zina, ngakhale kuchita zambiri kuposa zimene akanatha kuchita pamene anali mbeta.​—1 Akorinto 15:58.

Akula ndi Priskila anatumikira m’mipingo ingapo yosiyanasiyana. Mofanana nawo, Akristu amakono ambiri achangu adzipereka kusamukira kumene kuli kusoŵa. Iwonso amakhala ndi chimwemwe ndi chikhutiro chimene chimadza mwa kuona zinthu za Ufumu zikukula ndi mwa kukhoza kukulitsa maubwenzi achikristu apafupi kwambiri ndi amtengo wapatali.

Mwa chitsanzo chawo chabwino kwambiri pa chikondi chachikristu, Akula ndi Priskila analandira chiyamikiro kuchokera kwa Paulo ndi ena. Koma chofunika kwambiri ndicho chakuti anadzipangira mbiri yabwino kwa Yehova iyemwini. Malemba amatitsimikiza kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—Ahebri 6:10.

Mwinamwake tilibe mwaŵi wa kudzipereka monga momwe Akula ndi Priskila anachitira, komabe tingatsanzire chitsanzo chawo chabwino kwambiri. Tidzakhala ndi chikhutiro chenicheni pamene tipereka nyonga yathu ndi moyo wathu pa utumiki wopatulika, nthaŵi zonse kusaiŵala “kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.”​—Ahebri 13:15, 16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena