Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 1/15 tsamba 18-22
  • Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Malamulo Ake Sali Olemetsa”
  • Loŵetsani Chidziŵitso Chonena za Mulungu
  • Kufika pa Miyezo ya Mulungu
  • Lemekezani Moyo ndi Mwazi
  • Kutumikira Limodzi ndi Anthu a Yehova Olinganizidwa
  • Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Chikondi Cha Mulungu Sichimatha
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 1/15 tsamba 18-22

Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

“Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”​—1 YOHANE 5:3.

1, 2. Kodi nchifukwa ninji sikodabwitsa kuti pali zimene Mulungu amafuna kwa awo ofuna kumlambira movomerezeka?

“NDINE wokhutira ndi chipembedzo changa!” Kodi zimenezo si zimene anthu amatiuza kaŵirikaŵiri? Koma kwenikweni, funso liyenera kukhala lakuti, “Kodi chipembedzo changa chimamkondweretsa Mulungu?” Inde, Mulungu ali ndi zimene amafuna kwa awo amene akufuna kumlambira movomerezeka. Kodi zimenezo ziyenera kutidabwitsa? Osati kwenikweni. Tinene kuti munali ndi nyumba yokongola, imene munaikonzetsa posachedwapa ndi ndalama zambirimbiri. Kodi mungangolola munthu aliyense kuti akhalemo? Kutalitali! Munthu aliyense amene angakhalemo adzafunikira kukwaniritsa zofuna zanu.

2 Mofananamo, Yehova Mulungu anapereka kwa anthu mudzi uno wa padziko lapansi. Mu ulamuliro wa Ufumu wake, posachedwa dziko lapansi ‘lidzakonzedwanso’​—kusandutsidwa paradaiso wokongola. Yehova adzachita zimenezi. Mwa kutayikidwa kwakukulu, iye anapereka Mwana wake wobadwa yekha kuti zimenezi zitheke. Ndithudi, Mulungu ayenera kulandira zimene amafuna kwa amene adzakhalamo!​—Salmo 115:16; Mateyu 6:9, 10; Yohane 3:16.

3. Kodi Solomo anafotokoza motani mwachidule zimene Mulungu amafuna kwa ife?

3 Kodi tingazidziŵe bwanji zimene Mulungu amazifunazo? Yehova anauzira Mfumu yanzeru Solomo kufotokoza mwachidule zimene Iye amafuna kwa ife. Atasinkhasinkha zonse zimene anali atachita​—kuphatikizapo chuma, ntchito zomanga, zoimbaimba ndi chikondi cha mwamuna ndi mkazi​—Solomo anazindikira izi: ‘Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, [n]usunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’​—Mlaliki 12:13.

“Malamulo Ake Sali Olemetsa”

4-6. (a) Kodi tanthauzo lenileni nlotani la liwu lachigiriki lotembenuzidwa “cholemetsa”? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kunena kuti malamulo a Mulungu sali olemetsa?

4 “Kusunga malamulo ake.” Zimenezo makamaka nzimene Mulungu akufuna kwa ife. Kodi iye akupempha zopambanitsa? Kutalitali! Mtumwi Yohane akutiuza kanthu kena kolimbikitsa kwambiri ponena za malamulo a Mulungu, kapena zofuna zake. Analemba kuti: ‘Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.’​—1 Yohane 5:3.

5 Liwu lachigiriki lotembenuzidwa “olemetsa” kwenikweni limatanthauza “cholemera.” Lingatanthauze chinthu chovuta kuchita kapena kukwaniritsa. Pa Mateyu 23:4, liwulo lagwiritsiridwa ntchito kufotokoza “akatundu olemera,” malamulo ndi miyambo yopangidwa ndi anthu, zimene alembi ndi Afarisi anaika pa anthu. Kodi mukumvetsa lingaliro limene mtumwi Yohane wokalambayo akupereka? Malamulo a Mulungu sali mtolo wolemetsa, ndipo sali ovuta kwambiri kwa ife kuwamvera. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:11.) M’malo mwake, pamene tikonda Mulungu, kukwaniritsa zofuna zake kumatipatsa chimwemwe. Kumatipatsa mwaŵi wamtengo wapatali wa kusonyeza chikondi chathu kwa Yehova.

6 Kuti tisonyeze chikondi chathu kwa Mulungu, tifunikira kudziŵa zenizeni zimene Mulungu amafuna kwa ife. Tsopano tiyeni tikambitsirane zinthu zisanu mwa zimene Mulungu amafuna. Pamene tikutero, kumbukirani zimene Yohane analemba kuti: ‘Malamulo a Mulungu sali olemetsa.’

Loŵetsani Chidziŵitso Chonena za Mulungu

7. Kodi chipulumutso chathu chimadalira pa chiyani?

7 Chofunika choyamba ndicho kuloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu. Talingalirani mawu a Yesu olembedwa pa Yohane chaputala 17. Chochitikacho chinali pa usiku womaliza wa moyo wa Yesu monga munthu. Yesu anali atagwiritsira ntchito nthaŵi yaikulu ya usikuwo kukonzekeretsa atumwi ake za kuchoka kwake. Anali wodera nkhaŵa za mtsogolo mwawo, mtsogolo mwawo mosatha. Atakweza maso kumwamba, anawapempherera iwo. M’vesi 3 (NW) timaŵerenga kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kumaloŵetsa kwawo chidziŵitso cha inu, Mulungu yekha woona, ndi cha iye amene munamtuma, Yesu Kristu.” Inde, chipulumutso chawo chinadalira pa “kumaloŵetsa kwawo chidziŵitso” cha onse aŵiri Mulungu ndi Kristu. Zimenezo zimagwiranso ntchito kwa ife. Kuti tipeze chipulumutso tiyenera kuloŵetsa chidziŵitso chimenecho.

8. Kodi ‘kuloŵetsa chidziŵitso’ chonena za Mulungu kumatanthauzanji?

8 Koma kodi ‘kuloŵetsa chidziŵitso’ chonena za Mulungu kumatanthauzanji? Liwu lachigiriki lotembenuzidwa “kumaloŵetsa chidziŵitso” panopa limatanthauza “kufika pakudziŵa, kuzindikira,” kapena “kumvetsetsa.” Ndiponso, onani kuti mawuwo “kumaloŵetsa chidziŵitso” akusonyeza kuti kachitidwe kameneka ndi komapitirizabe. Chotero kuloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu kumatanthauza kufika pakumdziŵa iye, osati pamwamba chabe, koma mozama​—kukhala ndi ubwenzi womvana naye. Unansi wopitiriza ndi Mulungu umatipatsa chidziŵitso chomawonjezereka nthaŵi zonse ponena za iye. Kachitidwe kameneka kangapitirize kosatha, pakuti sitidzafika pakuphunzira zonse za Yehova.​—Aroma 11:33.

9. Kodi tingaphunzirenji ponena za Yehova m’buku la chilengedwe?

9 Kodi timaloŵetsa motani chidziŵitso cha Mulungu? Pali mabuku aŵiri amene angatithandize. Loyamba ndilo buku la chilengedwe. Zinthu zimene Yehova walenga​—zamoyo ndi zopanda moyo zomwe​—zimatipatsa chidziŵitso china chake ponena za umunthu wake. (Aroma 1:20) Talingalirani zitsanzo zina. Mkokomo wa mathithi amphamvu, kuwomba kwa mafunde ofika kugombe nthaŵi ya namondwe, maonekedwe okongola a thambo la nyenyezi usiku wopanda mitambo​—kodi zinthu zotero sizimatiphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu “wolimba mphamvu”? (Yesaya 40:26) Mwana woseka poona mwana wa galu akupitikitsa mchira wake kapena mwana wa mphaka akuseŵeretsa nchinchi ya thonje​—kodi zimenezo sizimasonyeza kuti Yehova, “Mulungu wachimwemwe,” amakonda zoseketsa? (1 Timoteo 1:11) Kukoma kwa chakudya chabwino, kununkhira kwa maluŵa m’dambo, maonekedwe okongola a gulugufe, kuimba kwa mbalame m’chilimwe, kukumbatirana mwaubwenzi ndi wokondedwa​—kodi sitimazindikira ndi zinthu zimenezo kuti Mlengi wathu ali Mulungu wachikondi, amene amafuna kuti tikondwere nawo moyo?​—1 Yohane 4:8.

10, 11. (a) Kodi ndi zinthu zanji ponena za Yehova ndi zifuno zake zimene sitingathe kuziphunzira m’buku la chilengedwe? (b) Kodi Baibulo lokha limapereka mayankho pa mafunso otani?

10 Komabe, zimene tingaphunzire ponena za Yehova mwa kupenda buku la chilengedwe zili ndi polekezera. Mwachitsanzo: Kodi dzina la Mulungu ndani? Nchifukwa ninji analenga dziko lapansi naikapo munthu? Nchifukwa ninji Mulungu amalola kuipa? Kodi mtsogolo mwatisungira chiyani? Kuti tipeze mayankho pa mafunsoŵa, tiyenera kupita ku buku lina limene limapatsa chidziŵitso chonena za Mulungu​—Baibulo. M’masamba ake, Yehova amavumbula zinthu ponena za iye mwini, kuphatikizapo dzina lake, umunthu wake, ndi zifuno zake​—chidziŵitso chimene sitingachipeze kwina kulikonse.​—Eksodo 34:6, 7; Salmo 83:18; Amosi 3:7.

11 M’Malemba, Yehova amaperekanso chidziŵitso chofunika kwambiri cha anthu omwe tiyenera kuwadziŵa. Mwachitsanzo, Kodi Yesu Kristu ndani, ndipo akuchita mbali yanji m’kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova? (Machitidwe 4:12) Kodi Satana Mdyerekezi ndani? Kodi amasocheza anthu m’njira zotani? Kodi tingapeŵe motani kusochezedwa naye? (1 Petro 5:8) Mayankho opulumutsa moyo pa mafunso ameneŵa akupezeka m’Baibulo mokha.

12. Kodi mungafotokoze motani chifukwa chake kuloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu ndi zifuno zake sikuli mtolo wolemetsa?

12 Kodi kuloŵetsa chidziŵitso chotero chonena za Mulungu ndi zifuno zake kuli mtolo wolemetsa? Kutalitali! Kodi mukukumbukira mmene munamvera nthaŵi yoyamba pamene munadziŵa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, kuti Ufumu wake udzabwezeretsa Paradaiso padziko lapansi pano, kuti anapereka Mwana wake wokondedwa monga dipo la machimo athu, limodzinso ndi mfundo zina za choonadi chamtengo wapatali? Kodi simunamve ngati kukuchotsani chophimba cha kupulukira moti munayamba kuona zinthu bwinobwino? Kuloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu si mtolo wolemetsa ayi. Kuli kosangalatsa!​—Salmo 1:1-3; 119:97.

Kufika pa Miyezo ya Mulungu

13, 14. (a) Pamene tiloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu, kodi tiyenera kupanga masinthidwe otani m’moyo wathu? (b) Ndi machitachita onyansa ati amene Mulungu akufuna kuti tisiye?

13 Pamene tiloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu, timazindikira kuti tifunikira kupanga masinthidwe m’moyo wathu. Zimenezi zikutifikitsa pa chofunika chachiŵiri. Tiyenera kufika pa miyezo ya Mulungu ya khalidwe labwino ndi kulandira choonadi chake. Kodi choonadi nchiyani? Kodi zimene timakhulupirira ndi zimene timachita Mulungu ali nazo kanthu? Mwachionekere anthu ambiri lerolino saganiza zimenezo. Lipoti lofalitsidwa ndi Tchalitchi cha England mu 1995 linasonyeza kuti kukhalira limodzi popanda ukwati sikuyenera kuonedwa ngati tchimo. “Mawuwo ‘kukhala mu uchimo’ amachititsa manyazi ndipo sathandiza,” anatero bishopu wina wa tchalitchi.

14 Chotero, kodi “kukhala mu uchimo” sikulinso tchimo? Yehova akutiuza motsimikiza mmene amaonera khalidwe limenelo. Mawu ake Baibulo, amati: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Ahebri 13:4) Kugonana anthu asanaloŵe muukwati kungakhale kusali tchimo malinga ndi kuganiza kwa atsogoleri achipembedzo ndi anthu atchalitchi olekerera zinthuwo, koma ndi tchimo lowopsa pamaso pa Mulungu! Chimodzimodzi ndi chigololo, kugona ndi wachibale, ndi wofanana naye ziŵalo. (Levitiko 18:6; 1 Akorinto 6:9, 10) Mulungu amafuna kuti tisiye machitachita otero, onyansa kwa iye.

15. Kodi zofuna za Mulungu zimaphatikizapo motani mmene timachitira ndi ena ndi zimene timakhulupirira?

15 Komabe, sikokwanira kungosiya machitachita amene Mulungu amawaona kukhala auchimo. Zofuna za Mulungu zimaphatikizaponso mmene timachitira ndi anthu ena. M’banja, iye amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azikondana ndi kulemekezana. Mulungu amafuna kuti makolo asamalire zofunika zakuthupi ndi zauzimu za ana awo ndi zokhumba mtima wawo. Amauza ana kumvera makolo awo. (Miyambo 22:6; Akolose 3:18-21) Nanga bwanji za zikhulupiriro zathu? Yehova Mulungu amafuna kuti tipeŵe zikhulupiriro ndi miyambo yochokera ku malambiridwe onyenga kapena zimene zimawombana ndi ziphunzitso zomveka za Baibulo.​—Deuteronomo 18:9-13; 2 Akorinto 6:14-17.

16. Fotokozani chifukwa chake sikuli mtolo wolemetsa kufika pa miyezo ya Mulungu ya khalidwe labwino ndi kulandira choonadi chake.

16 Kodi ndi mtolo wolemetsa kwa ife kufika pa miyezo ya Mulungu ya khalidwe labwino ndi choonadi chake? Osati ngati tilingalira za mapindu ake​—maukwati mmene mwamuna ndi mkazi amakondana ndi kukhulupirirana m’malo mwa maukwati osweka chifukwa cha kusakhulupirika; nyumba mmene ana amamva kukhala okondedwa ndi ofunika kwa makolo awo m’malo mwa mabanja amene ana amamva kukhala osakondedwa, onyanyalidwa, ndi osafunika; chikumbumtima choyera ndi thanzi labwino m’malo mwa kumva liwongo ndi thupi kusakazidwa ndi AIDS kapena matenda ena opatsirana mwa kugonana. Ndithudi, zimene Yehova amafuna sizimatimanitsa kalikonse kamene tifunikira kuti tikondwere nawo moyo!​—Deuteronomo 10:12, 13.

Lemekezani Moyo ndi Mwazi

17. Kodi Yehova amauona motani moyo ndi mwazi?

17 Pamene mugwirizanitsa moyo wanu ndi miyezo ya Mulungu, mumazindikira kuti moyo ulidi wamtengo wapatali. Tiyeni tsopano tikambitsirane chinthu chachitatu chimene Mulungu amafuna. Tiyenera kulemekeza moyo ndi mwazi. Moyo ngwopatulika kwa Yehova. Uyeneradi kukhala wotero, pakuti ndiye Chitsime cha moyo. (Salmo 36:9) Inde, pakuti ngakhale moyo wa mwana wosabadwa m’mimba mwa amake ngwamtengo wapatali kwa Yehova! (Eksodo 21:22, 23) Mwazi umaimira moyo. Choncho, mwazinso uli wopatulika kwa Mulungu. (Levitiko 17:14) Motero, siziyenera kutidabwitsa kuti Mulungu amafuna kuti tione moyo ndi mwazi mmene iye amazionera.

18. Kodi kaonedwe ka Yehova ka moyo ndi mwazi kamafuna kuti tichitenji?

18 Kodi kulemekeza moyo ndi mwazi kumafuna kuti tichitenji? Pokhala Akristu, sitiika dala moyo wathu pangozi kaamba kofuna kusanguluka chabe. Timasamala kupeŵa ngozi, chotero timatsimikiza kuti galimoto ndi nyumba zathu sizili zangozi. (Deuteronomo 22:8) Sitimasuta fodya, kutafuna mtedza wa betel, kapena kugwiritsira ntchito anamgoneka kuti tisanguluke. (2 Akorinto 7:1) Chifukwa timamvera Mulungu pamene anena kuti ‘musale mwazi,’ sitilola kuikidwa mwazi m’thupi. (Machitidwe 15:28, 29) Ngakhale kuti timakonda moyo, sitimayesa kupulumutsa moyo uno mwa kuswa lamulo la Mulungu ndipo motero tikumaika pangozi chiyembekezo chathu cha moyo wosatha!​—Mateyu 16:25.

19. Fotokozani mmene timapindulira mwa kulemekeza moyo ndi mwazi.

19 Kodi ndi mtolo wolemetsa kwa ife kulemekeza moyo ndi mwazi monga zinthu zopatulika? Kutalitali! Tangolingalirani. Kodi ndi mtolo wolemetsa kupeŵa kansa ya kumapapu yochititsidwa ndi kusuta fodya? Kodi ndi mtolo wolemetsa kupeŵa kugodomala maganizo ndi thupi ndi anamgoneka oononga? Kodi ndi mtolo wolemetsa kupeŵa AIDS, hepatitis, kapena nthenda iliyonse yopatsidwa mwa kuikidwa mwazi? Mwachionekere, kupeŵa kwathu zizoloŵezi ndi machitachita oipa otero kuli kotipindulitsadi.​—Yesaya 48:17.

20. Kodi banja lina linapindula motani mwa kukhala ndi kaonedwe ka Mulungu ka moyo?

20 Talingalirani chochitikachi. Zaka zingapo zapitazo, mkazi wina Mboni wa pathupi pa miyezi ngati itatu ndi theka anayamba kukha mwazi tsiku lina madzulo ndipo anamfulumizira ku chipatala. Dokotala atampima, mkaziyo anamumva akuuza nesi wina kuti adzafunikira kuchotsa mimbayo. Podziŵa mmene Yehova amaonera moyo wa mwana wosabadwa, iye anakana zolimba kuchotsa mimba, akumauza dokotalayo kuti: “Ngati ali wamoyo, msiyeni!” Anapitiriza kukha mwazi nthaŵi zina, koma patapita miyezi ingapo anabala mwana wamwamuna wathanzi miyezi isanakwane, amene tsopano ali ndi zaka 17. Mkaziyo anati: “Tinamuuza mwana wathu zonsezi, ndipo anati ali ndi mwaŵi kuti sanatayidwe. Amadziŵa kuti kutumikira kwathu Yehova ndiko kokha kwachititsa kuti akhalepobe ndi moyo.” Kunena zoona, kuona moyo mmene Mulungu amauonera sikunali mtolo wolemetsa pa banjali!

Kutumikira Limodzi ndi Anthu a Yehova Olinganizidwa

21, 22. (a) Kodi Yehova amafuna kuti timtumikire limodzi ndi yani? (b) Kodi anthu a Mulungu olinganizidwa angazindikiridwe motani?

21 Sitili tokha popanga masinthidwe ofunika kuti moyo wathu ugwirizane ndi miyezo ya Mulungu. Yehova ali nawo anthu ake padziko lino lapansi, ndipo amafuna kuti timtumikire limodzi nawo. Zimenezi zikutifikitsa pa chofunika chachinayi. Tiyenera kutumikira Yehova limodzi ndi gulu lake lotsogozedwa ndi mzimu.

22 Koma kodi tingawadziŵe motani anthu olinganizidwa a Mulungu? Molingana ndi miyezo yoperekedwa m’Malemba, iwo ali ndi chikondi chenicheni pakati pawo, amalemekeza Baibulo kwambiri, amalemekeza dzina la Mulungu, amalalikira za Ufumu wake, ndipo sali mbali ya dziko loipali. (Mateyu 6:9; 24:14; Yohane 13:34, 35; 17:16, 17) Pali gulu limodzi lokha lachipembedzo padziko lino lapansi limene lili ndi zizindikiro zonsezi za Chikristu choona​—Mboni za Yehova!

23, 24. Kodi tingachitire chitsanzo motani kusonyeza kuti sikuli mtolo wolemetsa kutumikira Yehova limodzi ndi anthu ake olinganizidwa?

23 Kodi ndi mtolo wolemetsa kutumikira Yehova limodzi ndi anthu ake olinganizidwa? Kutalitali! M’malo mwake, ndi mwaŵi wamtengo wapatali kukhala ndi chikondi ndi chichirikizo cha banja la padziko lonse la abale ndi alongo achikristu! (1 Petro 2:17) Tayerekezerani kuti mwapulumuka ngozi ya chombo chomwe chasweka ndipo muli m’madzi, mukulimbikira kusambira. Pamene muona kuti mukulephera, mungoona dzanja likufika kwa inu kuchokera m’bwato lopulumutsira. Inde, alipo opulumuka ena! M’bwato lopulumutsiralo, mulandizana kupalasa ndi ena kulinga kumtunda, mukumatola opulumuka ena m’njira.

24 Kodi sitili mumkhalidwe umodzimodzi? Tavuulidwa “m’madzi” angozi a dziko loipali kuloŵa “m’bwato lopulumutsira” la gulu la Yehova la padziko lapansi. Mmenemo, timatumikira mogwirizana pamene tikupalasira “kumtunda” wa dziko latsopano lolungama. Ngati zovuta za moyo zititopetsa m’njira, timayamikira chotani nanga chithandizo ndi chitonthozo cha mabwenzi enieni achikristu!​—Miyambo 17:17.

25. (a) Kodi tili ndi thayo lotani kwa awo omwe adakali “m’madzi” a dziko loipali? (b) Kodi ndi chofuna cha Mulungu chotani chomwe tidzakambitsirana m’nkhani yotsatirapo?

25 Koma bwanji ponena za ena​—aja oona mtima omwe adakali “m’madzi”? Tili ndi thayo la kuwathandiza kuloŵa m’gulu la Yehova, si choncho nanga? (1 Timoteo 2:3, 4) Amafunikira chithandizo kuti adziŵe zimene Mulungu amafuna. Zimenezi zikutifikitsa pa chachisanu pa zimene Mulungu amafuna: Tiyenera kukhala alaliki okhulupirika a Ufumu wake. Zoloŵetsedwamo zake tidzakambitsirana m’nkhani yotsatira.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nchifukwa ninji malamulo a Mulungu sali olemetsa?

◻ Kodi timaloŵetsa motani chidziŵitso chonena za Mulungu?

◻ Kodi nchifukwa ninji sikuli mtolo wolemetsa kufika pa miyezo ya Mulungu ya khalidwe labwino ndi kulandira choonadi chake?

◻ Kodi kaonedwe ka Mulungu ka moyo ndi mwazi kamafuna kuti tichitenji?

◻ Kodi Mulungu amafuna kuti timtumikire limodzi ndi yani, ndipo amenewo amazindikiridwa motani?

[Zithunzi patsamba 18]

Timaphunzira za Yehova m’buku la chilengedwe ndi m’Baibulo

[Mawu a Chithunzi]

Ng’ona: By courtesy of Australian International Public Relations; chimbalangondo: Safari-Zoo of Ramat-Gan, Tel Aviv

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena