Kodi Mumaopa Kukhulupirira Ena?
‘KULIBE amene ndingalankhule naye. Anthu sadzamva. Ngotanganidwa kwambiri ndi mavuto awo. Alibe nthaŵi yomvetsera kwa ine.’ Ambiri amaganiza zimenezo, choncho amangokhala osanena kanthu. Ena akawafunsa za umoyo, iwo kaŵirikaŵiri amafuna kufotokoza, koma amalephera. Satha kulankhula momasuka ayi.
Zoona, alipo anthu amene safuna ena kuwathandiza. Komabe, ambiri amalifunitsa thandizo koma amaopa kuulula malingaliro awo aumwini, mmene akumvera, ndi zowachitikira. Kodi inunso mulipo pa ameneŵa? Kodi nzoona kuti kulibiretu amene mungamkhulupirire?
Kuwamvetsa Manthawo
M’dziko lerolino muli mkhalidwe wa kusakhulupirirana. Achichepere samauza zinthu makolo awo. Makolo samalankhulana. Ndi oŵerengeka omwe amafuna kulankhula ndi audindo. Polephera kudalira ena, ena amayamba moŵa, anamgoneka, kapena moyo wosadzisunga pofuna kuiŵala mavuto awo.—Miyambo 23:29-35; Yesaya 56:12.
Chidaliro mwa okhala ndi udindo, monga atsogoleri achipembedzo, madokotala, akatswiri ochiritsa popanda mankhwala, ndi aphunzitsi, chawonongeka chifukwa cha kusaona mtima ndi chisembwere zimene zikuvumbuluka kosaleka. Mwachitsanzo, ziŵerengero zimasonyeza kuti oposa ngati 10 peresenti ya atsogoleri achipembedzo amachita chisembwere. “Owononga kukhulupirirana” ameneŵa, akutero mlembi wina, “amakumba mapompho ndi mipata m’maunansi a anthu.” Kodi zimenezi zimaikhudza motani mipingo yawo? Zimawononga kukhulupirirana.
Kunyonyotsoka kwa makhalidwe kofala kwabutsanso mavuto m’banja, kufika poti mabanja osagwirizana angokhala ponseponse. Kale panyumba panali malo olerera ana. Lero nyumba zambiri zangokhala ngati pomwetsera galimoto mafuta panthaŵi ya chakudya. Pamene mwana akulira m’banja lopanda “chikondi chachibadwidwe,” zimene zimachitika kaŵirikaŵiri nzakuti amalephera kukhulupirira ena atakula.—2 Timoteo 3:3.
Ndiponso, pamene mikhalidwe ya dziko ikuipiraipira, zinthu zimene zingakhale zosautsa mtima zimatichitikira kambiri. Mumkhalidwe wonga umenewo, mneneri Mika analemba kuti: “Musatama [“musakhulupirire,” NW] bwenzi loyanja.” (Mika 7:5) Mungamve mofananamo wina atakukhumudwitsani pang’ono, ataulula chinsinsi, kapena patachitika choopsa china choika moyo wanu pangozi. Mumayamba kuvutika kukhulupiriranso ena ndipo mtima wanu umakwinyirira, ndiyeno tsiku ndi tsiku mumalola mtima wanu kukupingani. (Yerekezerani ndi Salmo 102:1-7.) Zoona, khalidwe lotero lingakuthandizeni kupitiriza ndi moyo wanu, koma “zoŵaŵa za m’mtima” zimakulandani chimwemwe chenicheni chilichonse m’moyo. (Miyambo 15:13) Choonadi nchakuti, kuti mukhale wolimba mwauzimu, mumtima, m’maganizo, ndi kuthupi, muyenera kugwetsa chopingacho ndi kuyamba kukhulupirira ena. Kodi zimenezi zitheka? Inde.
Nchifukwa Ninji Muyenera Kugwetsa Chopingacho?
Kudalira ena kumasangulutsa mtima wosweka. Zimenezi ndizo zinachitikira Hana. Anali wokwatiwa bwino, ndi nyumba yachisungiko, koma anali wopsinjika mtima kwambiri. Ngakhale anali ndi “mtima woŵaŵa,” iye mwanzeru ‘anapemphera kwa Yehova’ ndi mphamvu moti milomo yake inali kutukula ngakhale anali kupemphera chamumtima. Inde, anadalira Yehova. Ndiyeno anaululira Eli woimira Mulungu zamumtima mwake. Kodi panatsatira zotani? “[Hana] anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.”—1 Samueli 1:1-18.
Mafuko ochuluka adziŵa za mapindu ake a kuululirana zamumtima. Mwachitsanzo, kuuzana malingaliro ndi kusimbirana zochitika ndi aja amene anakhalapo m’mikhalidwe yonga yanu kungakupindulitseni. Ofufuza akuti: “Kusunga zamumtima kumadwalitsa—tifunika kuululirana zamumtima kuti maganizo athu akhale bwino.” Zofufuza zomawonjezereka za sayansi zimatsimikiza choonadi cha mwambi wouziridwa wakuti: “Wopanduka [“wodzipatula,” NW] afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”—Miyambo 18:1.
Ngati sulankhula kwa ena, angakuthandize bwanji? Pamene kuli kwakuti Yehova Mulungu atha kudziŵa za mumtima wa munthu, abanja lanu ndi mabwenzi sangazidziŵe zolingilira za maganizo anu ndi za mtima wanu—pokhapokha mutawauza. (1 Mbiri 28:9) Pamene vutolo nlakuti munthu waswa lamulo la Mulungu, kulephera kuulula nkhaniyo kumangoipitsiratu zinthu.—Miyambo 28:13.
Indetu, mapindu a kuululira ena nsautso apambaniratu kusweka mtima kumene kungakhalepo. Ayi, zimenezo sizitanthauza kuti tiyenera kuulula nkhani zaumwini mosasamala. (Yerekezerani ndi Oweruza 16:18; Yeremiya 9:4; Luka 21:16.) “Alipo mabwenzi okonda kuswana okhaokha,” Miyambo 18:24, NW, imachenjeza, komanso imawonjeza kuti: “Lilipo bwenzi loumirira kwambiri kuposa ndi mbale.” Kodi mungalipeze kuti bwenzi lotero?
Kukhulupirira Banja Lanu
Ngati muli ndi vuto, kodi mwayesa kukambitsirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu, kapenanso ndi makolo anu? “Zimene mavuto ambiri amafuna ndizo kukambitsirana zonse mwatsatanetsatane basi,” akuvomereza phungu wina wachidziŵitso. (Miyambo 27:9) Amuna achikristu amene ‘akonda akazi awo monga adzikonda okha,’ akazi amene ‘amamvera amuna awo,’ ndiponso makolo amene amasamala thayo lawo lopatsidwa ndi Mulungu la ‘kulera ana awo ndi kuwongolera maganizo kwa Yehova’ adzayesetsa kukhala omvetsera achifundo ndi aphungu othandiza. (Aefeso 5:22, 33; 6:4, NW) Ngakhale analibe mkazi kapena ana aumunthu, Yesu analitu chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi!—Marko 10:13-16; Aefeso 5:25-27.
Bwanji ngati vutolo simungathe kulisamalira m’banja? Mumpingo wachikristu, sitili tokha. “Afooka ndani wosafooka inenso?” anatero mtumwi Paulo. (2 Akorinto 11:29) Analangiza kuti: “Nyamuliranani zothodwetsa.” (Agalatiya 6:2; Aroma 15:1) Pakati pa abale athu auzimu ndi alongo, mosakayika tingapeze ambiri amene ‘amakhala mbale panthaŵi ya tsoka.’—Miyambo 17:17, NW.
Kukhulupirira Ena Mumpingo
M’mipingo yoposa 80,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse, muli amuna odzichepetsa amene ali “othandizana nacho chimwemwe chanu.” (2 Akorinto 1:24) Ameneŵa ndiwo akulu. “Munthu,” akutero Yesaya, “adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” Akulu amakalimira kukhala otero.—Yesaya 32:2; 50:4; 1 Atesalonika 5:14.
Akulu amafitsa zofunika za m’Malemba ‘asanaikidwe ndi mzimu woyera.’ Kudziŵa zimenezi kudzalimbitsa chidaliro chanu mwa iwo. (Machitidwe 20:28; 1 Timoteo 3:2-7; Tito 1:5-9) Zimene mukambitsirana ndi mkulu zidzakhalabe zachinsinsi ndithu. Ziyeneretso zake zimaphatikizapo kukhala wokhulupirika.—Yerekezerani ndi Eksodo 18:21; Nehemiya 7:2.
Akulu mumpingo “alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera.” (Ahebri 13:17) Kodi zimenezi sizikukusonkhezerani kuika chidaliro chanu mwa amuna ameneŵa? Mwachibadwa, si akulu onse omwe apambana pamikhalidwe imodzimodzi. Ena angaoneke kukhala ofikirika, okoma mtima, kapena achifundo kwambiri kuposa ena. (2 Akorinto 12:15; 1 Atesalonika 2:7, 8, 11) Bwanji osabenthulira mkulu amene muli womasuka naye?
Amuna ameneŵa sali akatswiri olipidwa. M’malo mwake, ali “mphatso mwa amuna,” (NW) operekedwa ndi Yehova kuti akuthandizeni. (Aefeso 4:8, 11-13; Agalatiya 6:1) Motani? Mwa kugwiritsira ntchito Baibulo mwaluso, iwo adzagwiritsira ntchito mphamvu yake yochiritsa pamkhalidwe wanu wa inu mwini. (Salmo 107:20; Miyambo 12:18; Ahebri 4:12, 13) Adzapemphera nanu ndi kukupemphererani. (Afilipi 1:9; Yakobo 5:13-18) Thandizo la aphungu achikondi otero lingathandize kwambiri kuchiritsa mzimu wosweka ndi kubwezeretsa mtendere wa maganizo.
Mmene Mungakhalire ndi Maunansi Okhulupirirana
Kupempha thandizo, uphungu, kapena kungoti wina amvetsere sikutanthauza kuti ndinu wofooka kapena mwalephera. Kwangokhala kuvomereza moona mtima kuti ndife opanda ungwiro ndi kuti kulibe munthu amene ali ndi mayankho onse. Inde, phungu wamkulu koposa ndi wodalirika amene tili naye ndiye Atate wathu wakumwamba Yehova Mulungu. Tikuvomerezana ndi wamasalmo yemwe analemba kuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza.” (Salmo 28:7) M’pemphero ‘tingatsanulire mtima wathu’ wonse kwa iye panthaŵi iliyonse, ndi chidaliro chakuti adzatimva ndi kutisamalira.—Salmo 62:7, 8; 1 Petro 5:7.
Koma kodi mungayambe motani kukhulupirira akulu ndi ena mumpingo? Choyamba, tadzipendani inu eni. Kodi muli ndi zifukwa zenizeni zoopera? Kodi mukukayikira zolinga za ena? (1 Akorinto 13:4, 7) Kodi pali njira yochepetsera kukhumudwa? Inde. Motani? Yesani kuwadziŵa bwino ena pazochitika zauzimu. Lankhulani nawo pamisonkhano ya mpingo. Chitani ntchito ya kunyumba ndi nyumba pamodzi. Monga ulemu, pamakhala zimene munthu amachita kuti wina amkhulupirire. Chotero lezani mtima. Mwachitsanzo, pamene mumdziŵa mbusa wauzimu, chidaliro chanu mwa iye chidzakula. Vumbulani nkhaŵa zanu pang’onopang’ono. Ngati achita moyenera, mwachifundo, ndi mwanzeru, mwina mungayese kuulula zambiri.
Olambira nawo Yehova, makamaka akulu achikristu, amayesetsa kutsanza mikhalidwe yabwino ya Mulungu pamaunansi awo wina ndi mnzake. (Mateyu 5:48) Zimenezi zimadzetsa mkhalidwe wokhulupirirana mumpingo. Mkulu wina wakalekale akuti: “Abale ayenera kudziŵa chinthu chimodzi: Kaya munthu achite zotani, mkulu samataya chikondi chake chachikristu pa iye. Mwina sangakondwere ndi zimene zinachitika, koma amakondabe mbale wake ndipo afuna kumthandiza.”
Choncho palibe chifukwa choganizira kuti muli nokhanokha ndi vuto lanu. Lankhulani kwa munthu ‘wauzimu’ amene angakuthandizeni kunyamula zothodwetsa zanu. (Agalatiya 6:1) Kumbukirani kuti “nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu,” koma “mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.”—Miyambo 12:25; 16:24.
[Bokosi patsamba 26]
Mkristu aliyense angapemphedwe kuthandiza wachibale, bwenzi, kapena mbale wauzimu pavuto lake. Kodi mudziŵa mmene mungathandizire?
Phungu Wogwira Mtima
ngwofikirika: Mateyu 11:28, 29; 1 Petro 1:22; 5:2, 3
amasankha mkhalidwe woyenera: Marko 9:33-37
amayesa kumvetsa vutolo: Luka 8:18; Yakobo 1:19
samakwiya: Akolose 3:12-14
amathandiza kupirira kupsinjika mtima: 1 Atesalonika 5:14; 1 Petro 3:8
amadziŵa zopereŵera zake: Agalatiya 6:3; 1 Petro 5:5
amapereka uphungu wolunjika: Salmo 19:7-9; Miyambo 24:26
amasunga chinsinsi: Miyambo 10:19; 25:9