Olengeza Ufumu Akusimba
Kufesa Mbewu za Ufumu pa Mpata Uliwonse
MAWU a Mulungu Baibulo, amalimbikitsa khama. Mfumu Solomo anati: “Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziŵiri zidzakhala bwino.”—Mlaliki 11:6.
Pa mpata uliwonse woyenerera, Mboni za Yehova zimafesa “mbewu” mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. M’maiko ndi m’zilumba zoposa 230 iwo akupitiriza ‘osaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.’ (Machitidwe 5:42) Zokumana nazo zotsatirazi zikusonyeza mmene Mboni za Yehova ‘sizikulekerera manja awo kupumula’ pa ntchito yolalikira.
◻ Mu Republic of Cape Verde, mmodzi wa Mboni za Yehova anali kudutsa pa ndende ali mu utumiki wake wa m’munda. M’bwalo la ndendeyo, akaidi anali kupumula mumtengo. Ataona Mboniyo pansi, akaidiwo anafuula kupempha magazini. Mboniyo inamangirira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! angapo ku mwala nkuwaponya kudumphitsa linga la ndendeyo. Zotulukapo za chidwi choyamba chimenechi, maphunziro 12 a Baibulo anayambidwa. Atatu mwa akaidiwo anapatulira miyoyo yawo kwa Mulungu ndipo anadzipereka mu ubatizo wa m’madzi. Mmodzi wa akaidi amenewo wakhala akutumikira monga mlaliki wanthaŵi zonse, kapena kuti mpainiya, koposa chaka tsopano. Komabe, nanga, ndi motani mmene amachitira utumiki wakumunda m’ndendemo? Choyamba ndendeyo inagaŵidwa m’magawo. Ndiye magawowo amagaŵiridwa kwa Mboni zitatuzo ndipo zimalalikira chipinda ndi chipinda. Alengezi a Ufumu ameneŵa amakulitsa chidwi mwa anthu monga momwe Mboni za Yehova zina kuzungulira dziko lonse zimachitira—mwa kupanga maulendo obwereza. Komabe, chosiyana chimodzi, ndicho nthaŵi zimene maphunziro a Baibulo amachitidwa. M’malo mwa kuphunzira Baibulo kamodzi kapena kaŵiri pamlungu kwa ola limodzi kapena kuposerapo, akaidi ena amaphunzira tsiku lililonse! Ndiponso, Mbonizo zapatsidwa chilolezo ndi mkulu wa ndendeyo kuchita misonkhano yonse yampingo mkati mwa ndendemo.
◻ Mkazi wina ku Portugal anatenga zofalitsa za Watch Tower za agogo ake atamwalira. Poti iye sanali mmodzi wa Mboni za Yehova, analibe chidwi chosunga mabuku. Komabe, sanafune kuŵawononga. Tsiku lina anauza mmodzi wa Mboni za Yehova yemwe anafika kwa iye mu utumiki wake wa kunyumba ndi nyumba za laibulaleyo. Mboniyo inamfunsa ngati anadziŵa kalikonse za ubwino weniweni wa laibulaleyo. Mkaziyo anayankha kuti: “Kwenikweni, sindidziŵa ubwino wake weniweni, koma kodi ndingadziŵe motani?” Mkaziyo anavomera phunziro la Baibulo, ndipo posapita nthaŵi anadziŵa kufunika kwa laibulale ya agogo akeyo. Tsopano iyenso ndi Mboni ya Yehova yobatizidwa. Ndiponso, mwana wake wamkazi ndi bwenzi lapafupi la banjalo akuphunzira Baibulo. Mabukuwo anakhala cholowa chamtengo wapatali chotani nanga!