Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/1 tsamba 29
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Nthaŵi ya Kudikira
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Kukhalapo kwa Khristu Kumatanthauza Chiyani kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/1 tsamba 29

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi tinganene kuti kamvedwe kathu katsopano ka “mbadwo” pa Mateyu 24:34 kakupereka lingaliro lakuti mapeto a dongosolo la zinthu ali kutali kwambiri?

Kutalitali. M’malo mwake, kamvedwe katsopano pa nkhaniyi kayenera kutithandiza kuŵayembekezera kwambiri. Motani?

Chabwino, monga momwe Nsanja ya Olonda ya November 1, 1995 inanenera, Yesu anagwiritsira ntchito mawu akuti “mbadwo uwu” ponena za mtundu wa anthu oipa okhalako panthaŵi imodzimodziyo. (Mateyu 11:7, 16-19; 12:39, 45; 17:14-17; Machitidwe 2:5, 6, 14, 40) Kwenikweni sanali kunena za nthaŵi yakutiyakuti yoyambika patsiku lakutilakuti.

Ndipotu “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” m’kope limodzimodzilo la Nsanja Ya Olonda, anagogomezera zinthu ziŵiri zofunika: “Mbadwo wa anthu sungaonedwe kukhala nyengo ya nthaŵi ya chiŵerengero chakutichakuti cha zaka” ndi “Anthu a mbadwo umodzi amakhala ndi moyo kwa nyengo yofupikirapo.”

Nthaŵi zambiri timagwiritsira ntchito “mbadwo” mwanjira imeneyo. Mwachitsanzo, tinganene kuti: ‘Asilikali a mbadwo wa Napolèon sanadziŵe za ndege ndi mabomba a atomu.’ Kodi tingakhale tikunena za asilikali amene anabadwa chaka chimodzi ndi Napoléon? Kodi tingakhale tikutanthauza kokha asilikali a ku France amene anafa Napoléon asanafe? Iyayi; ndipo sitingakhale tikuyesa kukhazikitsa zaka zoikika mwa kugwiritsira ntchito “mbadwo” mwa njira imeneyo. Komabe, tingakhale tikunena za nyengo yofupikirapo, m’nthaŵi ya Napoléon, osati zaka mazana ambiri kuyambira m’nthaŵi ya Napoléon ndi mtsogolo mwake.

Ndi mmenenso kalili kamvedwe kathu ka zimene Yesu ananena mu ulosi wake woperekedwa pa Phiri la Azitona. Kukwaniritsidwa kwa mbali zosiyanasiyana za ulosi umenewo kumasonyeza kuti mapeto adongosolo lino ayandikira. (Mateyu 24:32, 33) Kumbukirani kuti malinga ndi Chivumbulutso 12:9, 10, Satana anaponyedwa kudziko lapansi Ufumu wakumwamba wa Mulungu utakhazikitsidwa mu 1914. Chivumbulutso chimawonjezera kunena kuti tsopano Satana ali ndi udani waukulu. Nchifukwa ninji? Chifukwa akudziŵa kuti ‘kamtsalira kanthaŵi.’​—Chivumbulutso 12:12.

Chotero kunali koyenera kuti Nsanja ya Olonda ya November 1 inali ndi kamutu kakuti: “Dikirani”! Ndime yotsatira inanena bwino lomwe kuti: “Sitifunikira kudziŵa nthaŵi yeniyeni ya zochitikazo. M’malo mwake, tiyenera kulimbikira kukhala odikira, tikumakulitsa chikhulupiriro cholimba, ndi kutanganidwa mu utumiki wa Yehova​—osati kuŵerengera masiku.” Ndiyeno inagwira mawu a Yesu akuti: “Yang’anirani, dikirani, . . . pakuti simudziŵa nthaŵi yake. Dikirani. Chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.”​—Marko 13:33, 37.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena