Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/1 tsamba 30-31
  • Chikhulupiriro cha Makolo Chifupidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikhulupiriro cha Makolo Chifupidwa
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchita mwa Chikhulupiriro
  • Mwanayo Apezedwa
  • Phunziro kwa Ife
  • Mose Anasankha Kuti Azilambira Yehova
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Chinthu Choposa Chuma cha Aigupto
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Mose Anali Munthu Weniweni Kapena Wongopeka?
    Galamukani!—2004
  • M’mene Mose Anapulumutsidwira
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/1 tsamba 30-31

Anachita Chifuniro cha Yehova

Chikhulupiriro cha Makolo Chifupidwa

AISRAYELI anali kusangalala kwambiri mwana wa mwamuna atabadwa. Zinkatanthauza kuti fuko lidzapitirizabe ndi kuti minda idzakhalabe ya banjalo. Koma pafupifupi chaka cha 1593 B.C.E., Ahebri ankaona kubala mwana wamwamuna monga themberero osati dalitso ayi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Farao wa ku Aigupto, poopa kuchulukitsa kwa Ayuda m’dziko lake, analamula kuti ana awo onse aamuna akabadwa aziphedwa.​—Eksodo 1:12, 15-22.

Pa nthaŵi ya kuyesa kupululutsa fuko mwa nkhalwe kumeneku, mpamene Amramu ndi Yokobedi, banja lachihebri, linabala mwana wamwamuna wokongola. Nkwapafupi kuganiza mmene chimwemwe chawo chinazimiririkira ndi mantha pamene anakumbukira lamulo la Farao. Komabe, pamene Amramu ndi Yokobedi anaona mwana wawoyo, molimba mtima analingalira zomsunga, mosasamala kanthu za zotsatirapo.​—Eksodo 2:1, 2; 6:20.

Kuchita mwa Chikhulupiriro

Miyezi itatu, Amramu ndi Yokobedi anabisa mwana wawo. (Eksodo 2:2) Komabe, izi zinali zangozi, chifukwa Ahebri ndi Aigupto amakhala moyandikana. Aliyense wopezeka akuyesa kukhotetsa lamulo la Farao mosakayikira akanapatsidwa chilango cha imfa​—ndipo khandalo likanayenera kuphedwanso. Tsopano, nchiyani chimene makolo odzipereka ameneŵa anayenera kuchita kuti asunge mwana wawo ndi kuti iwonso akhale amoyo?

Yokobedi anasokhanitsa gumbwa. Gumbwa ndi chomera cholimba, chofanana ndi nsungwi, ndipo phesi lake lili ndi mbali zitatu zaukulu monga chala. Utali wake ungafike mamita asanu ndi imodzi. Aigupto amagwiritsa ntchito chomera chimenechi kupanga mapepala, mphasa, mitanga, nsapato, ndiponso ngalawa zopepuka.

Yokobedi anapanga kabokosi ka gumbwa kakakulu mokwanira kuikamo mwana wakeyo. Kenaka anakapaka phula ndi nkhunga kuti akalimbitse ndiponso kuti musamaloŵe madzi. Ndiye Yokobedi anaikamo khandalo ndi kukaika pakati pa mabango m’mphepete mwa mtsinje wa Nile.​—Eksodo 2:3.

Mwanayo Apezedwa

Mwana wamkazi wa Yokobedi, Miriamu, amaima chapafupi kuti aziona chomwe chidzachitika. Ndiye mwana wamkazi wa Farao anabwera ku Nile kudzasamba.a Mwina Yokobedi ankadziŵa kuti mwana wamkazi wa mfumuyo ankakonda malo ameneŵa ndiye anasiya dala bokosilo poti likhoza kuonedwa msanga. Kaya zinalidi choncho, mwana wa Farao mwamsanga anakaona kabokosiko pakati pa mabango, ndipo anauza mmodzi wa adzakazi ake kukakatenga. Pamene anaona khanda likulira mkatimo, anamva chifundo. Ndipo anazindikira kuti ameneyo ndi mwana wa Mhebri. Koma, nkwanji kuti aphe mwana wokongolayo? Kuonjezera pa chifundo chachibadwa, mwina chimene chinasonkhezera mwana wa Farao ndi chikhulupiriro cha Aigupto chakuti, kuti uloledwe kupita kumwamba zimadalira pa zomwe unachita panthaŵi yomwe unali moyo.b​—Eksodo 2:5, 6.

Miriamu, yemwe amayang’ana ataima patali, anafikira mwana wamkazi wa Farao. “Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?” iye anafunsa. Ndipo mwana wamkazi wa Mfumu anayankha nati: “Pita.” Miriamu anathamangira kwa amayi ake. Posapita nthaŵi, Yokobedi anaima pamaso pa mwana wa Farao. “Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye,” mwana wa Mfumuyo anatero, “ndidzakupatsa mphotho yako.” Nkotheka kuti panthaŵiyi mwana wa Farao anali atazindikira kuti Yokobedi ndiwo anali amake a khandalo.​—Eksodo 2:7-9.

Yokobedi anasunga mwana wake mpaka ataleka kuyamwa.c Izi zinapereka mpata wabwino wakuti amphunzitse za Mulungu woona, Yehova. Ndiye Yokobedi anabwera naye mwanayo kwa mwana wamkazi wa Farao, yemwe anatcha mnyamatayo Mose, kutanthauza kuti “ndinamvuula m’madzi.”​—Eksodo 2:10.

Phunziro kwa Ife

Amramu ndi Yokobedi anagwiritsira ntchito mpata wochepa womwe anali nawo kuphunzitsa mwana wawo malamulo achipembedzo choona. Leronso makolo ayenera kuchita mofananamo. Ndithudi, ayenera kuti azitero zivute zitani. Satana Mdyerekezi “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Iye angakonde kulikwira achinyamata​—anyamata ndi atsikana​—omwe akufuna kudzakhala atumiki a Yehova abwino. Iye sawamvera chisoni! Pozindikira izi, makolo anzeru amaphunzitsa ana awo kuopa Mulungu woona, Yehova.​—Miyambo 22:6; 2 Timoteo 3:14, 15.

Pa Ahebri 11:23, khama la Amramu ndi Yokobedi pobisa mwana wawo miyezi itatu yoyamba ya moyo wake zikunenedwa kukhala chikhulupiriro. Makolo ameneŵa oopa Mulungu anasonyeza chidaliro m’mphamvu za Yehova zopulumutsa mwa kukana kutaya mwana wawo, ndipo chifukwa cha chimenechi anadalitsidwa. Ifenso tiyenera kutsatira mosamalitsa malamulo ndi mapulinsipulo a Yehova, tili ndi chikhulupiriro kuti zirizonse zomwe Yehova alola kutigwera potsiriza zidzakhala bwino kwa ife ndi kutipatsa chimwemwe chosatha.​—Aroma 8:28.

[Mawu a M’munsi]

a Aigupto ankalambira mtsinje wa Nile monga mulungu wa kubala. Ankakhulupirira kuti madzi ake anali ndi mphamvu zobalitsa ndipo ngakhale kutalikitsa moyo.

b Aigupto ankakhulupirira kuti munthu akafa mzimu wake umakatsimikizira pamaso pa Osiris kuti “Sindinazunze munthu aliyense,” “Sindinakanize mwana kuyamwa,” ndiponso “Ndinapatsa mkate kwa wanjala ndi madzi kwa waludzu.”

c Nthaŵi zakale, ana ambiri amayamwa nthaŵi yaitali kuposa mmene zilili masiku ano. Samueli ayenera kuti anali ndi zaka zitatu pamene analeka kuyamwa, ndipo Isake anali pafupifupi ndi zaka zisanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena