Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/15 tsamba 4-8
  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Kuti Munthu Akafa Amabadwanso m’Moyo Wina?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Kuti Munthu Akafa Amabadwanso m’Moyo Wina?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziŵa Kumene Chinachokera ndi Maziko Ake
  • Kodi “Mzimu” Sumafa?
  • Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Amavutika?
  • Mtsogolo Mwamtendere
  • Kodi Mawu a Mulungu Amaphunzitsa za Kubadwanso kwa Moyo?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Munthu Akamwalira Amakabadwanso Kwinakwake?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Moyo wa Pambuyo pa Imfa—Kodi Baibulo Limanenapo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Mumakhulupirira Kuti Musanabadwe Munakhalapo ndi Moyo Kwinakwake?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/15 tsamba 4-8

Kodi Muyenera Kukhulupirira Kuti Munthu Akafa Amabadwanso m’Moyo Wina?

MGIRIKI wafilosofi Plato anati mwamuna ndi mkazi amafunana chifukwa chakuti anali onse m’moyo wina. Anakhulupirira kuti thupi litafa, “mzimu” pokhala wosafa umasamukira komwe amati “malo a mtundu wake weniweni.” Umakhala kumeneko popanda thupi nthaŵi yaitali ndithu, ukuganiza za mitundu yosiyanasiyana. Utabadwiranso m’thupi lina, mzimuwo umakumbuka pang’ono malo a mtundu wake ndi kuulakalaka. Malinga ndi Plato, anthu amakondana poona mwa wokondedwa wawoyo mtundu wabwino wa kukongola komwe amakumbuka pang’ono ndi kumene amafuna.

Kudziŵa Kumene Chinachokera ndi Maziko Ake

Chiphunzitso chakuti munthu akafa amabadwanso m’moyo wina chimafuna kuti mzimu usafe paimfa. Chotero, tingati kukhulupirira kuti munthu akafa amabadwanso m’moyo wina kunachokera kwa anthu kapena mitundu imene inali kukhulupirira zimenezo. Chifukwa cha zimenezi, ena amaganiza kuti chinachokera ku Igupto wakale. Ena amati chinayambira ku Babulo wakale. Kuti chipembedzo chachibabulo chitchuke, ansembe ake anayambitsa chiphunzitso chakuti “mzimu” umasamuka paimfa. Motero anatha kunena kuti ngwazi zawo zachipembedzo anali makolo awo omveka omwe anabadwanso, ngakhale anali atamwalira kale kwambiri.

Komabe, chikhulupiriro chakuti munthu akafa amabadwanso m’moyo wina chinafala kwambiri ku India. Ahindu anzeru anali kuvutika maganizo ndi kuipa kumene kuli padziko lonse ndi mavuto a anthu. ‘Kodi zimenezi zikugwirizana bwanji ndi lingaliro lakuti Mlengi ali wolungama?’ iwo anafunsa. Anayesa kuthetsa kuwombana kwa chilungamo cha Mulungu ndi masoka osadziŵika ndi chisalungamo cha m’dziko. M’kupita kwa nthaŵi, anapanga “lamulo la karma,” lamulo lakuti chochitika chimakhala ndi chochititsa​—‘chilichonse chimene munthu afesa, adzatuta chomwecho.’ Anakonza mpambo watsatanetsatane wosonyeza zabwino ndi zoipa zomwe munthu wamoyo amachita zimene angalandirirepo mphotho kapena chilango m’moyo wotsatira.

Liwu loti “karma” limangotanthauza “ntchito.” Ahindu amati munthu amakhala ndi karma yabwino ngati atsatira mwambo wa kakhalidwe ndi wachipembedzo koma kuti amakhala ndi yoipa ngati satero. Ntchito zake, kapena kuti karma, ndiyo imamsankhira za mtsogolo mwake pakubadwanso kulikonse kotsatizana. “Anthu onse amabadwa yense ndi mtima wakewake, umene zinakonzeratu ntchito zake asanabadwe pamene anali ndi moyo kwina, ngakhale kuti thupi lawo limatenga la makolo,” akutero wafilosofiyo Nikhilananda. “[Choncho] munthu amadzikonzera yekha zamtsogolo, amalinganiza yekha zimene zidzamchitikira.” Koma cholinga chachikulu nchakuti akamasuke ku kachitidwe kameneka komabadwanso kuti akafike ku Brahman​—mtundu weniweni. Amakhulupirira kuti munthu amafika kumeneko mwa kulimbikira ndi makhalidwe abwino ndi kukhala ndi nzeru zapadera zachihindu.

Chotero maziko a chiphunzitso chakuti munthu akafa amabadwanso m’moyo wina ndiwo chiphunzitso chakuti “mzimu” sumafa ndipo lamulo la karma limachirikiza zimenezo. Tiyeni tione zimene Mawu a Mulungu ouziridwa, Baibulo, amanena pamalingaliro ameneŵa.

Kodi “Mzimu” Sumafa?

Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione zimene amanena Mawu ouziridwa a Mlengi omwe ali ndi ukumu waukulu pankhaniyi. M’buku lake loyamba la Genesis, Baibulo limatiphunzitsa tanthauzo lenileni la moyo. Za kulengedwa kwa Adamu munthu woyamba, Baibulo limati: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Inde, munthuyo sanaikidwe chinthu chamoyo m’thupi mwake, koma munthu mwiniyo ndiye anakhala wamoyo. Liwu lachihebri lotanthauza wamoyo panopa ndi neʹphesh. Limapezeka m’Baibulo nthaŵi ngati 700 ndipo silimanena za mbali ina yapadera yauzimu imene munthu ali nayo ayi koma nthaŵi zonse limanena za chinthu chogwirika ndi chathupi.​—Yobu 6:7; Salmo 35:13; 107:9; 119:28.

Nanga kodi chimachitikira munthu paimfa nchiyani? Talingalirani zimene zinachitika kwa Adamu atamwalira. Atachimwa, Mulungu anamuuza kuti: “Udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Taganizani za tanthauzo la zimenezo. Mulungu asanamlenge Adamu kuchokera kufumbi, iyeyo kunalibe. Atamwalira, Adamu sanakhalekonso monga poyamba paja.

Kunena mosavuta, Baibulo limaphunzitsa kuti pamene pali imfa palibe moyo. Pa Mlaliki 9:5, 10, timaŵerenga kuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiŵalika. Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”

Zimenezi zikutanthauza kuti akufa satha kuchita kanthu ngakhale kumva kanthu kalikonse. Saganizanso kalikonse, ngakhale kukumbuka kalikonse. Wamasalmo akuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”​—Salmo 146:3, 4.

Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti munthu akafa moyo wake sumasamukira m’thupi lina monga “mzimu.” “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa,” limatero Baibulo motsimikiza. (Ezekieli 18:4, 20; Machitidwe 3:23; Chivumbulutso 16:3) Chotero, chiphunzitso chakuti “mzimu” sufa​—maziko enieni a chiphunzitso chakuti munthu akafa amabadwanso m’moyo wina​—Malemba samachichirikiza. Popanda chimenecho, chiphunzitso cha kubadwanso chimapasuka. Nangano nchiyani chimachititsa mavuto omwe tikuona m’dziko?

Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Amavutika?

Chifukwa chachikulu chimene anthu amavutikira ndicho kupanda ungwiro kumene tinalandira kwa Adamu wochimwa. “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa,” limatero Baibulo. (Aroma 5:12) Popeza tinabadwa kwa Adamu, tonsefe timadwala, kukalamba, ndi kufa.​—Salmo 41:1, 3; Afilipi 2:25-27.

Ndiponso, lamulo la Mlengi losasintha la khalidwe limati: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi.” (Agalatiya 6:7, 8) Chifukwa chake, moyo wachiwerewere ungachititse munthu kupsinjika mtima, kutenga mimba ndi matenda opatsana mwa kugonana. “Chiŵerengero chodabwitsa cha imfa za kansa zokwanira 30 peresenti [ku United States] zimachitika makamaka chifukwa cha kusuta, ndiponso chiŵerengero chofanana chifukwa cha moyo wa munthu, makamaka kadyedwe ndi kusachita maseŵero olimbitsa thupi,” ikutero magazini yakuti Scientific American. Masoka ena amene amadzetsa mavuto amachitika chifukwa cha kulephera kwa munthu kusamalira bwino chuma cha dziko lapansi.​—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 11:18.

Inde, munthu mwini ndiye amachititsa masoka ochuluka. Komabe, popeza munthu alibe “mzimu” wosafa, sitingagwiritsire ntchito lamulo lakuti ‘umatuta chimene wafesa’ kunena kuti mavuto a munthu amadza chifukwa cha karma​—ntchito zimene amati munthu anazichita m’moyo wina asanabadwe. “Iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo,” Baibulo limatero. (Aroma 6:7, 23) Chotero sizimachitika kuti chilango cha uchimo nkupitiriza pambuyo pa imfa.

Nayenso Satana Mdyerekezi amachititsa mavuto. Kunena zoona, wolamulira dzikoli ndi Satanayo. (1 Yohane 5:19) Ndipo malinga ndi ulosi wa Yesu Kristu, ophunzira Ake ‘adzawada anthu onse chifukwa cha dzina lake.’ (Mateyu 10:22) Ndiye chifukwa chake olungama amavutika kwambiri kuposa oipa.

M’dzikoli mumachitika zinthu zina zimene zochititsa zake nzosadziŵika bwino. Munthu waliŵiro kwambiri angapunthwe ndi kulephera makani. Gulu la nkhondo lamphamvu angaligonjetse asilikali ochepa mphamvu. Munthu wanzeru angalephere kupeza ntchito yabwino ndi kuvutika ndi njala. Anthu odziŵa kwambiri kuyendetsa malonda angalephere kugwiritsira ntchito chidziŵitso chawocho chifukwa cha mikhalidwe yawo ndi kukhala amphaŵi. Anthu anzeru angakwiyitse akuluakulu moti sangaŵakondenso. Chifukwa ninji? “Chifukwa nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimawagwera iwo onse,” akuyankha Mfumu Solomo wanzeru.​—Mlaliki 9:11, NW.

Anthu anayamba kale kwambiri kuvutika Ahindu anzeru asanayese kufotokoza chifukwa chake mavutowo alipo. Koma kodi tingayembekeze kuti zinthu mtsogolo zidzakhala bwino? Ndipo kodi Baibulo limalonjeza zotani ponena za akufa?

Mtsogolo Mwamtendere

Mlengi walonjeza kuti posachedwa adzawononga dziko lilipoli limene Satana akulamulira. (Miyambo 2:21, 22; Danieli 2:44) Ndiye pambuyo pake padzatsatira dziko la anthu olungama​—“dziko latsopano.” (2 Petro 3:13) Panthaŵiyo “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ngakhale zoŵaŵa za imfa zidzachoka, pakuti Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

Za anthu okhala m’dziko latsopano limene Mulungu analonjeza, wamasalmo analosera kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Ndiponso, ofatsa “adzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:11.

Mukundbhai, wotchulidwa m’nkhani yoyamba, anamwalira osadziŵa malonjezo abwino kwambiri a Mulungu. Koma mamiliyoni ambiri omwe amwalira osamdziŵa Mulungu ali ndi chiyembekezo cha kuuka m’dziko latsopano limenelo lamtendere, pakuti Baibulo limalonjeza kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—Machitidwe 24:15; Luka 23:43.

Liwulo “kuuka” panopa likutembenuza liwu lachigiriki lakuti a·naʹsta·sis, limene kwenikweni limatanthauza “kuimiriranso.” Chotero chiukiriro chimaphatikizapo kuyambitsanso umoyo wa munthu.

Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi ngwanzeru zosatha. (Yobu 12:13) Kwa iye kukumbukira umoyo wa akufa si vuto ayi. (Yerekezerani ndi Yesaya 40:26.) Yehova Mulungu alinso ndi chikondi chochuluka. (1 Yohane 4:8) Chifukwa chake angagwiritsire ntchito kukumbuka kwake kwangwiro kuukitsa akufa padziko lapansi la paradaiso ndi umunthu womwe anali nawo asanafe, osati kuwalanga pazoipa zomwe anachita ayi.

Kwa mamiliyoni onga Mukundbhai, chiukiriro chidzawachititsa kuonananso ndi okondedwa awo. Koma taganizani mmene zimenezo zimakhalira kwa amene ali ndi moyo tsopano. Mwachitsanzo, titenge mwana wa Mukundbhai, amene wadziŵa choonadi chabwino kwambiri cha Mulungu ndi zifuno zake. Mmene mtima wake wakhalira m’malo podziŵa kuti atate wake sakubadwabadwanso, nkumakhala ndi moyo wodzala kuipa ndi mavuto! Iwo ali m’tulo ta imfa basi, kuyembekeza kuuka. Zimamsangalatsa kwambiri poganiza kuti tsiku lina angadzawauzeko atate wake zimene waphunzira m’Baibulo!

Mulungu afuna kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:3, 4) Nthaŵi ino njophunzira mmene inuyo, limodzi ndi ena mamiliyoni ambiri amene ayamba kale kuchita chifuniro cha Mulungu, mungakhalire ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso.​—Yohane 17:3.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimawagwera iwo onse.”​—Mlaliki 9:11, NW

[Bokosi patsamba 6]

Umunthu wa Mulungu ndi Lamulo la Karma

“Lamulo la Karma,” anatero Mohandas K. Gandhi, “nlosasintha ndipo nlosapeŵeka. Chotero palibe chimene Mulungu angaloŵererepo. Iye anaika lamulolo ndipo, kunena mophiphiritsa, anaiŵalako.” Zimenezi zinamvuta kwambiri Gandhi.

Komabe, lonjezo la chiukiriro limasonyeza kuti Mulungu amakonda chilengedwe chake kwambiri. Kuti Mulungu aukitse wakufa kukhala ndi moyo padziko lapansi la paradaiso, afunikira kudziŵa ndi kukumbukira zonse za munthuyo. Inde, Mulungu amasamaladi za yense wa ife.​—1 Petro 5:6, 7.

[Chithunzi patsamba 5]

Chizindikiro cha Ahindu cha moyo womasinthasintha

[Chithunzi patsamba 8]

Mawu a Mulungu amaphunzitsa za chiukiriro

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena