Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/15 tsamba 26-29
  • Chenjerani ndi Kukayikira Zolinga za Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chenjerani ndi Kukayikira Zolinga za Ena
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro Lakale
  • Mmene Timaonera Akulu
  • Zimene Mumaganizira Makolo
  • Mmene Timaonera Akristu Anzathu
  • Chikondi Chikusonkhezereni
  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Mfungulo ya Chikristu Chenicheni?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Tidzapulumuka mwa Chisomo Osati mwa Ntchito Zokha
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Mumaona Anthu Mmene Yehova Amawaonera?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kudera Nkhaŵa ndi Anthu Ena?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/15 tsamba 26-29

Chenjerani ndi Kukayikira Zolinga za Ena

MLALIKI wina wotchuka wa pawailesi yakanema anadzudzula zolimba mlaliki mnzake poyera kaamba ka kuchita chigololo. Komabe, chaka chimodzi chisanathe, mlaliki wodzudzula mnzakeyo anamgwira ndi hule.

Kwinanso, ulamuliro wina waukulu wa dziko lonse unatumiza nthumwi kuti zikasonkhezere magulu omenyana nkhondo a m’dziko lina kukambitsirana za mtendere. Zikali choncho, dziko limodzimodzilo mwa kazembera linatumiza amalonda ake ogulitsa zida ku maiko ena kukagulitsa zida za nkhondo za madola mamiliyoni zikwi zambiri.

Popeza chinyengo choonekeratu chafala chonchi, kodi nzodabwitsa kuti kukayikira ena kwalandadi malo kukhulupirira ena? Kwa ambiri, kukayikira zolinga za ena kwangokhala mkhalidwe wawo.

Monga Akristu, tiyenera kuchenjera kuti sitikulola malingaliro ameneŵa kuloŵa mu unansi wathu ndi okhulupirira anzathu okhulupirika. Ngakhale kuti Yesu Kristu anatilimbikitsa kukhala “ochenjera monga njoka” pamene tili pakati pa adani athu, sananene kuti tiyenera kukayikira otsatira ake oona. (Mateyu 10:16) Chotero, kodi kukayikira zolinga za ena kuli ndi ngozi zotani? Kodi ndi mbali ziti zimene tiyenera kusamala kwambiri kuti tipeŵe malingaliro ameneŵa? Ndipo tingautetezere motani unansi wathu wamtengo wapatali ndi Akristu anzathu?

Phunziro Lakale

Kukayikira zolinga za ena popanda chifukwa chabwino kuli ngati kuwaweruza. Kuli monga kuthamangira kunena kuti mawu kapena zochita zawo zangokhala chinyengo chophimba chinthu choipa chinachake ndipo chanjiru. Nthaŵi zambiri vuto lenileni limakhalapo chifukwa cha lingaliro lolakwika pa nkhaniyo, monga tingaonere m’nkhani ya m’Baibulo yopezeka mu Yoswa chaputala 22.

Aisrayeli anali atamaliza kulanda Dziko Lolonjezedwa ndipo anali atangolandira kumene magawo a mafuko awo. Fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi fuko logaŵika pakati la Manase anamanga guwa la nsembe “lalikulu maonekedwe ake” m’mbali mwa Mtsinje wa Yordano. Mafuko ena molakwa anaganiza kuti umenewu ndi mpatuko. Anaganiza kuti mafuko atatuwo anali kufuna kumagwiritsira ntchito chinthu chachikulu chimenechi monga poperekera nsembe m’malo mopita ku chihema chokumanira ku Silo, malo olambirirako oikidwa. Pomwepo, mafukowo oimba anzawo mlandu anakonzekera kukawathira nkhondo.​—Yoswa 22:10-12.

Ubwino wake ngwakuti analankhula ndi abale awo achiisrayeli mwa kuwatumizira nthumwi zotsogozedwa ndi Pinehasi. Atamva milandu imene anawapatsa ya kusakhulupirika, chipanduko, ndi mpatuko kwa Yehova, mafuko amene ankatiwo ndi opalamula mlandu anafotokoza chifukwa chimene anamangira guwa la nsembe lalikulu chotere. M’malo mokhala guwa loperekerapo nsembe, linali kudzakhala “mboni” ya umodzi wa mafuko a Israyeli pa kulambira Yehova. (Yoswa 22:26, 27) Nthumwizo zinabwerera kwawo zitakhutira kuti abale awo analibe cholakwa. Choncho anapeŵa nkhondo yachiŵeniŵeni ndi kukhetsa mwazi kwadzaoneni.

Ndi phunziro labwino chotani nanga kwa ife kuti sitiyenera konse kuthamangira kukayikira zolinga za ena! Kaŵirikaŵiri zinthu sizimakhala mmene zimaonekera mutazisanthula mosamalitsa. Zilidi choncho pazinthu zambiri m’moyo wa Mkristu.

Mmene Timaonera Akulu

Pochita ntchito yawo ‘yoŵeta mpingo wa Mulungu,’ nthaŵi zina akulu amaona kuti nkofunika kupatsa uphungu anthu osiyanasiyana mumpingo. (Machitidwe 20:28, NW) Mwachitsanzo, kodi timachita bwanji ngati mkulu walankhula nafe za ana athu pankhani yokhudza mayanjano oipa kapena khalidwe losayenera la anyamata ndi atsikana? Kodi timaganiza kuti ali ndi chifukwa china chobisika ndiye nkumanena mumtima kuti, ‘Sanalikondepo banja lathu’? Ngati tilola malingaliro otero kutilamulira, tingachite chisoni pambuyo pake. Mwina mkhalidwe wauzimu wa ana athu uli pangozi, ndipo tiyenera kuyamikira uphungu wothandiza wa m’Malemba.​—Miyambo 12:15.

Mkulu wa mumpingo atatipatsa uphungu, tisayambe kufunafuna chifukwa chobisika. M’malo mwake, tiyeni tidzifunse ngati pali njira ina imene tingapezere phindu la uphungu wake wa m’Baibulo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu choŵaŵa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Chotero tiyeni tiyamikire ndi kuiganizira nkhaniyo mwaufulu. Kumbukirani kuti nawonso akulu kaŵirikaŵiri zimawalimbira potipatsa uphungu monga momwe zimatilimbira poulandira.

Zimene Mumaganizira Makolo

Achinyamata ena, makolo awo atawaletsa zinthu zina, amakayikira zolinga za makolo awo. Achinyamata ena anganene kuti: ‘Makolo anga amapangiranji malamulo ambirimbiri chonchi? Sakufuna kuti ndisangalale ndi moyo eti?’ Komabe, m’malo mofika palingaliro limenelo, achinyamata ayenera kuusanthula mkhalidwewo mwaufulu.

Makolo atha zaka zambiri akusamalira ana awo. Kuti achite zimenezi, iwo ataya zinthu zambiri zakuthupi ndi zina. Kodi tinganenedi kuti iwo tsopano atsimikiza mtima kuti adzaipitsa moyo wa ana awo achinyamata? Sikwanzeru kodi kuganiza kuti chikondi chikusonkhezera makolowa kuti atetezere ana awo ndi kuwasamala? Chikondi chawo chomwecho kodi sichingawakakamize kuika ziletso zakutizakuti pa ana awo, amene tsopano ali ndi zothetsa nzeru zina? Kuwaganizira zoipa makolo achikondiwa kungakhale kuipa mtima ndi kusayamikira bwanji!​—Aefeso 6:1-3.

Mmene Timaonera Akristu Anzathu

Ambiri amakonda kuweruziratu ena ndi kuwaona molakwa nthaŵi zonse. Bwanji ngati ifeyo takhalapo ndi mzimu umenewo ndipo anthu ena tawakayikira m’njira ina yake? Kodi tingakhale titakhudzidwa ndi mzimu wa dziko pankhaniyi?

Mwachitsanzo, tinene kuti mmodzi wa abale athu auzimu ali ndi nyumba yabwino ndi galimoto lapamwamba. Kodi tiyenera kungothamangira kunena kuti ndi wokonda chuma ndipo sakuika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo? Akristu ena amatha kukhala ndi zinthu zabwino, koma zimenezo sizimatanthauza kuti ali ndi zolinga zoipa kapena kuti ‘sathanga afuna Ufumu.’ Mwina ali otanganitsidwa kwambiri ndi zinthu zauzimu, kugwiritsira ntchito chuma chawo mwaufulu kuti achirikize zinthu za Ufumu, mwinamwake mosaonekera.​—Mateyu 6:1-4, 33.

Mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba unali ndi anthu amtundu uliwonse​—olemera ndi osauka. (Machitidwe 17:34; 1 Timoteo 2:3, 4; 6:17; Yakobo 2:5) Mulungu samaona anthu malinga ndi chuma chimene ali nacho, ndipo ifenso sitiyenera kutero. Tiyenera kukonda okhulupirira anzathu otsimikizika ndi okhulupirika, “osachita kanthu monga mwa tsankhu.”​—1 Timoteo 5:21.

M’dziko lino limene likugona m’mphamvu ya Satana, kuona ena molakwa nthaŵi zonse ndi kuwakayikira kumaonekera mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, munthu angamuone monga wachiwawa kapena wokonda chuma chifukwa chabe cha kumene anakulira. Komabe, monga Akristu sitiyenera kutengako mzimu umenewu. M’gulu la Yehova simokhalira wouma khosi ndi wokayikira ena. Akristu onse oona ayenera kutsanzira Yehova Mulungu, amene ‘alibe chosalungama kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu.’​—2 Mbiri 19:7; Machitidwe 10:34, 35.

Chikondi Chikusonkhezereni

Malemba amanena momveka kuti “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Choncho tiyenera kuona olambira anzathu monga ogwirizana nafe pa kuyesetsa kuchita utumiki wolandirika kwa Yehova. Ngati talola zikayiko kapena maganizo ena oipa kusokoneza unansi wathu ndi mbale kapena mlongo wauzimu, tiyeni tipempherere thandizo la Mulungu kuti tilimbane ndi mzimu umenewu kuti Satana asatikole. (Mateyu 6:13) Iye ananyenga Hava kuti Yehova anali ndi zolinga zoipa, sanali kusamala za ubwino wake, ndipo anammana ufulu wina womwe ukanampatsa chimwemwe chenicheni. (Genesis 3:1-5) Timakwaniritsa zofuna zake ngati tikayikira zolinga za abale athu ndi alongo.​—2 Akorinto 2:11; 1 Petro 5:8.

Tikadziŵa kuti timakonda kukayikira zolinga za ena, tilingalire za chitsanzo cha Yesu Kristu. Ngakhale anali Mwana wangwiro wa Mulungu, sanawafunire zifukwa ophunzira ake. M’malo mwake, Yesu anafunafuna zabwino mwa iwo. Pamene ophunzira ake anali kulimbirana malo apamwamba, iye sanaganize kuti anali ndi zolinga zoipa ndiye nkusankha atumwi ena 12 atsopano. (Marko 9:34, 35) Pokhala opanda ungwiro, mwina anali atatengako mwambo wa Chiyuda champatuko, chimene chinkagogomezera kwambiri kunyada ndi kudzisiyanitsa malinga ndi zimene uli. Yesu anadziŵa kuti chimene chikusonkhezera kwambiri otsatira ake ndi chikondi cha Yehova. Chifukwa chosonyeza chikondi chimenechi ndi kummamatira Yesu, analandira mfupo yabwino kwambiri.​—Luka 22:28-30.

Ngati sitikuwaona bwino okhulupirira anzathu okhulupirika, zingakhale monga kuona zinthu mwa kugwiritsira ntchito galasi lowonongeka. Palibe chimene chidzaoneka mmene chililidi. Choncho tiyeni tione zinthu mwa kugwiritsira ntchito galasi lachikondi. Pali maumboni ambirimbiri akuti Akristu anzathu okhulupirika amatikonda ndipo timayenera kuwalingalira mokoma mtima. (1 Akorinto 13:4-8) Chotero tiyeni tiwasonyeze chikondi ndi kuchenjera kuti sitikukayikira zolinga zawo.

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi ena amene akulambira Mulungu mokhulupirika mumawaona motani?

[Chithunzi patsamba 27]

Kukhulupirirana ndi ulemu zimachititsa Mboni za Yehova kukhala banja limodzi lachimwemwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena