Bwerani ku Msonkhano Wachigawo wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”!
MAMILIYONI a anthu adzabwera mmalo mazanamazana kuzungulira dziko lonse lapansi. Mu Zambia mokha, mudzakhala misonkhano yachigawo 47. Woyamba udzakhala pa August 11-13 ndipo wotsiriza udzakhala pa August 29-31. Ina idzakhala ku Malaŵi, Mozambique ndi ku Zimbabwe. Mosakayika umodzi wa misonkhano ya masiku atatu imeneyi udzachitikira pafupi ndi kwanuko.
Mukapindula ndi chuma cha malangizo othandiza a m’Baibulo. Mmalo ambiri programu izikayamba ndi nyimbo zamalimba 9:30 mmaŵa. Tsiku loyamba m’maŵa kudzakhala mphindi 25 za kufunsa mafunso anthu omwe miyoyo yawo yasintha kotheratu chifukwa cha chikhulupiriro chawo m’Mawu a Mulungu. Chigawo choyamba chimenechi chidzatha ndi nkhani yakuti, “Kuyenda mwa Chikhulupiriro, Osati mwa Chionekedwe.”
Nkhani yoyamba patsiku loyamba masana idzalongosola mbali yofunika kwambiri yomwe achinyamata alinayo mumpingo wachikristu. Nkhani yotsatira yosiyirana ya mbali zitatu idzalongosola za momwe miyezo ya Baibulo imakhudzira makhalidwe achikristu m’kalankhulidwe, umunthu, ndiponso kavalidwe ndi kapesedwe. Kenaka nkhani yakuti “Chenjerani Kuti Mungasoŵe Chikhulupiriro” ndi yakuti “Mawu a Mulungu Ali Amoyo” zidzasumika pa machenjezo a mu Ahebri chaputala 3 ndi 4. Maprogramu patsiku loyamba adzatha ndi nkhani yakuti “Buku la Anthu Onse.”
Nkhani yoyamba patsiku lachiŵiri mmaŵa idzakhala yakuti “Chikhulupiriro Chopanda Ntchito Nchakufa.” Nkhani ina yofunika mmaŵawo, “Zikani Mizu ndi Kukhazikika m’Choonadi,” njofotokoza za momwe munthu angakulire mwauzimu. Chigawo chimenechi chidzatha ndi nkhani yaubatizo yozoloŵereka pa msonkhano yakuti, “Kukhulupirira Mawu a Mulungu Kumatsogolera ku Ubatizo,” ndipo pambuyo pake ophunzira atsopano adzapita ku ubatizo.
Nkhani yotsegulira patsiku lachiŵiri masana, “Menyerani Nkhondo Chikhulupiriro,” idzalongosola machenjezo a m’buku la m’Baibulo la Yuda. Nkhani yosiyirana ya ola lathunthu ya mutu wakuti “Tiyeni ku Nyumba ya Yehova” idzalongosola mapindu a misonkhano yachikristu. Programu patsikulo idzatha ndi nkhani yakuti “Mtundu wa Chikhulupiriro Chanu Ukuyesedwa Tsopano.”
Programu ya tsiku lachitatu mmaŵa idzakhala ndi nkhani yosiyirana ya mbali zitatu zimene zidzalongosola buku la m’Baibulo la Yoweli, ndiponso mmene limatikhudzira lerolino. Ndiye chotsatira chidzakhala seŵero lozikikidwa pa Baibulo lamutu wakuti “Khalani ndi Diso la Kumodzi.” Msonkhano udzafika pachimake masana ndi nkhani yapoyera, “Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu.”
Ndithudi mukadzakhalapo mudzalemerera mwauzimu. Mudzalandiridwa mwachikondi pachigawo chilichonse. Konzekerani tsopano kuti mudzapezekepo. Kuti mudziŵe malo a msonkhano apafupi ndi kwanuko, funsani pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko kapena lemberani ofalitsa magazini ano.