Yerusalemu m’Nthaŵi za Baibulo Kodi Kufukula m’Mabwinja Ake Kwasonyezanji?
NTCHITO yosangalatsa yofukula m’mabwinja ikuchitika ku Jerusalem, makamaka chiyambire 1967. Tsopano anthu angakaone malo ambiri okumba, choncho tiyeni tiwazonde ena ndi kuona mmene zofukula m’mabwinja ake zikugwirizanira ndi Baibulo.
Yerusalemu wa Mfumu Davide
Malo omwe Baibulo limatcha Phiri la Ziyoni, limene panamangidwa Mudzi wa Davide wakale, samaoneka apadera kwambiri mumzinda wamakono wa Jerusalem. Ntchito yokumba Mudzi wa Davide, yotsogozedwa ndi malemu profesa Yigal Shiloh pakati pa 1978-85, inavumbula mwala waukulu wopangidwa ngati makwerero, kapena kuti khoma lochirikiza, kummaŵa kwa phirilo.
Profesa Shiloh anatero kuti uyenera kukhala zotsala pamaziko aakulu a makoma onga makwerero omwe Ayebusi (okhalamo poyamba Davide asanaugonjetse) anamangapo malinga. Anafotokoza kuti mwalawo wopangidwa ngati makwerero womwe anapeza pamwamba pa makoma ameneŵa unali wa linga latsopano lomwe Davide anamanga pamalo a linga la Ayebusi. Pa 2 Samueli 5:9, timaŵerenga kuti: “Davide anakhala m’linga muja, nalitcha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi mkati momwe.”
Pafupi ndi chimango chimenechi pali makomo oloŵera kuzitsime za madzi a mudzi wakalewo, amene ena aoneka ngati ndi a panthaŵi ya Davide. Mawu ena m’Baibulo onena za ngalande za madzi a Yerusalemu abutsa mafunso. Mwachitsanzo, Davide anauza anyamata ake kuti ‘yense wokantha Ayebusi akumane ndi adani kudzera m’ngalande ya madzi.’ (2 Samueli 5:8, NW) Kazembe wa Davide Yoabu anatero. Kodi mawu akuti “ngalande ya madzi” kwenikweni atanthauzanji?
Mafunso ena abukanso onena za Ngalande ya Siloamu yotchuka, imene akatswiri omanga a Mfumu Hezekiya angakhale ataikumba m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E. yotchulidwanso pa 2 Mafumu 20:20 ndi 2 Mbiri 32:30. Kodi magulu aŵiri okumba ngalandewo, kuchokera kumbali ziŵiri zosiyana, anakumana bwanji? Nchifukwa ninji anasankha kukumba mokhotakhota, kutalikitsa kwambiri ngalandeyo m’malo molunjika? Nanga mpweya wokwana wopuma anaupeza bwanji, makamaka popeza angakhale atagwiritsira ntchito nyali za mafuta?
Magazini yakuti Biblical Archaeology Review yapereka omwe angakhale mayankho a mafunso ngati amenewo. Imagwira mawu Dan Gill, katswiri wa geology ndiponso phungu pa zakukumbako, kuti: “Pansi pa Mudzi wa Davide pali malo okhala ndi karst yachilengedwe. Karst ndi liwu mu geology lofotokoza malo osalongosoka okhala ndi migodi, mapanga ndi ngalande zopangidwa ndi madzi oloŵa pansi ndi kuyenda m’mipata ya miyala. . . . Kufufuza kwathu zitsime za madzi pansi pa nthaka ya Mudzi wa Davide malinga ndi geology kumasonyeza kuti anthu makamaka ndiwo anasintha mwaluso ngalande zachilengedwe (karstic) ndi migodi yopangika ndi madzi okokolola dothi, kuzikuza kukhala zitsime za madzi.”
Zimenezi zingathandize kufotokoza mmene anakumbira Ngalande ya Siloamu. Iyo ingakhale itatsatira njira yokhotakhota ya ngalande yachilengedwe m’phiri pansi. Magulu ogwira ntchito kumbali zake zonse ziŵiri angakhale atakumba ngalande yakanthaŵi mwa kusintha mapanga omwe analipo kale. Ndiyeno anakumba mchera wotsikira kumunsi kuti madzi aziyenda kuchokera ku kasupe wa Gihoni kupita ku Thamanda la Siloamu, limene mwina linali mkati mwake mwa makoma a mudziwo. Limenelitu linali luso lomanga pakuti kusiyana kwa msinkhu wa mbali ziŵirizo ndi masentimita 32 chabe, ngakhale kuti utali wake wonse ngwamamita 533.
Kwa nthaŵi yaitali akatswiri a maphunziro azindikira kuti chitsime chachikulu cha madzi a mudzi wakalewo anali kasupe wa Gihoni. Kasupeyo anali kunja kwa malinga a mudziwo koma pafupi ndithu poti nkulola kukumba ngalande ndi mgodi wakuya mamita 11, umene unalola anthu ake kutunga madzi popanda kutuluka kunja kwa malinga achitetezo. Mgodi umenewu umatchedwa Warren’s Shaft, kutsata dzina la Charles Warren, amene anapeza ngalandeyo mu 1867. Koma kodi ngalandeyo ndi mgodi wake anazipanga liti? Kodi zinaliko panthaŵi ya Davide? Kodi ngalande imeneyo ndiyo anagwiritsira ntchito Yoabu? Dan Gill akuyankha: “Pofuna kudziŵa ngati mgodi wa Warren’s Shaft unali wachilengedwe, tinapima chibulumwa chotengedwa mkati mwake kuona ngati chili ndi carbon-14. Chinalibe, kusonyeza kuti chibulumwacho chili ndi zaka zoposa 40,000: Zimenezi zimapereka umboni wosatsutsika wakuti munthu sindiye anaupanga mgodiwo.”
Zotsala Panthaŵi ya Hezekiya
Mfumu Hezekiya anakhalako panthaŵi imene Asuri anali kugonjetsa aliyense. Chaka chachisanu ndi chimodzi cha kulamulira kwake, Asuri analanda Samariya, likulu la ufumu wa mafuko khumi. Patapita zaka zisanu ndi zitatu (mu 732 B.C.E.) Asuri anafikanso, atakonzeka kuwononga Yuda ndi Yerusalemu. Pa 2 Mbiri 32:1-8 pamafotokoza njira ya Hezekiya yoteteza mudziwo. Kodi pali umboni uliwonse wooneka wa nyengo imeneyo?
Inde. Mu 1969, Profesa Nahman Avigad anapeza zotsala panyengoyo. Zofukula zinavumbula chigawo cha khoma lalikulu, mbali yake yoyamba njamamita 40 m’litali, mamita 7 m’mimba mwake, ndipo msinkhu wake mamita ngati 8. Khomalo mbali yake ina inaima pa thanthwe ndipo ina pa nyumba zatsopano zomwe anagumula kulimangapo. Kodi anamanga khomalo ndani ndipo liti? “Mavesi aŵiri m’Baibulo anamthandiza Avigad kudziŵa nthaŵi imene anamanga khomalo ndiponso cholinga chake,” ikutero magazini ina ya zofukula m’mabwinja. Mavesi amenewo amati: “Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake.” (2 Mbiri 32:5) “Munagwetsa nyumba, kuti mumangire linga.” (Yesaya 22:10) Lero alendo atha kuona mbali ya khomali lotchedwa Broad Wall m’Chigawo cha Ayuda cha Mudzi Wakale.
Zofukula zamitundumitundu zimavumbulanso kuti Yerusalemu panthaŵiyi anali wamkulu kuposa zimene anthu anali kuganiza asanafukule zimenezo, mwina chifukwa cha othaŵa kwawo ochuluka ochokera ku ufumu wa kumpoto ataugonjetsa Asuri. Profesa Shiloh ananena kuti mudzi wa Ayebusi unali waukulu mahekitala ngati 6. Panthaŵi ya Solomo unali wa mahekitala pafupifupi 16. Panthaŵi ya Mfumu Hezekiya, pambuyo pa zaka 300, malo amalinga a mudziwo anakula mpaka mahekitala ngati 60.
Manda a Nyengo ya Kachisi Woyamba
Manda a nyengo ya Kachisi Woyamba, kutanthauza Ababulo asanawononge Yerusalemu mu 607 B.C.E., aperekanso chidziŵitso china. Mu 1979/80 anapeza zodabwitsa pamene anakumba manda m’mapanga apamaterezi a Chigwa cha Hinomu. “M’mbiri yonse yofufuza mabwinja m’Yerusalemu, imeneyi ndi imodzi ya nkhokwe zoŵerengeka za Kachisi Woyamba yopezeka ndi zamkati mwake zonse. Inali ndi zinthu zoposa chikwi chimodzi,” akutero wofukula m’mabwinja Gabriel Barkay. Akupitiriza kuti: “Zimene aliyense wofukula m’mabwinja wogwira ntchito m’Israel amafuna kwambiri, makamaka m’Yerusalemu, ndi kupeza mipukutu yolembedwapo.” Anapeza mipukutu yaing’ono iŵiri yasiliva. Kodi panalembedwa chiyani?
Barkay akufotokoza: “Nditaona mpukutu wofunya wasiliva ndi kuikapo galasi lokuza maonekedwe a zinthu zazing’ono, ndinaona kuti panali zilembo zolemba bwinobwino, zozokota ndi cholembera chosongoka papepala lasiliva lopsapsala kwambiri ndi losalimba. . . . Dzina la Mulungu looneka bwino m’zolembazo lili ndi zilembo zinayi zachihebri m’kalembedwe kakale ka Chihebri, yod-he-waw-he.” M’buku la pambuyo pake, Barkay anawonjeza kuti: “Tinadabwa kwambiri kupeza kuti pamasamba aŵiriwo asiliva panalembedwa madalitso ofanana kwambiri ndi Madalitso a Wansembe a m’Baibulo.” (Numeri 6:24-26) Imeneyi inali nthaŵi yoyamba kupeza dzina la Yehova m’mipukutu yopezeka m’Yerusalemu.
Kodi akatswiri a maphunziro anaipeza bwanji nthaŵi yake imene mipukutu imeneyi yasiliva inalembedwa? Makamaka mwa kugwiritsira ntchito zofukula zina zomwe anapeza. M’nkhokwemo anapezamo mbiya zoposa 300 zimene nthaŵi yake ikudziŵika, zosonyeza kuti zinali za m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri kapena lachisanu ndi chimodzi B.C.E. Kalembedwe kake, atakayerekezera ndi zolemba zina zokhala ndi madeti ake, kamasonyeza kuti zili za panyengo imodzimodziyo. Mipukutuyo ili mu Israel Museum ku Jerusalem.
Chiwonongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E.
Baibulo, mu 2 Mafumu chaputala 25, 2 Mbiri chaputala 36, ndi Yeremiya chaputala 39, limasimba kuti Yerusalemu anawonongedwa mu 607 B.C.E. ndi kuti magulu a nkhondo a Nebukadinezara anatentha mzindawo. Kodi zokumba zaposachedwapa zatsimikiza kuti nkhani yakale imeneyo njoona? Malinga ndi Profesa Yigal Shiloh, “umboni wosakanika wa zofukula m’mabwinja umachirikiza . . . umboni wa m’Baibulo [wakuti Ababulo anauwonongadi]; kuwonongeratu nyumba zosiyanasiyana, ndi moto womwe unanyeketsa matabwa m’nyumba zawo.” Anapitiriza nati: “Umboni wa chiwonongeko chimenechi wapezeka pakukumba kulikonse kochitidwa m’Jerusalem.”
Alendo angaone zotsala pachiwonongeko chimenechi chochitika zaka zoposa 2,500 zapitazo. Nsanja ya Israyeli, Chipinda Chotenthedwa, ndi Nyumba ya Zidindo ndiwo maina a mabwinja otetezereka otchuka amene anthu amawalola kukaona. Ofukula m’mabwinja Jane M. Cahill ndi David Tarler akufotokoza mwachidule m’buku lakuti Ancient Jerusalem Revealed: “Umboni wakuti Ababulo anawonongeratu Yerusalemu umaoneka osati chabe m’muyalo wochindikala wa zotsala zonyeka zokumbidwa m’nyumba ngati ya Chipinda Chotenthedwa ndi Nyumba ya Zidindo, komanso m’mulu waukulu wa miyala ya nyumba zakugwa yopezeka itakuta terezi lakummaŵa. Kulongosola kwa Baibulo chiwonongeko cha mudziwo . . . kumachirikiza umboni wa zofukula m’mabwinja.”
Chotero, kufukula m’mabwinja kochitika pazaka 25 zapitazo kwatsimikiza m’njira zambiri chithunzi chimene Baibulo limapereka cha Yerusalemu, kuyambira panthaŵi ya Davide mpaka chiwonongeko chake mu 607 B.C.E. Nanga bwanji za Yerusalemu wa m’zaka za zana loyamba?
Yerusalemu m’Tsiku la Yesu
Zofukulafukula, Baibulo, Josephus Myuda wolemba mbiri wa m’zaka za zana loyamba, ndi maumboni ena zimathandiza akatswiri a maphunziro kuona Yerusalemu wa m’tsiku la Yesu, Aroma asanamuwononge mu 70 C.E. Chitsanzo chake, choonetsedwa kuseri kwa hotela yaikulu m’Jerusalem, amachikonza nthaŵi zonse malinga ndi zimene zofukula zatsopano zasonyeza. Chinthu chapadera kwambiri m’mudziwo chinali Phiri la Kachisi, limene Herode anakuza kuliŵirikiza kuposa mmene linalili panthaŵi ya Solomo. M’dziko lakalelo, linali maziko aakulu koposa onse opangidwa ndi anthu a mamita 480 m’litali ndi mamita 280 m’mimba mwake. Miyala ina yomangira inalemera matani 50, wina unatsala pang’ono kufika ngakhale matani 400 ndipo “kunalibe wina wolingana nawo ukulu wake m’dziko lakale,” anatero katswiri wina wa maphunziro.
Ndiye chifukwa chake anthu ena anadabwa atamva Yesu akunena kuti: “Pasulani kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.” Iwo anayesa kuti anatanthauza kachisi wamkuluyo, ngakhale kuti iye anatanthauza “kachisi wa thupi lake.” Choncho, iwo anati: “Zaka makumi anayi ndi zisanu ndi chimodzi analimkumanga Kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu?” (Yohane 2:19-21) Chifukwa chokumba pozinga Phiri la Kachisi ponse, alendo tsopano atha kuona mbali zina za makoma ake ndi kamangidwe kake panthaŵi ya Yesu ndipo akhoza ngakhale kuyenda njira imene iye mwina anayendamo, kukwera kumka ku zipata za kummwera kwa kachisiyo.
Pafupi ndi khoma lakumadzulo kwa Phiri la Kachisi, m’Chigawo cha Ayuda cha Mudzi Wakale, pali malo aŵiri okumba okonzedwa bwino a m’zaka za zana loyamba C.E., otchedwa Nyumba Yotenthedwa ndi Chigawo cha Aherode. Atapeza Nyumba Yotenthedwa, wofukula m’mabwinja Nahman Avigad analemba kuti: “Zinaonekeratu tsopano kuti nyumba imeneyi anaitentha ndi Aroma mu 70 A.D., powononga Yerusalemu. Nthaŵi yoyamba m’mbiri yofukula mabwinja m’mudziwu, umboni wosakanika wa zofukula m’mabwinja wakuti mudziwo anautentha unaonekera.”—Yang’anani zithunzi patsamba 12.
Zina mwa zopezeka zimenezi zimamasulira bwino zochitika zina pamoyo wa Yesu. Nyumba zinali m’Mudzi wa Kumtunda, kumene anthu olemera m’Yerusalemu anali kukhala, kuphatikizapo akulu a ansembe. Maiŵe ambiri aakulu osambiramo malinga ndi mwambo anapezeka m’nyumba zimenezo. Katswiri wina wa maphunziro akuti: “Maiŵe ambiriwo amasonyeza kuti anthu okhala m’Mudzi wa Kumtunda umenewo panyengo ya Kachisi Wachiŵiri anali kutsata kwambiri malamulo a mwambo wa kuyera. (Malamulo ameneŵa alembedwa m’Mishnah, imene ili ndi mitu khumi yofotokoza mikveh mwatsatanetsatane.)” Mawu ameneŵa akutithandiza kuzindikira zonena za Yesu pamiyambo imeneyi kwa Afarisi ndi alembi.—Mateyu 15:1-20; Marko 7:1-15.
Chodabwitsanso nchakuti mitsuko yambiri yamiyala yapezekanso m’Yerusalemu. Nahman Avigad akuti: “Nanga nchifukwa ninji inangopezeka mwadzidzidzi chonchi ndiponso yochuluka kwambiri m’nyumba za m’Yerusalemu? Yankho lake likupezeka mu halakhah, malamulo achiyuda a mwambo wa kuyera. Mishnah imatiuza kuti mitsuko yamiyala ili zina za zinthu zimene sizimadetsedwa . . . Malinga ndi mwambo, Miyala inali yosadetsedwa konse.” Ena akuti ndiye chifukwa chake madzi omwe Yesu anasandutsa vinyo anawasunga m’mitsuko yamiyala m’malo mwa mitsuko yadothi.—Levitiko 11:33; Yohane 2:6.
Mutapita ku Israel Museum mudzapeza zinthu ziŵiri zachilendo zosungiramo mafupa a anthu. Buku lakuti Biblical Archaeology Review likufotokoza kuti: “Zinthu zosungiramo mafupa a anthu ankazigwiritsira ntchito makamaka pazaka ngati zana limodzi Aroma asanawononge Yerusalemu mu 70 C.E. . . . Wakufa anali kumuika m’mphako yokumba m’phanga la manda; thupi litawola, anatenga mafupa ake nawaika mosungira—chotengera chimene nthaŵi zambiri anachikometsera ndi njereza.” Zosungiramo mafupa ziŵirizo zosonyezedwa anazipeza m’November 1990 m’phanga la manda. Wofukula m’mabwinja Zvi Greenhut akuti: “Liwu lakuti . . . ‘Kayafa’ lolembedwa pa zosungiramo mafupa ziŵirizo m’manda lapezeka panopa nthaŵi yoyamba m’mbiri yofukula za m’mabwinja. Mwina ndi dzina la banja la Mkulu wa Ansembe Kayafa, wotchulidwa . . . m’Chipangano Chatsopano . . . Kunyumba kwake m’Yerusalemu ndi kumene anamperekera Yesu kwa bwanamkubwa wa Aroma Pontiyo Pilato.” M’chosungiramo china munali mafupa a mwamuna wa zaka ngati 60. Akatswiri a maphunziro akhulupirira kuti ameneŵa ndi mafupa a Kayafa. Katswiri wa maphunziro wina akuti zopezekazo nzapanthaŵi ya Yesu: “Khobiri lopezeka m’chosungiramo china analisula ndi Herode Agripa (37-44 C.E.). Zosungiramo mafupa za Kayafa ziŵirizo zingakhale za kumayambiriro kwa zaka za zana loyamba.”
William G. Dever, profesa wa zofukula m’mabwinja a Near Eastern pa Yunivesite ya Arizona, anakambapo za Yerusalemu kuti: “Tikanena kuti taphunzira zambiri ponena za mbiri ya zofukulidwa pamalo ameneŵa ofunika kwambiri pazaka zosachepera 15 zokha kuposa pazaka 150 zonse zapitazo sindiye kuti tikukokomeza ayi.” Ntchito yochuluka yofukula m’mabwinja ku Yerusalemu pazaka makumi angapo posachedwa yatulutsa zinthu zimene zaimasulira bwino mbiri ya Baibulo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Chitsanzo cha Mudzi wa Yerusalemu panthaŵi ya Kachisi Wachiŵiri – ku Holyland Hotel, Jerusalem
[Zithunzi patsamba 10]
Pamwamba: Ngondya yakummwera koma chakumadzulo kwa Phiri la Kachisi wa Yerusalemu
Kulamanja: Kutsikira mu Warren’s Shaft