Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 8/1 tsamba 3-4
  • Chikumbumtima—Mtolo Kapena Chofunika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikumbumtima—Mtolo Kapena Chofunika?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikumbumtima​—Lingaliro la Baibulo
  • Kodi Chikumbumtima Chanu Ndi Chophunzitsidwa Bwino?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Mungatani Kuti Mukhalebe ndi Chikumbumtima Chabwino?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Mungatani Kuti Muzikhala Ndi Chikumbumtima Chabwino?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Mverani Chikumbumtima Chanu
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 8/1 tsamba 3-4

Chikumbumtima​—Mtolo Kapena Chofunika?

‘CHIKUMBUMTIMA changa chikundivutitsa!’ Pafupifupi tonsefe timayang’anizana ndi zoŵaŵa za chikumbumtima nthaŵi ndi nthaŵi. Kupwetekako kungayambire pa kusakhazikika m’maganizo chabe mpaka pa kusweka maganizo. Chikumbumtima chosweka chingadzetse tondovi kapena kudzimva kukhala wolephera.

Titalingalira zimenezi, kodi sitinganene kuti chikumbumtima ndi mtolo? Ena angaganize choncho. M’mibadwo yakale, anthu oganiza mozama ankalingalira kuti chikumbumtima ndi luso lachibadwa. Ambiri anaganiza kuti chinali chitetezo cha makhalidwe abwino chopatsidwa mwachindunji ndi Mulungu. Choncho, chikumbumtima chatchedwa “kukhalapo kwa Mulungu mwa munthu,” “chibadwa chathu chenicheni,” komanso “liwu la Mulungu.”

Komabe, zaka zingapo zapitazo, kwanenedwa kuti chikumbumtima kwenikweni ndi luso lochita kubwera​—chotulukapo cha chisonkhezero cha makolo ndi mabwenzi. Mwachitsanzo, akatswiri ena a zamaganizo amanena kuti mwana amaphunzira kupeŵa makhalidwe oipa chifukwa choopa chilango, pokhulupirira kuti chikumbumtima ndicho kutengera umunthu ndi zikhulupiriro za makolo athu. Ena amanena kuti chimakhalapo mwa kutengera makhalidwe ndi njira zimene anthu aunyinji amasonyeza. Enanso amanena kuti zoŵaŵa za chikumbumtima zimadza chifukwa cha kulimbana kwa zimene timafuna kuchita ndi zimene chitaganya chotsendereza chimafuna kuti tichite!

Mosasamala kanthu za zimene ena anena, anthu kaŵirikaŵiri amachita zimene afuna motsutsana ndi makolo, mabanja, ndi chitaganya chonse chifukwa chakuti chikumbumtima chawo chinawasonkhezera kutero. Ena akhala okonzekera ngakhale kutaya miyoyo yawo chifukwa cha chikumbumtima! Ngakhale kuti miyambo ndi yosiyanasiyana padziko lapansi, kupha munthu, umbala, chigololo, bodza, ndi kugonana ndi wachibale kumaoneka kukhala tchimo padziko lonse. Kodi zimenezi sizili umboni wakuti chikumbumtima ndi chachibadwa?

Chikumbumtima​—Lingaliro la Baibulo

Amene anganene zenizeni pankhani imeneyi ndi Yehova Mulungu. Zoonadi, “Iyeyu [Mulungu] anatilenga, ndipo ife ndife ake.” (Salmo 100:3) Iye amazindikira bwino lomwe chipangidwe chathu. Mawu a Mulungu, Baibulo, amafotokoza kuti munthu analengedwa “m’chifanizo” cha Mulungu. (Genesis 1:26) Munthu analengedwa ndi nzeru yakudziŵa chabwino ndi choipa; kuyambira pachiyambi, chikumbumtima chakhala mbali yachibadwa ya chilengedwe cha munthu.​—Yerekezerani ndi Genesis 2:16, 17.

Mtumwi Paulo akutsimikiza zimenezi m’kalata yake yolembera Aroma, motere: “Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo (la Mulungu), amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.” (Aroma 2:14, 15) Tingaone kuti ambiri amene sanaleredwe pansi pa chilamulo cha Mulungu chopatsidwa kwa Ayuda anatsatirabe ena a mapulinsipulo a Chilamulo cha Mulungu, osati mokakamizidwa ndi anthu, koma ndi “chibadwa”!

Choncho, chikumbumtima si mtolo ayi, koma ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, chinthu chofunika. Zoonadi, chingatisautse. Koma ngati tichilabadira, chingatipangitse kudzimva wokhutira, ndipo chingabweretse mtendere wa maganizo. Chingathe kutitsogolera, kutichinjiriza, ndi kutisonkhezera. The Interpreter’s Bible ikuthirira ndemanga motere: “Thanzi la maganizo ndi mtima lingatetezeredwe kokha ngati munthu ayesetsa kuchita zimene aona kuti ayenera kuchita, osati kungochita zinthu.” Kodi munthu angachite motani zimenezi? Kodi tingathe kuwongolera ndi kuphunzitsa chikumbumtima chathu? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena