Olengeza Ufumu Akusimba
Mphamvu Yoyeretsa ya Mawu a Mulungu
MALIPOTI akunena kuti omwe anazoloŵera anamgoneka amayambiranso chizoloŵezicho atachoka ku chipatala. Koma Mawu a Mulungu akhoza kukwanitsa zomwe zipatala kaŵirikaŵiri zimakanika kuchita. (Ahebri 4:12) Ambiri athandizidwa ndi Mawu a Mulungu ndiponso mzimu wake kugonjetsa chizoloŵezi chakumwerekera ndi anamgoneka ndi kuyamba kugwiritsira ntchito uphungu wakuti: “tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.”—2 Akorinto 7:1.
Chitsanzo cha zoterezi chinachitika ku Myanmar. Munthu yemwe anavutika ndi chizolowezi chakumwerekera ndi anamgoneka kwa zaka zambiri anati: “Ndinayamba kugwiritsira ntchito anamgoneka ndidakali mnyamata. Nthaŵi zambiri ndayesa kusiya, koma sinditha. Kuti ndizipeza ndalama zogulira anamgonekawo, ndinayamba kuba. Zotsatira zake, mu 1988, ndinaponyedwa m’ndende kwa chaka chimodzi.
“Nditamasulidwa ku ndendeko, ndinayambiranso kugwirizana ndi anzanga akale. Posapita nthaŵi chizoloŵezi cha anamgoneka chinayambanso. Kakhalidwe kodziwononga chonchika kanapangitsa kuti abale anga onse aleke kugwirizana nane. Kuwonjezera apo, kupanduka kwangaku kunapangitsa kuti anthu ambiri azindiopa, choncho nawonso anayamba kumandithaŵa.
“Ndiye tsiku lina chozemba chinakumana nchokwaŵa—Ndinamwa anamgoneka ambiri. Ndinatumizidwanso ku ndende, ulendo uno kwa zaka zitatu. Ngakhale kuti moyo kundende unali wovuta, mwamwaŵi ndinapulumuka osafa.
“Nditabwerera ku nyumba kuchokera ku ndende, ndinapempha achibale anga kuti andikhululukire pa zoipa zomwe ndimachita kale. Anandilandira mwachikondi, komabe kachiŵirinso, anzanga anandisonkhezera kuti ndiyambenso khalidwe langa lakale.
“Potsiriza pake, agogo anga anakalankhula ndi pasitala kuti ndiyambe Sukulu ya Baibulo inayake. Pasitalayo anavomera. Komabe, ndisanayambe kuphunzira, adzakhali anga, amene ndi amodzi a Mboni za Yehova, ananena kuti ngati ndikufunadi kuphunzira Baibulo, ndiyenera kuphunzira ndi Mboni.
“Ndinapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo anandipereka kwa munthu yemwe anavomera kuphunzira Baibulo ndi ine. Ambiri pamsonkhanopo anandilonjera mwachikondi ndipo zinandipangitsa kudzimva wolandiridwa.
“Nditayamba kuphunzira Baibulo ndiponso kupezeka pa misonkhano yachikristu, chilakolako cha anamgoneka chinaloŵedwa m’malo ndi kusirira kuyandikira kwa Mulungu. Chaka chimodzi chokha pambuyo pake ndinali nditapita patsogolo kufika popatulira moyo wanga kwa Yehova Mulungu, ndipo ndinasonyeza kudzipatulirako mwa ubatizo wa m’madzi.
“Posachedwapa, pamene ndinali kupita ku nyumba ndi nyumba, ndinakumana ndi mmodzi wa anzanga amene ndimamwa nawo anamgoneka. Sanathe kumvetsetsa poona kuti ndinali nditasintha kwambiri. Izi zinapereka mpata wochitira umboni, ndipo ndinatha kulankhula naye za chiyembekezo cha Ufumu.
“Potsiriza ndapeza cholinga chenicheni ndi tanthauzo la kukhala ndi moyo. Ndithokoza Mulungu chifukwa cha chithandizo ndi uphungu wake zopezeka m’Mawu ake, tsopano ndimatha kuthandiza ena kuthetsa chizoloŵezi chowononga makhalidwe abwino cha anamgoneka.”