Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 10/1 tsamba 21-25
  • Woyamikira Chifukwa Chotumikira Yehova Nthaŵi Yaitali

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Woyamikira Chifukwa Chotumikira Yehova Nthaŵi Yaitali
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusonkhezeredwa ndi Malingaliro Achipembedzo
  • Kuchirikiza Kwanga Choonadi cha Baibulo
  • Kutumikira pa Beteli
  • Kuyembekeza Ufumu Mwachidaliro
  • Ntchito m’Nthaŵi ya Nkhondo Yadziko II
  • Ntchito Iyambanso Kuyenda Bwino Nkhondo Itatha
  • Kuchita Zimene Ndingathe
  • Kukhulupirika Mpaka Mapeto
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Moyo Wanga m’Gulu Lotsogozedwa ndi Mzimu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Moyo Waulemerero Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mukuitanidwa!
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 10/1 tsamba 21-25

Woyamikira Chifukwa Chotumikira Yehova Nthaŵi Yaitali

YOSIMBIDWA NDI OTTILIE MYDLAND

Chakumapeto kwa zaka za zana la 19, sitima za m’madzi zinaima moyandikana padoko la Kopervik kumadzulo kwa dziko la Norway. M’masiku amenewo anthu ndi akavalo ndiwo ankakoka ngolo m’makwalala. Anthu ankagwiritsira ntchito nyali za palafini pounikira, ndipo ankaotha moto wa nkhuni ndi malasha m’nyumba zawo zamatabwa zopaka utoto woyera. Ndinabadwira kumeneko m’June 1898, wachiŵiri m’banja la ana asanu.

MU 1905, Atate anali paulova, choncho anapita ku United States. Anabwerako patatha zaka zitatu ndipo anabweretsa sutikesi yodzaza ndi mphatso zosangalatsa za anafe komanso nsalu zabafuta ndi zinthu zina za Amayi. Koma katundu wawo wamtengo wapatali zedi anali mabuku olembedwa ndi Charles Taze Russell otchedwa Studies in the Scriptures.

Atate anayamba kuuza mabwenzi ndi achibale zinthu zimene anaphunzira m’mabuku ameneŵa. Pamisonkhano m’nyumba yamapemphero yakumeneko, iwo ankagwiritsira ntchito Baibulo pofuna kutsimikiza kuti kulibe helo wamoto. (Mlaliki 9:5, 10) Mu 1909, patatha chaka chimodzi chibwerere Atate kuchokera ku United States, Mbale Russell anayendera Norway ndipo anakamba nkhani ku Bergen ndi ku Kristiania, malo amene tsopano akutchedwa Oslo. Atate anapita ku Bergen kukamumvetsera.

Anthu ambiri ankati Atate akufalitsa ziphunzitso zonyenga. Ndinawamvera chisoni ndipo ndinawathandiza kugaŵa matrakiti a Baibulo kwa anansi. Mu 1912, ndinagaŵira trakiti lonena za helo kwa mwana wamkazi wa mtsogoleri wachipembedzo. Anatinyoza kwambiri ineyo ndi Atate. Ndinadabwa kwambiri kuti mwana wa mtsogoleri wachipembedzo angalankhule monyoza chotero!

Ophunzira Baibulo ena, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo, anali kudzatichezera nthaŵi zina ku Kopervik, mmodzi wa iwo anali Theodor Simonsen, munthu wolankhula mwaluso. Ndinkaitana anthu kuti adzamvetsere nkhani zomwe ankaperekera kunyumba kwathu. Asanakambe nkhani yake ankaimba zeze motsagana ndi nyimbo, ndipo atakamba nkhaniyo ankaimba nyimbo yotsazika. Tinkamdalira kwambiri.

Mlendo wina kunyumba kwathu anali Anna Andersen, mtumiki wa nthaŵi zonse. Iye anayendera matauni onse ku Norway, nthaŵi zambiri panjinga, akumagaŵira zofalitsa zofotokoza Baibulo kwa anthu. Iye anakhalapo ofesala mu Salvation Army ndipo ankadziŵana ndi atsogoleri ena a mu Salvation Army okhala ku Kopervik. Anamloleza kukamba nkhani ya Baibulo m’nyumba yawo yosonkhaniramo, ndipo ndinaitana anthu kuti adzamumvetsere.

Mtumiki wina wa nthaŵi zonse amene anadzatichezera ku Kopervik anali Karl Gunberg. Mwamuna wodzichepetsa, wodekha, koma wanthabwalayu, ankatumikiranso nthaŵi zina monga wotembenuza pa ofesi ya nthambi ku Oslo. Patapita zaka tinakagwirira ntchito limodzi kumeneko.

Kusonkhezeredwa ndi Malingaliro Achipembedzo

Panthaŵi imeneyo anthu ambiri sanali nchikhulupiriro cholimba chabe mwa Mulungu ndi Baibulo komanso mu zikhulupiriro zozama, monga moto wa helo ndi Utatu. Choncho panali mkangano waukulu ndithu pamene Ophunzira Baibulo anaphunzitsa kuti ziphunzitso zimenezi zinali zosemphana ndi Baibulo. Ndinasonkhezeredwa ndi zinenezo zoopsa za anansi athu zoti Atate anali a mpatuko. Ndipo nthaŵi ina ndinawauza kuti: “Zimene mumaphunzitsazi sizoona. Nziphunzitso za mpatuko!”

“Tabwera kuno, Ottilie,” anandilimbikitsa motero, “uone zimene Baibulo likunena.” Ndipo anandiŵerengera Malembawo. Choncho, chidaliro changa mwa iwo ndi zimene ankaphunzitsa chinakula. Anandilimbikitsa kuti ndiŵerenge Studies in the Scriptures, choncho m’chilimwe cha 1914, ndinkakonda kukhala paphiri lalitali m’tauniyo nkumaŵerenga.

Mu August 1914, anthu anasonkhana panja pa nyumba ina ya nyuzipepala akumaŵerenga za kuulika kwa Nkhondo Yadziko I. Atate anafika ndi kuona zimene zinali kuchitika. “Mulungu Alemekezeke!” anadzuma motero. Anazindikira kuti kuulika kwa nkhondoko kunali kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo amene iwo anali kulalikira. (Mateyu 24:7) Ophunzira Baibulo ambiri panthaŵiyo anakhulupirira kuti anali pafupi kutengedwa kupita kumwamba. Pamene zimenezi sizinachitike, ena anakhumudwa.

Kuchirikiza Kwanga Choonadi cha Baibulo

Mu 1915, pamsinkhu wa zaka 17, ndinatsiriza maphunziro a sukulu yapulaimale ndipo ndinayamba kugwira ntchito ya muofesi. Ndiyeno ndinayamba kuŵerenga Nsanja ya Olonda mokhazikika. Koma munali mu 1918 pamene misonkhano inayamba kuchitika mokhazikika ku Kopervik. Poyamba, tinkapezekapo asanu. Tinkaŵerenga zofalitsa za Watch Tower Society, monga Studies in the Scriptures, ndipo tinakambitsirana nkhani za m’bukulo mwa mafunso ndi mayankho. Ngakhale kuti Amayi ankayamikira kwambiri Ophunzira Baibulo atamacheza ndi anthu ena, iwo sanakhale mmodzi wa ife.

Ku ofesi kumene ndinkagwira ntchito, kuyambira mu 1918, ndinadziŵana ndi Anton Saltnes, amene ndinamthandiza kukhala Wophunzira Baibulo. Panthaŵiyi ndinakhala wofalitsa wokhazikika ndipo ndinabatizidwa pamsonkhano ku Bergen mu 1921.

M’May 1925 kunali msonkhano wa maiko onse a ku Scandinavia ku Örebro, Sweden. Panasonkhana anthu oposa 500, kuphatikizapo Joseph F. Rutherford, pulezidenti wa Watch Tower Society. Pafupifupi 30 a ife tinayenda kuchokera ku Oslo pasitima ya pamtunda imene tinachita haya.

Pamsonkhano umenewo analengeza kuti Ofesi ya ku Northern Europe idzakhazikitsidwa ku Copenhagen, Denmark, kuti izidzayang’anira ntchito yolalikira m’dera lonse la Scandinavia ndi m’maiko a ku Baltic. William Dey wa ku Scotland anapatsidwa udindo woyang’anira ntchito yolalikira. Anali wokondedwa kwambiri, ndipo posapita nthaŵi anamutcha dzina lakuti Big Scotsman. Poyambirira, Mbale Dey sankadziŵa nkomwe chinenero chilichonse cha ku Scandinavia, choncho ankakhala kumbuyo nthaŵi ya misonkhano ndi kumasamalira ana pofuna kuti makolo awo asumike maganizo pa zimene zikunenedwa papulatifomu.

Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 1, 1925, inalongosola Chivumbulutso chaputala 12 ndipo inafotokoza kuti chaputala chimenechi chimanena za kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu ndiponso kuti kubadwa kumeneku kunachitikira kumwamba mu 1914. Zinali zovuta kuti ndimvetsetse, choncho ndinaŵerenga nkhaniyo mobwerezabwereza. Pomaliza pamene ndinaimvetsetsa, ndinasangalala kwambiri.

Pamene kamvedwe kathu ka nkhani za m’Baibulo kasintha, ena akhumudwa ndi kuchoka pakati pa anthu a Mulungu. Koma pamene kuwongolera koteroko kwakhala kovuta kumvetsetsa, nthaŵi zonse ndaŵerenga nkhaniyo mobwerezabwereza kuti ndimvetsetse mfundo yake. Ngati sindikumvetsetsabe mafotokozedwe atsopanowo, ndimayembekezera mafotokozedwe owonjezereka. Kaŵirikaŵiri ndimapindula ndi kuleza mtima kotero.

Kutumikira pa Beteli

Kwa zaka zingapo ndinagwira ntchito yolemba kayendetsedwe ka ndalama za kampani, yaulembi, komanso yopenda maakaunti a chigawo china cha dziko lathu. Mu 1928 munthu amene ankayang’anira akaunti ya Sosaite anadwala choncho anachoka pa Beteli. Popeza kuti ntchito imeneyo ndinkaidziŵa, ndinapemphedwa kutenga malo ake. Ndinayamba kutumikira pa Beteli m’June 1928. Mbale Dey ankatichezera apo ndi apo ndi kupenda maakaunti anga. Banja lathu la Beteli linatsogoleranso ntchito yolalikira ku Oslo, kumene nthaŵiyo tinali ndi mpingo umodzi wokha.

Ena a ife ankathandiza mtumiki wotumiza mabuku pa Beteli, Mbale Sakshammer, kulongedza ndi kutumiza The Golden Age (imene tsopano ikutchedwa Galamukani!). Mbale Simonsen ndi Mbale Gunberg anali ena mwa anthu amene anathandiza. Tinkasangalala kwambiri, nthaŵi zambiri tikumaimba nyimbo uku tikugwira ntchito.

Kuyembekeza Ufumu Mwachidaliro

Mu 1935 tinazindikira kuti “khamu lalikulu” silinali gulu lachiŵiri lakumwamba. Tinaphunzira kuti m’malo mwake limaimira gulu la anthu opulumuka chisautso chachikulu ndipo ali ndi mwaŵi wokhala m’Paradaiso padziko lapansi kosatha. (Chivumbulutso 7:9-14) Pokhala ndi kamvedwe katsopanoka, ena amene ankadya zizindikiro za Chikumbutso anazindikira kuti chiyembekezo chawo chinali cha padziko lapansi, ndipo anasiya kudya.

Ngakhale kuti sindinkakayikira za chiyembekezo changa chopita kumwamba, ndinkakonda kudzifunsa kuti, ‘Nchifukwa ninji Mulungu akufuna ine?’ Ndinaganiza kuti ndinali wosayenerera mwaŵi waukulu chotero. Monga mkazi wamng’ono ndi wamanyazi, ndinaganiza kuti zinali zosayenera kuti ineyo ndingakhale mfumu yolamulira pamodzi ndi Kristu kumwamba. (2 Timoteo 2:11, 12; Chivumbulutso 5:10) Komabe, ndinalingalira za mawu a mtumwi Paulo akuti “ambiri amphamvu” saitanidwa, koma “Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, . . . kuti akachititse manyazi zamphamvu.”​—1 Akorinto 1:26, 27.

Ntchito m’Nthaŵi ya Nkhondo Yadziko II

Pa April 9, 1940, dziko la Norway linaukiridwa ndi asilikali a Germany, ndipo posakhalitsa dzikolo linalandidwa. Chifukwa cha nkhondoyo, ambiri anayamba kulandira uthenga wa Ufumu. Kuyambira m’October 1940 mpaka m’June 1941, tinagaŵira unyinji wa mabuku ndi timabuku woposa 272,000. Izi zinasonyeza kuti aliyense mwa Mboni zoposa 470 ku Norway panthaŵiyo anagaŵira avareji ya mabuku ndi timabuku yoposa 570 m’miyezi isanu ndi inayiyo!

Pa July 8, 1941, a gulu la Gestapo anakumana ndi oyang’anira otsogoza onse ndi kuwauza kuti ngati sasiya ntchito yolalikira, adzatumizidwa ku misasa yachibalo. Apolisi asanu achijeremani anafika ku Beteli ndi kulanda katundu wambiri wa Watch Tower Society. Banja la Beteli linatengedwa ndi kufunsidwa, koma palibe amene anaponyedwa m’ndende. Pomaliza, pa July 21, 1941, nyumba ya Sosaite, ya Inkognitogaten 28 B, inalandidwa, ndipo ntchito yathu yolalikira inaletsedwa. Ndinabwerera ku Kopervik ndi kupeza ntchito yakuthupi kuti ndizipeza zosoŵa zanga.

Panthaŵiyo, Atate ankatumikira monga mpainiya. Tsiku lina Anazi anabwera ndi kusecha m’nyumba ya Atate. Anatenga mabuku awo onse, kuphatikizapo ma Baibulo awo ndi makonkodansi awo a Baibulo. Tinkalandira chakudya chauzimu chochepa kwambiri panthaŵi imeneyo. Kuti tikhale olimbabe mwauzimu, tinkaphunzira mabuku akale mobwerezabwereza, monga buku la Government, ndipo tinapitirizabe kulalikira.

Mwachisoni, kumalo ambiri abale anapatukana. Ena anaganiza kuti tiyenera kumalalikira poyera ndi kupita kunyumba ndi nyumba pamene ena anaganiza kuti tiyenera kumalalikira mobisa kwambiri, kufikira anthu mochenjera. Choncho, abale otchuka, amene poyambirira ankagwirizana bwinobwino amenenso tinkawakonda kwambiri, sankalankhulana. Kupatukana kwawoku kunandipweteka maganizo koposa chilichonse chikhalire Mboni.

Ntchito Iyambanso Kuyenda Bwino Nkhondo Itatha

Nkhondo itatha, m’chilimwe cha 1945, Mbale Dey anadzacheza ku Norway ndipo anachititsa misonkhano ku Oslo, Skien, ndi ku Bergen. Iye anapempha abalewo kuti ayanjanenso ndipo anapempha onse amene anafuna kutero kuti aimirire. Onse anaimirira! Nkhaniyi inathetsedwa kwenikweni m’December 1945, Nathan H. Knorr, pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, atachezera dzikoli.

Posapita nthaŵi, pa July 17, 1945, ndinalandira telegalamu kuchokera kwa mtumiki wanthambi, Mbale Enok Öman, yonena kuti: ‘Kodi mungabwerere liti ku Beteli?’ Ena ankanena kuti ndikhalebe panyumba kuti ndizisamalira atate anga, amene panthaŵiyo anali ndi zaka zoposa 70. Koma Atate anandilimbikitsa kuti ndikapitirize utumiki wa pa Beteli, zimenedi ndinachita. Mu 1946, Marvin F. Anderson, mbale wochokera ku United States, anakhala woyang’anira wathu wa nthambi, ndipo ntchito yolalikira inayambanso kuyenda bwino.

Nthaŵi zatchuti cha m’chilimwe ndinkapita ku Kopervik kukaona apabanja langa. Abale anga aŵiri ndi alongo anga aŵiri sanakhale Mboni, koma ankawakondabe Atate ndi ine yemwe. Mmodzi mwa abale angawa anali mkulu wapadoko ndi mkulu wa oyendetsa sitima za m’madzi, ndipo winayo anali mphunzitsi. Ngakhale kuti ndinali ndi zinthu zakuthupi zochepa, Atate ankawauza kuti: “Ottilie ngolemera kuposa inu.” Ndipo zinalidi zoona! Zinthu zimene iwo anali nazo zinali zosafanana ndi chuma chauzimu chimene ineyo ndinali nacho! Atate anamwalira pamsinkhu wa zaka 78 mu 1951. Amayi anamwalira mu 1928.

Chochitika chosangalatsa kwambiri m’moyo wanga chinali kukachita nawo msonkhano wa mitundu yonse wa anthu a Yehova ku New York City mu 1953. M’chaka chimenecho, chiŵerengero cha ofalitsa padziko lonse lapansi chinapambana 500,000, ndipo anthu oposa 165,000 anakachita nawo msonkhanowo! Msonkhano umenewu wa mu 1953 usanachitike, ndinagwira ntchito kwa mlungu umodzi pa Beteli ya ku Brooklyn, likulu la gulu la Yehova padziko lapansi.

Kuchita Zimene Ndingathe

M’zaka zaposachedwapa kupenya kwanga kwakhala kovutikira chifukwa cha ng’ala. Ndimaŵerengabe malemba akuluakulu pogwiritsira ntchito mandala amphamvu kwambiri ndi galasi lokuza zinthu. Ndiponso alongo achikristu amadzandichezera ndi kundiŵerengera kaŵiri pamlungu, zimene ndimayamikira kwambiri.

Sindilalikiranso kwambiri. M’chilimwe, alongo achikristu nthaŵi zina amandiyendetsa pampando wanga wamaŵiro kupita nane kumalo kumene ndingalalikire. Nthaŵi zonse ndimatumizanso magazini ndi mabrosha kusukulu za m’Kopervik, monga kusukulu yapulaimale kumene ndinkaphunzirako pafupifupi zaka 100 zapitazo. Ndili wosangalala kuti ndikukwanitsabe kukhala wofalitsa wokhazikika.

Mwamwaŵi nyumba yodyeramo ndi Nyumba ya Ufumu zili pansanja imodzi ndi chipinda changa pa Beteli, imene chiyambire 1983 ili ku Ytre Enebakk kunja kwa mzinda wa Oslo. Choncho ndimatha kupezeka pakulambira kwa mmaŵa, pachakudya, ndi pamisonkhano yathu mwa kugwiritsira ntchito mpando wamaŵiro. Ndipo ndikusangalala popeza kuti ndimapitabe kumisonkhano. Ndimasangalala kuonana ndi mabwenzi amene ndadziŵana nawo kwa zaka zambiri, komanso abale ndi alongo achatsopano ndi ana ambiri osangalatsa.

Kukhulupirika Mpaka Mapeto

Ndi dalitso lalikulu kukhala pamodzi ndi anthu achangu, osangalatsa, ndi ochita zinthu zauzimu pano pa Beteli. Pamene ndinayamba utumiki wanga wa pa Beteli, banja lonse linali ndi anthu amene anali ndi chiyembekezo chopita kumwamba. (Afilipi 3:14) Tsopano aliyense pa Beteli kusiyapo ine, akuyembekezera kudzakhala kosatha padziko lapansi.

Zoonadi, tinkayembekezera kuti Yehova adzaloŵererapo mwamsanga. Komabe, ndimasangalala nditaona kuwonjezereka kwa khamu lalikulu. Ndaona chiwonjezeko chotani nanga! Pamene ndinangoyamba utumiki, panali ofalitsa pafupifupi 5,000 padziko lonse lapansi. Tsopano pali ofalitsa oposa 5,400,000! Zoonadi, ndaona ‘wamng’ono akusanduka chikwi, ndi wochepa akusanduka mtundu wamphamvu.’ (Yesaya 60:22) Tiyenera kuyembekezera Yehova, monga momwe mneneri Habakuku analembera kuti: “Akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.”​—Habakuku 2:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena