“Lemekeza Yehova ndi Chuma Chako”—Motani?
“LEMEKEZA Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha.” M’mawu anzeru ouziridwa ameneŵa, olembedwa zaka ngati 2,600 zapitazo, muli mfungulo yokhalira ndi madalitso a Yehova ochuluka, popeza wolembayo akufotokozanso kuti: “Motero nkhokwe zako zidzangoti the, mbiya zako zidzasefuka vinyo.”—Miyambo 3:9, 10.
Koma kodi kulemekeza Mulungu kumatanthauzanji? Kodi chuma chimene tiyenera kulemekeza nacho Yehova ndicho chiyani? Ndipo kodi zimenezi tingazichite motani?
“Lemekeza Yehova”
M’Malemba, liwu lenileni lachihebri lotanthauza ulemu, ka·vohdhʹ, kwenikweni limatanthauza “kulemera.” Choncho kulemekeza munthu kumatanthauza kumuona ngati wolemerera, wochititsa chidwi, kapena wofunika kwambiri. Liwu linanso lachihebri lotanthauza ulemu, yeqarʹ, limatembenuzidwanso kukhala “cha mtengo wapatali” ndi “zinthu za mtengo wapatali.” Mofananamo, liwu lachigiriki lakuti ti·meʹ, lotembenuzidwa kuti “ulemu” m’Baibulo, limapereka lingaliro la kukwezeka, kufunika, ndi kukhala wa mtengo wapatali. Choncho munthu amalemekeza wina mwa kumsonyeza ulemu waukulu ndi kumkweza.
Kupereka ulemu kulinso ndi mbali ina. Talingalirani za nkhani yokhudza Myuda wokhulupirika Moredekai, amene panthaŵi ina anavumbula chiŵembu chofuna kupha Mfumu Ahaswero ya Perisiya wakale. Pambuyo pake, mfumu itadziŵa kuti Moredekai sanalemekezedwe chifukwa cha zimene anachitazo, mfumuyo inafunsa nduna yake yaikulu, Hamani, za njira yabwino kwambiri yosonyezera ulemu kwa munthu amene mfumu yakondwera naye. Hamani anaganiza kuti ulemu umenewo unayenerera iye, koma anaphonya chotani nanga! Ngakhale zili choncho, Hamani ananena kuti munthu woteroyo ayenera kuvekedwa “chovala chachifumu” ndi kukwera “kavalo amakwerapo mfumu.” Anamaliza kuti: “Namuyendetse pa kavaloyo m’khwalala la m’mudzi, nafuule pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.” (Estere 6:1-9) Pachochitikachi, kusonyeza munthu ulemu kunaloŵetsapo kumkweza poyera kotero kuti anthu onse ampatse ulemu waukulu.
Mofananamo, kulemekeza Yehova kuli ndi mbali ziŵiri: kumsonyeza ulemu waukulu pawekha ndi kumkweza poyera mwa kutengamo mbali ndi kuchirikiza ntchito yolengeza dzina lake poyera.
“Chuma Chanu”—Kodi Ndicho Chiyani?
Ndithudi chuma chathu chimaphatikizapo moyo wathu, nthaŵi yathu, maluso athu, ndi nyonga yathu. Bwanji za katundu wathu wakuthupi? Talingalirani zimene Yesu ananena ataona mkazi wamasiye waumphaŵi akuponya timakobiri tiŵiri tochepa mphamvu mosungiramo ndalama m’kachisi. Iye anati: “Wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse; pakuti onse ameneŵa [enanso amene anaikamo ndalama] anaika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma iye mwa kusoŵa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.” (Luka 21:1-4) Yesu anathokoza mkazi wamasiye ameneyu chifukwa chogwiritsira ntchito zinthu zake zakuthupi pochirikiza kulambira Yehova.
Choncho mwachionekere, chuma chotchulidwa ndi Solomo chimaphatikizaponso zinthu zilizonse zakuthupi zimene tingakhale nazo. Ndipo mawu akuti “zoyambirira kucha” amapereka lingaliro la kupatsa Yehova zinthu zabwino koposa zomwe tili nazo.
Komano, kodi kupereka zinthu zakuthupi kungamlemekeze motani Mulungu? Kodi zinthu zonse si zake kale? (Salmo 50:10; 95:3-5) “Zonsezi zifuma kwanu,” anavomereza motero Mfumu Davide m’pemphero lochokera pansi pa mtima kwa Yehova. Ndipo ponena za chopereka chachikulu chimene iye ndi anthu ake anapereka kaamba ka kumanga kachisi, Davide anati: “Takupatsani zofuma ku dzanja lanu.” (1 Mbiri 29:14) Choncho popereka mphatso kwa Yehova, timangobwezera zimene iye, watipatsa chifukwa cha kukoma mtima kwake. (1 Akorinto 4:7) Koma, monga taonera poyambapo, kulemekeza Yehova kumaphatikizapo kumkweza pamaso pa ena. Ndipo mphatso zakuthupi zogwiritsiridwa ntchito kupititsira patsogolo kulambira koona zimalemekeza Mulungu. Baibulo lili ndi zitsanzo zabwino kwambiri za njira imeneyi yolemekezera Yehova.
Zitsanzo Zakale
Zaka ngati 3,500 zapitazo, pamene nthaŵi inafika yoti Yehova apereke chihema m’chipululu monga malo olambiriramo a Aisrayeli, panafunikira zinthu zosiyanasiyana za mtengo wapatali malinga ndi njira yomangira yoperekedwa ndi Mulungu. Yehova analamula Mose kulola ‘aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho chopereka cha Yehova.’ (Eksodo 35:5) Nkhaniyo imapitiriza kusimba kuti: “Anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.” (Eksodo 35:21) Kwenikweni, zopereka zawo zaufulu zinali zochuluka kuposa zimene zinafunikira pantchitoyo moti anthu ‘anangowaletsa asabwere nazo zina.’—Eksodo 36:5, 6.
Talingalirani za chitsanzo china. Pamene chihema chinatha ntchito yake ndiponso pamene makonzedwe omanga kachisi anali mkati, Davide iyemwini anapereka chopereka chachikulu ku kachisi amene mwana wake wamwamuna Solomo anali kudzamanga. Anaitaniranso ena kugwirizana naye, ndipo anthu analabadira mwa kupereka mphatso za zinthu za mtengo wake kwa Yehova. Mtengo wa golidi ndi siliva yekhayo lero ungafike pafupifupi $50,000,000,000. “Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu.”—1 Mbiri 29:3-9; 2 Mbiri 5:1.
‘ZoperekaZaufulu’ m’Tsiku Lathu
Kodi ifenso tingakondwere motani ndi kupereka zopereka zaufulu m’tsiku lathu? Ntchito yaikulu koposa imene ikuchitika m’dziko panthaŵi ino ndiyo ija ya kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Ndipo Yehova waona kuti nkoyenera kuikiza zinthu za Ufumu za padziko lapansi kwa Mboni zake.—Yesaya 43:10.
Nzachidziŵikire kuti ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita lerolino imafunikira ndalama. Kumanga ndi kusamalira Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano, maofesi anthambi, mafakitale, ndi nyumba za Beteli kumafuna ndalama. Kufalitsa ndi kutumiza mabaibulo ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo m’zinenero zosiyanasiyana kumafunanso ndalama. Kodi ndalama za gulu zoyendetsera zinthu zimenezi zimapezedwa bwanji? Mwa zopereka zaufulu basi!
Zopereka zochuluka zimachokera kwa anthu amene—monga mkazi wamasiye amene Yesu anaona—siali achuma. Posafuna kuphonya mwaŵi umenewu wolemekeza Yehova, iwo amapereka ndalama zochepa “monga mwa mphamvu yawo” ndipo, nthaŵi zina, ngakhale “koposa mphamvu yawo.”—2 Akorinto 8:3, 4.
“Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera,” anatero mtumwi Paulo kwa Akristu a ku Korinto. (2 Akorinto 9:7) Kupereka mokondwera kumafuna kulinganiza bwino. Paulo anauza Akorinto kuti: “Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.” (1 Akorinto 16:2) Mofananamo, mwaumwini ndipo modzifunira, ofuna kupereka zopereka zopititsira patsogolo ntchito ya Ufumu lerolino angapatule zina mwa ndalama zawo zimene amapeza kaamba ka chifuno chimenecho.
Yehova Amadalitsa Amene Amamlemekeza
Pamene kuli kwakuti kukhala ndi chuma chakuthupi mwa iko kokha sikumachititsa kupita patsogolo kwauzimu, kugwiritsira ntchito chuma chathu mooloŵa manja—nthaŵi yathu, nyonga yathu, ndi zinthu zathu zakuthupi—polemekeza Yehova kumadzetsa madalitso ochuluka. Zimakhala chonchi chifukwa chakuti Mulungu, amene zinthu zonse nzake, akutitsimikiza kuti: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”—Miyambo 11:25.
Mfumu Davide itafa, mwana wake Solomo anagwiritsira ntchito zopereka zaufulu zimene atate wake anasonkhanitsa kuti amangire kachisi waulemerero, monga momwe Yehova analangizira. Ndipo kwa nthaŵi yonse imene Solomo anakhalabe wokhulupirika pa kulambira kwake Mulungu, “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, . . . kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.” (1 Mafumu 4:25) Nkhokwe zinadzaza, zoponderamo mpesa zinasefukira—kwa nthaŵi yonse imene Aisrayeli ‘analemekeza Yehova ndi chuma chawo.’
Pambuyo pake, kudzera mwa mneneri Malaki, Yehova anati: “Mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.” (Malaki 3:10) Kulemera kwauzimu kumene atumiki a Yehova ali nako lerolino kuli umboni wakuti Mulungu wasunga pangano lake.
Ndithudi Yehova amakondwera pamene tichita mbali yathu popititsa patsogolo zinthu za Ufumu. (Ahebri 13:15, 16) Ndipo akulonjeza kuti adzatichirikiza ngati ‘tithanga tafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.’ (Mateyu 6:33) Mwachisangalalo chachikulu cha mumtima, tiyeni ‘tilemekeze Yehova ndi chuma chathu.’
[Bokosi pamasamba 28, 29]
Njira Zimene Ena Amasankha Kupatsiramo Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse
Ambiri amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku malikulu a dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yakwawo.
Zopereka zaufulu zandalama zingatumizidwenso mwachindunji ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201-2483, kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lanu. Majuwelo kapena zinthu zina za mtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso yeniyeni iyenera kutsagana ndi zoperekazo.
Makonzedwe a Chopereka cha Conditional-Donation. Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society pamakonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo wakhala ndi kusoŵa kwaumwini, zoperekazo zidzabwezeredwa kwa iye. Kuti mudziŵe zambiri, chonde lemberani ku Treasurer’s Office pakeyala yosonyezedwa pamwambayo.
Kupatsa Kolinganiza
Kuwonjezera pa mphatso zenizeni za ndalama ndi zopereka za ndalama za conditional, pali njira zinanso zopatsiramo kuti tithandizire utumiki wa Ufumu wa padziko lonse. Zimenezo zikuphatikizapo:
Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse otero.
Maakaunti a ku Banki: Maakaunti a ku banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma pantchito angaikiziridwe kapena kulipiridwa pambuyo pa imfa ku Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki akwanu. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse otero.
Stock ndi Bond: Stock ndi Bond ingapatsidwe monga chopereka ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kakonzedwe kamene woperekayo angapitirize kumalipiridwa ndalama zopindulidwa.
Malo: Malo okhoza kugulitsidwa angaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kusunga malowo mwini wake, amene angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Munthuyo ayenera kudziŵitsa Sosaite asanailoŵetse m’pangano la malo alionse.
Chuma cha Masiye ndi Choikizira: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma cha masiye lochitidwa mwa lamulo, kapena Sosaite ingalembetsedwe kukhala yodzapindula ndi pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma chopindulitsa gulu la chipembedzo lingakhale ndi mapindu ena a kuchepetsa msonkho. Kope la pangano la chuma cha masiye kapena choikizira liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Monga mwa tanthauzo la mawuwo “kupatsa kolinganiza,” zopereka zotere zimafunadi kuti woperekayo alinganize bwino. Kuti ithandize anthu ofuna kupindulitsa Sosaite kudzera mwa mtundu wina wa kupatsa kolinganiza, brosha lakuti Planned Giving to Benefit Kingdom Service Worldwide [Kupatsa Kolinganiza Kopindulitsa Utumiki wa Ufumu Padziko Lonse] lakonzedwa. Brosha limeneli linalembedwa chifukwa cha mafunso ambiri amene Sosaite inafunsidwa ponena za mphatso, chuma cha masiye, ndi chuma choikizira. Lilinso ndi chidziŵitso china chothandiza chonena za malo, kulinganiza ndalama ndi misonkho, ndipo lakonzedwa kuti lithandize anthu ku United States ofuna kupindulitsa zinthu za Ufumu padziko lonse kuti asankhe njira zopindulitsa ndiponso zabwino kwambiri malinga ndi mikhalidwe ya banja lawo ndi mikhalidwe yawo yaumwini. Mwa kuŵerenga brosha limeneli ndi kukambirana ndi amene amagwira ntchito pa Planned Giving Desk, ambiri athandiza Sosaite ndiponso panthaŵi imodzimodziyo kupeza mapindu aakulu kwambiri a msonkho pochita zimenezo. Broshali lingatumizidwe kwa inu mutapempha, mwa kulemba kapena pafoni.
Awo amene akufuna kugwiritsira ntchito alionse a makonzedwewa a kupatsa kolinganiza ayenera kulankhula ndi Planned Giving Desk, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 100 Watchtower Drive, Patterson, New York 12563-9204, nambala ya telefoni (914) 878-7000, kapena ayenera kulankhula ndi ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lawo.