Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 4/1 tsamba 15-20
  • Buku Lochokera kwa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Buku Lochokera kwa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Buku Logwirizana ndi Sayansi
  • Buku Lothandiza pa Moyo Wamakono
  • Buku la Ulosi Woona
  • Kodi Buku Limeneli Limagwirizana ndi Sayansi?
    Buku la Anthu Onse
  • Buku la Ulosi
    Buku la Anthu Onse
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Buku Lothandiza pa Moyo Wamakono
    Buku la Anthu Onse
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 4/1 tsamba 15-20

Buku Lochokera kwa Mulungu

“Ulosi sunakhalako nthaŵi iliyonse mwa chifuniro cha munthu, koma anthu anauziridwa ndi Mulungu mmene anagwidwa ndi mzimu woyera.”​—2 PETRO 1:21, NW.

1, 2. (a) Kodi nchifukwa chiyani ena amakayikira zonena kuti Baibulo nlofunika pamoyo wamakono? (b) Kodi ndi maumboni atatu ati amene tingagwiritsire ntchito posonyeza kuti Baibulo nlochokera kwa Mulungu?

KODI Baibulo nlofunika kwa anthu amene ali pafupi kuloŵa m’zaka za zana la 21? Ena amaganiza kuti nlosafunika. “Palibe amene angalimbikitse kuti kalasi lamakono lophunzira zamakemikolo lizigwiritsira ntchito kope la mu 1924 la buku lophunzitsa zamakemikolo​—maphunziro a zamakemikolo apita patsogolo kwambiri kuchokera panthaŵi imeneyo,” analemba motero Dr. Eli S. Chesen, pofotokoza chifukwa chimene amaganizira kuti Baibulo linatha ntchito. Kuwatenga mwachisawawa, mawu ameneŵa akuoneka ngati anzeru. Ndi iko komwe, munthu waphunzira zambiri zokhudzana ndi sayansi, zamaganizo, ndi khalidwe la munthu kuchokera m’nthaŵi za Baibulo. Choncho, ena amafunsa kuti: ‘Kodi buku lakale chonchi lingakhale motani lopanda zolakwa pankhani zasayansi? Lingakhale motani ndi uphungu wothandiza pamoyo wamakono?’

2 Baibulo lenilenilo likuyankha. Pa 2 Petro 1:21, tikuuzidwa kuti aneneri a Baibulo “anauziridwa ndi Mulungu mmene anagwidwa ndi mzimu woyera.” Choncho Baibulo likusonyeza kuti lili buku lochokera kwa Mulungu. Komano kodi ena tingawakhutiritse motani kuti zili choncho? Tiyeni tikambitsirane maumboni atatu osonyeza kuti Baibulo ndilo Mawu a Mulungu: (1) Nlolondola pankhani za sayansi, (2) lili ndi mapulinsipulo ogwira ntchito nthaŵi zonse ofunika pamoyo wamakono, ndiponso (3) lili ndi maulosi olunjika amene akwaniritsidwa, monga momwe mbiri yakale imachitira umboni.

Buku Logwirizana ndi Sayansi

3. Kodi nchifukwa chiyani Baibulo silinatsutsidwe ndi zimene sayansi yapeza?

3 Baibulo si buku lophunzitsa sayansi. Komabe, ndi buku la choonadi, ndipo silingathe ntchito chifukwa chokhalapo kwa nthaŵi yaitali. (Yohane 17:17) Zimene sayansi yapeza sizinalitsutse Baibulo. Pamene litchula nkhani zokhudzana ndi sayansi, ilo lilibiretu ziphunzitso zakale “za sayansi” zimene zinadzadziŵika kuti ndi nthanthi wamba. Kwenikweni, ilo lili ndi mawu amene saali chabe oona pa za sayansi komanso amene anatsutsana kotheratu ndi malingaliro omwe anthu anali nawo panthaŵiyo. Mwachitsanzo, talingalirani za kugwirizana kwa Baibulo ndi sayansi ya zamankhwala.

4, 5. (a) Kodi nchiyani chimene asing’anga akale sanamvetse ponena za matenda? (b) Kodi nchifukwa chiyani Mose mosakayikira anali kudziŵa za machiritso a asing’anga a ku Igupto?

4 Asing’anga akale sanali kudziŵa bwino mmene matenda amafalikirira, ndiponso sanazindikire za kufunika kwa ukhondo poletsa matenda. Machiritso ambiri akale angaoneke kukhala aumbuli powayerekezera ndi machiritso amakono. Limodzi mwa mabuku akale kwambiri olongosola za mankhwala limene lilipo ndilo Ebers Papyrus, ndondomeko ya chidziŵitso cha ku Igupto cha zamankhwala, ya m’chaka cha 1550 B.C.E. Cholembedwa chimenechi chili ndi machiritso 700 a matenda osiyanasiyana, “kuchokera pa kulumidwa ndi ng’ona mpaka kupweteka kwa zikhadabo zakumiyendo.” Machiritso ambiri sanali kugwira ntchito, koma ena mwa iwo anali angozi kwambiri. Kuti munthu achiritse bala, malangizo ena anati kuli bwino kuikapo msanganizo wa zonyansa za munthu pamodzi ndi zinthu zina.

5 Cholembedwa chimenechi cha machiritso a ku Igupto chinalembedwa cha panthaŵi imodzimodzi ndi mabuku oyamba a Baibulo, amene anaphatikizapo Chilamulo cha Mose. Mose, amene anabadwa m’chaka cha 1593 B.C.E., anakulira ku Igupto. (Eksodo 2:1-10) Popeza kuti analeredwera m’nyumba ya Farao, Mose “anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto.” (Machitidwe 7:22) Iye anali kuwadziŵa “asing’anga” a ku Igupto. (Genesis 50:1-3) Kodi iye analemba za machiritso awo osagwira ntchito kapena angozi amenewo m’zolemba zake?

6. Kodi ndi malangizo ati osungitsa ukhondo a m’Chilamulo cha Mose amene sayansi yamakono ya zamankhwala ingawaone kuti ndi abwino?

6 Mosiyana ndi zimenezo, Chilamulo cha Mose chinali ndi malangizo onena za ukhondo amene sayansi yamakono ya zamankhwala ingawaone kuti ndi abwino. Mwachitsanzo, lamulo lonena za misasa ya asilikali linalamula kuti zonyansa zizifotseredwa kunja kwa msasa. (Deuteronomo 23:13) Imeneyi inali njira yapamwamba kwambiri yopeŵera matenda. Inathandiza kuti zitsime zizikhala ndi madzi opanda matenda ndiponso inawatchinjiriza ku matenda a kamwazi ofalitsidwa ndi ntchentche ndi matenda enanso otsegula m’mimba amene amapha anthu mamiliyoni ambiri chaka chilichonse, makamaka m’maiko amene akutukuka kumene.

7. Kodi ndi malangizo ati osungitsa ukhondo a m’Chilamulo cha Mose amene anathandizira kuti matenda opatsirana asafalikire?

7 Chilamulo cha Mose chinalinso ndi malangizo ena osungitsa ukhondo amene anathandizira kuti matenda ena opatsirana asafalikire. Munthu amene anali ndi matenda opatsirana kapena amene anamuganizira kuti ali nawo anali kubindikiritsidwa kwayekha. (Levitiko 13:1-5) Zovala kapena zotengera zimene zinakhudza nyama imene inadzifera yokha (mwinamwake ndi matenda) zinayenera kuchapidwa asanazigwiritsirenso ntchito kapena anayenera kuziwononga. (Levitiko 11:27, 28, 32, 33) Munthu aliyense amene anakhudza mtembo anali kumuona ngati wodetsedwa ndipo anayenera kuyeretsedwa kumene kunaphatikizapo kuchapa zovala zake ndiponso kusamba. Pamasiku asanu ndi aŵiri pamene ali wodetsedwa, iye anayenera kupeŵa kukhudzana ndi ena.​—Numeri 19:1-13.

8, 9. Kodi nchifukwa chiyani tinganene kuti malamulo onena za ukhondo m’Chilamulo cha Mose anali apamwamba kwambiri kuposa nzeru za panthaŵiyo?

8 Malangizo osungitsa ukhondo ameneŵa akusonyeza nzeru imene inali yapamwamba kwambiri kuposa nzeru za panthaŵiyo. Sayansi yamakono ya zamankhwala yaphunzira zambiri ponena za kufalikira kwa matenda ndi njira zake zowaletsera. Mwachitsanzo, kupita patsogolo kwa zamankhwala m’zaka za zana la 19 kunachititsa kuti ayambe njira yochepetsera matenda mwa kukhala aukhondo. Chotsatirapo chake chinali chakuti matenda ndi imfa za mwadzidzidzi zinachepa kwambiri. M’chaka cha 1900, anthu ku maiko ambiri a ku Ulaya ndi ku United States panthaŵi yawo ya kubadwa sanali kuyembekezeredwa kukhala moyo kwa zaka zoposa 50. Chiyambire nthaŵiyo, iwo ayamba kukhala ndi moyo wautali, osati chabe chifukwa cha kupita patsogolo kwa njira zoletsera matenda komanso chifukwa cha ukhondo ndi moyo wabwino.

9 Komabe, zaka zikwi zambiri sayansi ya zamankhwala isanaphunzire mmene matenda amafalikirira, Baibulo linapereka njira zabwino zodzitchinjirizira ku matenda. Mosadabwitsa, Mose ananena za Aisrayeli a m’tsiku lake kuti anali kukhala moyo zaka 70 kapena 80 zakubadwa. (Salmo 90:10) Kodi Mose anawadziŵa motani malangizo osungitsa ukhondo ameneŵa? Baibulo lenilenilo likufotokoza kuti: Mpambo wa Chilamulo ‘unatumizidwa kudzera mwa angelo.’ (Agalatiya 3:19, NW) Inde, Baibulo si buku la nzeru za anthu; ndi buku lochokera kwa Mulungu.

Buku Lothandiza pa Moyo Wamakono

10. Ngakhale kuti Baibulo linamalizidwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, kodi uphungu wake ngwotani?

10 Mabuku opereka uphungu amatha ntchito ndipo posapita nthaŵi amakonzedwanso kapena kuloŵedwa m’malo ndi ena. Koma Baibulo nlapaderadi. “Zikumbutso zanu zakhala zodalirika kwambiri,” limatero Salmo 93:5 [NW]. Ngakhale kuti anamaliza kulemba Baibulo pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, mawu ake akugwirabe ntchito. Ndipo ali ndi mphamvu imodzimodzi mosasamala kanthu za maonekedwe a khungu lathu kapena dziko limene tikukhalamo. Talingalirani za zitsanzo zina za uphungu wa m’Baibulo ‘wodalirika kwambiri’ ndiponso wogwira ntchito nthaŵi zonse.

11. Zaka makumi ambiri zapitazo, kodi nchiyani chimene makolo anaphuzitsidwa ponena za kulanga ana?

11 Zaka makumi ambiri zapitazo makolo ambiri​—mosonkhezeredwa ndi “malingaliro atsopano” onena za kulera ana​—anali kuganiza kuti “kuletsa nkoletsedwa.” Iwo anali kuopa kuti kuletsa ana kuchita zinthu zina kungachititse anawo mantha aakulu ndi kukhumudwa. Aphungu a zolinga zabwino analimbikira kunena kuti makolo ayenera kupeŵa kuwongolera ana awo mwamphamvu. Akatswiri ambiri ameneŵa tsopano “akulimbikitsa makolo kukhala olimba paziletso zawo, kuti ayambenso kulanga ana awo,” ikutero The New York Times.

12. Kodi nauni yachigiriki yotembenuzidwa kuti “chilango” imatanthauzanji, ndipo nchifukwa ninji ana amafunikira chilango?

12 Komabe, kuyambira kalekale, Baibulo lakhala likupereka uphungu wolunjika ndiponso wolinganizika bwino pankhani yophunzitsa ana. Ilo limalangiza kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Nauni yachigiriki yotembenuzidwa kuti “chilangizo” imatanthauza “kulera, kuphunzitsa, kulangiza.” Baibulo limanena kuti chilango, kapena kuti malangizo, ali umboni wa chikondi cha makolo. (Miyambo 13:24) Ana amakula bwino pamene alandira malangizo otsimikizirika amene amawathandiza kuzindikira chabwino ndi choipa. Chilango choperekedwa moyenerera chimawathandiza kudzimva kukhala osungika; chimawauza kuti makolo awo amasamala za iwo ndi mtundu wa munthu umene anawo akukhala.​—Yerekezerani ndi Miyambo 4:10-13.

13. (a) Ponena za chilango, kodi Baibulo limapereka chenjezo lotani kwa makolo? (b) Kodi ndi chilango chotani chimene Baibulo limanena kuti nchabwino?

13 Koma Baibulo limachenjeza makolo pankhani ya chilangoyi. Ulamuliro wa makolo suyenera kukhala wankhanza. (Miyambo 22:15) Palibe mwana amene ayenera kulangidwa mwankhanza. Chiwawa chenicheni sichiyenera kupezeka m’banja lotsatira Baibulo. (Salmo 11:5) Ngakhalenso chiwawa chokhudza maganizo​—mawu aukali, kusuliza kosalekeza, ndi kutukwana, zonse zomwe zingaswe mzimu wa mwana. (Yerekezerani ndi Miyambo 12:18.) Mwanzeru, Baibulo limachenjeza makolo kuti: “Musaputa ana anu, kuti angataye mtima [kapena kuti, “mungawafooketse,” Phillips].” (Akolose 3:21) Baibulo limapereka njira zopeŵera zimenezi. Pa Deuteronomo 11:19, makolo akulimbikitsidwa kugwiritsira ntchito nthaŵi zocheza kuti akhomereze malangizo a khalidwe labwino ndi auzimu mwa ana awo. Uphungu womveka ndiponso wabwino umenewu wa kulera ana ngwofunika lerolino monga momwe unalili m’nthaŵi za Baibulo.

14, 15. (a) Kodi ndi motani mmene Baibulo silimangoperekera uphungu wanzeru wokha? (b) Kodi ndi ziphunzitso za Baibulo zotani zimene zingathandizire amuna ndi akazi a mafuko ndi mitundu yosiyanasiyana kuonana kuti ndi olingana?

14 Baibulo silimangopereka uphungu wanzeru wokha. Uthenga wake umaloŵa mumtima. Ahebri 4:12 amati: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” Talingalirani chitsanzo cha mphamvu yosonkhezera ya Baibulo.

15 Lerolino anthu ngogaŵanika chifukwa cha ufuko ndi utundu. Zopinga zimenezi zonga makoma zasonkhezera anthu kuphana mwachisawawa m’nkhondo za padziko lonse. Komabe, Baibulo lili ndi ziphunzitso zimene zimathandiza amuna ndi akazi a mafuko osiyanasiyana kuonana kuti ali ofanana. Mwachitsanzo, Machitidwe 17:26 amanena kuti “ndi mmodzi [Mulungu] analenga mitundu yonse ya anthu.” Zimenezi zikusonyeza kuti kwenikweni pali fuko limodzi lokha​—fuko la anthu! Baibulo limapitirizanso kutilimbikitsa kuti ‘tikhale akutsanza a Mulungu,’ amene limanena kuti: “[Iye] alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Aefeso 5:1; Machitidwe 10:34, 35) Kwa awo amene amayesetsa kutsatira ziphunzitso za Baibulo, chidziŵitso chimenechi chimawagwirizanitsa. Chimaloŵa mkati mwenimweni​—mumtima​—kusungunula zopinga za anthu zimene zimawagaŵanitsa. Kodi zimathekadi m’dziko lamakono?

16. Simbani chochitika chosonyeza kuti Mboni za Yehova zili ndi ubale woona wapadziko lonse.

16 Ndithudi zimatheka! Mboni za Yehova zimadziŵika bwino lomwe chifukwa cha ubale wawo wapadziko lonse, umene umagwirizanitsa anthu a mitundu yosiyanasiyana amene mwachibadwa sakanakhalirana pamtendere. Mwachitsanzo, m’nkhondo yamafuko ku Rwanda, Mboni za Yehova za fuko lililonse zinatetezera abale awo ndi alongo awo achikristu a fuko lina, mwakutero zikumaika moyo wawo pachiswe. Nthaŵi ina yake, Mboni yachihutu inabisa m’nyumba mwake anthu asanu ndi mmodzi a m’banja lachitutsi la mumpingo mwake. Mwachisoni, banja lachitutsilo m’kupita kwa nthaŵi analipeza ndipo anawapha. Mbale wachihutuyo ndi banja lake tsopano anayang’anizana ndi akupha okwiyawo ndipo anathaŵira ku Tanzania. Zitsanzo zambiri zofanana ndi chimenechi zinasimbidwa. Mboni za Yehova zimavomereza motsimikiza kuti kugwirizana kotereku nkotheka chifukwa chakuti mitima yawo yakhudzidwa kwambiri ndi mphamvu yosonkhezera ya uthenga wa Baibulo. Kugwirizanitsa anthu kwa Baibulo m’dziko lino lodzala ndi udani kuli umboni wamphamvu wakuti linachokera kwa Mulungu.

Buku la Ulosi Woona

17. Kodi maulosi a m’Baibulo asiyana motani ndi maulosi a anthu?

17 “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pachokha,” amatero 2 Petro 1:20. Aneneri a m’Baibulo sanayambe apenda zochitika za m’dziko lapansi ndiyeno nkulosera malinga ndi kamasuliridwe kawo ka zochitika zimenezi. Ndiponso sananene maulosi osalunjika bwino amene akanasinthidwa kuti agwirizane pafupifupi ndi chochitika chilichonse chamtsogolo. Monga chitsanzo, tiyeni tilingalire za ulosi wina wa m’Baibulo umene unali wolunjika mwapadera ndiponso umene unaneneratu zosemphana kotheratu ndi zimene anthu okhalako panthaŵiyo anali kuyembekezera.

18. Kodi nchifukwa chiyani anthu a m’Babulo wakale mosakayikira anamva kukhala osungika kwambiri, komabe kodi nchiyani chimene Yesaya anali atalosera ponena za Babulo?

18 Podzafika m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., Babulo anali likulu looneka ngati losagonjetseka la Ufumu wa Babulo. Mzindawo unali mbali zonse ziŵiri za Mtsinje wa Firate, ndipo madzi a mtsinjewo anawagwiritsira ntchito kupanga chemba lalikulu lotetezera ndi mifuleni yambiri. Mzindawo unatetezeredwanso ndi makoma aŵiri aakulu ophatikana, okhala ndi nsanja za asilikali achitetezo. Mosakayikira, anthu a m’Babulo anali kumva kukhala osungika kwambiri. Komabe, m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., Babulo asanafike nkomwe paulemerero wake waukulu, mneneri Yesaya analosera kuti: “Babulo . . . adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora. Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; Mwarabu sadzamanga hema wake pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu awo kumeneko.” (Yesaya 13:19, 20) Taonani kuti ulosiwo sunaneneretu chabe kuti Babulo adzawonongedwa komanso kuti anthu sadzakhalamo nthaŵi zonse. Analimba mtima chotani nanga poneneratu zimenezo! Kodi zingakhale kuti Yesaya analemba ulosi wake ataona kuti Babulo ali wabwinja? Mbiri ikuyankha kuti ayi!

19. Kodi nchifukwa chiyani ulosi wa Yesaya sunakwaniritsidwe wonse pa October 5, 539 B.C.E.?

19 Usiku wa pa October 5, 539 B.C.E., Babulo anagonja kwa makamu ankhondo a Amedi ndi Aperisi otsogozedwa ndi Koresi Wamkulu. Komabe, ulosi wa Yesaya sunakwaniritsidwe wonse panthaŵiyo. Koresi atalanda mzindawo, Babulo wokhala ndi anthu​—ngakhale kuti sanali wamphamvu​—anakhalako zaka mazana ambiri. M’zaka za zana lachiŵiri B.C.E., chapanthaŵi imodzimodziyo imene Mpukutu wa Yesaya wa m’Nyanja Yakufa unajambulidwa, anthu a ku Parthia analanda Babulo, mzinda umene panthaŵiyo unali kuonedwa monga chinthu chamtengo wapatali chimene mitundu yoyandikana nawo inali kulimbanirana. Wolemba mbiri wachiyuda Josephus anasimba kuti m’zaka za zana loyamba B.C.E., Ayuda “ochuluka kwambiri” anali kukhala kumeneko. Malinga nkunena kwa The Cambridge Ancient History, eni malonda a ku Palmyra anatsegula msika wamphamvu kwambiri ku Babulo mu 24 C.E. Choncho, mpaka m’zaka za zana loyamba C.E., Babulo yense anali asanakhalebe wapululu; komatu, buku la Yesaya linali litamalizidwa kalekale nthaŵiyi isanakwane.​—1 Petro 5:13.

20. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti m’kupita kwa nthaŵi Babulo anangokhala “miunda” wamba?

20 M’moyo wake wonse, Yesaya sanamuone Babulo atakhala wapululu. Koma monga momwedi ulosi unanenera, m’kupita kwa nthaŵi Babulo anangokhala “miunda” wamba. (Yeremiya 51:37) Malinga nkunena kwa katswiri wamaphunziro wachihebri Jerome (yemwe anabadwa m’zaka za zana lachinayi C.E.), podzafika m’tsiku lake Babulo anali malo osakako nyama kumene kunali “zilombo za mtundu uliwonse,” ndipo adakali wabwinja mpaka lero. Kukonzanso Babulo m’njira iliyonse monga malo okopa alendo kungachititsedi alendo kupitako, koma “mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna” cha Babulo sadzakhalamonso kosatha, monga momwe Yesaya ananeneratu.​—Yesaya 14:22.

21. Kodi nchifukwa chiyani aneneri okhulupirika anatha kuneneratu zamtsogolo mosaphonya kalikonse?

21 Si kuti mneneri Yesaya anangolota molondola. Ndiponso sanalembenso mbiri yakale kuti ioneke ngati ulosi. Yesaya anali mneneri woona. Momwemonso aneneri ena onse okhulupirika a m’Baibulo. Kodi amunawa anatha bwanji kuchita zimene munthu wina aliyense sangathe​—kuneneratu zamtsogolo mosaphonya kalikonse? Yankho lake nlomveka. Maulosiwo anachokera kwa Mulungu Waulosi, Yehova, ‘wolalikira za chimariziro kuyambira pachiyambi.’​—Yesaya 46:10.

22. Kodi nchifukwa chiyani tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe polimbikitsa anthu oona mtima kuti adzifufuzire okha Baibulo?

22 Chotero, kodi tiyenera kulifufuza Baibulo? Tikudziŵa kuti tiyenera kutero! Koma anthu ambiri si okhutira kuti ayenera kutero. Iwo akhala ndi malingaliro ena ponena za Baibulo ngakhale kuti mwina sanaliŵerengepo. Kumbukirani profesa uja amene tatchula pachiyambi pa nkhani yoyamba. Iye anavomera kukhala ndi phunziro la Baibulo, ndipo atalifufuza mosamalitsa Baibulo, anafika poona kuti ndi buku lochokera kwa Mulungu. M’kupita kwa nthaŵi anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo lero iye akutumikira monga mkulu! Tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kulimbikitsa anthu oona mtima kuti adzifufuzire okha Baibulo kenako adziŵe chokambapo ponena za ilo. Tili ndi chidaliro chakuti akafufuza Baibulo lenilenilo moona mtima, adzazindikira kuti buku lapadera limeneli, Baibulo, lilidi buku la anthu onse!

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi Chilamulo cha Mose mungachigwiritsire ntchito motani posonyeza kuti Baibulo silinachokere kwa anthu?

◻ Kodi ndi mapulinsipulo ogwira ntchito nthaŵi zonse ati a m’Baibulo amene ali ofunika pamoyo wamakono?

◻ Kodi nchifukwa ninji sizingakhale kuti ulosi wa pa Yesaya 13:19, 20 unalembedwa zinthuzo zitachitika?

◻ Kodi anthu oona mtima tiyenera kuwalimbikitsa kuchitanji, ndipo chifukwa ninji?

[Bokosi patsamba 19]

Bwanji Ponena za Zinthu Zopanda Umboni?

Baibulo lili ndi mfundo zosiyanasiyana zimene zilibe umboni woonekera. Mwachitsanzo, zimene limanena ponena za malo ena kumene kuli zolengedwa zauzimu sizingatsimikiziridwe​—kapena kukanidwa​—mwa umboni wa sayansi. Kodi mawu opanda umboni ameneŵa amapangitsadi Baibulo kutsutsana ndi sayansi?

Ndilo vuto limene wasayansi wophunzira za nthaka ya mapulaneti ena amene anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova zaka zingapo zapitazo anali nalo. “Ndikuvomereza kuti poyamba zinali zovuta kuti ndilandire Baibulo chifukwa chakuti mawu ena a m’Baibulo sindinali kuwapezera umboni wa sayansi,” akukumbukira motero. Mwamuna woona mtima ameneyu anapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo m’kupita kwa nthaŵi anakhutira kuti umboni womwe ulipo umasonyeza kuti ndilo Mawu a Mulungu. “Zimenezi zinandichepetsera njala yofuna kupeza umboni wa mfundo iliyonse ya m’Baibulo payokha,” akufotokoza motero. “Munthu wokonda za sayansi ayenera kufunitsitsa kufufuza Baibulo m’lingaliro lauzimu, koma akapanda kutero sadzalandira choonadi. Sitingayembekezere sayansi kupereka umboni wa mawu alionse a m’Baibulo. Koma chabe chifukwa chakuti mawu ena sitingawapezere umboni, sizimatanthauza kuti mawuwo si oona. Chofunika kwambiri nchakuti ngati umboni wake ulipo, kulongosoka kwa Baibulo kumaonekera.”

[Chithunzi patsamba 17]

Mose analemba malangizo osungitsa ukhondo amene anali apamwamba kwambiri kuposa nzeru za panthaŵiyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena