Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 4/15 tsamba 31
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Madalitso Aakulu Kudzera m’Pangano Latsopano
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Madyerero Osaiŵalika a m’Mbiri ya Israyeli
    Nsanja ya Olonda—1998
  • ‘Mudzakhala Ufumu wa Ansembe’
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhosa Zina ndi Pangano Latsopano
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 4/15 tsamba 31

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapeza makope a Nsanja ya Olonda aposachedwapa kukhala othandiza kwa inu? Pamenepo bwanji osaona ngati mukukumbukira mwa mafunso otsatirawa?

◻ Kodi pali kusiyana kotani pakati pa “tsiku la Ambuye” ndi “tsiku la Yehova”? (Chivumbulutso 1:10; Yoweli 2:11)

“Tsiku la Ambuye” limaphatikizapo kukwaniritsidwa kwa masomphenya 16 ofotokozedwa m’Chivumbulutso machaputala 1 mpaka 22 ndi kukwaniritsidwa kwa zochitika zazikulu zimene Yesu analosera poyankha funso la ophunzira ake lonena za chizindikiro cha kukhalapo kwake. Tsiku loopsa la Yehova lidzaulika monga chimake cha tsiku la Ambuye pamene adzapereka chiweruzo padziko loipa la Satana. (Mateyu 24:3-14; Luka 21:11)​—12/15, tsamba 11.

◻ Kodi Baibulo la Makarios lili ndi zinthu zina ziti zapadera?

Dzina lakuti Yehova limaonekera nthaŵi zoposa 3,500 m’Baibulo la Makarios. Katswiri wina wa mabuku achipembedzo achirasha anati: “Matembenuzidwe ake ngogwirizana kwambiri ndi malemba achihebri, ndipo kalembedwe kake nkoyenereradi ndipo nkogwirizana ndi nkhani yake.”​—12/15, tsamba 27.

◻ Kodi “choonadi” chimene Yesu anati chidzatimasula ndicho chiyani? (Yohane 8:32)

Pamene anati “choonadi,” Yesu anatanthauza chidziŵitso chouziridwa ndi Mulungu​—makamaka chidziŵitso chonena za chifuniro cha Mulungu​—chimene chasungidwira ife m’Baibulo.​—1/1, tsamba 3.

◻ Kodi Yehu wamakono ndi Yehonadabu wamakono ndani?

Yehu akuchitira chithunzi Yesu Kristu, woimiridwa padziko lapansi ndi “Israyeli wa Mulungu,” Akristu odzozedwa. (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 12:17) Mongadi momwe Yehonadabu anachingamirira Yehu, “khamu lalikulu” lochokera m’mitundu labwera kudzachirikiza oimira a Yesu a padziko lapansi. (Chivumbulutso 7:9, 10; 2 Mafumu 10:15)​—1/1, tsamba 13.

◻ Kodi ‘kuyenda ndi Mulungu’ kumatanthauzanji? (Genesis 5:24; 6:9)

Kumatanthauza kuti ochita zimenezi, monga Enoke ndi Nowa, anali ndi makhalidwe amene anasonyeza kuti iwo ankakhulupirira Mulungu kwambiri. Iwo anachita monga momwe Yehova anawalamulira ndipo miyoyo yawo inali yogwirizana ndi zimene anadziŵa ponena za iye malinga ndi mmene amachitira ndi mtundu wa anthu.​—1/15, tsamba 13.

◻ Kodi nchifukwa ninji munthu ayenera kukonzeratu mtsogolo podziŵa kuti atha kumwalira?

M’lingaliro lina, kukonzekera zimenezo ndiko kupatsa banja lako mphatso. Kumasonyeza chikondi. Kumapereka umboni wa chikhumbo cha ‘kudzisungira a m’banja mwako’ ngakhale pamene sulinso nawo. (1 Timoteo 5:8)​—1/15, tsamba 22.

◻ Kodi “pangano lakale” linachita ntchito yanji? (2 Akorinto 3:14)

Linachitira chithunzi pangano latsopano ndipo, mwa nsembe zake zobwerezabwereza, linasonyeza kuti munthu akufunadi kuomboledwa mwamsanga ku uchimo ndi imfa. Linali ‘namkungwi wakuwafikitsa kwa Kristu.’ (Agalatiya 3:24)​—2/1, tsamba 14.

◻ Kodi pangano latsopano lili losatha motani? (Ahebri 13:20)

Choyamba, mosiyana ndi Chilamulo, ilo silidzaloŵedwa m’malo ndi lina. Chachiŵiri, zotsatirapo za ntchito yake nzosatha. Ndipo chachitatu, nzika za Ufumu wa Mulungu za padziko lapansi zidzapitirizabe kupindula ndi makonzedwe a pangano latsopano m’Zaka Chikwi.​—2/1, tsamba 22.

◻ Kodi kukhala woyamikira kuli ndi mapindu otani?

Chikondi chimene munthu amakhala nacho chifukwa chokhala woyamikira kuchokera pansi pa mtima chimamthandizira kukhala ndi chimwemwe ndi mtendere. (Yerekezerani ndi Miyambo 15:13, 15.) Popeza kuti ndi mkhalidwe wabwino, kuyamikira kumatetezera munthu kuti asakhale ndi malingaliro oipa monga mkwiyo, nsanje, ndi kuipidwa.​—2/15, tsamba 4.

◻ Kodi ndi mapangano ati amene anthu odzozedwa ndi mzimu aloŵetsedwamo?

Pangano latsopano, limene Yehova amapanga ndi mamembala a Israyeli wauzimu, ndiponso pangano la Ufumu, limene Yesu amapanga ndi otsatira ake odzozedwa omwe akutsatira mapazi ake. (Luka 22:20, 28-30)​—2/15, tsamba 16.

◻ Kodi ndi madyerero atatu ati aakulu amene Aisrayeli analamulidwa kupezekapo?

Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa, tsiku lotsatira Paskha wa Nisani 14; Madyerero a Masabata, patapita masiku 50 kuchokera pa Nisani 16; ndi Madyerero a Kututa, kapena kuti Madyerero a Misasa, m’mwezi wachisanu ndi chiŵiri. (Deuteronomo 16:1-15)​—3/1, masamba 8, 9.

◻ Kodi nchifukwa ninji uli mwayi kufika pamisonkhano yachikristu?

Yesu anati: “Kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pawo.” (Mateyu 18:20; 28:20) Ndiponso, njira yofunika kwambiri imene kudyetsedwa kwauzimu kumachitikira ndiyo misonkhano yampingo ndi misonkhano yaikulu. (Mateyu 24:45)​—3/1, tsamba 14.

◻ Kodi dzina lakuti Nimrode linayamba motani?

Akatswiri ambiri a zamaphunziro amavomerezana kuti dzina lakuti Nimrode si dzina la paukhanda. M’malo mwake amati ndi dzina lomwe anapatsidwa panthaŵi ina pomgwirizanitsa ndi mkhalidwe wake waupandu pamene unadziŵika.​—3/15, tsamba 25.

◻ Kodi Banja nlofunika motani kwa anthu?

Banja nlofunika kwa munthu aliyense. Mbiri yakale ikusonyeza kuti pamene mabanja anyonyosoka, midzi ya anthu ndi mtundu zimafooka. Choncho banja limathandizira mwachindunji kukhazikika kwa anthu ndi ubwino wa ana ndiponso mibadwo yamtsogolo.​—4/1, tsamba 6.

◻ Kodi ndi maumboni atatu ati amene amasonyeza kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu?

(1) Nlodalirika pankhani za sayansi; (2) lili ndi mapulinsipulo ogwira ntchito nthaŵi zonse amene ali ofunika pamoyo wamakono; (3) lili ndi maulosi olunjika amene akwaniritsidwa, monga momwe mbiri yakale imachitira umboni.​—4/1, tsamba 15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena