Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 6/1 tsamba 3-4
  • Chenjerani ndi Onyoza!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chenjerani ndi Onyoza!
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zinthu Sizinasinthe?
  • Kumbukirani Tsiku la Yehova Nthaŵi Zonse
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Tetezerani Chiyembekezo Chanu Chachikristu
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • “Tsiku la Yehova Lili Pafupi”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Dikirani Moleza Mtima
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 6/1 tsamba 3-4

Chenjerani ndi Onyoza!

Lerolino nkhani zonena za mtsogolo zikufalikira, ndipo pali anthu ambiri amene akufufuza zimene zidzachitika mtsogolo. “Pamene chaka cha 2000 chikuyandikira,” inatero nyuzipepala yotchedwa The Daily Telegraph ya ku London, “chinachake chachilendo komatu osati chosayembekezereka chikuchitika. Anthu zikwi zambiri kuzungulira dziko lonse akuganizira za zinthu zachilendo kwambiri ndipo nthaŵi zambiri zoopsa zokhudza zamtsogolo.” Kwa anthu ambiri amene akhala akufufuza zochitika, chidwi chachikulu chimenechi chofuna kudziŵa zimene zidzachitika mtsogolo changokhala kubwerezanso chiyembekezo cha kusintha kwa zinthu chimene anthu anali nacho kumbuyoko chimene sichinakwaniritsidwe.

M’ZAKA za zana la 19, pamene ngolo zokokedwa ndi akavalo zinali kuchuluka, mwamuna wina ananena kuti mtsogolo mizinda ya ku Ulaya inali kudzadzaza ndi ndoŵe za akavalo. Koma zonena zakezo zinapezeka kuti zinali zonama. Choncho, ponena za kusakwaniritsidwa koŵirikiza kwa zinthu zimene amati zidzachitika mtsogolo, nyuzipepala yotchedwa The Times ya ku London inati: “Mtsogolo mmodzala ndi ndoŵe za akavalo.”

Ena amanyoza anthu amene amaneneratu za ngozi yamtsogolo. Mwachitsanzo, profesa wina wa zamalonda pa yunivesite ina ya ku United States anatsutsa anthu amene anali kuchenjeza za kuwonongeka kwa malo okhala mtsogolo ndipo iye anawapempha kuti achite maere ofuna kupeza ngati malo okhala adzapitirizadi kuwonongeka. Malinga nkunena kwa magazini ya New Scientist, iye ananena kuti “moyo wathu ukutukuka ndipo udzapitirizabe kutero mpaka muyaya.”

Ngakhale kuti ena amanena zamtsogolo ndipo ena amatsutsa, ambiri amakhulupirira kuti zinthu sizidzasintha kwenikweni. Pamene atsutsa lingaliro lililonse lonena za kuloŵererapo kwa Mulungu m’zochita za anthu, iwo amasonyeza mzimu wofanana ndi umene unali ndi onyoza a m’zaka za zana loyamba C.E.

Kodi Zinthu Sizinasinthe?

Kalata yachiŵiri youziridwa ya mtumwi wachikristu Petro, yolembedwa cha mu 64 C.E., inachenjeza kuti: “Masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni.”​—2 Petro 3:3.

Onyoza amafuna kuti zinthu zimene akunyozazo zikhale ngati zopanda pake. Munthu amene amanyoza amagwera mumsampha wa kudzikonda chifukwa chakuti wonyoza nthaŵi zambiri amafuna kuti anthu amene akumumvetserawo agwirizane ndi malingaliro ake. Mwinamwake ena mwa onyoza amene Petro anachenjeza za iwo anali otere, “oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni.” Pochenjeza oŵerenga ake, mtumwiyo ananena mogogomezera. Iye anachenjeza za kufika kwa ‘onyoza ndi kuchita zonyoza.’

Onyoza amenewo a m’zaka za zana loyamba anali kukayikira za ‘kudza [“kukhalapo,” NW] kolonjezedwa’ kwa Kristu, akumati: “Lili kuti lonjezano la kudza [“kukhalapo,” NW] kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.” (2 Petro 3:4) Iwo anaona kuti zinali motero. Komatu kalelo m’chaka cha 33 C.E., Yesu analosera za kuwonongeka kwa mzinda wa Yerusalemu. “Masiku adzakudzera,” iye anatero, “ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake.” Anthu amene ananyoza chenjezo limenelo analakwa chotani nanga! Mu 70 C.E., magulu ankhondo a Roma anazinga Yerusalemu nawononga mzindawo, ndipo okhalamo ake ambiri anaphedwa. Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri okhala mumzindamo sanakonzekere za chiwonongeko chimenechi? Nchifukwa chakuti iwo sanazindikire kuti Mulungu anawayang’anira mwa Mwana wake, Yesu.​—Luka 19:43, 44.

Mtumwi Petro akunena za kuloŵererapo kwa mtsogolo kwa Mulungu Wamphamvuyonse. “Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala,” akuchenjeza motero Petro. (2 Petro 3:10) Panthaŵiyo Mulungu adzachotsa osapembedza padziko lonse lapansi ndipo adzasiya awo amene adzaweruzidwa kuti ali olungama. Monga momwe magazini ino yakhala ikufotokozera mobwerezabwereza, “kukhalapo” kwa Kristu Yesu kunayambika mu 1914. Koma kuchitapo kanthu kwake monga Wakupha wa Mulungu pofuna kuchotsa kuipa konse kudzachitika mtsogolo. Choncho, chenjezo la mtumwiyo lonena kuti tiyenera kuchenjera ndi onyoza likugwira ntchito kwambiri lerolino.

Mwina mwakhala mukuyembekezera kwa nthaŵi yaitali za kuloŵererapo kwa Mulungu m’zochita za anthu. Kodi nchiyani chimene chidzakuthandizani kupitirizabe kudikira moleza mtima mosanyengedwa ndi onyoza? Pitirizani kuŵerenga.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Masiku adzakudzera, ndipo adani ako . . . adzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo . . . ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake.” Chenjezo limenelo silinafunikire kunyozedwa. Magulu ankhondo a Roma anawononga Yerusalemu, ndipo anthu ambiri anaphedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena