Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 7/1 tsamba 30-31
  • Msamariya Apezeka Kuti Ndiye Mnansi Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msamariya Apezeka Kuti Ndiye Mnansi Wabwino
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Msamariya Wachifundo
  • Phunziro kwa Ife
  • Kodi Kukhala “Msamariya Wachifundo” Kumatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Msamariya Waunansi
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Msamariya Wachifundo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 7/1 tsamba 30-31

Anachita Chifuniro cha Yehova

Msamariya Apezeka Kuti Ndiye Mnansi Wabwino

M’TSIKU la Yesu, panali udani waukulu pakati pa Ayuda ndi Akunja. M’kupita kwa nthaŵi, Mishnah yachiyuda inaphatikizapo ngakhale lamulo lomwe linali kuletsa akazi achiisrayeli kuti asamathandize akazi osakhala Ayuda panthaŵi yobala mwana, popeza kuti kuteroko kukanakhala kuthandizira kudzetsa munthu wina Wakunja m’dziko.​—Abodah Zarah 2:1.

Asamariya ndi Ayuda anali paubale weniweni pa zonse ziŵiri chipembedzo ndi mtundu kusiyana ndi Akunja. Komatu iwo anali kuonedwanso monga odetsedwa. “Ayuda sayenderana nawo Asamariya,” analemba motero mtumwi Yohane. (Yohane 4:9) Ndithudi, Talmud inali kuphunzitsa kuti “mkate wopatsidwa ndi Msamariya ngwodetsedwa kwambiri kuposa nyama ya nkhumba.” Ayuda ena anali kugwiritsira ntchito dzina lakuti “Msamariya” monga mawu onyoza ndi kutonza.​—Yohane 8:48.

Polingalira za zochitika zimenezi, mawu amene Yesu anauza munthu wodziŵa bwino Chilamulo chachiyuda ngophunzitsa kwambiri. Munthuyo anafikira Yesu namfunsa kuti: “Mphunzitsi, ndidzaloŵa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?” Poyankha, Yesu anasumika maganizo pa Chilamulo cha Mose, chimene chinalamula kuti “uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse,” ndiponso ‘uzikonda mnansi wako monga iwe mwini.’ Kenaka wachilamuloyo anafunsa Yesu kuti: “Mnansi wanga ndani?” (Luka 10:25-29; Levitiko 19:18; Deuteronomo 6:5) Malinga nkunena kwa Afarisi, dzina lakuti “mnansi” linali kugwiritsiridwa ntchito kwa okhawo amene anali kutsatira ziphunzitso zachiyuda​—ndipo nzachidziŵikire kuti Akunja kapena Asamariya sanali kukhudzidwa ndi dzinali. Ngati wachilamulo wofuna kudziŵa ameneyu analingalira kuti Yesu agwirizana ndi kaonedwe kameneko, imeneyi inali nthaŵi yake yozizwa.

Msamariya Wachifundo

Yesu anayankha funso la munthuyo mwa fanizo.a “Munthu wina,” iye anatero, “anatsika kuchokera ku Yerusalemu kumka ku Yeriko.” Pakati pa Yerusalemu ndi Yeriko panali mtunda wa makilomita pafupifupi 23. Msewu wapakati pa mizinda iŵiriyi unali ndi ngodya zokhota kwambiri ndiponso unali ndi miyala yamapanga, zomwe zinapangitsa kuti akuba azibisala, kulanda, ndi kuthaŵa mosavuta. Malinga ndi mmene zinakhalira, wapaulendo wa m’fanizo la Yesu “anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.”​—Luka 10:30.

“Kudangotero,” anapitiriza motero Yesu, “kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina. Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina.” (Luka 10:31, 32) Ansembe ndi Alevi anali aphunzitsi a Chilamulo​—kuphatikizapo lamulo la chikondi cha pa mnansi. (Levitiko 10:8-11; Deuteronomo 33:1, 10) Zoonadi, iwowo ndiwo anayenera kukhudzidwa kwambiri kuti athandize wapaulendo wovulazidwayo kusiyana ndi anthu ena onse.

Yesu anapitiriza kunena kuti: “Msamariya wina ali paulendo wake anadza pali iye.” Mosakayika konse, kutchulidwa kwa Msamariya kunapangitsa kuti wachilamuloyo akhale tcheru kwambiri. Kodi Yesu adzavomereza kuti mtundu umenewu uyenera kuonedwabe monga wodetsedwa? Mosiyana ndi zimenezo, ataona wapaulendo wovulazidwayo, Msamariyayo “anagwidwa chifundo.” Yesu anati: “Nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye panyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.b Ndipo mmaŵa mwake anatulutsa malupiya atheka aŵiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.”​—Luka 10:33-35.

Tsopano Yesu anafunsa wofuna kudziŵa uja kuti: “Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?” Wachilamuloyo anadziŵa yankho lake, koma anaoneka kuti sanafune kunena kuti “Msamariya.” M’malo mwake, iye anangoyankha kuti: “Iye wakumchitira chifundo.” Ndipo Yesu anati: “Pita, nuchite iwe momwemo.”​—Luka 10:36, 37.

Phunziro kwa Ife

Munthu amene anafunsa Yesuyo anatero pofuna “kudziyesa yekha wolungama.” (Luka 10:29) Mwinamwake iye analingalira kuti Yesu amtama chifukwa cha kuumirira kwake komkitsa ku Chilamulo cha Mose. Koma munthu wodzilungamitsa ameneyu anafunikira kuphunzira choonadi cha mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake; koma Yehova ayesa mitima.”​—Miyambo 21:2.

Fanizo la Yesuli likusonyeza kuti munthu wolungamadi ndiye amene samvera chabe malamulo a Mulungu koma amatsanziranso mikhalidwe yake. (Aefeso 5:1) Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza kuti “Mulungu alibe tsankhu.” (Machitidwe 10:34) Kodi timatsanzira Mulungu pazimenezi? Fanizo losonkhezera maganizo la Yesu limasonyeza kuti tiyenera kuona aliyense monga mnansi wathu mosasamala kanthu za mtundu wake, mwambo wake, kapena chipembedzo chake. Ndithudi, Akristu amalimbikitsidwa ‘kuchitira onse chokoma’​—osati anthu okha amene timafanana nawo m’zochita, kufanana nawo fuko, kapena mtundu ndiponso osati kuchitira chokoma okhulupirira anzathu okha ayi.​—Agalatiya 6:10.

Mboni za Yehova zimayesetsa kutsatira uphungu wa m’Malemba umenewu. Mwachitsanzo, kukagwa masoka, iwo amathandiza okhulupirira anzawo pamodzinso ndi anthu amene sali Mboni.c Kuwonjezera pamenepo, iwo onse amathera maola oposa 1,000,000,000 chaka chilichonse akuthandiza anthu kuti akhale ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo. Iwo amayesetsa kufikira aliyense ndi uthenga wa Ufumu, popeza kuti chifuniro cha Mulungu nchakuti “anthu a mtundu uliwonse apulumuke nafike pa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi.”​—1 Timoteo 2:4, NW; Machitidwe 10:35.

[Mawu a M’munsi]

a Panopo, fanizo ndilo nkhani yaifupi yomwe nthaŵi zambiri imakhala yopeka yophunzitsa choonadi cha makhalidwe kapena chauzimu.

b Nyumba zina za alendo za m’tsiku la Yesu mwachionekere sizinali kupereka chabe malo ogona komanso chakudya ndi zinthu zina. Mwina umenewu ndiwo umene unali mtundu wa nyumba zimene Yesu anali kulingalira, popeza kuti mawu achigiriki ogwiritsiridwa ntchito panopo ngosiyana ndi amene anatembenuzidwa kuti “nyumba ya alendo” pa Luka 2:7.

c Ngati mufuna kuona zitsanzo zina, onani Nsanja ya Olonda, ya December 1, 1996, masamba 3-8, ndi January 15, 1998, masamba 3-7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena