Kodi Muli ndi “Mtima Womvera”?
PAMENE Solomo anakhala mfumu ya Israyeli wakale, iye anadzimva kukhala wopereŵera. Choncho anapempha Mulungu kuti ampatse nzeru ndi chidziŵitso. (2 Mbiri 1:10) Solomo anapempheranso kuti: “Patsani . . . kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu.” (1 Mafumu 3:9) Chikhala kuti Solomo anali ndi “mtima womvera,” iye akanatha kutsatira malamulo ndi mapulinsipulo a Mulungu ndi kudalitsidwa ndi Yehova.
Mtima womvera si wolemetsa koma umadzetsa chimwemwe. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Ndithudi, tiyenera kumvera Mulungu. Ndipotu Yehova ndiye Mlengi wathu Wamkulu. Dziko lapansi ndi zonse zili momwemo nzake, ngakhale siliva ndi golidi yense. Choncho Mulungu sitingampatse chuma chilichonse chakuthupi, ngakhale kuti amatilola kugwiritsira ntchito chuma chathu chakuthupi kusonyeza kuti timamkonda. (1 Mbiri 29:14) Yehova amafuna kuti tizimkonda ndi kuyenda naye modzichepetsa, kuchita chifuniro chake.—Mika 6:8.
Yesu Kristu atafunsidwa za lamulo lalikulu m’Chilamulo, iye anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba.” (Mateyu 22:36-38) Njira imodzi yosonyezera chikondi chimenecho ndiyo kumvera Mulungu. Choncho aliyense wa ife ayenera kumapemphera kuti Yehova ampatse mtima womvera.
Anali ndi Mtima Womvera
Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri za anthu amene anali ndi mtima womvera. Mwachitsanzo, Yehova anauza Nowa kuti amange chingalawa chachikulu chopulumutsiramo miyoyo. Imeneyi inali ntchito yakalavula gaga imene inatenga zaka 40 kapena 50. Ngakhale patakhala ziŵiya zonse zamagetsi zamakono ndi ziŵiya zina zimene zilipo tsopano, lingakhale luso lapamwamba kupanga chinthu chachikulu ngati chimenecho chimene chingayandame. Ndiponso, Nowa anachenjeza anthu amene mosakayikira anamseka ndi kumnyodola. Koma iye anatsatira zonse zimene anauzidwa. Baibulo limati: “Momwemo anachita.” (Genesis 6:9, 22; 2 Petro 2:5) Nowa anasonyeza chikondi chake pa Yehova mwa kumvera mokhulupirika kwa zaka zambiri. Chimenechitu nchitsanzo chabwino kwambiri kwa tonsefe!
Lingaliraninso za kholo lakale Abrahamu. Mulungu anamuuza kusamuka kuchoka ku dziko lotukuka la Uri wa Akaldayo kupita ku dziko losadziŵika. Abrahamu anamvera mosakayika. (Ahebri 11:8) Kwa moyo wake wonse kuyambira pamenepo, iye ndi banja lake anakhala m’mahema. Atakhala zaka zambiri m’dziko lachilendo, Yehova anamdalitsa iye ndi mkazi wake womverayo, Sara, mwa kuwapatsa mwana wamwamuna wotchedwa Isake. Abrahamu wazaka 100 zakubadwa ayenera kuti anamkonda kwambiri mwana wakeyo wa muukalamba wake! Patapita zaka zingapo, Yehova anapempha Abrahamu kuti apereke Isake monga nsembe yopsereza. (Genesis 22:1, 2) Ziyenera kuti zinali zopweteka kwa Abrahamu kungoganizira kuchita zimenezo. Komabe, iye anamvera chifukwa chakuti anali kukonda Yehova ndipo anali ndi chikhulupiriro chakuti mbewu yolonjezedwa idzadzera mwa Isake, ngakhale Mulungu atachita kumuukitsa kwa akufa. (Ahebri 11:17-19) Koma Abrahamu atatsala nenene kuti aphe mwana wake, Yehova anamletsa nati: “Tsopano ndidziŵa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.” (Genesis 22:12) Chifukwa cha kumvera kwake, Abrahamu woopa Mulunguyo anadzadziŵika kuti “bwenzi la Mulungu.”—Yakobo 2:23.
Yesu Kristu ndiye chitsanzo chathu chabwino koposa cha kumvera. Asanakhale munthu, iye anasangalala ndi kutumikira Atate wake momvera kumwamba. (Miyambo 8:22-31) Atakhala munthu, Yesu anamvera Yehova pa zilizonse, ndipo anakondwera kuchita chifuniro chake nthaŵi zonse. (Salmo 40:8; Ahebri 10:9) Chotero, Yesu ananenadi zoona kuti: “Sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi. Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiya Ine pandekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthaŵi zonse.” (Yohane 8:28, 29) Pomalizira pake, kuti akweze uchifumu wa Yehova ndi kupulumutsa anthu omvera, Yesu anapereka moyo wake mofunitsitsa, kufa imfa yodzetsa chitonzo kwambiri ndiponso yopweteka koopsa. Ndithudi, “popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.” (Afilipi 2:8) Chimenechitu nchitsanzo chabwino kwambiri cha kusonyeza mtima womvera!
Kumvera Kosakwanira Nkosayenera
Si onse amene anena kuti amamvera Mulungu amene akhaladi omvera kwa iye. Lingalirani za Mfumu Sauli wa Israyeli wakale. Mulungu anamlangiza kuti awononge Aamaleki onse oipawo. (1 Samueli 15:1-3) Ngakhale kuti Sauli anawawononga monga mtundu, iye anasiya mfumu yawo ndi kusiyanso nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo zina. Samueli anafunsa kuti: “Chifukwa ninji . . . simunamvera mawu a . . . Yehova?” Poyankha Sauli anati: “Koma ndinamvera mawu a Yehova . . . Anthuwo [a Israyeli] anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng’ombe, zoposa za zija . . . , kuziphera nsembe kwa Yehova.” Pogogomezera kufunika kwa kumvera kotheratu, Samueli anayankha nati: “Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mawu a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo. Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mawu a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.” (1 Samueli 15:17-23) Sauli anataya zinthu zofunika kwambiri chifukwa chakuti analibe mtima womvera!
Ngakhale Mfumu Solomo yanzeruyo, amene anapempherera mtima womvera, sanapitirize kumvera Yehova. Mosemphana ndi chifuniro cha Mulungu, iye anakwatira akazi achilendo amene anampangitsa kuchimwira Mulungu. (Nehemiya 13:23, 26) Solomo anataya chiyanjo cha Mulungu chifukwa chakuti sanapitirize kukhala ndi mtima womvera. Ndi chenjezotu kwa ife limenelo!
Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake aumunthu azichita zinthu mwangwiro. Iye “akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Tonsefe tikudziŵa kuti tidzalakwitsabe nthaŵi zina, koma Mulungu amatha kuona ngati pansi pa mtima tikukhumbadi kumkondweretsa. (2 Mbiri 16:9) Ngati tilakwitsa chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu koma tilapa, tingapemphe chikhululukiro pamaziko a nsembe ya dipo ya Kristu, ndi chidaliro chakuti Yehova “adzakhululukira koposa.” (Yesaya 55:7; 1 Yohane 2:1, 2) Thandizo la akulu achikondi achikristu lingafunikirenso kuti tichire mwauzimu ndi kukhala ndi chikhulupiriro chabwino ndi mtima womvera.—Tito 2:2; Yakobo 5:13-15.
Kodi Kumvera Kwanu Nkokwanira Motani?
Monga atumiki a Yehova, ambiri a ife mosakayikira timadzimva kuti tili ndi mtima womvera. Tingaganize kuti, Kodi sindichita nawo ntchito yolalikira Ufumu? Kodi sindichirimika pamene nkhani zazikulu monga za uchete zibuka? Ndipo kodi sindipezeka pamisonkhano yachikristu mokhazikika, monga momwe mtumwi Paulo anatilimbikitsira? (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Yohane 17:16; Ahebri 10:24, 25) Zoonadi, anthu onse a Yehova amasonyeza kumvera kochokera pansi pa mtima pankhani zazikulu zimenezi.
Koma nanga bwanji za khalidwe lathu pazochitika zamasiku onse, mwinamwake pankhani zooneka ngati zazing’ono? Yesu anati: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’onong’ono alinso wosalungama m’chachikulu.” (Luka 16:10) Choncho aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, Kodi ndili ndi mtima womvera pa zinthu zazing’ono kapena pankhani zimene ena sazidziŵa nkomwe?
Wamasalmo anasonyeza kuti ngakhale m’nyumba mwake mmene ena sanamuone ‘anayenda ndi mtima wangwiro.’ (Salmo 101:2, NW) Mutakhala m’nyumba mwanu, mungayatse wailesi yakanema ndi kuyamba kupenyerera filimu. Pamenepo, kumvera kwanu kungayesedwe. Filimuyo ingayambe kusonyeza khalidwe loipa. Kodi mudzapitirizabe kuipenyerera, mukumadzikhululukira kuti ndiwo mtundu wa mafilimu amene amasonyezedwa masiku ano? Kapena kodi mtima wanu womvera udzakupangitsani kutsatira malangizo a m’Malemba akuti, ‘musalole dama ndi chidetso kutchulidwa ndi kutchulidwa komwe mwa inu’? (Aefeso 5:3-5) Kodi mudzaizima TV, ngakhale kuti nkhani yake njochitisa chidwi? Kapena kodi mudzasintha matchanelo ngati programu yayamba kusonyeza chiwawa? “Yehova ayesa wolungama mtima,” anaimba motero wamasalmo, “koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.”—Salmo 11:5.
Mtima Womvera Umadzetsa Madalitso
Ndithudi, pali mbali zambiri pamoyo wathu pazimene tingadzipende mopindulitsa kuti tione ngati timamveradi Mulungu kuchokera mumtima. Chikondi chathu pa Yehova chiyenera kutisonkhezera kumkondweretsa ndi kuchita zimene akutiuza m’Mawu ake, Baibulo. Mtima womvera udzatithandiza kukhalabe paunansi wabwino ndi Yehova. Ndithudi, ngati timamvera mokwanira, ‘mawu a m’kamwa mwathu ndi maganizo a m’mtima wathu adzakhala ovomerezeka pamaso pa Yehova.’—Salmo 19:14.
Chifukwa chakuti Yehova amatikonda, iye amatiphunzitsa kumvera kuti tipindule. Ndipo timapindula kwambiri mwa kumvetsera ziphunzitso za Mulungu ndi mtima wonse. (Yesaya 48:17, 18) Choncho, tiyeni tilandire mwachimwemwe thandizo limene Atate wathu wakumwamba amapereka kudzera mwa Mawu ake, mzimu wake, ndi gulu lake. Tikuphunzitsidwa bwino kwambiri moti zikukhala monga kuti tikumva liwu kumbuyo kwathu limene likuti: “Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo.” (Yesaya 30:21) Pamene Yehova akutiphunzitsa kudzera m’Baibulo, zofalitsa zachikristu, ndi misonkhano yampingo, tiyeni tizimvetsera, kutsatira zimene tikuphunzira, ndi kukhala “omvera m’zonse.”—2 Akorinto 2:9.
Mtima womvera udzatipatsa chimwemwe chachikulu ndi madalitso ambiri. Udzatipatsa mtendere wamaganizo, popeza tidzadziŵa kuti tikukondweretsa Yehova Mulungu ndipo tikukondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Mtima womvera udzatitetezera pamene tiyesedwa kuti tichite choipa. Ndithudi, tiyeneradi kumvera Atate wathu wakumwamba ndipo tiyenera kupemphera kuti: “Patsani . . . kapolo wanu mtima womvera.”
[Mawu a Chithunzi patsamba 29]
Chotengedwa m’Baibulo la Self-Pronouncing Edition of the Holy Bible, lokhala ndi Baibulo la King James ndi la Revised