Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 8/1 tsamba 7-12
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chilungamo cha Yehova Nchotonthoza
  • Kufotokoza Bwino Tanthauzo la Chilungamo
  • Chilungamo cha Mulungu Chitsutsana ndi Chilungamo Chopotoka
  • Chilungamo Chimasonyezedwa kwa Aliyense
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yehova Wokonda Chilungamo ndi Chiweruzo
    Nsanja ya Olonda—1996
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
  • Yesu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 8/1 tsamba 7-12

Yehova​—Gwero la Chilungamo Chenicheni

“Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo [“nzolungama,” NW]; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo.”​—DEUTERONOMO 32:4.

1. Kodi nchifukwa chiyani mwachibadwa timafuna chilungamo?

MONGA momwe aliyense mwachibadwa amafunira kukondedwa, tonsefe timafuna kutichitira mwachilungamo. Monga momwe wandale wa ku Amereka Thomas Jefferson analembera, “[chilungamo] nchachibadwa, . . . monga momwe malingaliro, kuyang’ana, ndi kumva zakhalira.” Zimenezi nzosadabwitsa chifukwa chakuti Yehova anatilenga m’chifanizo chake. (Genesis 1:26) Ndithudi, iye anatipatsa mikhalidwe imene imasonyeza umunthu wake, ndipo umodzi mwa mikhalidweyo ndiwo chilungamo. Ndiye chifukwa chake mwachibadwa timafuna chilungamo ndiponso nchifukwa chake tikufunitsitsa kukhala m’dziko lachilungamo chenicheni.

2. Kodi chilungamo nchofunika motani kwa Yehova, ndipo nchifukwa chiyani tiyenera kumvetsa tanthauzo la chilungamo cha Mulungu?

2 Ponena za Yehova, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Njira zake zonse nzolungama.” (Deuteronomo 32:4, NW) Koma m’dziko lokanthidwa ndi chisalungamo, nkovuta kudziŵa bwino tanthauzo la chilungamo cha Mulungu. Komabe, mwa kufufuza m’masamba a Mawu a Mulungu, tingaone mmene Mulungu amachitira chilungamo, ndipo tingaonenso ngakhale njira zina zosangalatsa kwambiri za Mulungu. (Aroma 11:33) Kumvetsa lingaliro la m’Baibulo la chilungamo nkofunika chifukwa chakuti kaonedwe kathu ka chilungamo kangakhudzidwe ndi malingaliro a anthu. Malinga nkaonedwe ka anthu, chilungamo amangochiona ngati kutsatira lamulo mopanda tsankhu. Kapena monga momwe wafilosofi Francis Bacon analembera, “chilungamo ndicho kupatsa munthu aliyense chinthu chomuyenerera.” Komabe, chilungamo cha Yehova chimaloŵetsapo zina zambiri.

Chilungamo cha Yehova Nchotonthoza

3. Kodi tingaphunzireponji mwa kusanthula mawu a m’chinenero choyambirira ogwiritsiridwa ntchito m’Baibulo otanthauza chilungamo?

3 Ukulu wa chilungamo cha Mulungu tingaudziŵe bwino mwa kusanthula mmene mawu a m’chinenero choyambirira anagwiritsidwira ntchito m’Baibulo.a Chochititsa chidwi nchakuti m’Malemba mulibe kusiyana kwenikweni pakati pa mawu achingelezi akuti justice ndi righteousness otembenuzidwa kuti chilungamo m’Chicheŵa. Kwenikweni, mawu ake achihebri nthaŵi zina anagwiritsiridwa ntchito m’lingaliro lofanana, monga momwe timaonera pa Amosi 5:24, pamene Yehova akulangiza anthu ake kuti: “Chiweruzo [“Chilungamo,” NW (justice)] chiyende ngati madzi, ndi chilungamo (righteousness) ngati mtsinje wosefuka.” Komanso, nthaŵi zambiri mawu achingeleziwo “justice ndi righteousness” amaonekera pamodzi m’Baibulo lachingelezi pofuna kugogomezera mfundo.​—Salmo 33:5, NW; Yesaya 33:5, NW; Yeremiya 33:15, NW; Ezekieli 18:21, NW; 45:9, NW.

4. Kodi kuchita chilungamo kumatanthauzanji, ndipo chitsanzo choposa cha chilungamo nchiyani?

4 Kodi mawu achihebri ndi achigiriki ameneŵa akupereka lingaliro lotani? Kuchita chilungamo m’lingaliro la m’Malemba kumatanthauza kuchita cholondola ndiponso choyenerera. Popeza kuti Yehova ndiye amene amakhazikitsa malamulo a makhalidwe abwino ndi mapulinsipulo, kapena kuti chimene chili cholondola ndiponso choyenerera, mmene Yehova amachitira zinthu ndicho chitsanzo chabwino koposa cha chilungamo. Buku lakuti Theological Wordbook of the Old Testament limafotokoza kuti liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti chilungamo (tseʹdheq) “limanena za lamulo la khalidwe labwino ndipo lamulo limenelo mu Chipangano Chakale ndilo mkhalidwe ndi chifuniro cha Mulungu.” Choncho mmene Mulungu amagwiritsirira ntchito mapulinsipulo ake, ndipo makamaka mmene amachitira ndi anthu opanda ungwiro, zimasonyeza kufunikadi kwa chilungamo chenicheni.

5. Kodi chilungamo cha Mulungu nchogwirizana ndi mikhalidwe iti?

5 Malemba amasonyeza bwino lomwe kuti chilungamo cha Mulungu nchotonthoza osati chaukali kapena chopanda chifundo. Davide anaimba kuti: “Yehova akonda chiweruzo [“chilungamo,” NW], ndipo sataya okondedwa.” (Salmo 37:28) Chilungamo cha Mulungu chimamsonkhezera kusonyeza kukhulupirika ndi chifundo kwa atumiki ake. Chilungamo cha Mulungu chimadziŵa zosoŵa zathu ndipo chimalolera zophophonya zathu. (Salmo 103:14) Zimenezo sizikutanthauza kuti Mulungu amalekerera zoipa, popeza kuchita motero kungasonkhezere chisalungamo. (1 Samueli 3:12, 13; Mlaliki 8:11) Yehova anafotokozera Mose kuti Iye ali “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza [“wosakwiya msanga,” NW], ndi waukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” Pamene kuli kwakuti ngwofunitsitsa kukhululukira zolakwa, Mulungu adzalangabe oyenerera kulangidwa.​—Eksodo 34:6, 7.

6. Kodi Yehova amachita nawo motani ana ake a padziko lapansi?

6 Tikamalingalira za mmene Yehova amachitira chilungamo, sitiyenera kumuona monga woweruza wouma mtima, amene amangosamala za kulanga olakwa. M’malo mwake, tiyenera kumuona monga atate wachikondi koma wosalekerera zolakwa amene nthaŵi zonse amakhala bwino koposa ndi ana ake. “Yehova, Inu ndinu Atate wathu,” anatero mneneri Yesaya. (Yesaya 64:8) Monga Atate wolungama, Yehova ngwolinganizika poumirira cholondola ndi kusonyeza chifundo kwa ana ake a padziko lapansi, amene amafuna thandizo kapena chikhululukiro chifukwa cha mikhalidwe yovuta kapena zofooka zakuthupi.​—Salmo 103:6, 10, 13.

Kufotokoza Bwino Tanthauzo la Chilungamo

7. (a) Kodi tikuphunziranji ponena za chilungamo cha Mulungu mu ulosi wa Yesaya? (b) Kodi Yesu anachita mbali yotani pophunzitsa amitundu chilungamo?

7 Mkhalidwe wachifundo wa chilungamo cha Yehova unaonekera kwambiri Mesiya atadza. Yesu anaphunzitsa chilungamo cha Mulungu ndipo anachitsatira, monga momwe mneneri Yesaya analoserera. Ndithudi, chilungamo cha Mulungu chimaphatikizapo kuchita mwachifundo ndi anthu otsenderezedwa kuti asathyokeretu. Yesu, “mtumiki” wa Yehova, anabwera padziko lapansi ‘kudzafotokoza bwino kwa amitundu’ za mkhalidwe umenewu wa chilungamo cha Mulungu. Iye anachita zimenezi, makamaka mwa kutipatsa chitsanzo chenicheni cha zimene chilungamo cha Mulungu chili. Monga “mphukira ya chilungamo” ya Mfumu Davide, Yesu anali wofunitsitsa ‘kufunafuna chilungamo ndi kuchichita mofulumira.’​—Yesaya 16:5, NW; 42:1-4; Mateyu 12:18-21; Yeremiya 33:14, 15.

8. Kodi nchifukwa ninji kunalibe chilungamo chenicheni m’zaka za zana loyamba?

8 Kufotokoza bwino mkhalidwe wa chilungamo cha Yehova kumeneku kunali kofunika kwambiri makamaka m’zaka za zana loyamba C.E. Akulu a m’Chiyuda ndi atsogoleri achipembedzo​—alembi, Afarisi, ndi ena​—anali kulalikira ndi kupereka chitsanzo cha lingaliro lopotoka la chilungamo. Ndiye chifukwa chake anthu wamba, amene analephereratu kutsatira zofunika zoikidwa ndi alembi ndi Afarisi, ayenera kuti ankaganiza kuti nkosatheka kufika pachilungamo cha Mulungu. (Mateyu 23:4; Luka 11:46) Yesu anasonyeza kuti si mmene zinthu zilili. Iye anasankha ophunzira ake pakati pa anthu wamba ameneŵa, ndipo anawaphunzitsa chilungamo cha Mulungu.​—Mateyu 9:36; 11:28-30.

9, 10. (a) Kodi alembi ndi Afarisi ankayesa kusonyeza motani chilungamo chawo? (b) Kodi ndi motani ndipo nchifukwa ninji Yesu anasonyeza kuti zochita za alembi ndi Afarisi zinali zachabe?

9 Komabe, Afarisi anali kufunafuna mpata wosonyezera ‘chilungamo’ chawo mwa kupemphera kapena kupanga zopereka poyera. (Mateyu 6:1-6) Anayesanso kusonyeza chilungamo chawo mwa kutsatira malamulo ndi malangizo osaŵerengeka​—ambiri odzipangira okha. Zoyesayesa zimenezi zinawapangitsa ‘kupitirira chilungamo ndi chikondi cha Mulungu.’ (Luka 11:42, NW) Mwina kunja anaoneka olungama, koma mkati anali ‘odzala ndi kusayeruzika,’ kapena kuti chisalungamo. (Mateyu 23:28) Kunena mwachidule, sanali kudziŵa kalikonse ponena za chilungamo cha Mulungu.

10 Pachifukwa chimenecho, Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:20) Kusiyana kwakukulu pakati pa chilungamo cha Mulungu chosonyezedwa ndi Yesu ndi kudzilungamitsa kopanda nzeru kwa alembi ndi Afarisi nkumene kunapangitsa kuti azikangana nthaŵi zambiri.

Chilungamo cha Mulungu Chitsutsana ndi Chilungamo Chopotoka

11. (a) Kodi nchifukwa ninji Afarisi anafunsa Yesu za kuchiritsa pa Sabata? (b) Kodi yankho la Yesu linavumbulanji?

11 Pamene anali kuchita utumiki ku Galileya m’ngululu ya m’chaka cha 31 C.E., Yesu anaona mwamuna wina wadzanja lopuwala m’sunagoge. Popeza kuti panali pa Sabata, Afarisi anafunsa Yesu kuti: “Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata?” M’malo modera nkhaŵa za mavuto a mwamuna wovutikayu, cholinga chawo chinali kupeza chifukwa choimbira mlandu Yesuyo, monga momwe funso lawo linasonyezera. Ndiye chifukwa chake Yesu anachita chisoni ndi kuuma kwa mitima yawo! Kenako iye anafunsanso Afarisiwo mosapita m’mbali funso lofanana kuti: “Kodi nkuloledwa dzuŵa la Sabata kuchita zabwino?” Popeza kuti iwo sanayankhe, Yesu anadziyankhira funso lake mwa kuwafunsa ngati sangapulumutse nkhosa imene yagwera m’dzenje pa Sabata.b “Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani!” Yesu anatero, atafotokoza mfundo zosatsutsika. “Chifukwa cha ichi nkuloleka [kapena kuti, nkolondola] kuchita zabwino tsiku la Sabata,” iye anatero. Chilungamo cha Mulungu sichiyenera kutsekerezedwa ndi miyambo ya anthu. Atafotokoza bwino mfundo imeneyo, Yesu anachiritsa dzanja la mwamunayo.​—Mateyu 12:9-13; Marko 3:1-5.

12, 13. (a) Mosiyana ndi alembi ndi Afarisi, kodi Yesu anasonyeza motani kuti akufuna kuthandiza ochimwa? (b) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa chilungamo cha Mulungu ndi kudzilungamitsa?

12 Ngati Afarisi sanali kusamala kwenikweni za anthu ovutika mwakuthupi, iwo sanali kusamala mpang’ono pomwe za anthu osauka mwauzimu. Chifukwa cha lingaliro lawo lopotoka la chilungamo, iwo anali kunyalanyaza ndi kunyansidwa ndi amisonkho ndi ochimwa. (Yohane 7:49) Komabe, ambiri otere analabadira kuphunzitsa kwa Yesu, mosakayikira atazindikira chikhumbo chake chowathandiza m’malo mowaweruza. (Mateyu 21:31; Luka 15:1) Koma Afarisi ananyozerabe zoyesayesa za Yesu za kuchiritsa odwala mwauzimu. Iwo anang’ung’udza monyozera kuti: “Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nawo.” (Luka 15:2) Poyankha chidzudzulo chawo, Yesu anagwiritsiranso ntchito fanizo la mbusa. Monga momwe mbusa amasangalalira atapeza nkhosa yotayika, angelonso kumwamba amasangalala wochimwa atalapa. (Luka 15:3-7) Yesu iyemwini anasangalala pamene anathandiza Zakeyu kuti alape nasiye njira yake yakale yauchimo. “Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho,” iye anatero.​—Luka 19:8-10.

13 Mikangano imeneyi ikusonyeza bwino lomwe kuti chilungamo cha Mulungu, chimene chimafuna kuchiritsa ndi kupulumutsa, nchosiyana ndi kudzilungamitsa, kumene kumafuna kukweza anthu ochepa ndi kutsutsa anthu ambiri. Miyambo yopanda pake ndiponso yopangidwa ndi anthu inachititsa alembi ndi Afarisi kukhala odzigangira ndiponso odzikuza, koma Yesu anafotokoza mosabisa kanthu kuti iwo ‘anasiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro.’ (Mateyu 23:23) Tiyeni titsanzire Yesu posonyeza chilungamo chenicheni pazonse zimene tikuchita ndiponso tichenjere ndi msampha wa kudzilungamitsa.

14. Kodi chimodzi mwa zozizwitsa za Yesu chinasonyeza motani kuti chilungamo cha Mulungu chimakhudzidwa ndi mikhalidwe ya munthu?

14 Pamene kuli kwakuti Yesu ananyalanyaza malamulo odzipangira a Afarisi, iye anasunga Chilamulo cha Mose. (Mateyu 5:17, 18) Pochita zimenezi, iye sanalole mawu a Chilamulo cholungama chimenecho kutsekereza mapulinsipulo a Chilamulocho. Pamene mkazi amene anadwala nthenda yakukha mwazi kwa zaka 12 anagwira zovala zake nachiritsidwa, Yesu anamuuza kuti: “Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.” (Luka 8:43-48) Mawu achifundo a Yesu anapereka chitsimikizo chakuti chilungamo cha Mulungu chinakhudzidwa ndi mkhalidwe wa mkaziyo. Ngakhale kuti mwamwambo anali wodetsedwa ndipo pochita zimenezo anaswa mawu a m’Chilamulo cha Mose mwa kukhala m’khamu la anthu, chikhulupiriro chake chinayenerera kufupidwa.​—Levitiko 15:25-27; yerekezerani ndi Aroma 9:30-33.

Chilungamo Chimasonyezedwa kwa Aliyense

15, 16. (a) Kodi fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo limatiphunzitsanji ponena za chilungamo? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kukhala ‘olungama mopambanitsa’?

15 Kuwonjezera pa kugogomezera za chifundo cha chilungamo cha Mulungu, Yesu anaphunzitsanso ophunzira ake kuti icho chiyenera kukhudza anthu onse. Chifuniro cha Yehova chinali chakuti Yesuyo ‘adzetsere amitundu chilungamo.’ (Yesaya 42:1, NW) Imeneyi ndiyo inali mfundo yaikulu m’limodzi la mafanizo otchuka a Yesu, fanizo la Msamariya wachifundo. Fanizo limenelo linali yankho la funso lofunsidwa ndi mwamuna wina wachilamulo amene anafuna “kudziyesa yekha wolungama.” “Ndipo mnansi wanga ndani?” anafunsa motero mwamunayo, mosakayikira pofuna kusonyeza kuti Ayuda okha ndiwo anansi ake amene angawasonyeze chikondi. Msamariya wa m’fanizo la Yesu anasonyeza chilungamo cha Mulungu, popeza kuti iye anali wofunitsitsa kuthera nthaŵi yake ndi ndalama zake kuti athandize munthu wachilendo wa mtundu wina. Yesu anamaliza fanizo lake mwa kulangiza wofunsayo kuti: ‘Uzichita iwe momwemo.’ (Luka 10:25-37) Ifenso ngati tichitira anthu onse zabwino mosasamala kanthu za fuko lawo kapena mtundu wawo, tidzakhala tikuchita chilungamo cha Mulungu.​—Machitidwe 10:34, 35.

16 Koma chitsanzo cha alembi ndi Afarisi chikutikumbutsa kuti ngati tikufuna kuchita chilungamo cha Mulungu, sitiyenera kukhala ‘olungama mopambanitsa.’ (Mlaliki 7:16) Kuyesa kukondweretsa ena mwa kudzionetsera kuti ndife olungama kapena kuumirira malamulo a anthu momkitsa sikudzatidzetsera chiyanjo cha Mulungu.​—Mateyu 6:1.

17. Kodi nchifukwa chiyani kusonyeza chilungamo cha Mulungu kuli kofunika kwambiri kwa ife?

17 Chifukwa china chimene Yesu anafotokozerera bwino mkhalidwe wa chilungamo cha Mulungu kwa amitundu chinali chakuti ophunzira ake onse aphunzire kusonyeza mkhalidwe umenewu. Kodi nchifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika kwambiri? Malemba amatilangiza kuti ‘tikhale akutsanza a Mulungu,’ ndipo njira zonse za Mulungu nzolungama. (Aefeso 5:1) Momwemonso, Mika 6:8 akufotokoza kuti chimodzi mwa zinthu zimene Yehova amafuna ndicho kuti ‘tichite cholungama’ pamene tikuyenda ndi Mulungu wathu. Ndiponso, Zefaniya 2:2, 3 akutikumbutsa kuti ngati tikufuna kubisika patsiku la mkwiyo wa Yehova, tiyenera ‘kufuna chilungamo’ tsikulo lisanafike.

18. Kodi ndi mafunso ati amene adzayankhidwa m’nkhani yotsatira?

18 Choncho, masiku ovuta otsirizawa ndiyo “nyengo yabwino yolandiridwa” yoti tichite chilungamo. (2 Akorinto 6:2) Tingakhale otsimikizira kuti ngati tipanga “chilungamo” kukhala ‘chovala chathu’ ndi “mwinjiro” wathu monga Yobu, Yehova adzatidalitsa. (Yobu 29:14) Kodi kukhulupirira chilungamo cha Mulungu kudzatithandiza motani kukhala ndi chidaliro poyembekezera zamtsogolo? Ndiponso, pamene tikuyembekezera “dziko latsopano” lolungama, kodi chilungamo cha Mulungu chikutitetezera motani mwauzimu? (2 Petro 3:13) Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

a M’Malemba Achihebri, pali mawu atatu aakulu amene akuloŵetsedwamo. Limodzi mwa mawuwo (mish·patʹ) kaŵirikaŵiri latembenuzidwa kukhala “justice” m’Chingelezi. Aŵiri enawo (tseʹdheq ndi lina lofanana nalo tsedha·qahʹ) nthaŵi zambiri atembenuzidwa kuti “righteousness.” Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “righteousness” [“chilungamo”] (di·kai·o·syʹne) amasuliridwa kukhala “mkhalidwe wa chinthu choyenera kapena cholungama.”

b Chitsanzo cha Yesu chinali choyenerera chifukwa chakuti chilamulo chapakamwa cha Ayuda chinkawavomereza kuthandiza nyama yomwe yaloŵa m’vuto pa Sabata. Nthaŵi zinanso zingapo, panali mikangano pankhani imodzimodziyi, yakuti kaya kunali kololeka kuchiritsa pa Sabata.​—Luka 13:10-17; 14:1-6; Yohane 9:13-16.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi chilungamo cha Mulungu chimatanthauzanji?

◻ Kodi ndi motani mmene Yesu anaphunzitsira amitundu chilungamo?

◻ Kodi nchifukwa ninji chilungamo cha Afarisi chinali chopotoka?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita chilungamo?

[Chithunzi patsamba 8]

Yesu anafotokoza bwino ukulu wa chilungamo cha Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena