Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 9/1 tsamba 19-21
  • Tsimikizani Kuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsimikizani Kuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba!
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chimene Tiyenera Kuyambira Kuchita?
  • Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba
  • Mmene Ena Lerolino Amaikira Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba
  • Konzekeranitu!
  • Kodi Nthaŵi Yochita Homuweki Ndingaipeze Kuti?
    Galamukani!—2004
  • Ndingatani Kuti Ndimalize Homuweki Yanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kupezeka Pamisonkhano Nthaŵi Zonse Kukhale Patsogolo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 9/1 tsamba 19-21

Tsimikizani Kuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba!

Usiku walero mumasonkhana, koma pali ntchito yoti mugwire. Kodi mudzayambira kuchita chiyani?

NDINU mwamuna wokwatira ndiponso ndinu tate. Pamene tsiku lalitali ndi lotopetsa likutha, mukulingalira zokapezeka pamsonkhano wampingo womwe umachitika madzulowo. Ngati muŵeruka mosataya nthaŵi, mudzakhala ndi nthaŵi yokwanira yosamba, kusintha zovala zanu, ndiponso kudya chakudya msanga musanapite kumsonkhanoko. Mwadzidzidzi, bwana wanu akukupezani ndipo akukupemphani kuti mugwire ntchito maola ena owonjezereka. Akukulonjezani kuti adzakupatsani malipiro ochuluka. Ndalamazo mukuzifunadi.

Kapena ndinu mkazi wokwatiwa ndiponso mayi. Pamene mukuphika chakudya chamadzulo, mukuona mulu wa zovala zofunika kusita, ndipo zina mwa zimenezi zikufunika maŵa. Mukudzifunsa kuti, ‘Ngati ndipita kumsonkhano madzulo ano, kodi ndidzapeza nthaŵi yositira zovalazi?’ Popeza kuti munapeza ntchito yokhazikika posachedwapa, mukuzindikira kuti nkovuta kusamalira ntchito zapanyumba kwinaku mukugwira ntchito yolembedwa.

Kapenanso ndinu mwana wasukulu. M’chipinda mwanu, pathebulo pali homuweki yambiri yoti muchite. Yambiri mwa homuweki imeneyi munapatsidwa masiku apitawo, koma mwazengereza kuichita, ndipo tsopano homuwekiyo yawonjezereka. Mukulingalira zopempha makolo anu kuti akuloleni kukhala kumisonkhano kuti muchite homuwekiyo.

Kodi nchiti chimene inuyo mudzayambira kuchita: kugwira ntchito yolembedwa maola owonjezerekayo, kusita, homuweki, kapena misonkhano yampingo? Kunena mwauzimu, kodi kumatanthauzanji kuika zinthu zofunika pamalo oyamba? Kodi Yehova amaiona motani nkhaniyi?

Kodi Nchiyani Chimene Tiyenera Kuyambira Kuchita?

Aisrayeli atangolandira Malamulo Khumi, mwamuna wina anapezeka akutola nkhuni pa Sabata. Zimenezi zinali zoletsedwa kotheratu m’Chilamulo. (Numeri 15:32-34; Deuteronomo 5:12-15) Kodi mukanamuweruza motani munthuyo? Kodi mukanamchitira chifundo, mukumanena kuti iye sanali kugwira ntchito kuti atukule moyo wake koma anali kupeza zosoŵa za m’banja lake? Kodi mukananena kuti pali nthaŵi zambiri pachaka pamene angathe kusunga Sabata ndi kuti munthu angakhululukidwe mosavuta ngati walephera kuchita mwambowo mwinamwake chifukwa chakuti sanakonzekere bwino?

Yehova sanaione mopepuka nkhaniyi. Baibulo limati: “Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu.” (Numeri 15:35) Kodi nchifukwa ninji Yehova anaipidwa kwambiri ndi zimene munthuyo anachita?

Anthuwo anali ndi masiku asanu ndi limodzi otola nkhuni ndiponso kupeza chakudya, zovala, ndi pogona. Tsiku lachisanu ndi chiŵiri anafunikira kulipatula kaamba ka zosoŵa zawo zauzimu. Ngakhale kuti kutola nkhuniko sikunali kulakwa, kugwiritsira ntchito nthaŵi imene anafunikira kuipatula kuti azilambira Yehova ndiko kunali kulakwa. Ngakhale kuti Akristu sagwiritsira ntchito Chilamulo cha Mose, kodi chochitika chimenechi sichikutiphunzitsa kuti tifunikira kumaika zinthu zofunika pamalo oyamba?​—Afilipi 1:10.

Atakhala m’chipululu kwazaka 40, Aisrayeli anakonzekera kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Ena anatopa ndi kudya mana opatsidwa ndi Mulungu m’chipululumo ndipo mosakayika anali kuyembekezera kudya chakudya chamtundu wina. Powathandiza kulingalira bwino poloŵa m’dziko “moyenda mkaka ndi uchi,” Yehova anawakumbutsa kuti: “Munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka mkamwa mwa Yehova.”​—Eksodo 3:8; Deuteronomo 8:3.

Aisrayeliwo anafunikira kugwira ntchito mwakhama kuti apeze “mkaka ndi uchi” umenewo. Anafunikira kugonjetsa magulu ankhondo, kumanga nyumba, ndi kulima minda. Ngakhale zinali choncho, Yehova analamulira anthuwo kuti azipatula nthaŵi yosinkhasinkha pazinthu zauzimu tsiku lililonse. Anafunikiranso kukhala ndi nthaŵi yophunzitsa ana awo njira za Mulungu. Yehova anati: “Ndipo muziwaphunzitsa [malamulo anga] ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m’nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.”​—Deuteronomo 11:19.

Mwamuna aliyense wachiisrayeli ndiponso mwamuna aliyense wotembenukira kuchiyuda m’dzikomo analamulidwa kukaonekera pamaso pa Yehova katatu pachaka. Pozindikira kuti banja lonse linafunikira kupindula mwauzimu panthaŵi zimenezi, mitu yambiri ya mabanja inali kutsagana ndi akazi ndi ana awo. Koma kodi ndani amene anali kutetezera nyumba ndi minda yawo kwa adani pamene mabanjawo anachokapo? Yehova anawalonjeza kuti: “Palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.” (Eksodo 34:24) Aisrayeliwo anafunikira kukhala ndi chikhulupiriro kuti azindikire kuti ngati aika zinthu zauzimu pamalo oyamba, iwo sadzataya zinthu zawo zakuthupi. Kodi Yehova anakwaniritsa mawu ake? Inde anawakwaniritsadi!

Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba

Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti aziyambira kuchita zinthu zauzimu. Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, iye analangiza omvetsera ake kuti: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani? . . . Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo [zinthu zofunika] zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:31, 33) Yesu atangofa, Akristu obatizidwa chatsopano anatsatira uphungu umenewu. Ambiri a iwo anali Ayuda kapena otembenukira kuchiyuda amene anapita ku Yerusalemu kukachita phwando la Pentekoste wa 33 C.E. Akali komweko, kunachitika chinachake chosayembekezereka. Anamva ndi kulandira uthenga wabwino wonena za Yesu Kristu. Iwo anakhalabe ku Yerusalemu popeza kuti anafunitsitsa kudziŵa zambiri ponena za chikhulupiriro chawo chatsopanocho. Zinthu zawo zakuthupi zinayamba kutha, koma iwo anaziona kuti sizinali zofunika kwambiri. Anapeza Mesiya! Abale awo achikristu anali kugaŵana nawo zimene anali nazo pofuna kuti onse apitirize kukhala “chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi . . . mapemphero.”​—Machitidwe 2:42.

M’kupita kwa nthaŵi, Akristu ena anayamba kunyalanyaza kufunika kwa kusonkhana ndi anzawo. (Ahebri 10:23-25) Mwinamwake anayamba kudera nkhaŵa kwambiri zinthu zakuthupi, akumanyalanyaza zinthu zauzimu kwinaku akuyesetsa kupeza chuma cha iwo eni ndi mabanja awo. Atalimbikitsa abale ake kuti asaleke kusonkhana, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”​—Ahebri 13:5.

Uphungu wa Paulo umenewu unalidi wapanthaŵi yake. Patapita zaka ngati zisanu Paulo atalemba kalata yake yopita kwa Ahebri, gulu la ankhondo achiroma lotsogozedwa ndi Cestius Gallus linazinga Yerusalemu. Akristu okhulupirika anakumbukira chenjezo la Yesu lakuti: “Pamene mukaona [chimenechi] . . . , iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asaloŵe kukatulutsa kanthu m’nyumba mwake; ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake.” (Marko 13:14-16) Iwo anadziŵa kuti chipulumutso chawo sichinadalire pa kukhala ndi ntchito yokhazikika kapena kukhala ndi katundu wofunika ayi, koma chinadalira pa kumvera malangizo a Yesu. Amene anamvera uphungu wa Paulo ndi kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba mosakayika konse anaona kuti kunali kosavuta kusiya nyumba, ntchito, zovala, ndi katundu wawo nathaŵira kumapiri mosiyana ndi anthu amene anapitirizabe kukonda ndalama.

Mmene Ena Lerolino Amaikira Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba

Akristu okhulupirika lerolino amaona kuti nkofunika kwambiri kuyanjana ndi abale awo nthaŵi zonse, ndipo ambiri amadzimana kuti apezeke pamisonkhano. M’madera ena, ntchito zokha zomwe zimapezeka zimakhala zashifiti. Mbale wina amapempha anzake kuti awagwirire ntchito Loŵeruka lililonse usiku, nthaŵi yomwe ambiri m’deralo amakonda kukasanguluka, kuti anzakewo akamgwirire ntchitoyo pausiku umene iye amakapezeka pamisonkhano. Abale ena omwe amagwira ntchito yashifiti amakapezeka pamisonkhano ya pampingo wapafupi ngati ntchito yawo imawalepheretsa kukapezeka pamisonkhano ya kumipingo yawo. Potero, iwo amapezeka pafupifupi pamisonkhano yonse. Munthu wina wokondwerera ku Canada anazindikira msanga za kufunika kwa Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndiponso Msonkhano Wautumiki, koma ntchito yake inali kumlepheretsa kukapezekapo. Choncho, iye anali kulipira wantchito mnzake kuti azimgwirira ntchito yashifitiyo pofuna kuti iye azipeza mpata wokapezeka pamisonkhano yofunika imeneyi.

Ambiri amene amadwala matenda osatha samaphonyaphonya misonkhano. Iwo amamvetsera programuyo kunyumba kwawo pogwiritsira ntchito telefoni kapena mwa kujambula programuyo pakaseti ngati iwo sangathe kukafika ku Nyumba ya Ufumu. Iwo amayamikira kwambiri zogaŵira zauzimu za Yehova kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”! (Mateyu 24:45) Akristu amene amasamalira makolo awo okalamba amayamikira kwambiri pamene abale ndi alongo ena amadzipereka kuti akhale ndi makolowo kuti Mkristu wosamalira makolowa akapezeke nawo pamsonkhano wampingo.

Konzekeranitu!

Makolo amene amazindikira zosoŵa zawo zauzimu amathandiza ana awo kuti azikonda kupezeka pamisonkhano yachikristu. Iwo amauza ana awo kuti azichita homuweki yawo nthaŵi imene angopatsidwa homuwekiyo m’malo moyembekeza kuti iunjikane. Ngati kuli msonkhano usikuwo, anawo amachita homuweki yawo atangofika kuchokera kusukulu. Zosangulutsa zawo ndi zinthu zina siziyenera kuwalepheretsa kukapezeka pamisonkhano.

Monga mwamuna wokwatira ndiponso tate, kodi kupezeka pamisonkhano kuli chinthu choyamba pamoyo wanu? Monga mkazi wokwatiwa ndiponso mayi, kodi mumayesetsa kulinganiza bwino ntchito zanu kuti mukhale ndi mpata wokapezeka pamisonkhano? Monga wachinyamata wapasukulu, kodi mumaona kuti misonkhano njofunika kwambiri kuposa homuweki kapena kuti homuweki njofunika kwambiri kuposa misonkhano?

Msonkhano wampingo uli makonzedwe achikondi a Yehova. Muyenera kuyesetsa kwambiri kukhala ndi mbali pamakonzedwe ameneŵa. Yehova adzakudalitsani kwambiri ngati muika zinthu zofunika pamalo oyamba!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena