Ndinaphunzira Kudalira Yehova
YOSIMBIDWA NDI JÁN KORPA-ONDO
Munali mu 1942, ndipo asilikali a ku Hungary ndiwo anali kundiyang’anira pafupi ndi Kursk, Russia. Tinali andende a maiko a m’gulu lotchedwa Axis omwe anali kuthirana nkhondo ndi Arasha m’Nkhondo Yadziko II. Manda anga anakumbidwiratu, ndipo anandipatsa mphindi khumi kuti ndilingalire zosaina chikalata chonena kuti sindinenso mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndisanafotokoze zotsatirapo zake, ndifuna ndikuuzeni mmene ndinafikira kumeneko.
NDINABADWA mu 1904 m’mudzi waung’ono wa Zahor, umene tsopano uli kummaŵa kwa Slovakia. Nkhondo Yadziko I itatha, Zahor anakhala mbali ya dziko longokhazikitsidwa kumene la Czechoslovakia. Mudzi wathu unali ndi mabanja pafupifupi 200 ndi matchalitchi aŵiri, ina inali ya Greek Catholic ndipo inayo inali ya Calvinist.
Ngakhale kuti ndinkapita ku Tchalitchi cha Calvinist, ndinali ndi makhalidwe oipa. Mwamuna wina amene ankakhala pafupi ndi nyumba yanga anali wosiyana ndi ena onse. Tsiku lina anayamba kukambitsirana nane ndipo anandibwereka Baibulo. Inali nthaŵi yanga yoyamba kugwira buku limenelo. Panthaŵiyi, mu 1926, ndinakwatira Barbora, ndipo kenaka tinali ndi ana aŵiri, Barbora ndi Ján.
Ndinayamba kuŵerenga Baibulolo, koma panali zinthu zambiri zimene sindinazimvetsetse. Choncho, ndinapita kwa pasitala wanga ndipo ndinampempha kuti andithandize. “Baibulo ndi buku la anthu ophunzira okha,” anandiuza motero, “usayese nkomwe kulimvetsetsa.” Kenaka anandiuza kuti tiyambe kuseŵera makhadi.
Nditachoka kumeneko ndinapita kwa munthu amene anandibwereka Baibulo uja. Iye anali Wophunzira Baibulo, dzina lapanthaŵiyo la Mboni za Yehova. Anali wokondwa kundithandiza, ndipo kenaka maso anga anayamba kutseguka. Ndinasiya kumwa moŵa mwauchidakwa ndipo ndinayamba kukhala ndi makhalidwe abwino; ndipo ndinayambanso kuuza ena za Yehova. Choonadi cha Baibulo chinakhazikika ku Zahor cha m’ma 1920, ndipo posakhalitsa gulu lokangalika la Ophunzira Baibulo linakhazikitsidwa.
Komabe, panali chitsutso chachikulu chochokera kwa zipembedzo zina. Wansembe wa m’mudzimo anasonkhezera anthu ambiri a m’banja langa kuti anditsutse, akumanena kuti ndachita msala. Koma moyo wanga unayamba kukhala watanthauzo, ndipo ndinatsimikiza mtima kutumikira Mulungu woona, Yehova. Choncho, mu 1930, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa.
Kuyambika kwa Ziyeso Zoopsa
Mu 1938, dera lathu linayamba kulamuliridwa ndi Hungary, dziko limene linali kugwirizana ndi Germany m’Nkhondo Yadziko II. Panthaŵiyo, m’mudzi mwathu munali Mboni pafupifupi 50 ndipo mudziwo unali ndi anthu osakwana chikwi. Tinapitirizabe kulalikira ngakhale kuti kuteroko kunali kuika miyoyo yathu ndi ufulu wathu pangozi.
Mu 1940, anandiuza kuti ndiloŵe m’gulu lankhondo la Hungary. Kodi ndikanachitanji? Chabwino, ndinali nditaŵerenga maulosi a m’Baibulo onena kuti anthu adzasula zida zawo zankhondo kuti zikhale zipangizo zamtendere, ndipo ndinadziŵa kuti, m’kupita kwa nthaŵi, Mulungu adzathetsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi. (Salmo 46:9; Yesaya 2:4) Choncho, ndinayamba kudana ndi nkhondo, ndipo ndinaganiza kuti ndisaloŵe m’gulu lankhondo, mosasamala kanthu za zotsatirapo zake.
Anandilamula kuti ndikhale m’ndende kwa miyezi 14 ndipo anandiika m’ndende ya ku Pécs, Hungary. Mboni zina zisanu zinali m’ndende yomweyo, ndipo tinasangalala kuti tinali kukhalira pamodzi. Komabe, nthaŵi inayake anakandiika kwandekha ndipo anamanga mapazi anga ndi unyolo. Anatimenya chifukwa chokana kugwira ntchito yothandizira nkhondo. Ndiponso, anatikakamiza kuti tiime njo tsiku lonse, kupatulapo maola aŵiri okha masana. Nkhanza imeneyi inachitika kwa miyezi yambiri. Koma tinali okondwa kuti tinali ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu.
Kodi Ndigonje?
Tsiku lina, gulu la ansembe 15 achikatolika anafika nayesa kutikakamiza kuti tichirikize nkhondo mwa kuloŵa m’gulu lankhondo. Pamakambitsiranowo, ifeyo tinati: “Ngati mungatitsimikizire pogwiritsira ntchito Baibulo kuti moyo sumafa ndipo tidzapita kumwamba tikadzafa m’nkhondo, tiloŵa m’gulu lankhondolo.” Ndithudi, iwo analephera kutsimikiza zimenezo, ndipo sanafunenso kupitiriza makambitsiranowo.
Mu 1941, nthaŵi yanga yokhala m’ndende inatha, ndipo ndinali kuyembekezera kukakumananso ndi banja langa. M’malo mwake, ananditenga atandimanga unyolo, nakanditula kumudzi wa asilikali ku Sárospatak, Hungary. Titafika kumeneko, ndinali ndi mwayi womasulidwa. ‘Ungosaina chikalata ichi cholonjeza kuti udzalipira 200 pengö utabwerera kunyumba,’ anandiuza motero.
Ndinafunsa kuti: “Zimenezo zidzatheka bwanji? Ndalamazo nzachiyani?”
Anandiuza kuti: “Utadzapereka ndalamazo udzalandira chikalata chonena kuti atakuyesa kuchipatala, anapeza kuti sungathe kuloŵa m’gulu lankhondo.”
Zimenezi zinandisoŵetsa chochita. Ndinali nditazunzidwa mochititsa mantha kwanthaŵi yoposa chaka chimodzi; ndinatopa nazo. Tsopano, mwa kungopereka ndalama pang’ono, ndikanamasulidwa. “Ndilingalire bwino,” ndinadziuza motero.
Kodi ndikanasankha kuchitanji? Ndinalingalira za mkazi wanga ndi ana anga. Panthaŵiyo ndinali nditalandira kalata yochokera kwa Mkristu mnzanga yondilimbikitsa. Iye anagwira mawu Ahebri 10:38, pamene mtumwi Paulo anagwira mawu a Yehova akuti: “Wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m’chikhulupiriro: ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.” Patangopita nthaŵi yochepa, asilikali aŵiri a Hungary a pamudzipo analankhula nane, ndipo mmodzi anati: “Ifeyotu timakulemekeza kwambiri chifukwa chakuti umatsatira mapulinsipulo a m’Baibulo molimba mtima! Usagonje!”
Tsiku lotsatira ndinapita kwa aja amene anandipempha kuti ndilipire 200 pengö kuti andimasule ndipo ndinawauza kuti: “Popeza kuti Yehova Mulungu ndiye amene walola kuti ndiikidwe m’ndende, iye adzasamaliranso za kumasulidwa kwanga. Sindilipira ndalama kuti mundimasule.” Choncho, anandiuza kuti ndikhale m’ndende zaka khumi. Koma zimenezo sizinali zoyesayesa zomaliza zofuna kuti ndigonje. Khoti linanena kuti lindikhululukira ngati nditavomera zokatumikira m’gulu lankhondo kwa miyezi iŵiri yokha, ndipo pautumikiwo sindidzagwira chida chankhondo! Ndinakananso zimenezo, ndipo anandiika m’ndende.
Chizunzo Chikula
Ananditengeranso kundende ya ku Pécs. Panthaŵiyi, anandizunza koposa. Anandimanga manja kumbuyo, nandipachika kwa maola aŵiri, ndipo pondipachikapo anamanganso manja omwewo. Choncho, mapeŵa anga onse anathyoka. Anandizunza chotero mobwerezabwereza kwa miyezi pafupifupi isanu ndi umodzi. Ndimayamika Yehova kuti sindinagonje.
Mu 1942, gulu lathu lonse—oikidwa m’ndende pazifukwa zandale, Ayuda, ndiponso Mboni za Yehova zokwana 26—anatisamutsira kumzinda wa Kursk m’dera lomwe munali asilikali achijeremani. Anatipereka kwa ajeremani, ndipo iwo anauza andende onse kuti azipereka chakudya, zida zankhondo, ndiponso zovala kwa asilikali kumalo omenyera nkhondo. Koma Mbonife tinakana kugwira ntchito imeneyo chifukwa chakuti inali yosemphana ndi uchete wathu wachikristu. Chotsatirapo chake, anatibwezera kwa asilikali a Hungary.
Kenaka anatiika m’ndende yakomweko ku Kursk. Anali kutimenya ndi zikoti zamphira katatu patsiku kwa masiku angapo. Tsiku lina anandimenya chibakhela m’litsipa ndipo ndinagwa pansi. Pamene anali kundimenya, ndinalingalira kuti, ‘Kufa nkosavuta.’ Thupi langa lonse linachita dzanzi, choncho, sindinkamva kupweteka. Sanatipatse chakudya chilichonse kwa masiku atatu. Kenaka anatitengera kukhoti, ndipo Mboni zisanu ndi imodzi anazilamula kuti ziphedwe. Atawapha, tinakhala anthu 20.
Ziyeso za chikhulupiriro zomwe tinayang’anizana nazo m’masiku amenewo ku Kursk mu October 1942 zinali zoopsa kuposa zonse zimene ndinakumana nazo. Tinadzimva monga momwe anafotokozera Mfumu Yehosafati wakale pamene anthu ake anakumana ndi vuto lalikulu kwambiri. Iye anati: “Mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nawo aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziŵa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.”—2 Mbiri 20:12.
Tonsefe 20 anatitenga kuti tikadzikumbire manda, ndipo asilikali 18 a Hungary ndiwo amene anali kutiyang’anira. Titamaliza kukumba mandawo, anatipatsa mphindi khumi kuti tisaine chikalata, chimene ena mwa mawu ake anati: “Chiphunzitso cha Mboni za Yehova ncholakwika. Sindidzachikhulupiriranso kapena kuchichirikiza. Ndidzamenyera dziko langa la Hungary . . . Ndikutsimikiza ndi siginecha yanga kuti ndikuloŵa Tchalitchi cha Roma Katolika.”
Mphindi khumizo zitatha, anatilamula kuti: “Tembenukirani kulamanja! Gubani ulendo wakumanda!” Ndipo analamulanso kuti: “Wandende woyamba ndi wachitatu loŵani m’dzenjemo!” Anthu aŵiri ameneŵa anawapatsanso mphindi khumi kuti alingalire pankhani yosaina chikalata chija. Mmodzi mwa asilikaliwo anawauza kuti: “Mungosiya chikhulupiriro chanu ndi kutuluka m’mandamo!” Onse anangokhala chete. Kenaka msilikali wamkulu anawawombera.
Msilikali wina anafunsa msilikali wamkuluyo kuti: “Nanga enawa titani nawo?”
“Amangeni,” iye anayankha motero. “Tiwazunza kwambiri ndipo tidzawawombera pa 6 koloko mmaŵa.”
Mwadzidzidzi ndinachita mantha, osati chifukwa choopa kufa ayi, koma chifukwa chakuti mwina sindikanatha kupirira ndipo mwina ndikanagonja. Choncho ndinapita kutsogoloko ndipo ndinamuuza kuti: “Bwana, ifenso talakwa monga momwe alakwira abale athu omwe mwawomberawa. Bwanji osangotiwomberanso?”
Koma sanatiwombere. Anatimanga manja kumbuyo natipachika ndipo potipachikapo anamanganso manja omwewo. Titakomoka, anali kutithira madzi. Tinamva kupweteka kwambiri popeza kuti mapeŵa athu anathyoka chifukwa cha kulemera kwa matupi athu. Chizunzo chimenechi chinachitika kwa maola atatu. Kenaka, mwadzidzidzi, anapereka lamulo loti Mboni za Yehova asaziwomberenso.
Kusamukira Kummaŵa—Kenako Kuthaŵa
Patapita milungu itatu, anatigubitsa kwa masiku angapo paulendo wopita kugombe la Mtsinje wa Don. Amene anatitengawo anatiuza kuti kumeneko sitikabwerako amoyo. Masana ankatipatsa ntchito yopanda tanthauzo yokumba ngalande ndi kuzifotseranso. Madzulo anali kutipatsako mpata woyenda.
Monga momwe ndinazionera, panali zinthu ziŵiri. Kufera komweko, kapena kuthaŵa Ajeremani ndi kukadzipereka kwa Arasha. Atatu okha a ife tinaganiza zothaŵa mwa kuwoloka Mtsinje wa Don womwe madzi ake anali ataundana. Pa December 12, 1942, tinapemphera kwa Yehova ndipo tinanyamuka. Tinakafika kwa asilikali a Russia ndipo nthaŵi yomweyo anatiika mumsasa wa andende momwe munali andende pafupifupi 35,000. Pomadzafika m’nyengo yangululu andende pafupifupi 2,300 okha ndiwo anatsala amoyo. Ena onsewo anafa ndi njala.
Kumasulidwa Koma Kukumanabe ndi Mavuto Owonjezereka
Panthaŵi yonse yankhondo kuphatikizaponso miyezi ingapo nkhondoyo itatha ndinali wandende wa Russia. Pomalizira pake, mu November 1945, ndinabwerera kumudzi wathu wa Zahor. Famu yathu inasakazidwa kotheratu, kotero kuti ndinayambiranso kuikonza. Mkazi wanga ndi ana anga anali kusamalira famuyo panthaŵi yankhondo, koma mu October 1944, pamene Arasha anali kuyandikira, anawasamutsira kummaŵa. Analanda katundu yense amene tinali naye.
Chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti, nthaŵi imene ndinabwerera kumudzi, mkazi wanga anadwala kwambiri. M’February 1946, iye anamwalira. Anali ndi zaka 38 zokha zakubadwa. Tinangokhala pamodzi nthaŵi yochepa titakumananso pambuyo pa kulekana kwazaka zisanu zazitali ndiponso zovuta.
Ndinapeza chitonthozo pakati pa abale anga auzimu, mwa kupezeka pamisonkhano ndiponso mwa kuchita nawo utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Mu 1947, ndinabwereka ndalama zomwe ndinayendera popita kumsonkhano waukulu wa ku Brno, ndipo umenewo unali ulendo wa makilomita pafupifupi 400. Kumeneko ndinalandira chitonthozo ndi chilimbikitso chachikulu pakati pa abale anga achikristu amene anaphatikizapo Nathan H. Knorr, pulezidenti wa panthaŵiyo wa Watch Tower Bible and Tract Society.
Ufulu umene tinali nawo nkhondo itatha sunakhalitse. Mu 1948 Akomyunisiti anayamba kutizunza. Abale ambiri amene anali kutsogolera pantchito ya Mboni za Yehova ku Czechoslovakia anamangidwa mu 1952, ndipo ndinapatsidwa udindo wosamalira mipingo. Mu 1954, inenso anandigwira ndipo anandilamula kuti ndikhale m’ndende kwa zaka zinayi. Mwana wanga, Ján pamodzi ndi mwana wake Juraj anawaikanso m’ndende chifukwa chosunga uchete wawo wachikristu. Ndinakhala m’ndende ya Pankrác ku Prague kwa zaka ziŵiri. Mu 1956 analengeza kuti omangidwa onse akhululukidwe ndipo ndinamasulidwa panthaŵiyo.
Ufulu Pomalizira Pake!
Pomalizira pake, mu 1989, Chikomyunizimu chinachepa mphamvu ku Czechoslovakia, ndipo ntchito ya Mboni za Yehova inaloledwa mwalamulo. Choncho, tinali ndi ufulu wosonkhana ndi kulalikira poyera. Panthaŵiyo Zahor anali ndi Mboni pafupifupi zana limodzi, zimene zinatanthauza kuti munthu mmodzi mwa anthu pafupifupi khumi alionse m’mudzimo anali Mboni. Zaka zingapo zapitazo, tinamanga Nyumba ya Ufumu yokongola ndiponso yaikulu ku Zahor, ndipo mungakwanire anthu pafupifupi 200.
Tsopano thanzi langa linafooka, choncho, abale amandinyamula pagalimoto kupita nane ku Nyumba ya Ufumu. Kuyanjana ndi abale kumandipatsa chimwemwe ndipo ndimasangalalanso ndikamapereka ndemanga pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Ndilinso wosangalala kwambiri chifukwa choona ana a m’mibadwo itatu ya banja langa akutumikira Yehova, kuphatikizapo zidzukulu zambirimbiri. Mmodzi mwa ameneŵa anatumikirapo monga woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova ku Czechoslovakia mpaka nthaŵi imene anasiya utumikiwo chifukwa cha maudindo a m’banja lake.
Ndikuyamika Yehova chifukwa chondilimbikitsa paziyeso zambiri. Ndinachirikizidwa chifukwa chakuti ndinapitirizabe kuyang’ana kwa iye—“monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Inde, ndaonadi dzanja lake lamphamvu lolanditsa. Nchifukwa chake, ngakhale tsopano lino, ndikupitirizabe kuyesetsa kupezeka pamisonkhano yampingo ndiponso kulalikira nawo dzina lake muutumiki wapoyera monga momwe ndingathere.
[Chithunzi patsamba 25]
Nyumba ya Ufumu ya ku Zahor
[Chithunzi patsamba 26]
Ndimayamikira kwambiri mwayi wa kupereka ndemanga pa Phunziro la Nsanja ya Olonda