“Choonadi Chidzakumasulani”
“Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” Anatero Yesu kwa makamu a anthu powaphunzitsa pakachisi wa ku Yerusalemu. (Yohane 8:32) Atumwi a Yesu anali okhutira kuti ziphunzitso za Yesu nchoonadi. Iwo anaona maumboni ochuluka akuti mphunzitsi wawo anachokera kwa Mulungu.
KOMABE, ena lerolino amavutika kudziŵa choonadi chimene Yesu anatchula. Monga m’masiku a mneneri Yesaya, lerolino pali “iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima; amene aika zoŵaŵa m’malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m’malo mwa zoŵaŵa!” (Yesaya 5:20) Pokhala pali malingaliro, mafilosofi, ndi makhalidwe osiyanasiyana amene akufala masiku ano, anthu ambiri amalingalira kuti zonse zimangosinthasintha ndipo kulibe chinthu chimene chingakhale choonadi.
Pamene Yesu anauza omvetsera ake kuti choonadi chidzawamasula, iwo anati: “Tili mbewu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthaŵi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa aufulu?” (Yohane 8:33) Iwo sanalingalirepo kuti akufunikira winawake kapena chinachake choti chiwamasule. Komano Yesu anafotokoza kuti: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.” (Yohane 8:34) Choonadi chimene Yesu anali kunena chingamasule munthu ku uchimo. Yesu anati: “Ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.” (Yohane 8:36) Choncho choonadi chimene chimamasula anthu ndi choonadi chonena za Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. Munthu angamasuke ku uchimo ndi imfa kokha mwa kukhulupirira nsembe ya Yesu ya moyo wake wangwiro waumunthu.
Panthaŵi inayake Yesu anati: “Patulani iwo m’choonadi; mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Mawu a Mulungu omwe ali m’Baibulo ndiwo choonadi chimene chingatimasule pa malodza ndi kulambira konyenga. Baibulo lili ndi choonadi chonena za Yesu Kristu, chimene chimapangitsa anthu kumkhulupirira ndiponso chimapereka chiyembekezo chabwino zedi cha zamtsogolo. Kudziŵa choonadi cha Mawu a Mulungu nkonyaditsa zedi!
Kodi kudziŵa choonadi nkofunika motani? Ngakhale kuti zipembedzo zambiri lerolino zimati zikutsatira Baibulo, izo zili ndi ziphunzitso zambiri zochokera m’mafilosofi ndi m’miyambo ya anthu. Nthaŵi zambiri, atsogoleri achipembedzo amaoneka kuti amangosamala zoti anthu akugwirizana ndi uthenga wawo koma osati za kulongosoka kwa uthengawo. Ena amalingalira kuti Mulungu amakhutira ndi kulambira kulikonse, malinga ngati nkochokera pansi pa mtima. Koma Yesu Kristu anafotokoza kuti: “Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.”—Yohane 4:23.
Ngati tikufuna kuti Mulungu alole kulambira kwathu, tiyenera kudziŵa choonadi. Imeneyi ndi nkhani yaikulu. Chimwemwe chathu chamuyaya chimadalira pankhaniyi. Chotero, aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amalola kulambira kwanga? Kodi ndikufunitsitsadi kuphunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu? Kapena kodi ndikuopa zimene ndingapeze nditafufuza mosamalitsa?’