Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 11/1 tsamba 19-23
  • Chachikulu Chimene Ndimafuna Ndicho Kukondweretsa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chachikulu Chimene Ndimafuna Ndicho Kukondweretsa Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo wa Utumiki Wodzipatulira
  • Chikhulupiriro Chiyesedwa Kusukulu
  • Ndiyesedwa pa Uchete Wanga Wachikristu
  • Kuyambiranso Ntchito Nditamasulidwa
  • Moyo Wolemerera ndi Wofupa
  • Kutumikira Pansi pa Dzanja la Yehova Lachikondi
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mwana Wamasiye Wosowa Wom’samala Apeza Atate Womukonda
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Zaka Zoposa 50 za ‘Kuwolokerako’
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Ndine Msilikali wa Khristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 11/1 tsamba 19-23

Chachikulu Chimene Ndimafuna Ndicho Kukondweretsa Yehova

YOSIMBIDWA NDI THEODOROS NEROS

Chitseko cha chipinda changa m’ndende chinatseguka, ndipo ofesala anafuula nati: “Kodi Neros ndani?” Nditayankha, anati: “Nyamuka. Tikupha.” Zimenezo zinachitika mu 1952 m’kampu ya asilikali ku Corinth, Greece. Nanga nchifukwa chiyani moyo wanga unali pangozi yotere? Ndisanafotokoze, ndikuuzeni kaye pang’ono za moyo wanga.

CHA m’ma 1925, atate wanga anakumana ndi Ophunzira Baibulo (dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo). Posakhalitsa anakhala mmodzi wa iwo ndipo anaphunzitsa abale ndi alongo awo asanu ndi atatu zikhulupiriro zawo, ndipo onsewo analandira choonadi cha Baibulo. Makolo awonso anatero. Pambuyo pake, anakwatira, ndipo ndinabadwa mu 1929 ku Agrinio, Greece.

Zaka zimenezo zinali zovuta zedi m’Greece! Choyamba panali ulamuliro wotsendereza wa General Metaxas. Kenako Nkhondo Yadziko II inaulika mu 1939 ndipo posakhalitsa Anazi analanda dzikolo. Matenda ndi njala zinachuluka. Mitembo yotupikana inali kunyamulidwa m’mawiribala aang’ono. Kuipa m’dziko kunali kuonekeratu, monganso kufunika kwa Ufumu wa Mulungu.

Moyo wa Utumiki Wodzipatulira

Pa August 20, 1942, pamene kagulu kathu kanasonkhana kunja kwa Thessalonica, woyang’anira wotsogoza wathu analoza ndege zankhondo zachibritishi zomwe zinali kuponya mabomba m’mzinda ndipo anagogomezera mmene tinalili otetezeka mwa kumvera lamulo la ‘kusaleka kusonkhana kwathu pamodzi.’ (Ahebri 10:25) Panthaŵiyo, tinasonkhana kugombe la nyanja, ndipo ndinali mmodzi wa amene anadzipereka ndi kubatizidwa. Titatuluka m’madzi, tinaima mumzere, ndipo abale athu ndi alongo athu achikristu anaimba nyimbo kutithokoza pa zimene tinasankha. Tsiku limenelo nlosaiŵalika ayi!

Posakhalitsa, pamene ineyo ndi mnyamata wina tinali kuchezera anthu mu utumiki wathu wa kunyumba ndi nyumba, apolisi anatigwira natipereka kupolisi. Pofuna kugogomezera kuti anali kutiona ngati Akomyunizimu ndi kuti ntchito yathu yolalikira inali yoletsedwa, anatimenya ndi kutiuza kuti: “Yehova ndiye Stalin amene, zitsiru inu!”

Nthaŵiyo nkuti nkhondo yachiŵeniŵeni ili mkati ku Greece, ndipo panali chizondi chachikulu kwa Akomyunizimu. Tsiku lotsatira anatiyendetsa mumsewu kudutsa nyumba zathu atatimanga maunyolo kumanja, monga apandu. Koma ziyeso zomwe ndinakumana nazo si zokhazo.

Chikhulupiriro Chiyesedwa Kusukulu

Kuchiyambiyambi kwa 1944, ndinali mwana wa sukulube, ndipo Anazi anapitiriza kukhala m’Thessalonica. Tsiku lina kusukulu, wansembe wa Greek Orthodox, mphunzitsi wathu wa zachipembedzo, anandiuza kuti andipatsa mayeso a zimene tinaphunzira tsikulo. “Si Mkristu wa Orthodox ameneyu,” ana ena anatero.

“Nanga amaloŵa mpingo uti?” mphunzitsiyo anafunsa.

“Ndine wa Mboni za Yehova,” ndinayankha.

“Mmbulu pakati pa nkhosa,” anafuula pondigwira nandiomba pama.

‘Zitheka bwanji,’ ndinaganiza choncho, ‘kuti nkhosa nkuluma mmbulu?’

Patapita masiku angapo, ife okwanira ngati 350 tinakhala pamathebulo kuti tidye chakudya cha masana. Woyang’anira anati: “Neros pemphera.” Ndinapereka pemphero la ‘Atate Wathu Wakumwamba,’ limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake, lolembedwa pa Mateyu 6:9-13. Woyang’anirayo sanakondwere nazo zimenezo, chotero anandifunsa mwaukali atakhala pamalo ake kuthebulo kuti: “Chifukwa chiyani wapemphera choncho?”

“Chifukwa ndine wa Mboni za Yehova,” ndinatero. Atamva zimenezo, iyenso anandigwira ndi kundimenya patsaya. Pambuyo pake tsiku lomwelo mphunzitsi wina anandiitana kuofesi kwake nandiuza kuti: “Wachita bwino, Neros, limbikira zimene ukhulupirira, ndipo osasiya.” Usiku womwewo, atate anandilimbikitsa ndi mawu a mtumwi Paulo awa: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.”​—2 Timoteo 3:12.

Nditamaliza sukulu ya sekondale, ndinafunikira kusankha ntchito imene ndidzagwira. Chifukwa cha nkhondo yachiŵeniŵeni m’Greece, ndinayesedwanso pankhani ya uchete wachikristu. (Yesaya 2:4; Mateyu 26:52) Pomaliza, kuchiyambiyambi kwa 1952, anandilamula kukhala zaka 20 m’ndende chifukwa chokana kumenya nawo nkhondo panthaŵi yovuta kwambiri imeneyo m’mbiri ya Greece.

Ndiyesedwa pa Uchete Wanga Wachikristu

Pamene ndinali m’kampu ya asilikali ku Mesolóngion ndi Corinth, ndinapeza mpata wofotokozera akuluakulu a asilikali kuti chikumbumtima changa chophunzitsidwa ndi Baibulo sichindilola kukhala msilikali kuchirikiza zolinga zandale. “Ndine kale msilikali wa Yesu,” ndinafotokoza, ndikumawalozera 2 Timoteo 2:3. Atandiuza kuganizapo bwino, ndinati sindinafulumire kugamula zimenezo koma ndinatero ntaganizapo kwambiri ndipo ntalingalira za kudzipatulira kwanga kwa Mulungu kuchita chifuno chake.

Chotero, ndinapatsidwa ntchito ya kalavulagaga, ndinali kudya tsiku limodzi pamasiku aŵiri alionse kwa masiku 20, ndipo ndinkagona pansi m’chipinda chamita imodzi m’lifupi ndi mamita aŵiri m’litali. Ndipo m’chipinda chimenecho ndinalimo ndi Mboni zinanso ziŵiri! Panthaŵiyo, ndili m’kampu ya ku Corinth, mpamene anandiitana m’chipindacho kuti akandiphe.

Popita kophera anthu, ofesala anafunsa kuti, “Kodi sunena kalikonse?”

“Ayi,” ndinayankha.

“Sulembera kalata kunyumba kwanu?”

“Ayi,” ndinayankhanso. “Akudziŵa kuti ndingaphedwe nthaŵi ina iliyonse.”

Titafika kubwalolo anandiuza kuima kukhoma. Kenako, m’malo molamula asilikaliwo kundiombera, ofesalayo anati, “Mloŵetseni mkati.” Anali kungoyerekeza kundipha pofuna kuona kutsimikiza mtima kwanga pachosankha changa.

Pambuyo pake, ndinatumizidwa ku chilumba cha Makrónisos, kumene sanandilole kukhala ndi mabuku alionse kusiyapo Baibulo. Mboni 13 zinkasungidwa pazokha m’nyumba yaing’ono kutali ndi akaidi aupandu pafupifupi 500. Komabe, mabuku anatifikabe chozemba. Mwachitsanzo, tsiku lina bokosi la loukoúmia (maswiti otchuka) linatumizidwa kwa ine. Ofufuza analakalaka kulaŵa loukoúmia koti sanaone magazini ya Nsanja ya Olonda yobisika pansi pake. “Asilikaliwo anadya loukoúmia, koma ife ‘tinadya’ Nsanja ya Olonda!” inatero Mboni ina.

Kope la buku latsopano lomwe linangotulutsidwa panthaŵiyo lakuti What Has Religion Done for Mankind? linatifika, ndipo mkaidi wina, Mboni yodziŵa Chingelezi, analitembenuza. Tinkaphunziriranso limodzi Nsanja ya Olonda mwamseri. Ndende tinaiona ngati sukulu, ngati mpata wolimbitsa uzimu wathu. Ndiponso, tinali achimwemwe chifukwa tinadziŵa kuti njira yathu ya kukhulupirika inakondweretsa Yehova.

Ndende yomaliza imene ndinakhalako inali ya Týrintha kummaŵa kwa Pelopónnisos. Kumeneko ndinaona mlonda amene anali kutiyang’ana kwambiri pamene ndinkaphunzitsa mkaidi mnzanga Baibulo. Patapita zaka zambiri, ndinadabwa kwabasi kukumana ndi mlonda uja ku Thessalonica! Panthaŵiyo iyenso anali Mboni. Pambuyo pake, mmodzi wa ana ake anapita ku ndende, osati kukagwira ntchito yaulonda koma monga mkaidi. Anaponyedwa m’ndende pachifukwa chomwenso ine ndinakhaliramo.

Kuyambiranso Ntchito Nditamasulidwa

Ndinangokhala zaka zitatu zokha pazaka 20 zimene ndinalamulidwa kukhala m’ndende. Nditamasulidwa ndinasankha kukakhala ku Athens. Koma posakhalitsa ndinadwala matenda a mtundu wa chibayo ndipo ndinakakamizika kubwerera ku Thessalonica. Ndinakhala miyezi iŵiri ndiligone pamphasa. Pambuyo pake ndinakumana ndi mtsikana wokongola dzina lake Koula, ndipo tinakwatirana m’December 1959. Mu 1962 anayamba kutumikira monga mpainiya, dzina la atumiki anthaŵi zonse a Mboni za Yehova. Patapita zaka zitatu inenso ndinayamba ntchito ya upainiya kugwirizana naye.

Mu January 1965, tinatumizidwa m’ntchito yadera, kuchezera mipingo ncholinga choilimbikitsa mwauzimu. Chilimwe chomwecho tinakhalanso ndi mwayi wokapezeka pamsonkhano wachigawo waukulu ku Vienna, Austria. Unasiyana ndi imene tinkachita m’Greece kumene tinkakumana mseri m’nkhalango chifukwa chakuti ntchito yathu inali yoletsedwa. Chakumapeto kwa 1965, tinaitanidwa kukagwira ntchito paofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Athens. Komabe, chifukwa cha kudwaladwala kwa achibale anga ena, tinabwerera ku Thessalonica mu 1967.

Pamene tinkasamalira maudindo a banja, tinapitiriza kukangalika pantchito yolalikira. Tsiku lina pocheza ndi mbale wanga Kostas, ndinamfotokozera ukoma wa gulu la Mulungu ndi chikondi, umodzi, ndi kumvera Mulungu zimene zili mmenemo. Poyankha anati, “Zimenezi zikanakhala zabwino ngati kukanakhala Mulungu.” Analola nditamupempha kupenda naye ngati Mulungu alikodi kapena kulibe. Ndinamuuza kuti tidzapita ku msonkhano wamitundu yonse wa Mboni za Yehova ku Nuremberg, Germany, mu August 1969. Anapempha kupita limodzi nane, ndipo mnzake Alekos, amenenso tinali kuphunzira naye Baibulo, analinso kufuna kupita.

Msonkhano wa ku Nuremberg unali wochititsa chidwi zedi! Msonkhanowo unachitikira m’bwalo la maseŵero lalikulu limene Hitler ankakondwereramo zipambano zake pankhondo. Osonkhana tinafika pa chiŵerengero chapamwamba choposa 150,000, ndipo mzimu wa Yehova unaonekera mwa zochitika zonse. Mwamsanga pambuyo pake Kostas ndi Alekos anabatizidwa. Onse aŵiriwo tsopano ndi akulu achikristu, ndipo mabanja awonso ndi Mboni.

Ndinayamba kuphunzira ndi mayi wina wokondwerera. Mwamuna wake anati anafuna kufufuza zikhulupiriro zathu, ndipo posakhalitsa anandiuza kuti waitana a Sakkos, katswiri wa zaumulungu wa Greek Orthodox, kumakambirano. Mwamunayo anafuna kutifunsa mafunso aŵirife. A Sakkos anafika, limodzi ndi wansembe. Munthu amene tinali kucheza nayeyo anayamba mwa kunena kuti, “Choyamba, ndikufuna kuti a Sakkos ayankhe mafunso atatu.”

Atanyamula Baibulo limene tinali kugwiritsa ntchito pamakambirano athu, mwamunayo anafunsa kuti, “Funso loyamba: Kodi Baibulo ili nlenileni, kapena ndi Baibulo la Mboni?” A Sakkos anayankha kuti linalidi lenileni, ndi kutinso Mboni za Yehova “zimakonda Baibulo.”

Popitiriza, mwamunayo anafunsanso, “Funso lachiŵiri: Kodi Mboni za Yehova ali anthu akhalidwe?” Kwenikweni, anali kufuna kudziŵa mtundu wa anthu amene mkazi wake anayamba kuyanjana nawo. Katswiri wa zaumulunguyo anayankha kuti iwo alidi anthu akhalidwe.

“Funso lachitatu,” anapitiriza mwamunayo, “Kodi Mboni za Yehova zimalipidwa?” “Ayi,” anayankha katswiri wa zaumulungu ameneyo.

“Ndapeza mayankho a mafunso anga, ndipo ndasankha zochita,” anatero pomaliza mwamunayo. Pambuyo pake anapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo posakhalitsa anabatizidwa monga wa Mboni za Yehova.

Moyo Wolemerera ndi Wofupa

Ndinayambiranso kutumikira monga woyang’anira dera mu January 1976. Patapita zaka zisanu ndi chimodzi, ndinakhala ndi mwayi woyamba ulaliki watsopano m’Greece​—umboni wa mu msewu. Kenako mu October 1991, ine ndi mkazi wanga tinayamba kutumikira monga apainiya apadera. Patapita miyezi ingapo, ndinachitidwa opaleshoni ya mtima yotchedwa quadruple bypass imene mwamwayi inachitika bwino. Tsopano thanzi langa lili bwino, ndipo ndayambiranso ntchito yolalikira yanthaŵi zonse. Ndipo ndine mkulu mumpingo wina mu Thessalonica, ndiponso ndili mu Komiti Yolankhulana ndi Chipatala kwathuko yopereka thandizo lokhudzana ndi zachipatala kwa ofuna.

Ndikayang’ana moyo wanga wonse, ndimaona kukhutiritsa kwake kwa kukondweretsa Atate wathu wakumwamba. Ndine wokondwa kuti kalelo ndinamvetsera pempho lake lochonderera lakuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Mtima wanga umasangalaladi kuona chiŵerengero chikuwonjezeka padziko lonse lapansi cha anthu oona mtima amene akuloŵa m’gulu la Yehova. Ndi mwayi waukulu zedi kuchita nawo ntchito yomasula anthu ndi choonadi cha Baibulo ndi kuwapatsa mpata wokhala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’dziko latsopano lolungama.​—Yohane 8:32; 2 Petro 3:13.

Nthaŵi zonse timalimbikitsa atumiki achinyamata a Yehova kuika utumiki wanthaŵi zonse kukhala cholinga chawo, kumpatsa nthaŵi ndi nyonga zawo. Inde, kukhulupirira Yehova ndi kupeza chimwemwe chochuluka mwa kukondweretsa mtima wake ndiwo moyo wokhutiritsa kwambiri umene munthu angakhale nawo!​—Miyambo 3:5; Mlaliki 12:1.

[Zithunzi patsamba 21]

(Kumanzere kumka kulamanja)

Ndinkagwira ntchito ku Beteli m’khichini mu 1965

Ndikukamba nkhani mu 1970 pamene kulalikira kwathu kunali koletsedwa

Ine ndi mkazi wanga mu 1959

[Chithunzi patsamba 23]

Ine ndi mkazi wanga, Koula

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena