Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 11/15 tsamba 8-9
  • Dariyo—Mfumu Yokonda Chilungamo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dariyo—Mfumu Yokonda Chilungamo
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MFUMU YOSADZIŴIKA BWINO MBIRI YAKE
  • DANIELI APEZA CHIYANJO
  • Alanditsidwa ku Mano a Mikango!
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Danieli Anaponyedwa M’dzenje la Mikango
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Danieli Anatumikira Mulungu Mosalekeza
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Danieli m’Dzenje la Mikango
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 11/15 tsamba 8-9

Dariyo​—Mfumu Yokonda Chilungamo

PONENA za zimango zake, mfumu ina yotchuka kalelo inadzitama kuti: “Mzinda wa Babulo ndinaukweteza ndi linga lolimba chakummaŵa. Ndinakumba chemba . . . Ndinamanga ndi njerwa ndi phula linga lamphamvu limene, monga phiri, silingasunthidwe.” Inde, Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inali itamanga zinthu zambirimbiri ndipo inachita zambiri kulimbitsa likulu la ufumu wake. Koma mzinda wa Babulo sunakhale wosagonjetseka monga momwe inaganizira.

Umboni wa zimenezi unaonekera pa October 5, 539 B.C.E. Atatsagana ndi gulu lankhondo la ku Mediya, wolamulira wa Perisiya Koresi II analanda Babulo panthaŵiyo ndi kupha wolamulira wake, Belisazara Mwakaldayo. Kodi ndani tsopano anali kudzakhala wolamulira woyamba wa mzinda wolandidwa chatsopanowu? Mneneri wa Mulungu Danieli, amene anali mumzindamo pamene unagonjetsedwa, analemba kuti: “Dariyo Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziŵiri.”​—Danieli 5:30, 31.

Kodi Dariyo anali yani? Kodi anakhala wolamulira wotani? Kodi anakhala naye motani mneneri Danieli, amene anali mu ukapolo ku Babulo kwa zaka zoposa 70?

MFUMU YOSADZIŴIKA BWINO MBIRI YAKE

Mbiri yonena za Dariyo Mmedi njosadziŵika bwino. Mwachionekere Amedi sanasiye mbiri iliyonse yolembedwa. Ndiponso, miyala zikwi mazana ambiri yofukulidwa ku Middle East imene ili ndi zolemba zozokotedwa siikusimba mbiriyo mwatsatanetsatane. Zolembedwa zina zakale zimene zidakalipo nzochepa ndipo zikusimba zinthu zimene zinachitika patapita zaka zana limodzi kapena kuposapo kuchokera pamene Dariyo anakhalako.

Ngakhale zili choncho, umboni ukusonyeza kuti atalanda Ecbatana, likulu la Mediya, Amedi anakhala okhulupirika kwa wolamulira wa Perisiya, Koresi II. Kenako, Amedi ndi Aperisi motsogozedwa ndi wolamulirayo, anamenya nkhondo mogwirizana. Ponena za unansi wawo, wolemba Robert Collins m’buku lake lakuti The Medes and Persians anati: “Pamtendere Amedi sanali kusiyana ndi Aperisi. Nthaŵi zambiri anali kupatsidwa maudindo apamwamba m’boma ndi utsogoleri m’gulu lankhondo la Aperisi. Alendo ankanena za Amedi ndi Aperisi, osasiyanitsa pakati pa wogonjetsedwa ndi wogonjetsa.” Choncho Mediya inagwirizana ndi Perisiya kupanga Ufumu wa Amedi ndi Aperisi.​—Danieli 5:28; 8:3, 4, 20.

Amedi anachitadi zambiri pogonjetsa Babulo. Malemba amanena kuti “Dariyo mwana wa Ahaswero, wa mbewu ya Amedi” anali mfumu yoyamba ya Ufumu wa Amedi ndi Aperisi, kulamulira Babulo. (Danieli 9:1) Mphamvu yake yaufumu inaphatikizapo mphamvu yopanga malamulo “monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.” (Danieli 6:8) Zimene Baibulo limanena ponena za Dariyo zimatisonyezanso zinthu zingapo ponena za umunthu wake ndi chifukwanso chomveka chimene palibe zolembedwa zambiri zakudziko zonena za iye.

DANIELI APEZA CHIYANJO

Atangokhala mfumu m’Babulo, Dariyo anaika “akalonga zana limodzi mphambu makumi aŵiri akhale m’madera onse a ufumu,” Baibulo limatero, “ndi akuyang’anira iwo akulu atatu, woyamba wawo ndi Danieli.” (Danieli 6:1, 2) Komabe, malo apamwamba a Danieli anawanyansa zedi akuluakulu enawo. Mosakayikira, kukhulupirika kwake kunkatsekereza ukatangale, zimene ziyenera kuti zinawapangitsa kuipidwa naye. Kusiriranso kuyenera kuti kunasonkhezera akuluakuluwo, popeza kuti mfumu inamkonda Danieli ndipo inali kuganiza zompanga kukhala nduna yaikulu.

Pofuna kuthetsa mkhalidwewu, akuluakulu aŵiriwo ndi akalonga anapanga chiŵembu pogwiritsa ntchito malamulo. Iwo anapereka lamulo kwa mfumu ndi kuipempha kuti isaine, lamulo loletsa ‘kupempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense’ kusiyapo kwa Dariyo pamasiku 30. Iwo anati aliyense woswa lamulo limeneli aponyedwe m’dzenje la mikango. Iwo anapangitsa Dariyo kukhulupirira kuti lamulo limenelo lidzasangalatsa nduna zonse za boma, ndiponso lamulolo linaonekanso ngati kuti ndunazo zikusonyeza kukhulupirika kwawo kwa mfumu.​—Danieli 6:1-3, 6-8.

Dariyo anasaina lamulolo ndipo posachedwa anayang’anizana ndi zotsatirapo zake. Danieli anakhala woyamba kuswa lamulolo, popeza kuti anapitiriza kupemphera kwa Yehova Mulungu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 5:29.) Danieli wokhulupirikayo anaponyedwa m’dzenje la mikango mosasamala kanthu zoti mfumu inayesetsadi kupeza njira yozembera lamulo losasinthikalo. Dariyo anafotokoza kuti anali ndi chidaliro chakuti Mulungu wa Danieli ali ndi mphamvu yopulumutsa mneneriyo.​—Danieli 6:9-17.

M’maŵa mwake, pambuyo posapeza tulo ndi kusala kudya usiku wonse, Dariyo anathamangira ku dzenje la mikango. Anakondwera chotani nanga kupeza Danieli ali wamoyo ndiponso wosavulazidwa! Powabwezera chilango, mfumuyo inalamula kuti awo amene anaimba mlandu Danieli ndi mabanja awo aponyedwe m’dzenje la mikango nthaŵi yomweyo. Anaperekanso lamulo lakuti ‘m’maiko onse a ufumu wake anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Danieli.’​—Danieli 6:18-27.

Ndithudi, Dariyo analemekeza Mulungu wa Danieli ndi chipembedzo chake ndipo anali wofunitsitsa kuwongolera zinthu zolakwika. Komabe, kulanga oimba mlandu Danieli kuyenera kuti kunachititsa akuluakulu otsalawo kukwiya kwambiri. Ndiponso, chilengezo cha Dariyo cholamula anthu onse a mu ufumu wake kuti ‘aziopa Mulungu wa Danieli’ chiyenera kuti chinachititsa atsogoleri achipembedzo amphamvu a m’Babulo kuipidwa kwambiri. Popeza kuti alembi anasonkhezeredwa ndi nkhani zimenezi mosakayikira, sizodabwitsa ngati zolembedwa za anthu zinasinthidwa kuti zisasimbe nkhani zonena za Dariyo. Komabe, nkhani yaifupiyo ya m’buku la Danieli imatisonyeza kuti Dariyo anali wolamulira wosakondera ndi wokonda chilungamo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena