Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 12/15 tsamba 3-4
  • Kodi Khirisimasi Yanyalanyaza Kristu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Khirisimasi Yanyalanyaza Kristu?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambi cha Krisimasi Yamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Miyambo ya Khirisimasi—Kodi Ndi Yachikristu?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Nkhani Yaikulu Panyengo ya Khirisimasi Imakhala Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Krisimasi Imatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 12/15 tsamba 3-4

Kodi Khirisimasi Yanyalanyaza Kristu?

“Chikondwerero cha panthaŵi ya Khirisimasi sindichimvetsa. Kwa ine, chimaoneka kukhala chosiyana kotheratu ndi moyo ndi ziphunzitso za Yesu.”​—Mohandas K. Gandhi.

ANTHU ambiri angatsutse zonena za Gandhi. Angaganize kuti, ‘Kodi wandale wachihindu angadziŵenji ponena za holide yachikristu?’ Komano nzoona kuti Khirisimasi yafalikira kulikonse padziko lapansi, ikukhudza zikhalidwe zonse zosiyanasiyana. Mwezi wa December uliwonse holide imeneyi imaoneka kuti ili paliponse.

Mwachitsanzo, Amwenye ngati 145 miliyoni amakondwerera Khirisimasi, kuposapo ndi 40 miliyoni pachiŵerengero cha amene anali kuikondwerera zaka zoposa khumi zapitazo. Ndipo ngati mwakunena kuti “chikondwerero” Gandhi anali kutanthauza zinthu zakudziko zophatikizidwa pa Khirisimasi yamakono, kugula katundu motengeka mtima kumene tonsefe timaona, sitingakane kuti mbali imeneyi ya phwandoli ndiyo imakhala yaikulu nthaŵi zambiri. Magazini ya Asiaweek inati: “Khirisimasi ku Asia​—kuyamba ndi nyali za pamapwando za ku Hong Kong mpaka pamitengo italiitali ya panyengo ya Khirisimasi m’mahotela a ku Beijing mpakanso pachithunzi cha Kubadwa kwa Yesu kumadera a malonda a ku Singapore​—kwenikweni nchochitika wamba (makamaka chamalonda).”

Kodi phwando lamakono la Khirisimasi lanyalanyaza Kristu? Mwamwambo, December 25 yakhala ikusungidwa chiyambire zaka za zana lachinayi C.E., pamene Tchalitchi cha Roma Katolika chinaika tsikulo kuti likhale tsiku lachipembedzo lokumbukira kubadwa kwa Yesu. Koma malinga ndi kufufuza kwaposachedwapa kumene kunachitika ku United States, 33 peresenti okha mwa amene anafunsidwa ndiwo anati amaona kuti kubadwa kwa Kristu ndiko kofunika koposa pa Khirisimasi.

Inuyo mukuganizapo bwanji? Kodi nthaŵi zina mumafika poganiza kuti kusatsa malonda konseko, kugula mphatso kolimbirana, kukongoletsa mitengo, kukonzekera ndiponso kupita kumapwando, kutumiza makadi​—kwamchotsapo Yesu pachochitika chonsecho?

Ambiri akuoneka kuti amaganiza kuti njira ina yobwezeretsera Yesu pa Khirisimasi ndiyo mwa kukhala ndi chithunzi cha Kubadwa kwake. Muyenera kuti mwaonapo ziboliboli zimenezi, zosonyeza Yesu ali wakhanda modyera nyama ndipo Mariya, Yosefe, abusa angapo, “amuna atatu anzeru,” kapena kuti “mafumu atatu,” ng’ombe kapena abulu, ndi openyerera ena atamzungulira. Ambiri amati zithunzi zimenezi zimakumbutsa anthu za tanthauzo lenileni la Khirisimasi. Malinga ndi kunena kwa U.S. Catholic, “chithunzi cha Kubadwa kwa Yesu chimasimba bwino nkhani yonse kuposa zimene uthenga wabwino uliwonse ungasimbe pawokha, ngakhale kuti chimasonyezanso kuti zinthu zosimbidwa m’nkhani zimenezi sizinachitikedi.”

Koma kodi chithunzi cha Kubadwa kwa Yesu chingasonyeze motani kuti zinthu zosimbidwa m’nkhani za m’Mauthenga Abwino a Baibulo sizinachitike? Eya, ndi zoona kuti tiziboliboli topakidwa utoto mwaluso timapangitsa kubadwa kwa Kristu kuoneka ngati nthano wamba kapena nthanthi yosokeretsa. Chithunzi cha Kubadwa kwa Yesu, chimene chinatchukitsidwa ndi mmonke wina m’zaka za zana la 13, chinkasonyeza zenizeni pachiyambipo. Lerolino, mofanana ndi zinthu zina zambiri za paholide imeneyi, zithunzi za Kubadwa kwa Yesu zakhala malonda aakulu. Ku Naples, Italy, masitolo ambirimbiri amagulitsa zithunzi zosonyeza Kubadwa kwa Yesu, kapena kuti presepi, chaka chonse. Zina mwa zithunzi zotchuka kwambiri sizisonyeza anthu a m’nkhani za m’Mauthenga Abwino, koma anthu otchuka amakono, monga Princess Diana, Amayi Teresa, ndi wopanga zovala Gianni Versace. Kumalo ena, ma presepi amenewa amapangidwa ndi chokoleti, pasta, ngakhale zikamba za nkhono. Mutha kumvetsa chifukwa chake nkovuta kugwirizanitsa mbiri ndi zithunzi zimenezi.

Choncho ndi motani mmene zithunzi zosonyeza Kubadwa kwa Yesu zimenezo ‘zimasimbira bwino nkhani yonse kuposa zimene uthenga wabwino uliwonse ungasimbe pawokha’? Kodi nkhani za m’Mauthenga Abwino si zinthu zimene zinachitikadi? Ngakhale anthu amene amakayikira zedi amavomereza kuti Yesu analikodi. Ndiye kuti panthaŵi ina anakhalapo khanda lenileni, lobadwira pamalo ena enieni. Payenera kukhala njira yabwinopo yodziŵira zonse zimene zinachitika pakubadwa kwake kuposa kungoyang’ana pachithunzi cha Kubadwa kwakeko!

Ndipotu njirayo ilipo. Olemba mbiri aŵiri, aliyense payekha, analemba nkhani za kubadwa kwa Yesu. Ngati mukuona kuti Kristu samalingaliridwa nkomwe panthaŵi ya Khirisimasi, bwanji osapenda nkhani zimenezi panokha? M’nkhani zimenezo simudzapezamo nthano kapena nthanthi, koma nkhani yochititsa chidwi​—nkhani yake yeniyeni ya kubadwa kwa Kristu.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Mzere wa m’mbali mwa masamba 3-6, 8, ndi 9: Fifty Years of Soviet Art

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena