Kubadwa kwa Yesu Nkhani Yake Yeniyeni
TAGANIZANI za chochitika chotchuka m’mbiri ya dziko lanu. Nchotsimikizidwa bwino, chofotokozedwa ndi olemba mbiri yakale angapo. Tsopano, bwanji ngati wina atakuuzani kuti chinthu chimenechi sichinachitike, kuti ndi nthano wamba? Kapena, tinene zokukhudzani mwachindunji, bwanji ngati wina akunena kuti zambiri zimene a m’banja mwanu anakuuzani ponena za kubadwa kwa agogo anu ndi moyo wawo adakali mwana nzabodza? Ponse paŵiri, kungoyerekeza kutchula zimenezo kungakukwiyitseni. Kunena zoona simungavomereze zonenazo popanda kufufuza umboni wake.
Komabe, otsutsa ambiri lerolino amati nkhani za Mauthenga Abwino za kubadwa kwa Yesu zolembedwa ndi Mateyu ndi Luka nzabodza. Iwo amanena kuti nkhani zimenezi zimatsutsana kotheratu ndipo palibe mafotokozedwe ozigwirizanitsa ndi kutinso zonse ziŵiri ndi mabodza a mkunkhuniza ndiponso kupotoza mbiri yakale kwakukulu. Kodi zimenezo zingakhale zoona? M’malo mongovomereza mawuwo, tiyeni tidzipendere tokha Mauthenga Abwinowo. Potero, tiyeni tione zimene akutiphunzitsa lerolino.
Zolinga Zowalembera
Nkothandiza kukumbukira kaye cholinga cha nkhani za m’Baibulozi. Sizili mbiri wamba za munthu; ndi Mauthenga Abwino. Kusiyanaku nkofunika kwambiri. Polemba mbiri ya munthu, wolembayo angadzaze masamba mazana ambiri, pofuna kusonyeza mmene munthu amene akumsimbayo anadzakhalira munthu wotchuka chotero. Ndiye chifukwa chake mabuku ena osimba mbiri ya munthu amakhala ndi masamba ambirimbiri ofotokoza mwatsatanetsatane makolo a anthu amene akuwasimbawo, kubadwa kwake, ndi ubwana wake. Si mmene Mauthenga Abwino alili. Pa Mauthenga Abwino anayiwo, Mateyu ndi Luka ndiwo okha amene amanena za kubadwa kwa Yesu ndi ubwana wake. Koma cholinga chawo sindicho kusonyeza mmene Yesu anafikira pokhala mmene analili. Kumbukirani kuti otsatira a Yesu ankadziŵa kuti iye analiko monga cholengedwa chauzimu asanadze padziko lapansi. (Yohane 8:23, 58) Choncho Mateyu ndi Luka sanalongosole za ubwana wa Yesu ncholinga chofotokoza mtundu wa munthu amene iye anadzakhala. M’malo mwake, iwo anasimba zochitika zimene zinagwirizana ndi cholinga cha Mauthenga awo Abwino.
Kodi cholinga chawo chowalemberacho chinali chiyani? Amuna aŵiriwo uthenga wawo unali umodzimodzi—wakuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwayo, kapena kuti Kristu; kuti anafera machimo a mtundu wa anthu; ndi kuti anaukitsidwira kumwamba. Koma olemba aŵiriwo anali anthu osiyana kwambiri ndipo mbiriyo anailembera anthu osiyana. Mateyu, wamisonkho, nkhani yake anailembera Ayuda makamaka. Luka, sing’anga, anailembera “Teofilo wabwinotu”—amene ayenera kuti anali ndi malo audindo—ndiponso, monga opezerapo mwayi, Ayuda ndi Akunja ambirimbiri. (Luka 1:1-3) Wolemba aliyense anasankha zochitika zimene zinali zofunika kwambiri kwa anthu amene anali kuwalemberawo ndiponso zokhoza kuwakhutiritsa. Ndiye chifukwa chake nkhani ya Mateyu imalankhula kwambiri za maulosi a m’Malemba Achihebri onena za Yesu amene anakwaniritsidwa. Koma Luka anangoilemba monga mbiri yeniyeni imene anthu osakhala Ayuda, amene anali kuwalemberawo, anaizindikira.
Ndiye nzosadabwitsa kuti nkhani zawo zikusiyana. Koma nkhani ziŵirizo sizikutsutsana, monga momwe otsutsa amanenera. Izo zimachirikizana, kukwaniritsana bwino ndi kupereka chithunzi chokwanira bwino.
Kubadwa kwa Yesu m’Betelehemu
Onse aŵiri Mateyu ndi Luka analemba za chozizwitsa chapadera chokhudza kubadwa kwa Yesu—anabadwa kwa namwali. Mateyu akusonyeza kuti chozizwitsa chimenechi chinakwaniritsa ulosi umene unaperekedwa zaka mazana ambiri kalelo ndi Yesaya. (Yesaya 7:14; Mateyu 1:22, 23) Luka akufotokoza kuti Yesu anabadwira ku Betelehemu chifukwa chakuti kaundula amene Kaisara anayambitsa anakakamiza Yosefe ndi Mariya kupita kumeneko. (Onani bokosi patsamba 7.) Zimenezo zinali zochititsa chidwi kuti Yesu anabadwira ku Betelehemu. Zaka mazana ambiri zimenezi zisanachitike, mneneri Mika anali ataneneratu kuti Mesiya adzachokera m’mudzi wosatchuka umenewu woyandikana ndi Yerusalemu.—Mika 5:2.
Usiku wa kubadwa kwa Yesu ndiwo wakhala maziko a zithunzi zambiri zosonyeza Kubadwa kwake. Komabe, nkhani yake yeniyeni njosiyana kwambiri ndi imene nthaŵi zambiri imasonyezedwa. Wolemba mbiri Luka, amene akutiuza za kaundula amene anapangitsa Yosefe ndi Mariya kubwera ku Betelehemu, akutiuzanso za abusa amene anali kunja ndi nyama zawo usiku wofunikawo. Zochitika ziŵirizi zachititsa ofufuza Baibulo ambiri kufika pamfundo yakuti Yesu sanabadwe m’December. Iwo amanena kuti sizikanatheka kuti Kaisara nkukakamiza Ayuda a mtima wapachalawo kuti apite kumidzi yakwawo m’nyengo yozizira ndiponso yamvula, zimene zikanakwiyitsiratu anthu opandukawo. Akatswiri a zamaphunziro amanena kuti sizikanathekanso kuti abusa nkukhala kutchire ndi nyama zawo m’nyengo yovuta imeneyo.—Luka 2:8-14.
Taonani kuti Yehova sanasankhe kuuza atsogoleri achipembedzo ophunzirawo ndiponso achisonkhezero champhamvu a m’tsikulo za kubadwa kwa Mwana wake koma anasankha antchito osauka amene anali kutchire. Alembi ndi Afarisi sanali kuwaŵerengera abusa, amene ntchito yawo inawapangitsa kusasunga mbali zina za chilamulo cha pakamwa. Koma Mulungu anawasonyeza ulemu waukulu amuna odzichepetsa ndiponso okhulupirika amenewa—angelo otumidwa anawauza kuti Mesiya, amene anthu a Mulungu anali kumyembekeza kwa zaka zikwi zambiri, wangobadwa kumene ku Betelehemu. Ndi amuna amenewa, osati “mafumu atatu” amene zithunzi zambiri za Kubadwa kwa Yesu zimasonyeza, amene anapita kwa Mariya ndi Yosefe naona khanda losadziŵa kanthulo litagona modyera nyama.—Luka 2:15-20.
Yehova Amayanja Anthu Odzichepetsa Ofunafuna Choonadi
Mulungu amayanja anthu odzichepetsa amene amamkonda ndipo alidi nchidwi choona zolinga zake zikukwaniritsidwa. Ndiyo mfundo imene zochitika zokhudzana ndi kubadwa kwa Yesu zikusonyeza mobwerezabwereza. Pamene, patapita ngati mwezi mwanayo atabadwa, Yosefe ndi Mariya akumsonyeza ku kachisi motsatira Chilamulo cha Mose, iwo akupereka nsembe kumeneko ya “njiwa ziŵiri, kapena maunda aŵiri.” (Luka 2:22-24) Kwenikweni, Chilamulo chinkafuna nkhosa yaimuna, koma chinalolanso kupereka zinthu zotsika mtengozi ngati munthu anali waumphaŵi. (Levitiko 12:1-8) Tangolingalirani. Yehova Mulungu, Mfumu ya chilengedwe chonse, anasankha banja losauka, osati lachuma, loti Mwana wake wokondedwa, wobadwa yekha akakuliremo. Ngati ndinu kholo, zimenezi ziyenera kukhala chikumbutso chabwino kwambiri chakuti mphatso yabwino kwambiri imene mungapatse ana anu—yoposatu chuma chakuthupi kapena maphunziro onyaditsa—ndiyo mkhalidwe wapanyumba woika zinthu zauzimu patsogolo.
Kukachisi, olambira enanso aŵiri okhulupirika ndiponso odzichepetsa akuyanjidwa ndi Yehova. Mmodzi ndiye Anna, mkazi wamasiye wazaka 84 zakubadwa amene “sanachoka ku Kachisi.” (Luka 2:36, 37) Wina ndi mwamuna wokhulupirika wachikulire wotchedwa Simeoni. Onse aŵiri akusangalala kwambiri ndi mwayi umene Mulungu wawapatsa—kuona amene adzakhala Mesiya wolonjezedwayo iwo asanafe. Simeoni alankhula ulosi wokhudza mwanayo. Uli ulosi wodzaza chiyembekezo komanso wachisoni. Iye akuneneratu kuti mayi wachitsikana ameneyu, Mariya, tsiku lina adzapyozedwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wake wokondedwayo.—Luka 2:25-35.
Mwanayo Akhala Pangozi
Ulosi wa Simeoni nchikumbutso chomvetsa chisoni chakuti mwana wopanda mlanduyu adzadedwa. Ngakhale adakali wakhanda, chidani chimenechi chinali chitayamba kale. Nkhani ya Mateyu imafotokoza mwatsatanetsatane mmene zinalili. Papita miyezi ingapo tsopano, ndipo Yosefe, Mariya, ndi Yesu akukhalano panyumba ina m’Betelehemu. Iwo, mosayembekezereka, akulandira alendo angapo ochokera kunja. Mosasamala kanthu za zimene zithunzi zosonyeza Kubadwa kwa Yesu zimaonetsa, Mateyu sakutchula chiŵerengero cha anthu anabwerawa, ndiponso sakuwatcha kuti “amuna anzeru,” ngakhalenso “mafumu atatu.” Iye akugwiritsa ntchito liwu lachigiriki lakuti maʹgoi, lotanthauza “openda nyenyezi.” Mfundo yokhayi iyenera kupangitsa woŵerenga kudziŵa kuti china chake choipa chili kuchitika pamenepa popeza Mawu a Mulungu amaletsa kupenda nyenyezi ndipo Ayuda okhulupirika anakupeŵeratu.—Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 47:13, 14.
Openda nyenyeziwa atsatira nyenyezi kuchokera kummaŵa ndipo ali ndi mphatso za “amene anabadwa Mfumu ya Ayuda.” (Mateyu 2:2) Koma nyenyeziyo siikuwatsogolera ku Betelehemu. Ikuwapereka ku Yerusalemu kwa Herode Wamkulu. Munthuyu ndiye akanatha kupha Yesu wamng’onoyo mosavuta ndipo analidi ndi cholinga chomwecho. Munthu wopondereza ndiponso wakupha ameneyu anali atapha kale achibale ake enieni angapo amene anawaona ngati omsoŵetsa mtendere.a Povutika maganizo atamva za kubadwa kwa “Mfumu ya Ayuda” yam’tsogolo, akutumiza openda nyenyeziwo kuti akampeze Ameneyo ku Betelehemu. Pamene akuyenda, chinachake chachilendo chikuchitika. “Nyenyezi” imene inawatsogolera kupita ku Yerusalemu ikuoneka kuti ikuyenda!—Mateyu 2:1-9, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.
Tsopano, kaya kumeneku kunali kuunika kwenikweni kwamumlengalenga kapena anali masomphenya, sitikudziŵa. Koma tikudziŵa kuti “nyenyezi” imeneyi sinali ya Mulungu. Mosaphonya pokhala ncholinga choipa, ikutsogolera olambira achikunja amenewa pamalo enieni pamene anali Yesu—mwana wopanda chitetezo chenicheni, wotetezedwa ndi munthu wamba wopala matabwa ndi mkazi wake basi. Openda nyenyeziwo, osadziŵa kuti Herode akuwagwiritsa ntchito, akanabwerera kwa wolamulira wachiwembuyo, zimene zikanaphetsa mwanayo. Koma Mulungu akuloŵererapo m’maloto nawayendetsa njira ina pobwerera kwawo. Ndiye kuti “nyenyezi” ija iyenera kuti inali chiŵiya cha Satana mdani wa Mulungu, amene akanayesetsa njira zonse kuti awononge Mesiya. Nzodabwitsa chotani nanga kuti “nyenyeziyo” ndi openda nyenyeziwo amasonyezedwa monga nthumwi za Mulungu pazithunzi za Kubadwa kwa Yesu!—Mateyu 2:9-12.
Koma Satana sakulekera pomwepo. Mtumiki wake pa nkhaniyo, Mfumu Herode, akulamula kuti makanda onse m’Betelehemu azaka zosakwanira ziŵiri aphedwe. Koma Satana sangapambane nkhondo ndi Yehova. Mateyu akusonyeza kuti Mulungu anali ataoneratu kale ngakhale nkhanza ya kupha ana osadziŵa kanthu imeneyi. Yehova anampambananso Satana, nachenjeza Yosefe kudzera mwa mngelo kuti athaŵire kuchisungiko ku Igupto. Mateyu akusimba kuti patapita nthaŵi Yosefe anasamutsanso banja lake laling’onolo nakhazikika ku Nazarete pomalizira pake, kumene Yesu ndi aphwake ndi alongo ake aang’ono anakulira.—Mateyu 2:13-23; 13:55, 56.
Kubadwa kwa Kristu—Tanthauzo Lake kwa Inu
Kodi mukudabwa ndi chidulechi cha zinthu zimene zinachitika panthaŵi ya kubadwa kwa Yesu ndiponso pamene anali wamng’ono kwambiri? Ambiri amadabwa. Amadabwa kuona kuti kwenikweni nkhanizo zimagwirizana ndipo nzolondola, ngakhale kuti anthu ena mwaliuma amati zikutsutsana. Amadabwa kumva kuti zochitika zina zinanenedweratu zaka mazana ambiri pasadakhale. Ndiponso amadabwa kuti mfundo zina zofunika za m’Mauthenga Abwino zimasiyana kwambiri ndi zimene zimasimbidwa m’nthano zanthaŵi zonse za Kubadwa kwa Yesu ndi zimene zithunzi zimasonyeza.
Ngakhale zili choncho, mwinamwake chodabwitsa kwambiri pa zonsezi nchakuti mapwando a nthaŵi zonse a Khirisimasi kwakukulukulu amasiya mfundo zofunika za nkhani za m’Mauthenga Abwino. Mwachitsanzo, samaganizapo kwenikweni za Atate wake wa Yesu—osati Yosefe, koma Yehova Mulungu. Tangolingalirani mmene anamvera poikiza Mwana wake wokondedwa m’manja mwa Yosefe ndi Mariya kuti amlere ndi kumsamalira. Tangolingalirani kupwetekedwa mtima kwa Atate wake polola Mwana wake kukulira m’dziko limene mfumu yaudani imene inali kudzampangira chiwembu chomupha ngakhale adakali mwana wamng’ono! Chikondi chachikulu pa mtundu wa anthu ndicho chinasonkhezera Yehova kuti achite kudzimana kotere.—Yohane 3:16.
Nthaŵi zambiri Yesu weniweni amanyalanyazidwa pamapwando a Khirisimasi. Eyatu, palibe paliponse polembedwa kuti ophunzira ake anawauzapo tsiku lake la kubadwa; ndiponso palibe chilichonse chosonyeza kuti otsatira ake ankakondwerera tsiku la kubadwa kwake.
Si kubadwa kwa Yesu koma kufa kwake—ndi kufunika kwake kopanga mbiri—kumene analamula otsatira ake kukumbukira. (Luka 22:19, 20) Ayi ndithu, Yesu sanafune kuti azikumbukidwa monga khanda lopanda chitetezo limene lili modyera nyama, popeza si mmene alili tsopano. Patapita zaka 60 kuchokera pamene anaphedwa, Yesu anadzivumbula m’masomphenya kwa mtumwi Yohane monga Mfumu yamphamvu imene yakwera kavalo kuloŵa m’nkhondo. (Chivumbulutso 19:11-16) Lerolino, tiyenera kudziŵa Yesu pamalo amenewo, monga Wolamulira wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu, popeza ndiyo Mfumu imene idzasintha dziko lapansi.
[Mawu a M’munsi]
a Ndipo Kaisara Augusto anati kunali bwino kukhala nkhumba ya Herode kuposa kukhala mwana wamwamuna wa Herode.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]
Kodi Luka Analakwitsa?
KODI zikanatheka bwanji kuti Yesu, amene anakulira ku Nazarete ndipo wodziŵika ndi onse kuti Mnazara, abadwire ku Betelehemu, ulendo wa makilomita 150? Luka akufotokoza kuti: “Ndipo kunali masiku aja [Yesu asanabadwe], kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe; ndiko kulembera koyamba pokhala Kureniyo kazembe wa Suriya. Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumudzi wake.”—Luka 1:1; 2:1-3.
Otsutsa ambiri amati ndime imeneyi njolakwika kwambiri, kapenanso kuti njopeka. Iwo amalimbikira kunena kuti kuŵerenga anthu kumeneku ndi ukazembe wa Kureniyo zinaliko mu 6 kapena 7 C.E. Ngati ngolondola, zimenezi zingatipangitse kuikayikira kwambiri nkhani ya Luka, popeza umboni ukusonyeza kuti Yesu anabadwa mu 2 B.C.E. Koma otsutsa amenewa akunyalanyaza mfundo ziŵiri zofunika. Mfundo yoyamba, Luka akuvomereza kuti kuŵerenga anthu kumeneku sikunachitike kamodzi—onani kuti akunena kuti “ndiko kulembera koyamba.” Anali kudziŵa kuti kulembera kwina kunachitikanso pambuyo pake. (Machitidwe 5:37) Kulembera kotsatira kumeneku nkumene wolemba mbiri Josephus anafotokoza, kumene kunachitika mu 6 C.E. Mfundo yachiŵiri, ukazembe wa Kureniyo sukutikakamiza kunena kuti Yesu anabadwa panthaŵiyo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Kureniyo, malinga ndi umboni umene ulipo, anatumikira paudindo umenewo kaŵiri. Akatswiri ambiri a maphunziro amanena kuti nthaŵi yoyamba imene anatumikira inali cha mu 2 B.C.E.
Otsutsa ena amanena kuti Luka anangopeka za kuŵerenga anthu kumeneko pofuna kupeka chifukwa chonenera kuti Yesu anabadwira ku Betelehemu, ndi kukwaniritsa ulosi wa pa Mika 5:2. Mafotokozedwe amenewa angapangitse Luka kukhala wabodza lamkunkhuniza, ndipo palibe wotsutsa aliyense amene anganene kuti wolemba mbiri wosamala kwambiri amene analemba Uthenga Wabwinowo ndi buku la Machitidwe analidi wotero.
Chinachakenso chimene wotsutsa aliyense sangachilongosole: Kuŵerenga anthu kwenikweniko kunakwaniritsa ulosi wina! M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., Danieli analosera za wolamulira amene ‘adzapititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo.’ Kodi zimenezi zinagwirizana ndi Augusto ndi lamulo lake loti pakhale kuŵerenga anthu m’Israyeli? Eya, ulosiwo unapitiriza kuneneratu kuti Mesiya, kapena kuti “kalonga . . . wa chipangano,” ‘adzatyoledwa’ mu ulamuliro wa wolamulira wotsatira. Ndithudi Yesu ‘anatyoledwa,’ kuphedwa, mu ulamuliro wa Tiberiyo, woloŵa m’malo mwa Augusto.—Danieli 11:20-22.
[Zithunzi]
Kaisara Augusto (27 B.C.E.–14 C.E.)
Tiberiyo Kaisara (14-37 C.E.)
[Mawu a Chithunzi]
Musée de Normandie, Caen, France
Chithunzi chotengedwa mwachilolezo cha British Museum
[Chithunzi patsamba 8]
Mngelo wa Yehova anayanja abusa odzichepetsa mwa kuwapatsa uthenga wabwino wonena za kubadwa kwa Kristu