Otsimikiza Mtima Kutsatira Njira ya Moyo ya Mulungu
Misonkhano Yachigawo ya “Njira ya Moyo ya Mulungu” inali ndi zabwino zambiri kwa awo ofuna kutumikira Mulungu! Nthumwi ina inanena kuti msonkhanowo unali “nthaŵi yosangalatsa ya kulangizidwa, kulimbikitsidwa, ndi kuunikiridwa.”
WINANSO anati “panali zambiri zosangalatsa, zozisinkhasinkha, ndi zoloŵetsa mumtima.” Tsopano tiyeni tipende pologalamu imeneyo.
Yesu Kristu—Njira, Choonadi, ndi Moyo
Umenewu ndiwo unali mutu wa tsiku loyamba la msonkhanowo. (Yohane 14:6) Nkhani yoyamba inalongosola cholinga cha kusonkhana kwathu pamsonkhanowo: kuti tiphunzitsidwe zowonjezeka ponena za njira yabwino koposa ya moyo imene ilipo, njira ya moyo ya Mulungu. Yehova amaphunzitsa anthu ake mmene angayendere m’njira zake. Amatero kudzera m’Baibulo, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndi mzimu woyera. (Mateyu 24:45-47; Luka 4:1; 2 Timoteo 3:16) Ndi mwayitu waukulu kwambiri kulangizidwa ndi Mfumu ya chilengedwe chonse!
Mogwirizana ndi mutu wa tsikulo, nkhani yaikulu inali yakuti “Dipo la Kristu—Njira ya Mulungu ya Chipulumutso.” Ngati tikufuna kutsatira njira ya moyo ya Mulungu, n’kofunika kuti tizindikire ntchito ya Yesu Kristu pazolinga za Yehova. Wokamba nkhaniyo anati: “Popanda nsembe ya dipo la Yesu Kristu, kulibe munthu, kaya akhale ndi zikhulupiriro zotani kapena ntchito zotani, amene angalandire moyo wosatha kuchokera kwa Mulungu.” Ndiyeno anagwira mawu Yohane 3:16, amene amati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Kusonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Kristu kumafuna kuti tikhale ndi chidziŵitso cholongosoka cha choonadi. Kumaloŵetsaponso kupatulira miyoyo yathu kwa Yehova, kusonyeza kuti tatero mwa ubatizo wa m’madzi, ndi kumatsatira chitsanzo chimene Yesu Kristu anapereka.—1 Petro 2:21.
Chigawo chamasana chinayamba ndi nkhani ya mutu wakuti “Chikondi Sichitha.” Imeneyi inaphatikizapo kulongosola vesi lililonse la mafotokozedwe a Paulo ogwira mtima a chikondi, olembedwa pa 1 Akorinto 13:4-8. Omvera anakumbutsidwa kuti chikondi chodzimana n’chimene chimadziŵikitsa Chikristu ndi kuti kukonda Mulungu ndi mnansi kuli mbali zofunika za kulambira kumene Yehova amavomereza.
Kenako panatsatira nkhani yosiyirana ya mbali zitatu ya mutu wakuti “Makolo—Phunzitsani Ana Anu Njira ya Mulungu.” Makolo angathandize ana awo kutumikira Mulungu mwa kupereka chitsanzo chabwino cha kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu ake. Atha kuphunzitsa ana awo choonadi mwa phunziro la banja lokhazikika, kulichita mogwirizana ndi zosoŵa za banjalo. N’kofunikanso kuthandiza ana kuti azichita nawo ntchito za mumpingo ndi utumiki wakumunda. Ngakhale kuti kulera ana kuti aziopa Mulungu m’dziko loipali n’kovuta, kukuchita kumadzetsa madalitso aakulu kwambiri.
Itatha nkhani yosiyiranayi panatsatira nkhani yakuti “Lolani Yehova Kukuumbani Kaamba ka Ntchito Yopereka Ulemu.” Monga momwe woumba mitsuko amaumbira mtsuko wadothi, Mulungu amaumbanso awo amene amafuna kumtumikira. (Aroma 9:20, 21) Amachita zimenezi mwa kupereka uphungu m’Mawu ake ndiponso kudzera mwa gulu lake. Yehova adzatithandiza kugwiritsa ntchito maluso athu onse ngati tidzipereka, kuchitapo kanthu pakapezeka mpata, ndiponso ngati timlola kutsogoza mapazi athu.
Ndiyeno panatsatira mbali yosangalatsa ya pologalamu imeneyo—“Kutumikira m’Munda wa Amishonale.” Panopo, pali atumiki achikristu 2,390 amene akutumikira monga amishonale m’mayiko 148 padziko lonse lapansi. Iwo akupereka chitsanzo chabwino cha kukhulupirika ndi changu ndipo amaikonda kwambiri ntchito yawo yotumikira m’minda ya mayiko ena. M’nkhani imeneyi ya pologalamuyi pamisonkhano ya mitundu yonse, amishonale anasimba za zovuta ndiponso zinthu zosangalatsa za moyo waumishonale.
Nkhani yomaliza patsiku loyambalo inali ndi mutu wakuti “Kodi Kuli Moyo Pambuyo pa Imfa?” Funso limeneli lazunguza anthu kwa zaka zosaŵerengeka. Anthu kulikonse ayesetsa kuifotokoza nkhaniyi. Pali mayankho ambirimbiri amene amawayesa olondola. Mayankhowo n’ngosiyanasiyana malinga ndi miyambo ndi zipembedzo za anthu amene amawapereka. Koma anthu afunikabe kuphunzira choonadi.
Kenako, wokamba nkhaniyo analengeza kutulutsidwa kwa bolosha lokongola lamasamba 32 lakuti What Happens to Us When We Die? (Kodi N’chiyani Chimachitika kwa Ife Tikamwalira?) Bolosha limeneli likufotokoza chiyambi cha chiphunzitso chakuti munthu ali ndi mbali inayake imene sifa ndipo likusonyeza mmene lingaliro limenelo lakhalira lofunika kwambiri pafupifupi m’zipembedzo zonse padziko lapansi lerolino. M’njira yomveka ndiponso yosangalatsa, likulongosola zimene Baibulo limanena ponena za chifukwa chake timafa, ndi zimene zimachitika kwa ife tikamwalira. Boloshalo likufotokozanso chiyembekezo chimene chilipo kwa akufa ndi amoyo. Chofalitsa chimenechi chidzakhala dalitso lalikulu kwambiri kwa ofunafuna choonadi kulikonse!
Penyani Bwino Umo Muyendera
Umenewu unali mutu woyenerera kwambiri wa tsiku lachiŵiri la msonkhano! (Aefeso 5:15) Pologalamu ya mmaŵa inafotokoza kwambiri za ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. Makambirano a lemba latsiku atatha, pologalamu inapitiriza ndi nkhani yakuti “Kuthandiza Anthu Kuyenda m’Njira Yopatsa Moyo.” Pochita ntchito yofuna changu imeneyi, n’kofunika kukhala ndi maganizo abwino, kuzindikira kuti kugaŵira ena choonadi ndi mwayi ndiponso udindo. M’zaka za zana loyamba C.E., anthu ambiri anakana Mawu a Mulungu. Koma mosasamala kanthu za chitsutsocho, panali awo ‘ofuna moyo wosatha amene anakhala okhulupirira.’ (Machitidwe 13:48, 50, NW; 14:1-5) Ndi mmenenso zilili lerolino. Ngakhale kuti ambiri amakana choonadi cha Baibulo, tikupitirizabe kufunafuna anthu amene adzamvetsera ndi kuchitapo kanthu.—Mateyu 10:11-13.
Nkhani yotsatira inalongosola za ntchito yovuta ya kufikira ena ndi uthenga wa moyo. Popeza kuti tsopano kupeza anthu panyumba n’kovuta kwambiri, tiyenera kumayesetsa ndi kukhala akhama kuti tifikire anthu ambiri ndi uthenga wa Ufumu. M’mayiko ambiri, ofalitsa a uthenga wabwino amakhala ndi zotsatirapo zabwino mwa umboni wa patelefoni ndiponso mwa kulalikira m’magawo amalonda, motero akumafikira aja amene sapezekapezeka.
Nkhani ya mutu wakuti “Kuphunzitsa Ophunzira Zinthu Zonse Zimene Yesu Analamulira” inalongosola kwambiri za kufunika kwa kukhala aluso mu utumiki wathu. Maluso athu a kuphunzitsa amawonjezeka pamene tiphunzira kwa ena ndi kugwiritsa ntchito maphunziro abwino kwambiri amene timalandira pamisonkhano yachikristu. Pamene tikhala aphunzitsi aluso, timapeza chimwemwe ndi chikhutiro chowonjezeka pantchito yathu yothandiza anthu kuphunzira choonadi cha Baibulo.
Chigawo cha mmaŵa chinatha ndi nkhani yofotokoza tanthauzo la kudzipatulira ndi ubatizo. Imodzi mwa mfundo zimene wokamba nkhaniyo anafotokoza inali yakuti ngati tikhulupirira Mulungu kotheratu ndi kuyesetsa kuchita chifuniro chake ndi mtima wonse, adzatidalitsa ndi kutichirikiza. Mwamuna wanzeru analemba kuti: “Umlemekeze [Mulungu] m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:6) Ubatizo wosangalatsa umenewo unali chochitika chachikulu pa msonkhanowo chosonyeza kuti ambiri anayamba kutsatira njira ya moyo ya Mulungu.
Pambuyo pa chakudya chamasana, chigawo chamasana chinayamba ndi nkhani yakuti “Kutumikira ndi Chiyembekezo cha Moyo Wosatha.” Cholinga cha Mulungu chakuti anthu omvera amtumikire kosatha padziko lapansi chidzakwaniritsidwa. Ndiye chifukwa chake n’koyenereradi kusumika maganizo athu, zolinga, ndi ziyembekezo zathu pa kutumikira Yehova kosatha! Ngakhale kuti tiyenera kukumbukirabe ‘tsiku la Yehova,’ n’kofunika kwambiri kukumbukira kuti cholinga chathu ndicho kutumikira kwamuyaya. (2 Petro 3:12) Kusadziŵa nthaŵi yeniyeni imene Yesu adzapereka chiweruzo cha Mulungu kumatipangitsa kukhalabe atcheru ndipo masiku onse kumatipatsa mwayi wopereka umboni wakuti Yehova sitikumtumikira ndi zolinga zadyera.
Nkhani ziŵiri zimene zinatsatira zinalongosola chaputala chachinayi cha kalata ya Paulo kwa Aefeso. Chimodzi mwa zinthu zimene zinafotokozedwa ndicho madalitso amene tili nawo mu “mphatso mwa amuna,” amuna oyeneretsedwa mwauzimu amene amaikidwa ndi mzimu woyera. Akulu amenewa amapereka uphungu ndi chitsogozo kuti tipindule mwauzimu. Kalata youziridwa ya Paulo imalimbikitsanso Akristu kuvala “umunthu watsopano.” (Aefeso 4:8, 24, NW) Umunthu waumulungu umakhala ndi mikhalidwe monga chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima, ndi chikondi.—Akolose 3:12-14.
Kupenya bwino umo tiyendera kumafuna kuti tikhalebe osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi—imene inali nkhani yotsatira. Pamafunika kusamala posankha zosangulutsa, zochita zatsiku ndi tsiku, ndi zinthu zakuthupi zimene tikulondola. Mwa kugwiritsa ntchito uphungu wa pa Yakobo 1:27 wakuti tikhale osachitidwa maŵanga ndi dziko, timakhala ndi kaimidwe kabwino pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chabwino. Tingakhalenso ndi moyo watanthauzo ndipo tidzadalitsidwa ndi mtendere, kulemerera kwauzimu, ndi mayanjano abwino kwambiri.
Ndiyeno panatsatira nkhani yosiyirana ya mbali zitatu yamutu wakuti “Achinyamata—Tsatirani Njira ya Mulungu.” Podziŵa kuti Mulungu amawakonda ndipo amayamikira zoyesayesa zawo pochirikiza kulambira koyera, achinyamata ayenera kuphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kuti am’tumikire mokhulupirika. Njira imodzi yokhalira ndi mphamvu za kuzindikira ndiyo kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku. Ngati tichita zimenezi, tingadziŵe njira za Yehova. (Salmo 119:9-11) Munthu amakhalanso ndi mphamvu za kuzindikira mwa kulandira uphungu wauchikulire wochokera kwa makolo, akulu, ndi m’zofalitsa za Sosaite. Mwa kugwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo za kuzindikira, achinyamata amapeŵa kutanganidwa ndi kufunafuna chuma, kalankhulidwe koipa, ndi zosangulutsa zopambanitsa zimene zadzaza dzikoli lotayana ndi Mulungu. Mwa kutsatira njira ya moyo ya Mulungu, achinyamata ndi akulu omwe angakhale ndi chipambano chenicheni.
Nkhani yomaliza tsikulo inali yakuti “Mlengi—Umunthu Wake ndi Njira Zake.” Atafotokoza kuti miyandamiyanda ya anthu padziko lapansi sam’dziŵa Mlengi, wokamba nkhaniyo anati: “Moyo umakhala watanthauzodi pamene tidziŵa Mlengi, Mulungu wathu; pamene tizindikira umunthu wake; ndiponso pamene tichita mogwirizana ndi njira zake. . . . Pali mfundo zokhudza dziko lathu lapansili ndiponso zokhudza ifeyo zomwe mungagwiritsire ntchito pothandiza anthu kuti avomereze kuti Mlengi alipo ndi kupeza tanthauzo la kukhalapo kwake.” Ndiyeno wokamba nkhaniyo analongosola umboni wosonyeza kuti kuli Mlengi wanzeru ndiponso wachikondi. Nkhaniyo inafika pachimake ndi kutulutsidwa kwa buku latsopano—Is There a Creator Who Cares About You? (Kodi Kuli Mlengi Yemwe Amasamala za Inu?)
“Njira Ndi Iyi, Yendani Inu Mmenemo”
Umenewu ndiwo unali mutu wa tsiku lachitatu la msonkhanowo. (Yesaya 30:21) Pologalamu inayamba ndi nkhani yosiyirana ya mbali zitatu yochititsa chidwi, yonena za masomphenya a Ezekieli a kachisi. Masomphenya amenewa akutanthauza zambiri kwa anthu a Mulungu lerolino, popeza akukhudza kulambira koyera kwa m’nthaŵi yathu. Kuti timvetse masomphenyawa, nayi mfundo yake: Kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova amaimira makonzedwe ake a kulambira koyera. Pamene zinthu za m’masomphenyawo zinali kulongosoledwa, omvera anasinkhasinkha za ntchito yawo yochirikiza ntchito yochitidwa ndi oyang’anira achikondi a m’gulu la otsalira odzozedwa ndi ya oyembekezera kukhala m’gulu la akalonga.
Pambuyo pake mmaŵa womwewo, kunali seŵero lokongola la m’Baibulo limene oseŵera ake anavala zovala za nthaŵi zakale. Seŵerolo linali ndi mutu wakuti “Mabanja—Pangani Kuŵerenga Baibulo kwa Tsiku ndi Tsiku Kukhala Chizoloŵezi Chanu!” Linasonyeza chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwa Ahebri atatu amene anakana kugwadira fano lagolidi limene Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inaimika. Cholinga cha seŵerolo chinali kusonyeza kuti Baibulo si buku la mbiri yamakedzana chabe koma uphungu wake n’ngwopindulitsadi kwa achinyamata ndi achikulire omwe lerolino.
Nkhani yapoyera yakuti “Njira Yokha ya Moyo Wosatha” inaliko m’chigawo chamasana. Atasimba mbiri ya mmene mtundu wa munthu unagwera mu uchimo ndi imfa, wokamba nkhani anamaliza ndi mawuwa ochititsa kuganizirapo: “Lemba la m’Baibulo la mutu walero ndi Yesaya chaputala 30, vesi 21, lomwe limati: ‘Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.’ Kodi mawu amenewa timawamva bwanji? Mwa kumvetsera Mawu a Mulungu, Baibulo Lopatulika, ndi mwa kutsata malangizo amene Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu, akupereka kudzera mwa iwo ndi mwa gulu lamakono lachikristu. Inde, kuchita zimenezi ndiko njira yokha ya moyo wosatha.”
Pambuyo pa chidule cha nkhani ya phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo panabwera nkhani yomaliza, yamutu wakuti “Pitirizani Kuyenda m’Njira ya Yehova.” Mbali yake ina inafotokoza mfundo zazikulu za pologalamuyo. Kenako wokamba nkhani anaŵerenga chosankha chosonyeza kutsimikiza mtima kwa osonkhana kwakuti adzapitirizabe kukhala ndi moyo m’njira ya Mulungu.
Chosankhacho chinamaliza ndi mawu ogwira mtimawa akuti: “Timakhulupirira kuti kukhala mogwirizana ndi mapulinsipulo, malangizo, ndi uphungu wa m’Malemba ndiyo njira yabwino koposa ya moyo lerolino ndipo kumayala maziko abwino a m’tsogolo, kuti tigwiritsitse moyo weniweniwo. Komanso chachikulu n’chakuti, tapanga chosankha chimenechi chifukwa chakuti timakonda Yehova Mulungu ndi mtima wathu wonse, ndi moyo wathu wonse, ndi nzeru zathu zonse, ndi mphamvu zathu zonse!” Onse amene analipo anamveketsa kuvomereza kwawo mwa kuyankha mofuula kuti akuvomereza!
[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]
Kodi Kuli Mlengi Yemwe Amasamala za Inu?
Buku latsopano lachingelezi la mutu umenewo likupereka umboni wothetsa makani wakuti Mlengi, Yehova, aliko, ndipo likufotokoza mikhalidwe yake. Kwenikweni, linakonzedwera anthu ophunzira kwambiri m’maphunziro akudziko koma amene sakhulupirira Mulungu. Buku lamasamba 192 limeneli lidzalimbitsanso chikhulupiriro cha anthu amene ndi kale amakhulupirira Mulungu, kuwonjezera chidziŵitso chawo cha umunthu wake ndi njira zake.
Buku la Is There a Creator Who Cares About You? silitenga woŵerenga monga kuti amakhulupirira Mulungu. M’malo mwake, likufotokoza mmene zinthu zimene asayansi apeza posachedwapa ndi malingaliro amene akhala nawo zimasonyezera kuti Mlengi aliko. Mwa machaputala ake pali ena akuti “What Can Add Meaning to Your Life?” (Kodi N’chiyani Chomwe Chingapangitse Moyo Wanu Kukhala Watanthauzo?), “How Did Our Universe Get Here?—The Controversy” (Kodi Thamboli Linakhalapo Motani?—Kusagwirizana Kumene Kulipo), ndi “How Unique You Are!” (Mulitu Wapadera Kwambiri!) Machaputala ena akulongosola chifukwa chimene tingakhalire otsimikiza kuti Baibulo n’louziridwa ndi Mulungu. Buku latsopanoli limafotokozanso mfundo zazikulu za m’Baibulo, zimene zimafotokoza umunthu ndi njira za Mlengi. Bukuli silingofotokoza chifukwa chimene Mulungu walolera kuvutika koma likufotokozanso mmene adzakuthetsera kosatha.
[Zithunzi patsamba 7]
Ambiri anabatizidwa
[Zithunzi patsamba 7]
Bolosha latsopanolo linatulutsidwa ndi A.D. Schroeder, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova
[Zithunzi pamasamba 8, 9]
Seŵero losangalatsa kwambiri linalimbikitsa kumaŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku