Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 1/15 tsamba 28-31
  • “Mfumukazi ya Tsitsi Lakuda ya m’Chipululu cha ku Suriya”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mfumukazi ya Tsitsi Lakuda ya m’Chipululu cha ku Suriya”
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mzinda wa Kumapeto kwa Chipululu
  • Zenobia Ayesetsa Kufutukula Ufumu
  • Mfumu ‘Iutsa Mtima Wake’ Kuyambana ndi Zenobia
  • Mzinda wa m’Chipululu Uwonongedwa
  • Mafumu Aŵiriwo Asintha
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Ku Syria Kumatikumbutsa Zinthu Zochititsa Chidwi Zamakedzana
    Galamukani!—2003
  • Mphamvu ya Dziko ya Chisanu ndi Chimodzi—Roma
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi “Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi ya Mapeto Ndi Ndani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 1/15 tsamba 28-31

“Mfumukazi ya Tsitsi Lakuda ya m’Chipululu cha ku Suriya”

MFUMUKAZI imeneyi inali yakuda, ya mano oyera kwambiri, ya maso akuda ndiponso onyezimira. Inali yophunzira kwambiri ndipo imadziŵa zilankhulo zochuluka. Mfumukazi imeneyi yomwe inalinso wankhondo amati inali yanzeru kwambiri kuposa Cleopatra koma mwina yokongola mofanana naye. Inakwaniritsa mbali ya ulosi wa zochitika za m’Malemba, chifukwa cholimba mtima kumenyana ndi ulamuliro wa dziko lonse wa m’nthaŵi yake. Ngakhale kuti inali itafa kalekale, olemba nkhani ankalembabe za iyo moitama, ndipo ojambula anali kuijambula mokongola kwambiri kuposa mmene inalili. Wolemba ndakatulo wina wa m’zaka za zana la 19 anati ndi “mfumukazi ya tsitsi lakuda ya m’chipululu cha ku Suriya.” Mkazi wotchuka ameneyu anali Zenobia​—mfumukazi ya mzinda wa ku Suriya wa Palmyra.

N’chifukwa chiyani Zenobia anali wotchuka? Kodi ndale zinali zotani kuti iye afike pa kulamulira? Tinganenepo chiyani pa zochita zake? Ndipo kodi ndi mbali ya ulosi uti umene mfumukazi imeneyi inakwaniritsa? Choyamba tione kumene kunachitikira zimenezi.

Mzinda wa Kumapeto kwa Chipululu

Mzinda umene Zenobia amakhala unali Palmyra. Unali pamtunda wa pafupifupi makilomita 210 kumpoto chakummawa kwa Damasiko, kumapeto kwa chipululu cha Suriya kumpoto kumene mapiri a Anti-Lebanon anatsikira kuchigwa. Mzinda wokhala ndi zitsime umenewu unali pakati pa Nyanja ya Mediterranean kumadzulo ndi Mtsinje wa Firate kummawa. Mfumu Solomo ankadziŵa mzindawu ndi dzina loti Tadimori, ndipo mudzi umenewu unali wofunika m’dziko lake pazifukwa ziŵiri: anali malo okhala asilikali oteteza malire akumpoto ndiponso anali malo ofunika kwambiri pakati pa mizinda ya anthu a paulendo. Choncho, Solomo “anamanga Tadimori m’chipululu.”​—2 Mbiri 8:4.

Mbiri ya zaka chikwi pambuyo pa kulamulira kwa Mfumu Solomo sinena chilichonse cha Tadimori. Ngati Tadimori ndiye Palmyra, kutchuka kwake kunayamba m’chaka cha 64 B.C.E. pamene Suriya anakhala dera la mu Ufumu wa Roma. “Palmyra anali wofunika ku Roma m’njira ziŵiri, m’zachuma ndi m’nkhondo,” akutero Richard Stoneman m’buku lake la Palmyra and Its Empire​—Zenobia’s Revolt Against Rome. Popeza mzinda wokhala ndi mitengo ya kanjedza umenewu unali wamalonda kwambiri unali njira ya ku Roma ndi ku Mesopotamiya ndiponso Kummawa. Inalinso njira yodutsa chuma cha dziko lakale​—zokometsera chakudya za ku East Indies, silika wa ku China, ndi katundu wina wa ku Perisiya, kuchigawo cha Mesopotamiya chakumunsi, ndi kumadera a Mediterraean. Roma ankadalira pa kugula katundu ameneyu woitanitsa kunja.

Pazankhondo, dera la Suriya linali ngati chotchinga pakati pa maulamuliro odana a Roma ndi Perisiya. Mtsinje wa Firate ndiwo unalekanitsa Roma ndi dziko loyandikana nalo la kummawa, m’zaka 250 zoyambirira za Nyengo Yathu. Mzinda wa Palmyra unali kumapeto kwa chipululu, kumadzulo kwa mzinda wa Dura-Europos ku mtsinje wa Firate. Poona za kufunika kwa malo amenewa, mafumu a Roma, Hadrian ndi Valerian, anapita ku Palmyra. Hadrian anamangako nyumba zabwino ndiponso anaperekako ndalama mooloŵa manja. Valerian anapereka mphatso kwa Odaenathus munthu wotchuka m’Palmyra​—mwamuna wa Zenobia​—mwa kumkweza kukhala nduna ya Roma m’chaka cha 258 C.E. chifukwa anagonjetsa Perisiya ndi kufutukula malire a Ufumu wa Roma kukafika ku Mesopotamiya. Zenobia ndiye amene anachita mbali yaikulu pa kukwezedwa kwa mwamuna wake. Wolemba mbiri Edward Gibbon analemba kuti: “Kupambana kwa Odenathus n’chifukwa cha nzeru ndi kulimba mtima kwa [Zenobia].”

Panthaŵi imeneyi, Mfumu Sapor ya ku Perisiya inaganiza zotsutsa mphamvu ya Roma ndi kukhazika ufumu wake kumadera akale onse a m’Perisiya. Iye ndi magulu oopsa ankhondo, anakamenya nkhondo kumadzulo, ndi kulanda matauni a asilikali a ku Roma a Nisibis ndi Carrhae (Harana), ndipo anapitiriza kuwononga kumpoto kwa Suriya ndi Kilikiya. Mfumu Valerian inatsogolera asilikali ake kukachita nkhondo koma inagonjetsedwa ndi kutengedwa ukapolo ndi Aperisi.

Tsopano Odaenathus anaganiza kuti n’nthaŵi yabwino yoti atumize mphatso zamtengo wapatali ndi uthenga wamtendere kwa mfumu ya Aperisi. Mfumu Sapor anakana monyada ndipo analamula kuti mphatsozo zikaponyedwe mu mtsinje wa Firate ndiponso kuti Odaenathus akaonekere kwa iye monga kapolo wopemphapempha. M’malo mwake, Apamirene anasonkhanitsa asilikali mwa anthu a m’chipululu ndi asilikali a Roma omwe anatsala nayamba kumenyana ndi Aperisi omwe anabwerera kwawo. Chifukwa cha khalidwe la asilikali la m’chipululu lomaukira nkumathaŵa, magulu a asilikali a Sapor​—pokhala atatopa nayo nkhondo ndi kufunkha​—analibe chitetezo chokwanira ndipo anathaŵa.

Chifukwa chogonjetsa Sapor, Odaenathus anapatsidwa dzina ndi mwana wamwamuna wa Valerian ndiponso woloŵa m’malo mwake, Gallienus, loti corrector totius Orientis (bwanamkubwa wa kummawa konse). M’kupita kwa nthaŵi, Odaenathus anadzipatsa dzina loti “mfumu ya mafumu.”

Zenobia Ayesetsa Kufutukula Ufumu

Mu chaka cha 267 C.E., pachimake pa ntchito yake, Odaenathus ndi woloŵa m’malo mwake anaphedwa, ndi mwana wa mbale wake wongoganiziridwa kuti ndiye anabwezera. Zenobia analoŵa m’malo a mwamuna wake, popeza mwana wake wamwamuna anali wamng’ono kwambiri. Zenobia anali wokongola, wofuna udindo, ndipo wokhoza kuyang’anira. Analinso wozoloŵera kugwira ntchito ndi mwamuna wake, ndipo anali kulankhula bwino zilankhulo zambiri. Chifukwa cha zimenezi iye anapeza ulemu ndi thandizo kwa nzika zake​—zinthu zosatheka pakati pa Abedowini. Zenobia anali wokonda kuphunzira ndipo ankakhala pamodzi ndi anthu ophunzira kwambiri. M’modzi wa aphungu ake anali Cassius Longinus, filosofa komanso wodziŵa kulankhula ndi kulemba​—yemwe ankatchedwa kuti “nkhokwe ya chidziŵitso.” Wolemba nkhani Stoneman ananena kuti: “Zaka zisanu kuchokera pamene Odenathus anamwalira . . . Zenobia ankadziŵika monga mfumukazi ya Kummawa.”

Kumbali ina ya ufumu wa Zenobia kunali Perisiya, dera lomwe iye ndi mwamuna wake analanda, kwinaku kunali Roma amenenso anali kuchepa mphamvu. Ponena za mmene zinthu zinaliri mu Ufumu wa Roma panthaŵiyo, wolemba mbiri J. M. Roberts anati: “M’zaka za zana lachitatu . . . zinthu zinali zovuta kwambiri kumalire a kummawa ndi kumadzulo kwa Roma, pamene ku Roma kwenikweniko nkhondo yachiweniweni ndi kulimbirana ufumu zinali zitayambikanso. Mafumu 22 (kuchotsapo odzinenera) anali atalamulira.” Kumbali ina, mfumukazi ya Suriya, inali yamphamvu kwambiri m’dera lake. “Pokhala pakati pa maufumu aŵiri [Perisiya ndi Roma], anali wokhoza kuyamba ufumu wina wachitatu umene ukanaposa onsewa,” anatero Stoneman.

M’chaka cha 269 C.E., inafika nthaŵi yoti Zenobia afutukule ulamuliro wake, pamene munthu wina wodzinenera kukhala mfumu ya Igupto anayamba kutsutsa ulamuliro wa Roma. Asilikali a Zenobia mofulumira anakamenya nkhondo ku Igupto, ndi kuwononga adaniwo, nalanda dzikolo. Podzidziŵikitsa kuti anali mfumukazi ya Igupto, iye anapanga ndalama yokhala ndi dzina lake. Ufumu wake tsopano unayambira ku Mtsinje wa Nile mpaka ku Mtsinje wa Firate. Nthaŵi imeneyi, iye ndiye anaimira “mfumu ya kumwera” yotchulidwa m’Baibulo mu ulosi wa Danieli, popeza ufumu wake panthaŵiyo unali kummwera kwa dziko la kwawo kwa Danieli. (Danieli 11:25, 26) Iye anagonjetsanso mbali yaikulu ya Asia Minor.

Zenobia analimbitsa chitetezo ndi kukongoletsa mzinda wake wa Palmyra, kotero kuti unali kufanana ndi mizinda ikuluikulu ya m’dziko la Roma. Unali ndi chiŵerengero cha anthu oposa 150,000. Munali zinthu zokongola monga nyumba, akachisi, minda, zipilala, ndi malo a zikumbutso, zimene anazimanga mkati mwa linga la makilomita 21. Msewu waukulu m’mzindawu unali ndi zipilala zakamangidwe ka Agirisi zokwanira pafupifupi 1,500 zautali wokwanira mamita 15. Mafano osonyeza munthu yense ndi osonyeza kumtunda kokha, a ngwazi ndiponso anthu olemera amene ankathandiza ena analinso m’mzindawu. Mu chaka cha 271 C.E., Zenobia anaimika mafano aŵiri, lake ndi la malemu mwamuna wake. Kumapeto kwa chipululu, Palmyra anali kuwala ngati mwala wamtengo wapatali.

Kachisi wa Dzuŵa anali imodzi mwa nyumba zokongola kwambiri m’Palmyra ndipo mosakayika inaposa malo ena achipembedzo a m’mzindawu. Ndithudi, Zenobia analinso kulambira mulungu dzuŵa. Koma m’zaka za zana lachitatu, Suriya anali ndi zipembedzo zochuluka. Kumene Zenobia amalamulira kunali odzitcha Akristu. Kunalinso Ayuda, openda nyenyezi, ndi olambira dzuŵa ndi mwezi. Kodi anali kuona motani njira zosiyanasiyana zolambirira zimenezi? Wolemba nkhani Stoneman anati: “Mfumu yanzeru siletsa mwambo ulionse umene anthu ake amaona kuti ndi wabwino. . . . Anali kukhulupirira kuti, . . . milungu inali kumbali ya Apamirene.” Mwachionekere, Zenobia sanali kutsutsa zipembedzo. Koma kodi milungu inalidi “kumbali ya Palmyra”? Nchiyani chinali kudzachitika kwa Palmyra ndi ‘mfumu yake yanzeruyo’?

Mfumu ‘Iutsa Mtima Wake’ Kuyambana ndi Zenobia

Mu chaka cha 270 C.E., Aurelian anakhala mfumu ya Roma. Gulu la asilikali ake linagonjetsa anthu otchedwa barbarians akumpoto. Mu chaka cha 271 C.E.,​—monga woimira “mfumu ya kumpoto” yotchulidwa mu ulosi wa Danieli​—Aurelian ‘anautsa mphamvu yake ndi mtima wake kuyambana ndi mfumu ya kumwera,’ yoimiriridwa ndi Zenobia. (Danieli 11:25a) Aurelian anatumiza asilikali ake ena ku Igupto ndi kutsogolera gulu lake lina la asilikali lalikulu kummawa kudzera ku Asia Minor.

Mfumu ya kumwera​—ulamuliro wotsogozedwa ndi Zenobia​—‘inachita nkhondo’ ndi Aurelian “ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu” lotsogozedwa ndi nduna ziŵiri, Zabdas ndi Zabbai. (Danieli 11:25b) Koma Aurelian analanda dziko la Igupto. Kenako anapita ku Asia Minor ndi ku Suriya. Zenobia anagonjetsedwa ku Emesa (kumene tsopano kukutchedwa Homs) ndipo anathaŵira ku Palmyra.

Pamene asilikali a Aurelian anazungulira mzinda wa Palmyra, Zenobia ndi mwana wake wamwamuna anathaŵira cha ku Perisiya kumene anaganiza kuti angapezeko thandizo, koma anakagwidwa ndi Aroma pamtsinje wa Firate. Mu chaka cha 272 C.E. anthu a ku Palmyra anapereka mzinda wawo kwa Aurelian. Koma Aurelian anawakomera mtima anthuwa, anafunkha zinthu zambiri, kudzanso fano la m’Kachisi wa Dzuŵa, napita nazo ku Roma. Mfumu ya Roma sinamuphe Zenobia, koma m’chaka cha 274 C.E. anamuika pa chionetsero chokondwerera kupambanako mwa kumuyendetsa m’Roma monse. Anakhala moyo wake wonse monga mayi wolemekezeka wa ku Roma.

Mzinda wa m’Chipululu Uwonongedwa

Patapita miyezi ingapo Aurelian atalanda mzinda wa Palmyra, Apamirenewo anapha asilikali achiroma omwe anasiyidwa m’mbuyo. Aurelian atamva zimenezi, mofulumira analamula asilikali ake kupitanso, ndipo panthaŵiyi anali kubwezera chilango choopsa kwa anthuwo. Amene anapulumuka pamenepa anatengedwa ukapolo. Mzinda wokongolawo unafunkhidwa ndi kuwonongedwa kotheratu. Choncho likulu limeneli la anthu ambiri linakhalanso mmene linalili kale.​—“Tadimori m’chipululu.”

Pamene Zenobia anamenyana ndi Roma, iye ndi Mfumu Aurelian mosadziŵa anachita mbali ya “mfumu ya kumwera” ndi “mfumu ya kumpoto,” chotero akumakwaniritsa mbali ya ulosi wolembedwa mwatsatanetsatane ndi mneneri wa Yehova zaka 800 m’mbuyo mwake. (Danieli, chaputala 11) Zochita za Zenobia zinakopa chidwi cha anthu ambiri. Komabe, chofunika kwambiri ndi mbali yake yoimira ulamuliro wandale wonenedweratu mu ulosi wa Danieli. Ufumu wake sunakhale zaka zoposa zisanu. Lerolino, mzinda wa Palmyra womwe unali likulu la ufumu wa Zenobia, ndi mudzi wokha basi. Ndiponso ufumu wa Roma wamphamvu unatha kalekale ndipo walowedwa m’malo ndi maufumu amakono. Kodi tsogolo la maufumu ameneŵa n’lotani? Ulosi wa Baibulo umene sulephera kukwaniritsidwa unaneneratu mmene tsogolo lawo lidzakhalira.​—Danieli 2:44.

[Bokosi patsamba 29]

Zimene Zenobia Anasiya

Mfumu Aurelian atagonjetsa Zenobia mfumukazi ya Palmyra, anabwerera ku Roma ndi kumanga kachisi wa dzuŵa. Mkati mwake anaikamo mafano a mulungu Dzuŵa amene anatenga ku Palmyra. Kunena za zimene zinachitika pambuyo pake, magazini ya History Today imati: “Pa zonse zimene Aurelian anachita zimene zakhalitsa ndi madyerero a pachaka okondwerera dzuŵa amene anakhazikitsa mu AD 274, ochitika patsiku la winter solstice, pa December 25. Pamene ufumuwo unakhala wachikristu, tsiku limeneli analisankha kukhala tsiku lobadwa Kristu kuti chipembedzo chatsopanochi chikhale chovomerezeka kwa amene ankasangalala ndi madyerero akale. N’zodabwitsa kuti . . . [anthu] kwenikweni amakondwerera Khirisimasi chifukwa cha Mfumukazi Zenobia.”

[Mapu/​Chithunzi pamasamba 28, 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NYANJA YA MEDITERRANEAN

SURIYA

Antiokeya

Emesa (Homs)

PALMYRA

Damasiko

MESOPOTAMIYA

Firate

Carrhae (Harana)

Nisibis

Dura-Europos

[Mawu a Chithunzi]

Mapu: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

Zipilala: Michael Nicholson/​Corbis

[Chithunzi patsamba 29]

Ndalama ya Roma imene mwina ili ndi nkhope ya Aurelian

[Chithunzi patsamba 30]

Kachisi wa dzuŵa ku Palmyra

[Mawu a Chithunzi]

The Complete Encyclopedia of Illustration/​J. G. Heck

[Chithunzi patsamba 31]

Mfumukazi Zenobia akulankhula kwa asilikali ake

[Mawu a Chithunzi]

Giovanni Battista Tiepolo, Queen Zenobia Addressing Her Soldiers, Samuel H. Kress Collection, Photograph © Board of Trustees, National Gallery of Art, Washington

[Mawu a Chithunzi patsamba 28]

Chitunzi: Giovanni Battista Tiepolo, Queen Zenobia Addressing Her Soldiers, Samuel H. Kress Collection, Photograph © Board of Trustees, National Gallery of Art, Washington

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena