Zotsatirapo za Kunyada—Kodi N’zoipa Motani?
KODI munachitapo zinthu ndi munthu amene anangofuna kukupangitsani kudzimva ngati wopanda phindu? Kaya anali manijala, kaya bwana wanu, kaya wokuyang’anirani, kapena ngakhale wachibale amene anangokunyozerani ndi kukuonani ngati munthu wonyansa? Kodi munamuona bwanji munthuyo? Kodi munakopeka nawo umunthu wake? Kutalitali! Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kunyada kumapinga zambiri ndipo kumatsekereza kuyankhulana.
Kunyada kumapangitsa munthu kunyoza wina aliyense, kotero kuti wonyadayo nthaŵi zonse amaoneka ngati wapamwamba. Munthu wotero nthaŵi zambiri sanena mawu abwino ponena za ena. Nthaŵi zonse pamakhala mawu ena osuliza—“zimenezo n’zoona, koma amene uja ali ndi vuto lakuti kapena amalakwitsa pakuti.”
Buku lakuti Thoughts of Gold in Words of Silver, limati kunyada ndicho “chinthu choipa chowonongetsa zinthu nthaŵi zonse. Kunyada kumawononga munthu, kum’siya alibe kalikonse kokhumbirika.” Kodi n’zodabwitsa kuti palibe munthu amene amamasuka akakhala pafupi ndi munthu wonyada? Kwenikweni, chotsatirapo cha kunyada nthaŵi zonse chimakhala kusakhala ndi mabwenzi oona. Bukulo likupitiriza kuti, “Koma dziko limakonda anthu odzichepetsa—osati onyadira kudzichepetsa kwawo, koma odzichepetsadi.” Ndiye chifukwa chake Baibulo limati: “Kunyada kwa munthu kumam’chepetsa, koma wodzichepetsa yekha alemekezedwa.”—Miyambo 29:23, The Jerusalem Bible.
Komabe, koposa ubwenzi kapena ulemu wa anthu, kodi kunyada kumakhudza motani unansi wa munthu ndi Mulungu? Kodi Mulungu amawaona motani anthu onyada, odzikuza, ndi odzitukumula? Kunyada kapena kudzichepetsa—kodi pali chimene chimam’khudza?
Phunziro la Kudzichepetsa
Wolemba Miyambo wouziridwayo anati: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa. Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugaŵana zofunkha ndi onyada.” (Miyambo 16:18, 19) Nzeru ya mawuwo ikusonyezedwa bwino lomwe pa zimene zinachitikira Namani kazembe wa ku Suriya, amene analiko m’nthaŵi ya mneneri Elisa Mwisrayeli.
Namani anali wakhate. Pofunafuna chithandizo cha mankhwala, anapita ku Samariya akumaganiza kuti adzalankhula mwachindunji ndi Elisa. M’malo mwake, mneneriyo anatumiza mnyamata wake kuti alangize Namani kuti akasambe kasanu ndi kaŵiri m’Mtsinje wa Yordano. Namani anakhumudwa kuti analandiridwa motero ndi kupatsidwa malangizo oterowo. Kodi bwanji mneneriyo sanatuluke kudzalankhula naye mwachindunji m’malo motumiza mnyamata wake? Ndipotu Yordano anali wofanana ndi mitsinje ya ku Suriya! Kumeneko kunali kunyada. Chotsatirapo chake? Mwamwayi, anatsatira uphungu wanzeruwo. “Potero anatsika, namira m’Yordano kasanu ndi kaŵiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng’ono, nakonzeka.”—2 Mafumu 5:14.
Nthaŵi zina kungodzichepetsa pang’ono kumadzetsa madalitso aakulu.
Zotsatirapo za Kudzikweza
Komatu zotsatirapo za kunyada kwathu zingakhale zazikulu kwambiri kuposa kungomanidwa zinthu zina zopindulitsa. Pali kunyada kwina kumene kumatanthauzidwa ndi liwu lachigiriki lakuti “hybris.” Malinga n’kunena kwa katswiri wa Chigiriki William Barclay, “hubris ndi kunyada kosakanikira ndi nkhanza . . . , kunyansidwa kodzikweza kumene kumapangitsa [munthu] kusaŵerengera anthu anzake.”
Chitsanzo chabwino kwambiri cha kunyada komkitsa kumeneku chikupezeka m’Baibulo. Ndicho nkhani ya Hanuni, mfumu ya Amoni. Buku la Insight on the Scriptures limati: “Chifukwa chakuti Nahasi anam’komera mtima, Davide anatumiza amithenga kuti akatonthoze Hanuni atate wakeyo atamwalira. Koma Hanuni, atakhulupirira zonena za akalonga ake kuti Davide anali kungofuna kuzonda mudziwo mwamachenjera, anawachita chipongwe anyamata a Davide mwa kuwameta ndevu zawo mbali imodzi ndi kudula zovala zawo pakati kufika m’matako ndi kuwasiya kuti apite.”a Ponena za chochitikachi, Barclay anati: “M’chitidwewo unali hubris. Chinali chipongwe, nkhanza, kuchititsa manyazi pagulu, zonsezi pamodzi.”—2 Samueli 10:1-5.
Inde, munthu wonyada amatha kukhala wonyada momkitsa, wamwano, wonyazitsa ena. Amasangalala kukhumudwitsa ena mopanda chifundo, mosawaganizira m’pang’ono pomwe ndiyeno amamva bwino akamaona munthu winayo akuvutika ndiponso akuchititsidwa manyazi kwambiri. Koma kusokoneza kapena kuwonongetsa munthu ulemu wake kumawononga zinthu m’njira ziŵiri. Kumapangitsa munthu kutaya bwenzi lake ndiponso, nthaŵi zambiri, kumapanga bwenzilo kukhala mdani.
Kodi Mkristu woona aliyense angasonyezerenji kunyada koipa koteroko pamene Mbuyake anam’lamula kuti ‘azikonda mnzake monga adzikonda iyemwini’? (Mateyu 7:12; 22:39) N’zosiyana kotheratu ndi mmene Mulungu ndi Kristu alili. Pamenepa, Barclay akufotokoza mawu ofunika kuwaganizira kwambiri akuti: “Hubris ndiko kunyada kumene kumapangitsa munthu kunyoza Mulungu.” Ndiko kunyada kumene kumati: “Kulibe Mulungu.” (Salmo 14:1) Kapena monga momwe Salmo 10:4 limanenera kuti: “Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.” Kunyada koteroko, kapena kuti kudzikuza, sikumangopatutsa munthu kwa mabwenzi ndi achibale ake komanso kwa Mulungu. N’chotsatirapo choopsa chotani nanga!
Musalole Kunyada Kukuipitsani
Kunyada kungaonekere m’njira zosiyanasiyana—kunyada kwautundu, kwaufuko, kulekanitsa anthu malinga ndi ntchito zawo ndi mabanja awo, maphunziro, chuma, kutchuka, ndiponso mphamvu. Mwa njira ina iliyonse, kunyada kungakuloŵeni mumtima ndi kuipitsa umunthu wanu.
Anthu ambiri amaoneka kukhala odzichepetsa pochita zinthu ndi owalamulira awo kapena ngakhale anzawo. Koma kodi n’chiyani chimachitika pamene munthu wooneka ngati wodzichepetsayo apatsidwa mphamvu zaulamuliro? Mwadzidzidzi, amakhala munthu wopondereza, wosautsa anthu amene amawayesa apansi kwa iye! Zimenezi zingachitike kwa ena atavala yunifomu kapena baji yosonyeza kuti ali ndi mphamvu zakutizakuti. Ngakhale antchito a boma angakhale onyada pochita zinthu ndi anthu, akumaganiza kuti anthuwo ayenera kuwatumikira, osati iwo kutumikira anthuwo. Kunyada kungakupangitseni kukhala waukali, wouma mtima; kudzichepetsa kungakupangitseni kukhala wokoma mtima.
Yesu akanatha kukhala wonyada ndiponso waukali kwa ophunzira ake. Iye anali munthu wangwiro, Mwana wa Mulungu, wochita zinthu ndi otsatira ake opanda ungwiro, aphuma, ndiponso ansontho. Koma, kodi anapereka chiitano chotani kwa awo amene anamumvera? “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
Kodi nthaŵi zonse timafuna kutsatira chitsanzo cha Yesu? Kapena kodi timakhala aukali, osalolera, opondereza, ouma mtima, onyada? Monga Yesu, yesani kumapumulitsa, osati kupondereza. Kanani mphamvu yoipitsa ya kunyada.
Kusiyana Pakati pa Kudzilemekeza ndi Kudzitukumula
Malingaliro ena ofanana nawo koma abwino ndiwo kudzilemekeza kwabwino kapena koyenera. Kudzilemekeza kumatanthauza kudzipatsa ulemu. Kumatanthauza kuti mumasamala zimene ena amakuganizirani. Mumasamala za kaonekedwe kanu ndi mbiri yanu. Mwambi wachisipanya umanenadi zoona kuti, “Ndiuze amene umacheza nawo ndipo ndidzakuuza kuti ndiwe munthu wotani.” Ngati mumakonda kuyanjana ndi anthu osadzisamala, aulesi, amakhalidwe osasangalatsa, ndiponso owola pakamwa, ndiye kuti mudzakhala monga iwo. Mudzatengerako maganizo awo, ndiponso mudzakhala wosadzilemekeza, monga mmene iwo alili.
Komanso pali kunyada kwina komkitsa—kunyada kodzitukumula kapena kopanda pake. Alembi ndi Afarisi a m’tsiku la Yesu ankanyadira miyambo yawo ndi kaonekedwe kawo kakuti ndi anthu opembedza kwambiri. Ponena za iwo, Yesu anachenjeza kuti: “Koma amachita ntchito zawo zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zawo, nakulitsa mphonje [kuti aoneke kukhala opembedza kwambiri], nakonda malo aulemu pamapwando, ndi mipando yaulemu m’masunagoge, ndi kulankhulidwa m’misika, ndi kutchedwa ndi anthu, Rabi.”—Mateyu 23:5-7.
Choncho, chofunika ndicho kukhala ndi maganizo abwino. Kumbukiraninso kuti Yehova amaona zamumtima, osati zakunja zokha. (1 Samueli 16:7; Yeremiya 17:10) Kudzilungamitsa sindiko chilungamo cha Mulungu. Komabe, funso n’lakuti, Kodi tingakulitse motani kudzichepetsa koona ndi kupeŵa zotsatirapo zoipa za kunyada?
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 4]
Kungodzichepetsa pang’ono kunadzetsera Namani mapindu aakulu