Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 3/1 tsamba 18-23
  • Madalitso a Yehova pa “Dziko” Lathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madalitso a Yehova pa “Dziko” Lathu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtsinje Uyenda m’Dziko Lobwezeretsedwa
  • Madalitso Ayenda Monga Mtsinje Wamphamvu
  • Madziwo Apatsa Moyo!
  • Mtsinjewo Uyenda m’Paradaiso
  • “Kulikonse Kumene Mtsinjewo Ukupita, Chilichonse Chidzakhala ndi Moyo”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezekieli—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda—2007
  • ‘Ika Mtima Wako pa’ Kachisi wa Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—1999
  • ‘Ufotokoze za Kachisiyu’
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 3/1 tsamba 18-23

Madalitso a Yehova pa “Dziko” Lathu

“Kulikonse mtsinje ufikako zilizonse zidzakhala ndi moyo.”​—EZEKIELI 47:9.

1, 2. (a) Kodi madzi n’ngofunika motani? (b) Kodi madzi a m’mtsinje wa m’masomphenya a Ezekieli akuimira chiyani?

MADZI n’chinthu chapadera. Zamoyo zonse zimadalira madzi. Palibe aliyense wa ife angakhale ndi moyo popanda madzi. Timafunikiranso madzi poyeretsa zinthu, popeza amasungunula ndi kuchotsa litsiro lonse. Chotero timasamba, kuchapa zovala zathu, ngakhale kutsuka chakudya chathu ndi madzi. Kuchita zimenezo kungapulumutse moyo wathu.

2 Baibulo limagwiritsa ntchito madzi kuimira makonzedwe a Yehova opatsa moyo. (Yeremiya 2:13; Yohane 4:7-15) Makonzedwe ameneŵa amaphatikizapo kuyeretsa anthu ake kudzera m’nsembe ya dipo la Kristu ndi chidziŵitso cha Mulungu chopezeka m’Mawu ake. (Aefeso 5:25-27) M’masomphenya a Ezekieli onena za kachisi, mtsinje wozizwitsa wotuluka m’kachisi ukuimira madalitso otero opatsa moyo. Koma kodi mtsinjewo uyamba liti kuyenda, ndipo zimenezo zikutanthauzanji kwa ife lerolino?

Mtsinje Uyenda m’Dziko Lobwezeretsedwa

3. Kodi Ezekieli anaona zotani, monga momwe Ezekieli 47:2-12 akunenera?

3 Pokhala andende ku Babulo, anthu a m’nthaŵi ya Ezekieli anafunika kwambiri makonzedwe a Yehova. Mmene zinamulimbikitsira Ezekieli nanga kuona madontho a madzi akutuluka m’malo opatulika ndi kutuluka m’kachisi wa m’masomphenya! Mngelo akuyesa mtsinjewo danga ndi danga pamlingo wa mikono chikwi chimodzi. Kuya kwake kukuwonjezeka kuchokera m’mapazi kufika m’mawondo, kenako m’chuuno mpaka utakhala mtsinje woti munthu n’kusambira. Mtsinjewo ukudzetsa moyo ndi chonde. (Ezekieli 47:2-11) Ezekieli akuuzidwa kuti: “Kumtsinje, kugombe kwake tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uliwonse wa chakudya.” (Ezekieli 47:12a) Mtsinjewo utaloŵa m’Nyanja Yakufa​—m’madzi opanda zamoyowo​—mukhala zamoyo! Nsomba zichuluka. Malonda a nsomba afala.

4, 5. Kodi ulosi wa Yoweli wonena za mtsinje ukufanana motani ndi wa Ezekieli, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezo n’zochititsa chidwi?

4 Ulosi umenewu wochititsa chidwi ungakhale utakumbutsa Ayuda andende za ulosi wina wolembedwa zaka zoposa mazana ambiri kumbuyoko: “Madzi a kasupe adzatuluka m’nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.”a (Yoweli 3:18) Ulosi wa Yoweli, mofanana ndi wa Ezekieli, ukulosera kuti mtsinje udzatuluka m’nyumba ya Mulungu, kachisi, ndi kudzetsa moyo kudera louma.

5 Kwa zaka zambiri, Nsanja ya Olonda yafotokoza kuti ulosi wa Yoweli ukukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu.b Ndithudi, ndi mmenenso zilili ndi masomphenya ofananawo a Ezekieli. M’dziko lobwezeretsedwa la anthu a Mulungu lerolino, monga m’Israyeli wakale, mulidi madalitso a Yehova.

Madalitso Ayenda Monga Mtsinje Wamphamvu

6. Kodi kuwaza mwazi pa guwa la nsembe la m’masomphenya kuyenera kuti kunawakumbutsa chiyani Ayuda?

6 Kodi gwero la madalitso amene akudza pa anthu a Mulungu obwezeretsedwa ndi liti? Chabwino, taonani kuti madziwo akutuluka m’kachisi wa Mulungu. Momwemonso lerolino, madalitso akuchokera kwa Yehova kudzera m’kachisi wake wamkulu wauzimu​—makonzedwe a kulambira koyera. Masomphenya a Ezekieli akuwonjezapo mbali yofunika kwambiri. M’bwalo lamkati, mtsinjewo ukudutsa kuguwa la nsembe, kummwera kwake. (Ezekieli 47:1) Guwalo lili pakati penipeni pa kachisi wa m’masomphenyawo. Yehova akum’longosolera bwinobwino Ezekieli za guwalo nalamula kuti aliwaze mwazi wa nsembe. (Ezekieli 43:13-18, 20) Guwa la nsembe limenelo linali ndi tanthauzo lalikulu kwa Aisrayeli onse. Pangano lawo ndi Yehova linali litatsimikizidwa kalekale pamene Mose anawaza mwazi pa guwa la nsembe mmunsi mwa Phiri la Sinai. (Eksodo 24:4-8) Chotero kuwaza mwazi pa guwa la nsembe la m’masomphenya kungakhale kutawakumbutsa kuti atangobwerera kudziko lawo lobwezeretsedwa, madalitso a Yehova adzawadzera malinga atasunga pangano lawo ndi iye.​—Deuteronomo 28:1-14.

7. Kodi Akristu amapeza tanthauzo lotani lerolino pa guwa la nsembe lophiphiritsira?

7 Mofananamo, anthu a Mulungu lerolino akudalitsidwa kudzera m’pangano​—labwino kwambiri, pangano latsopano. (Yeremiya 31:31-34) Ilinso linatsimikizidwa kalekale ndi mwazi, inde, mwazi wa Yesu Kristu. (Ahebri 9:15-20) Lerolino, kaya ndife odzozedwa, amene ali m’pangano limenelo, kapena a “nkhosa zina,” amene akupindula nalo, timapeza tanthauzo lalikulu m’guwa la nsembe lophiphiritsira. Limaimira chifuniro cha Mulungu mogwirizana ndi nsembe ya Kristu. (Yohane 10:16; Ahebri 10:10) Monga momwe guwa la nsembe lophiphiritsira lilili pakati penipeni pa kachisi wauzimu, nsembe ya dipo la Kristu n’njofunika kwambiri pa kulambira koyera. Ndiyo maziko a chikhululukiro cha machimo athu ndipo mwanjira imeneyonso maziko a ziyembekezo zathu zonse za m’tsogolo. (1 Yohane 2:2) Motero timayesetsa kutsata chilamulo cha pangano latsopano, “chilamulo cha Kristu.” (Agalatiya 6:2) Malinga ngati tichita zimenezo, tidzapindula ndi makonzedwe a Yehova opatsa moyo.

8. (a) Kodi m’bwalo lamkati la kachisi wa m’masomphenya munalibe chiyani? (b) Kodi ansembe a m’kachisi wa m’masomphenya anali kudziyeretsa motani?

8 Limodzi mwa mapindu amenewo ndilo kaimidwe koyera pamaso pa Yehova. M’kachisi wa m’masomphenyawo, bwalo lamkati lilibe chinthu chimene chinali choonekera kwambiri m’bwalo la chihema ndi m’kachisi wa Solomo​—mkhate waukulu, umene pambuyo pake unatchedwa thawale, losambamo ansembe. (Eksodo 30:18-21; 2 Mbiri 4:2-6) Nanga tsono ansembe m’masomphenya a Ezekieli onena za kachisi akanagwiritsa ntchito chiyani podziyeretsa? Eya, mtsinje wozizwitsawo woyenda kudutsa m’bwalo lamkati! Inde, Yehova akawadalitsa ndi njira yokhalira ndi kaimidwe koyera kapena kopatulika.

9. Kodi odzozedwa ndi a m’khamu lalikulu angakhale motani ndi kaimidwe koyenera lerolino?

9 Momwemonso lerolino, odzozedwa adalitsidwa ndi kaimidwe koyera pamaso pa Yehova. Yehova amawaona kukhala oyera, akumawatcha olungama. (Aroma 5:1, 2) Nanga bwanji za “khamu lalikulu,” loimiridwa ndi mafuko osakhala ansembe? Iwo amalambira m’bwalo lakunja, ndipo mtsinje umodzimodziwo umadutsa mbali yomweyo ya kachisi wa m’masomphenya. Pamenepa, n’koyenera chotani nanga kuti mtumwi Yohane anaona khamu lalikululo litavala zovala zoyera pamene likulambira m’bwalo la kachisi wauzimu! (Chivumbulutso 7:9-14) Kaya awachite motani m’dziko loipali, iwo n’ngotsimikiza kuti malinga ngati asonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya dipo la Kristu, Yehova amawaona kukhala oyera. Kodi iwo amasonyeza motani chikhulupiriro? Mwa kutsatira mapazi a Yesu, kukhala ndi chidaliro chonse m’nsembe ya dipo.​—1 Petro 2:21.

10, 11. Kodi madzi ophiphiritsirawo ali ndi mbali iti yofunika kwambiri, ndipo zimenezi zikugwirizana motani ndi kukula kwa mtsinjewo?

10 Monga momwe tanenera kale, madzi ophiphiritsira ameneŵa alinso ndi mbali ina yofunika kwambiri​—chidziŵitso. Mu Israyeli wobwezeretsedwa, Yehova anadalitsa anthu ake ndi malangizo a Malemba kudzera mwa ansembe. (Ezekieli 44:23) Mofananamo, Yehova wadalitsa anthu ake lerolino ndi malangizo okwanira a Mawu ake a choonadi, kupyolera mwa “ansembe achifumu.” (1 Petro 2:9) Chidziŵitso ponena za Yehova Mulungu, zifuno zake kwa anthu, ndipo makamaka cha Yesu Kristu ndi Ufumu Waumesiya chakhala chikusefukira masiku ano otsiriza. N’zabwino chotani nanga kulandira chitsitsimulo chauzimu chimenechi chakuya ndiponso chosefukira!​—Danieli 12:4.

11 Monga momwe mtsinje umene mngelo anayesa umamka ukuya pang’onopang’ono, madalitsonso opatsa moyo ochokera kwa Yehova awonjezeka modabwitsa kulola unyinji wa anthu kuloŵa m’dziko lathu lauzimu lodalitsidwa. Ulosi wina wa kubwezeretsa unaneneratu kuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yesaya 60:22) Mawu ameneŵa akwaniritsidwa​—anthu miyandamiyanda adza muunyinji wawo kudzagwirizana nafe pakulambira koyera! Yehova wapereka “madzi” ochuluka kwa onse otembenukira kwa iye. (Chivumbulutso 22:17) Akuonetsetsa kuti gulu lake looneka la padziko lapansi likugaŵira mabaibulo ndi mabuku ofotokoza za Baibulo m’zinenero mazanamazana padziko lonse. Mofananamo, misonkhano yachikristu yaing’ono ndiponso yaikulu yakonzedwa padziko lonse kuti onse apeze madzi a choonadi oyera kuti mbe. Kodi makonzedwe ameneŵa amawakhudza motani anthu?

Madziwo Apatsa Moyo!

12. (a) Kodi n’chifukwa chiyani mitengo ya m’masomphenya a Ezekieli ikubala zipatso motero? (b) Kodi mitengo yobala zipatso zambiri imeneyi ikuimira chiyani m’masiku otsiriza?

12 Mtsinje wa m’masomphenya a Ezekieli upatsa moyo ndi thanzi. Ezekieli atadziŵa za mitengo imene idzamera kugombe kwa mtsinjewo, akuuzidwa kuti: “Osafota tsamba lake, zipatso zake zomwe zosasoŵa. . . . Ndi zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake lakuchiritsa.” N’chifukwa chiyani mitengo imeneyi ikubala zipatso mozizwitsa chonchi? “Popeza madzi ake atumphuka m’malo opatulika.” (Ezekieli 47:12b) Mitengo yophiphiritsira imeneyi ikuchitira chithunzi makonzedwe onse a Mulungu opatsanso anthu ungwiro pamaziko a nsembe ya dipo la Yesu. Padziko lapansi nthaŵi ino, otsalira a odzozedwa akutsogolera kupereka chakudya chauzimu ndi kuchiritsa kwauzimu. A 144,000 onse akadzalandira mphotho yawo yakumwamba, mapindu a utumiki wawo wansembe monga olamulira anzake a Kristu adzapitiriza m’tsogolo, kufikira pomalizira pake adzagonjetseratu imfa ya Adamu.​—Chivumbulutso 5:9, 10; 21:2-4.

13. Kodi n’kuchiritsa kotani kumene kwachitika m’nthaŵi yathu?

13 Mtsinje wa m’masomphenyawo utsikira ku Nyanja Yakufa yopanda zamoyo ndipo uchiritsa zonse zomwe zili kumene ufikako. Nyanjayo ikuimira malo akufa mwauzimu. Koma zamoyo zichuluka “kulikonse mtsinjewo ufikako.” (Ezekieli 47:9) Mofananamo, anthu m’masiku otsiriza akukhala amoyo mwauzimu kulikonse kumene madzi a moyo aloŵako. Amene anayamba kupezanso nyonga anali otsalira odzozedwa mu 1919. Anakhalanso amoyo mwauzimu kuchoka mumkhalidwe wosagwira ntchito wonga imfa. (Ezekieli 37:1-14; Chivumbulutso 11:3, 7-12) Madzi amenewo ofunika kwambiri afika kwa enanso akufa mwauzimu chiyambire pamenepo, ndipo ameneŵa akhala amoyo ndipo apanga khamu lalikulu lomawonjezereka nthaŵi zonse la nkhosa zina zimene zimakonda Yehova ndi kumutumikira. Posakhalitsa, makonzedwe ameneŵa adzafika kwa makamu oukitsidwa.

14. Kodi malonda ansomba amene akufala kugombe la Nyanja Yakufa akuimira chiyani lerolino?

14 Nyonga yauzimu imabalitsa zipatso. Zimenezi zikusonyezedwa ndi malonda ansomba amene afala kugombe la nyanjayo imene kale inali yakufa. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” (Mateyu 4:19) M’masiku otsiriza, ntchito yosodza inayamba ndi kusonkhanitsa otsalira a odzozedwa, koma sinathere pompo ayi. Madzi opatsa moyo otuluka m’kachisi wa Yehova, kuphatikizapo dalitso la chidziŵitso cholongosoka, zafika kwa anthu a mitundu yonse. Kulikonse kumene mtsinjewo wafikako, kwakhala moyo wauzimu.

15. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti si aliyense amene adzalandira makonzedwe a Mulungu opatsa moyo, ndipo kodi n’chiyani chidzachitikira otere?

15 Inde, si onse amene amalabadira uthenga wa moyo tsopano; ndipo si onse amene adzatero mwa oukitsidwa mu Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. (Yesaya 65:20; Chivumbulutso 21:8) Mngeloyo akunena kuti mbali zina za nyanjayo sizikuchira. Zithaphwi zimenezi, zopanda moyo ‘zikuperekedwa kumchere.’ (Ezekieli 47:11) Ponena za anthu a m’tsiku lathu, atapatsidwa madzi opatsa moyo a Yehova, si onse amene amawalandira. (Yesaya 6:10) Pa Armagedo, onse amene asankha kukhalabe akufa mwauzimu ndi odwala ‘adzaperekedwa kumchere,’ ndiko kuti, kuwonongedwa kosatha. (Chivumbulutso 19:11-21) Komabe, amene akhala akumwa madzi ameneŵa mokhulupirika akuyembekezera kupulumuka ndi kudzaona kukwaniritsidwa komaliza kwa ulosi umenewu.

Mtsinjewo Uyenda m’Paradaiso

16. Kodi masomphenya a Ezekieli adzakwaniritsidwa liti komaliza ndipo motani?

16 Mofanana ndi maulosi ena a kubwezeretsa, masomphenya a Ezekieli onena za kachisi adzakwaniritsidwa komaliza m’Zaka Chikwi. Panthaŵiyo kagulu ka ansembe sikadzakhalanso pano padziko lapansi. “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye [kumwamba] zaka chikwizo.” (Chivumbulutso 20:6) Ansembe akumwamba ameneŵa adzagwirizana ndi Kristu kupereka mapindu onse a nsembe ya dipo la Kristu. Motero anthu olungama adzapulumuka, kubwezeretsedwa ku ungwiro!​—Yohane 3:17.

17, 18. (a) Kodi mtsinje wopatsa moyo ukufotokozedwa motani pa Chivumbulutso 22:1, 2, ndipo kodi kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenyawo kukuchitika liti? (b) M’Paradaiso, kodi n’chifukwa chiyani mtsinje wa madzi a moyo udzakula kwambiri?

17 Kwenikweni, panthaŵiyo mtsinje umene Ezekieli anaona udzayenda madzi a moyo amphamvu koposa. Inoyi ndiyo nthaŵi pamene kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi wolembedwa pa Chivumbulutso 22:1, 2 kukuchitika: “Anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.”

18 Mkati mwa Zaka Chikwi, matenda onse​—a m’thupi, a m’maganizo, ndi a mumtima​—adzachiritsidwa. Zimenezi zikuimiridwa bwino ndi ‘kuchiritsa amitundu’ ndi mitengo yophiphiritsirayo. Chifukwa cha makonzedwe operekedwa ndi Kristu ndi a 144,000, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ndipo mtsinjewo udzafika panthaŵi yake yakufutukuka koposa ndi kalelonse. Udzayenera kukula ndi kuya kwambiri kuti uchirikize anthu mamiliyoni, mwinamwake mamiliyoni zikwi zambiri, oukitsidwa amene adzamwa madzi oyera ameneŵa a moyo. Mtsinje wa m’masomphenyawo unachiritsa Nyanja Yakufa, kupereka moyo kulikonse kumene madzi ake anafikako. M’Paradaiso, amuna ndi akazi adzakhala amoyo m’lingaliro lokwanira, kuchiritsidwa pa imfa ya choloŵa ya Adamu ngati adzasonyeza chikhulupiriro m’mapindu a dipo operekedwa kwa iwo. Chivumbulutso 20:12 chimalosera kuti “mabuku” adzatsegulidwa masikuwo, kupereka kuunika kowonjezereka kwa chidziŵitso chimene akufa oukitsidwawo adzapindula nacho. N’zachisoni kuti ena adzakana kuchiritsidwa, ngakhale m’Paradaiso. Opanduka ameneŵa ndiwo ‘operekedwa kumchere’ wa chiwonongeko chosatha.​—Chivumbulutso 20:15.

19. (a) Kodi kugaŵa dziko kudzakwaniritsidwa motani m’Paradaiso? (b) Kodi mudziwo udzaimira chiyani m’Paradaiso? (c) Kodi malo a mudziwo kutali ndi kachisi akutanthauzanji?

19 Komanso panthaŵiyo, kugaŵa dziko kwa m’masomphenya a Ezekieli kudzakwaniritsidwa komaliza. Ezekieli anaona dziko likugaŵidwa bwino; mofananamo, Mkristu aliyense wokhulupirika angatsimikize kuti adzakhala ndi malo, choloŵa, m’Paradaiso. Chikhumbo chokhala ndi nyumba yakoyako yokhalamo ndi kuisamalira chiyenera kuti chidzakhutiritsidwa mwadongosolo. (Yesaya 65:21; 1 Akorinto 14:33) Mudzi umene Ezekieli anaona moyenerera umaimira makonzedwe auyang’aniro amene Yehova akulinganiza kaamba ka dziko lapansi latsopano. Kagulu ka ansembe odzozedwa sikadzakhalanso m’thupi pakati pa anthu. Masomphenyawo akupereka lingaliro lomwelo mwa kusonyeza kuti mudziwo uli m’dziko “lodetsedwa” kutali ndi kachisi. (Ezekieli 48:15, NW) Pamene a 144,000 akulamulira ndi Kristu kumwamba, Mfumuyo idzakhalanso ndi oiimira ake padziko lapansi. Anthu ake adzapindula kwambiri ndi chitsogozo ndi malangizo achikondi a kagulu ka kalonga. Komabe, likulu lenileni la bomalo silidzakhala padziko lapansi, koma kumwamba. Aliyense amene adzakhala padziko lapansi, kuphatikizapo kagulu ka kalonga, adzakhala akulamuliridwa ndi Ufumu Waumesiya.​—Danieli 2:44; 7:14, 18, 22.

20, 21. (a) Kodi n’chifukwa chiyani dzina la mudziwo lili loyenerera? (b) Kodi kumvetsa kwathu masomphenya a Ezekieli kuyenera kutipangitsa kudzifunsa mafunso ati?

20 Taonani mawu omaliza a ulosi wa Ezekieli akuti: “Dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.” (Ezekieli 48:35) Mudzi umenewu sunakhalirepo kupatsa anthu mphamvu kapena ulamuliro; ndiponso sunakhalirepo kuchirikiza chifuniro cha munthu aliyense ayi. Ndi mudzi wa Yehova. Udzaonetsa maganizo ake ndi njira zake zachikondi ndiponso zabwino zochitira zinthu. (Yakobo 3:17) Zimenezi zikutipatsa chitsimikizo cholimbitsa mtima chakuti Yehova adzadalitsa “dziko [lake] latsopano” la dongosolo la mtundu wa anthu ku umuyaya wonse.​—2 Petro 3:13.

21 Kodi sitikusangalala ndi zimene zili m’tsogolo mwathu? Moyenerera, aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimawalabadira motani madalitso abwino kwambiri ovumbulidwa ndi masomphenya a Ezekieli? Kodi ndikuchirikiza mokhulupirika ntchito imene oyang’anira achikondi akuchita, kuphatikizapo aja a otsalira odzozedwa ndi amene akuyembekezera kukhala mamembala a kagulu ka kalonga? Kodi ndapanga kulambira koyera kukhala chinthu chofunika kwambiri m’moyo wanga? Kodi ndikugwiritsa ntchito mokwanira madzi a moyo ochulukawo omwe akuyenda lerolino?’ Aliyense wa ife apitirize kuchita zimenezo ndi kukondwera ndi makonzedwe a Yehova ku umuyaya wonse!

[Mawu a M’munsi]

a Chigwa chimenechi mwina chinali chigwa cha Kidroni, chimene chimachokera ku Yerusalemu kupita kummwera cha kummaŵa mpaka m’Nyanja Yakufa. Cha kumunsi kwake makamaka kumakhala kulibe madzi ndipo kumakhala kouma chaka chonse.

b Onani makope a Nsanja ya Olonda achingelezi a May 1, 1881, ndi June 1, 1981.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi madzi otuluka m’kachisi akuimira chiyani?

◻ Kodi Yehova wachita kuchiritsa kotani pogwiritsa ntchito mtsinje wophiphiritsirawo, ndipo n’chifukwa chiyani mtsinjewo ukukula?

◻ Kodi mitengo ya kugombe kwa mtsinje ikuimira chiyani?

◻ Kodi mudzi ukuimira chiyani mu Ulamuliro wa Zaka Chikwi, ndipo n’chifukwa chiyani dzina la mudziwo lili loyenerera?

[Zithunzi patsamba 23]

Mtsinje wa moyo ukuimira makonzedwe a Mulungu a chipulumutso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena