Kufunafuna Paradaiso
YOSIMBIDWA NDI PASCAL STISI
Unali usiku kwambiri, ndipo m’misewu ya m’tauni ya Béziers, kummwera kwa France, munalibe anthu. Titapeza khoma la nyumba yogulitsiramo mabuku achipembedzo yomwe inali itangopakidwa kumene penti, ine ndi mnzanga wina tinalembapo ndi zilembo zikuluzikulu zakuda mawu a wafilosofi wa ku Germany Nietzsche akuti: ‘Milungu ndi yakufa. Akhale ndi moyo wautali Munthu Woganiza!’ Koma kodi ndi chiyani chimene chinandichititsa kuchita zimenezi?
NDINABADWIRA ku France mu 1951, m’banja lachikatolika lochokera ku Italy. Pamene ndinali mwana, tinali kupita kukachita tchuthi kummwera kwa Italy. Kumeneko, mudzi uliwonse unali ndi chifanizo chakechake cha Namwali Mariya. Ndikuyenda ndi agogo anga aamuna, ndinali kutsatira zifanizo zikuluzikulu zovekedwa zovala zimenezi zomwe zinali mu mzere wosatherapo kudutsa m’mapiri—komatu ndinalibiretu chikhulupiriro chilichonse. Ndinachita maphunziro anga oyambirira pasukulu yachipembedzo ya Ajezwiti. Komabe, palibe chilichonse chimene ndimakumbuka kuti ndinamvapo chimene chinandipangitsa kukhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.
Ndinayamba kulingalira za chifuno cha moyo panthaŵi imene ndinalembetsa kuti ndiphunzire udokotala payunivesite ina ku Montpellier. Bambo anga anali atavulala ku nkhondo ndipo nthaŵi zonse madokotala anali kukhala pabedi pawo. Kodi sikukakhala bwino kuthetsa nkhondo m’malo mothera nthaŵi ndi zoyesayesa zambiri kuchiritsa anthu ovulazidwa ndi nkhondoyo? Komabe, Nkhondo ya ku Vietnam inali pachimake. Kwa ineyo, njira yomveka yothetsera kansa ya m’mapapu, mwachitsanzo, inali kuchotsa chochititsa chake chachikulu—fodya. Nanga bwanji za matenda amene amayamba chifukwa cha kupereŵera kwa zakudya m’mayiko amene akutukuka kumene ndiponso aja amene amayamba chifukwa cha kudya kwambiri m’mayiko olemera? Kodi si kwabwino kuchotsa zomwe zimawayambitsa m’malo moyesa kuthetsa zotsatirapo zake zopwetekazo? Kodi ndi chifukwa chiyani padziko lapansi pali kuvutika kwambiri? Ndinali kuona kuti pali chinachake chimene chinalakwika kwambiri ndi anthu odziwononga okha ameneŵa, ndipo ndinali kuimba mlandu maboma.
Buku lomwe ndinali kulikonda kwambiri linalembedwa ndi chigandanga, ndipo ndinali kulemba pazipupa ziganizo zochokera m’bukulo. Mwapang’opang’ono, inenso ndinasanduka chigandanga, ndinalibe chikhulupiriro chilichonse kapenanso malamulo alionse a chikhalidwe, ndipo sindinali kufuna Mulungu kaya wondilamulira. Kwa ineyo, Mulungu ndi chipembedzo zinali zimene anthu olemera ndi amphamvu anakonza pofuna kulamulira ndi kudyera masuku pamutu ena tonsefe. ‘Tigwirireni ntchito kwambiri pano padziko lapansi, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu m’paradaiso kumwamba,’ ankaoneka kuti anali kunena tero. Koma nthaŵi yolamulidwa ndi milungu inali itatha. Anthu anafunika kuuzidwa. Kulemba mawu m’zipupa inali njira imodzi yowauzira.
Chotsatira chake chinali chakuti ndinaika maphunziro pamalo achiŵiri. Zili choncho ndinali nditalembetsa kuphunzira za malo ndi kaimidwe ka dziko ndiponso za kugwirizana kwa chilengedwe pa yunivesite inanso ku Montpellier pamene anthu ake anali kukhala ngati oukira. Pamene ndinali kuphunzira mowonjezereka za kugwirizana kwa chilengedwe, ndinali kunyansidwanso mowonjezereka poona mmene pulaneti lathu lokongolali likuipitsidwira.
Chaka chilichonse patchuthi cha m’chilimwe, ndinali kukwera galimoto za anthu ndi kuyenda makilomita zikwi zochuluka mu Ulaya yense. Pamene ndinali pamaulendowo ndi kulankhula ndi madirayivala ambirimbiri, ndinadzionera ndi maso anga zoipa ndi zovuta zimene anthu anali kuvutika nazo. Nthaŵi ina, pamene ndinali kufunafuna paradaiso, ndinafika ku magombe okongola kwambiri a chisumbu chokongola cha Crete koma ndinaona kuti pansi ponse panali mafuta okhaokha. Ndinavutika kwambiri mumtima. Kodi panali kaparadaiso kamene kanatsalirako penapake padziko lapansi?
Kubwerera Kumudzi
Ku France akatswiri a kugwirizana kwa chilengedwe anali kunena kuti njira yothetsera masoka a anthu ndi yakuti anthuwo abwerere kumidzi. Ndinafuna kugwira ntchito ndi manja anga. Motero ndinagula nyumba yamiyala yakalekale pa kamudzi kena m’tsinde mwa Mapiri a Cévennes kummwera kwa France. Ndinalemba pachitseko kuti “Paradaiso Tsopano,” mawu odzichemerera a anyamata otayirira a ku America. Mtsikana wina wa ku Germany amene anali kudutsa m’deralo anakhala mnzanga wokhala naye m’nyumbayo. Sindikanapita kwa mkulu wa mzinda, munthu woimira boma, kuti akatikwatitse. Bwanji ku tchalitchi? Iŵalaniko!
Nthaŵi zambiri tinali kuyenda opanda nsapato, ndipo ndinali ndi tsitsi lalitali ndi ndevu zosameta. Kulima zipatso ndi ndiwo za masamba kunali kundipatsa chidwi. M’nthaŵi ya chilimwe thambo linali la bluu ndipo nyenje zinali kulira. Maluŵa a scrubland anali kununkhira bwino kwambiri, ndipo zipatso za ku Mediterranean zimene tinali kulima—mpesa ndi nkhuyu—zinali zokoma kwambiri! Zinali kuoneka kuti tinapeza malo athu a paradaiso.
Kuyamba Kukhulupirira Mulungu
Ku yunivesite, ndinaphunzira sayansi ya maselo, kukula kwa mluza, ndi mapangidwe a matupi a zamoyo, ndipo ndinachita chidwi kwambiri ndi kucholowana komanso kugwirizana kwa zinthu zimenezi. Tsopano popeza ndinali kusinkhasinkha pa chilengedwe ndiponso kuchiona tsiku lililonse, ndinali kukopeka ndi kukongola kwake komanso zimene chikanatha kuchita. Tsiku ndi tsiku buku la chilengedwe linali kunditsegukira tsamba ndi tsamba. Tsiku lina nditayenda mtunda wautali m’mapiri ndiponso nditalingalira mozama za moyo, ndinafika ponena kuti kuyenera kukhala Mlengi. Ndinaganiza zokhulupirira Mulungu. Poyambirira, mumtima mwanga munalibe chilichonse, ndinali wosungulumwa kwabasi. Tsiku limene ndinayamba kukhulupirira Mulungu, ndinadziyankhulira kuti, ‘Pascal, sudzakhalanso wekhawekha.’ Ndinazindikira m’njira yapadera.
Mwamsanga pambuyo pake, ine ndi mnzanga amene ndinkakhala naye m’nyumba uja tinali ndi kamwana kakakazi—Amandine. Ndinali kumukonda kwambiri. Tsopano popeza ndinali kukhulupirira Mulungu, ndinayamba kulemekeza malamulo ochepa achikhalidwe amene ndinali kuwadziŵa. Ndinasiya kuba ndi kunama, ndipo mwamsanga ndinaona kuti zimenezi zinandithandiza kupewa kukhala m’mavuto osiyanasiyana ndi anthu amene ndinayandikana nawo. Inde, tinali ndi mavuto athu, ndipo paradaiso wanga sanali paradaiso yense wathunthu amene ndinali kumufuna. Anthu a m’deralo amene anali kulima zinthu zopangira vinyo anali kugwiritsa ntchito mankhwala ophera tizilombo ndi oletsa zomera zina kumera amene analinso kuwononga mbewu zanga. Funso langa lonena za chochititsa kuipa linali losayankhidwabe. Ndiponso, ngakhale kuti ndinaŵerenga mabuku ambiri onena za moyo wa banja, ine ndi mnzanga tinali kukanganabe kwambiri. Tinali ndi mabwenzi ochepa, ndipo amene tinali nawowo anali osakhulupirika; ena ankayesa ngakhale kuchita chiŵereŵere ndi mnzangayo. Panayenera kukhala paradaiso wabwinopo.
Yankho la Mapemphero Anga
M’njira yangayanga, ndinali kupemphera nthaŵi zochuluka kwa Mulungu kuti anditsogolere. Lamlungu lina mmaŵa, mkazi wina waubwenzi wotchedwa Irène Lopez ndi kamwana kake kamnyamata anafika panyumba yathu. Anali wa Mboni za Yehova. Ndinamvetsera zimene ananena ndipo ndinavomera kuti adzabwerenso. Kunabwera amuna aŵiri kudzandiona. Pa zokambirana zathu ndinasungapo zinthu ziŵiri—Paradaiso ndi Ufumu wa Mulungu. Ndinali kuzikumbukira mfundozo mosamalitsa, ndipo pamene miyezi inali kupita, ndinazindikira kuti tsiku lina ndidzafunika kuwongolera zinthu pamaso pa Mulungu ngati ndikufuna kukhala ndi chikumbumtima chabwino ndi kupeza chimwemwe chenicheni.
Kuti tigwirizanitse moyo wathu ndi Mawu a Mulungu, poyamba mnzanga anali kufuna kuti tikwatirane. Kenaka anadzayamba kuyanjana ndi anthu oipa amene anali kutonza Mulungu ndi malamulo ake. Pamene ndinafika kunyumba tsiku lina madzulo mu dzinja, ndinadzidzimuka kwabasi. M’nyumba mwathu munalibe kanthu. Mnzanga anali atachoka, anapita pamodzi ndi mtsikana wathu wa zaka zitatuyo. Kwa masiku angapo ndinali kuyembekeza kuti abwerako—koma ayi ndithu. M’malo moti ndiimbe Mulungu mlandu, ndinamupempha kuti andithandize.
Patapita nthaŵi yochepa, ndinatenga Baibulo, n’kukhala patsinde la mtengo wanga wa nkhuyu, ndi kuyamba kuŵerenga. Kwenikweni, ndinamwerera mawu ake. Ngakhale kuti ndinali nditaŵerenga mabuku amtundu uliwonse olembedwa ndi akatswiri a anthu osokonezeka maganizo komanso akatswiri a zamaganizo ndi chikhalidwe, ndinali ndisanapezepo nzeru zotero. Buku limeneli liyenera kuti linauziridwa ndi Mulungu. Ndinadabwa ndi chiphunzitso cha Yesu ndi mmene anali kumvetsetsera chibadwa cha munthu. Masalmo ananditothoza ndipo Miyambo inandichititsa chidwi ndi nzeru zake zothandiza. Mwamsanga ndinazindikira kuti pamene kuli kwakuti chilengedwe chingakokere bwino kwambiri munthu kwa Mulungu, chingangovumbula kokha “malekezero a njira zake.”—Yobu 26:14.
Mbonizo zinandisiyiranso mabuku akuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe.a Ndinatsegulidwa maso powaŵerenga. Buku la Coonadi linandithandiza kuzindikira chifukwa chake dziko likuipitsidwa, chifukwa chake kuli nkhondo, kuwonjezereka kwa chiwawa, ndi chiopsezo cha kupululuka ndi nyukiliya. Ndipo monga momwe thambo lofiira limene ndinali kuona ndili m’munda mwanga linali kusonyeza kuti tsiku lotsatira kudzacha bwino, zochitika zimenezinso zinasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Ndipo ponena za buku la Moyo wa Banja, ndinali kulakalaka kuti ndikanamusonyeza mnzanga ndi kumuuza kuti tingakhale achimwemwe mwa kugwiritsa ntchito malangizo a Baibulo. Koma zinali zosathekanso.
Kupita Patsogolo Mwauzimu
Ndinafuna kudziŵa zambiri, motero ndinauza Robert, wa Mboni, kuti adzandichezere. Ndinamudabwitsa kwambiri pomuuza kuti ndinali kufuna kubatizidwa, chotero tinayamba phunziro la Baibulo. Mwamsanga ndinayamba kulankhula ndi ena za zimene ndinali kuphunzira, ndi kumagaŵira mabuku amene ndinali kuombola ku Nyumba ya Ufumu.
Kuti ndizitha kudzithandiza, ndinalembetsa kosi ya zomangamanga. Pozindikira ubwino umene Mawu a Mulungu angachitire munthu, ndinagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti ndilalikire mwamwayi kwa ophunzira anzanga ndi aphunzitsi. Tsiku lina madzulo, ndinakumana ndi Serge mu likole. Ananyamula magazini. “Ndikuona kuti umakonda kuŵerenga,” ndinatero. “Inde, koma aŵa ndatopa nawo.” “Kodi ukufuna utaŵerenga ena amene alidi abwino?” Ndinamufunsa motero. Tinakambirana bwino kwambiri za Ufumu wa Mulungu, pambuyo pake anatenga mabuku ena okamba za mu Baibulo. Mlungu wotsatira tinapitira limodzi ku Nyumba ya Ufumu, ndipo anayamba kuphunzira Baibulo.
Tsiku lina ndinafunsa Robert ngati ndingalalikire nawo kunyumba ndi nyumba. Anatsegula mmene amaikamo zovala zake ndi kunditengeramo suti. Lamlungu lotsatira, kwanthaŵi yoyamba ndinatsagana naye mu utumiki. Potsirizira pake, pa March 7, 1981, ndinasonyeza poyera kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa kubatizidwa.
Kuthandizidwa Nditavutika Maganizo
Zili choncho ndinali nditadziŵa kumene Amandine ndi amayi ake anali kukhala. Wogo! Amayi ake—ndi mphamvu za lamulo, mogwirizana ndi malamulo a dziko limene anali kukhala—anandiletsa kupita kukaona mwana wanga. Ndinalefulidwa. Mayi ake a Amandine anakwatiwa, ndipo kusautsidwa mtima kwanga kunafika pachimake pamene ndinalandira kalata yochokera ku boma kundidziŵitsa kuti mwamunayo anatenga mwana wangayo kuti akhale mwana wake—zomwe ine sindinagwirizane nazo m’pang’onong’ono pomwe. Ndinalibe mphamvu iliyonse pa mwana wanga tsopano. Mosasamala kanthu kuti ndinayesa kugwiritsa ntchito lamulo, sindinathe kupeza chilolezo chilichonse choti ndikamuone. Ndinali kumva ngati kuti ndanyamula chinthu kumsana cholemera makilogalamu 50, ndimo mmene ululu wanga unalili.
Koma Mawu a Yehova anandichirikiza m’njira zambiri. Tsiku lina pamene ndinavutika maganizo kwambiri, ndinanena mobwerezabwereza mawu a pa Miyambo 24:10: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Vesili linandithandiza kuti ndisathyoke m’nkhongono. Panthaŵi ina, nditakanizidwa kukaona mwana wanga, ndinapita mu utumiki ndipo ndinagwira zolimba monga momwe ndikanathera chikwewe cha chikwama changa cha mabuku. Mwa nthaŵi zovuta zimenezo, ndinatha kuzindikira choonadi cha mawu a Salmo 126:6, amene amati: “Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbewu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.” Phunziro lofunika kwambiri limene ndinaphunzira ndi lakuti pamene ukumana ndi ziyeso zikuluzikulu, ukachita zonse zimene ungathe kuti uzithetse, uziike kumbuyo kwako ndi kupitiriza kutumikira Yehova motsimikiza mtima. Ndiyo njira yokha yokhalirabe wachimwemwe.
Kukalimira Chinachake Chabwinopo
Poona mmene ndinasinthira, makolo anga okondedwawo anadzipereka kuti andithandize kuti ndipitirize maphunziro anga ku yunivesite. Ndinawathokoza, koma tsopano ndinali ndi cholinga china. Choonadi chinali chitandimasula ku filosofi ya anthu, kukhulupirira zinsinsi, ndi kupenda nyenyezi. Tsopano ndinali ndi mabwenzi enieni amene sakanaphana m’nkhondo. Ndipo tsopano ndinali nditapeza mayankho a mafunso anga onena chifukwa chake pali mavuto ambiri padziko lapansi. Ndinafuna kutumikira Mulungu ndi mphamvu zanga zonse posonyeza kuyamikira. Yesu anadzipereka kotheratu pa utumiki wake, ndipo ndinafuna kutsatira chitsanzo chake.
Mu 1983, ndinasiya ntchito yanga ya zomangamanga ndi kukhala mtumiki wa nthaŵi zonse. Poyankhidwa mapemphero anga, ndinapeza ntchito yaganyu mu paki kuti ndizidzithandiza. Zinalidi zosangalatsa kwambiri kupezeka pa sukulu ya apainiya pamodzi ndi Serge, mnyamata amene ndinamuchitira umboni kusukulu ya zomangamanga kuja! Nditachita upainiya wokhazikika kwa zaka zitatu, ndinali ndi chikhumbo chochita zowonjezerekabe mu utumiki wa Yehova. Motero mu 1986, ndinaikidwa kukhala mpainiya wapadera ku tauni yosangalatsa ya Provins, kufupi ndi Paris. Nthaŵi zambiri, nditafika kunyumba madzulo, ndinali kugwada n’kupemphera, kuyamika Yehova chifukwa cha tsiku labwino limene ndinatha kulankhula ndi anthu ena za iyeyo. Kwenikweni, zinthu ziŵiri zimene ndimasangalala nazo kwambiri pamoyo ndizo kulankhula ndi Mulungu ndi kulankhula za Mulungu.
China chimene chinandisangalatsanso kwambiri chinali kubatizidwa kwa amayi anga azaka 68 amene anali kukhala ku Cébazan, kamudzi kena kakang’ono kummwera kwa France. Pamene mayi anga anayamba kuŵerenga Baibulo, ndinawatumizira masabusikiripishoni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anali munthu woganiza, ndipo mosakhalitsa anazindikira kuti munali choonadi mu zimene anali kuŵerenga.
Beteli—Paradaiso Wauzimu Wochititsa Chidwi
Pamene Watch Tower Society inaganiza zochepetsa nambala ya apainiya apadera, ndinafunsira Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndiponso kukatumikira pa Beteli, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku France. Ndinafuna kumusiyira Yehova kuti asankhe njira imene ndingamutumikire nayo bwino kwambiri. Patapita miyezi yoŵerengeka, mu December 1989, ndinaitanidwa ku Beteli ku Louviers, kumpoto cha kumadzulo kwa France. Izi zinali zabwino kwambiri, popeza kuti malowo ananditheketsa kuthandiza mchimwene wanga ndi mulamu wanga kusamalira makolo anga pamene anadwala. Sindikanatha kuchita zimenezi ndikanakhala kuti ndinali mu utumiki wa umishonale kutali kwambiri.
Amayi anga ankabwera kudzandiona pa Beteli nthaŵi zochuluka. Ngakhale kuti anali kupirira kuti azikhala kutali ndi ine, kaŵirikaŵiri anali kundiuza kuti: “Khala pa Beteli Mwana wanga. Ndili wokondwa kuti ukutumikira Yehova moteremu.” Mwachisoni, makolo anga onse aŵiri tsopano anamwalira. Mmene ndikulakalakira kudzawaonanso m’dziko losandutsidwa paradaiso weniweni!
Ndimakhulupiriradi kuti ngati pali nyumba imene imayenera kunenedwa kuti “Paradaiso Tsopano,” ndiye ndi Beteli—“Nyumba ya Mulungu”—chifukwa paradaiso weniweni, m’chenicheni, ndi wauzimu, ndipo pali mkhalidwe wauzimu waukulu pa Beteli. Tili ndi mwayi wokulitsa zipatso za mzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Chakudya chauzimu chokwana bwino chimene timalandira pokambirana lemba la Baibulo tsiku lililonse ndiponso pa phunziro la banja la Nsanja ya Olonda chimandilimbikitsa pa utumiki wa pa Beteli. Ndiponso, kuyanjana ndi abale ndi alongo amene amalingalira zinthu zauzimu amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka makumi ambiri kumapangitsa Beteli kukhala malo apadera amene munthu ungakulirepo mwauzimu. Ngakhale kuti tsopano sindinaonane ndi mwana wanga kwa zaka 17, ndapeza achinyamata achangu ambiri pa Beteli, amene ndimawatenga ngati ana anga, ndi amene amandisangalatsa chifukwa cha kupita kwawo patsogolo mwauzimu. M’zaka zisanu ndi zitatu zapitazi, ndagwirapo ntchito zamitundu isanu ndi iŵiri. Pamene kuli kwakuti kusinthasintha kumeneku sikunali kwapafupi, maphunziro otereŵa ndi opindulitsa m’kupita kwanthaŵi.
Ndinali kulima mtundu winawake wa nyemba umene umabereka nyemba makumi khumi. Mofananamo, ndapeza kuti pamene ufesa chimene chili choipa, umakolola choipa kuŵirikiza makumi khumi—ndipo sututa ulendo umodzi wokha. Zokuchitikira pamoyo ndiyo sukulu imene ili ndi maphunziro odula kwambiri. Ndikanakonda kusalembetsa m’sukulu imeneyo koma m’malo mwake, kuleredwa m’njira za Yehova. Ulidi mwayi waukulu kwa achinyamata amene amaleredwa ndi makolo achikristu! Mosakayikira, ndi bwino kufesa zimene zili zabwino mu utumiki wa Yehova ndi kututa mtendere ndi kukhutiritsidwa maganizo kuŵirikiza makumi khumi.—Agalatiya 6:7, 8.
Pamene ndinali mpainiya, nthaŵi zina ndinali kudutsa pa nyumba yogulitsiramo mabuku achipembedzo imene tinalemba mawu amene zigandanga zimadzichemerera nawo. Ndinaloŵamonso mkati mwake ndi kulankhulana ndi mwiniwakeyo za Mulungu wamoyo ndi chifuno chake. Inde, Mulungu ndi wamoyo! Ndiponso, Yehova, Mulungu woona yekha, ndi Atate wokhulupirika, amene sasiya ana ake. (Chivumbulutso 15:4) Khamu lowonjezereka la anthu a mitundu yonse lipezetu paradaiso wauzimu tsopanoli—ndiponso Paradaiso wobwezeretsedwa amene akudza—mwa kutumikira ndi kutamanda Mulungu wamoyo, Yehova!
[Mawu a M’munsi]
a Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Zithunzi patsamba 26]
Nditasonkhezeredwa ndi kudabwitsa kwa chilengedwe, ndinaganiza zokhulupirira Mulungu (Kumanja) Pa utumiki wa pa Beteli lerolino