Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 4/15 tsamba 15-17
  • Kodi Mumayamikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayamikira?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amayamikira
  • Yesu​—Munthu Woyamikira Kwambiri
  • Mzimu wa Satana Wopeza Ena Zifukwa
  • Tsanzirani Mulungu ndi Kristu
  • “Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Yehova Ndi Mulungu Woyamikira
    Nsanja ya Olonda—2007
  • ‘Khalani Oyamikira’
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu Ndi Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 4/15 tsamba 15-17

Kodi Mumayamikira?

Nthaŵi inayake pa nyumba ya amishonale ina ku West africa, Panali galu wotchedwa Teddy. Teddy amati munthu akamuponyera nyama, amameza nthaŵi yomweyo, osayamba wainunkhiza kaya kuitafuna. Akupuma wefuwefu padzuŵa lotentha, anali kuyembekezera kuti amuponyerenso nyama ina. Nyamayo ikatha, iye anali kuchokapo.

Teddy sanali kusonyeza mpang’ono pomwe kuti anali kuyamikira zimene anali kulandira. Palibenso amene anali kumuyembekezera kuti aziyamikira. Ndi iko komwe, iye anali galu.

PONENA za kuyamikira, nthaŵi zambiri timayembekeza anthu anzathu kuyamikira kwambiri kuposa nyama. Kaŵirikaŵiri timakhumudwa. Anthu ambiri amatsomphola zimene angathe kutsomphola m’moyo ndi kumafunabe zina. Izinso ndi zosadabwitsa. Baibulo linalosera kuti m’masiku otsiriza, anthu adzakhala osayamika.​—2 Timoteo 3:1, 2.

Komabe, atumiki a Mulungu ali ndi mzimu wamtundu wina. Iwo amalabadira uphungu wa mtumwi Paulo amene analangiza okhulupirira anzake kuti: “Khalani akuyamika.”​—Akolose 3:15.

Yehova Amayamikira

Yehova Mulungu amapereka chitsanzo changwiro cha kuyamikira. Talingalirani mmene amaonera atumiki ake okhulupirika. Mouziridwa, Paulo analembera Akristu achihebri kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—Ahebri 6:10.

Pali zitsanzo zambiri za mmene Yehova anayamikirira atumiki ake okhulupirika. Anadalitsa Abrahamu mwa kuchulukitsa mbadwa zake zenizeni, kotero kuti anakhala “monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” (Genesis 22:17) Poyamikira kukhulupirika kwa Yobu pamene anali kuyesedwa, Yehova sanangomubwezera Yobu chuma chake chambiricho komanso anamupatsa ‘mowirikiza.’ (Yobu 42:10) Zochita za Yehova ndi anthu m’zaka zikwi zonsezi zasonyeza kuti mawu aŵa ndi oona: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”​—2 Mbiri 16:9.

Kuti Mulungu amayamikira ndiponso amafunitsitsa kupereka mphotho kwa awo amene amafuna kuchita chifuno chake, ili mbali yaikulu ya umunthu wake. Kuzindikira zimenezi ndi kofunika kwambiri pa chikhulupiriro chachikristu. Paulo analemba kuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumukondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira . . . kuti ali wobwezera mphotho iwo akumufuna Iye.”​—Ahebri 11:6.

Ngati m’malo mwake Yehova anali waukali, wokonda kupeza ena zifukwa, tonsefe tikanaimbidwa mlandu. Wamasalmo anatchula zimenezi kalekale m’mbuyomo kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Yehova amayamikira ena ndipo sawapeza zifukwa. Amawakonda amene akumutumikira. Iye amayamikira.

Yesu​—Munthu Woyamikira Kwambiri

Posonyeza bwino lomwe mikhalidwe ya Atate ake akumwamba, Yesu Kristu anali kuyamikira zinthu zimene anthu ena anachita mwachikhulupiriro. Talingalirani zimene zinachitika nthaŵi ina mu kachisi ku Yerusalemu: “Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zawo mosungiramo ndalama. Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphaŵi alikuika momwemo timakobiri tiŵiri. Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse; pakuti onse ameneŵa anaika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.”​—Luka 21:1-4.

Kutengera pa malingaliro a zandalama, choperekachi chinachepa, makamaka poyerekezera ndi zija za anthu olemera. Anthu ambiri amene analipo sakanamuona mkazi wamasiyeyu. Komatu, Yesu anamuona. Anazindikira mkhalidwe wake. Yesu anamuona ndi kumuyamikira.

Chochitika china chinakhudza mkazi wolemera, Mariya. Pamene Yesu anali kuseyama pa chakudya, mkaziyu anathira mapazi ndi mutu wa Yesu mafuta onunkhira a mtengo wapatali. Ena sanazione bwino zimenezi, akumati mafutawo akanagulitsidwa ndipo ndalama zake zikanathandiza anthu osauka. Kodi Yesu anachitanji? Iye anati: “Mlekeni, mumuvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino. Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomukumbukira nacho.”​—Marko 14:3-6, 9; Yohane 12:3.

Yesu sananene mopserera kuti mafuta a mtengo wapataliwo sanagwiritsidwe ntchito ina. Iye anayamikira kusonyezedwa mowolowa manja kwa chikondi ndi chikhulupiriro cha Mariya. Nkhaniyi inalembedwa m’Baibulo monga chikumbukiro cha ntchito yake yabwino. Nkhani zimenezi ndi zinanso zimasonyeza kuti Yesu anali munthu amene anali kuyamikira ena kwambiri.

Ngati ndinu mtumiki wa Mulungu, mungakhale otsimikiza kuti onse aŵiri Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu amayamikira kwambiri zoyesayesa zanu za kuchirikiza kulambira koyera. Kudziŵa zimenezi kumatikokera kwa iwo ndipo kumatisonkhezera kuwatsanzira mwa kukhala oyamikira.

Mzimu wa Satana Wopeza Ena Zifukwa

Tsopano tiyeni tione chitsanzo cha munthu amene sayamikira​—Satana Mdyerekezi. Kusayamikira kwa Satana ndi kumenenso kunapangitsa kuti atsogolere kupandukira Mulungu kowononga kwambiri.

Atakulitsa mwa iye mwini mzimu wosakhutira ndi zochita za anthu ena, Satana anayamba kuufesa mwa ena. Talingalirani zimene zinachitika m’munda wa Edene. Yehova analenga mwamuna ndi mkazi oyambirira, nawaika m’munda wa paradaiso, ndipo anawauza kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko.” Anawaletsa chinthu chimodzi chokha. Mulungu anati: “Mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”​—Genesis 2:16, 17.

Koma mosapita nthaŵi Satana anati Yehova sananene zoona. Mwa zina, iye anafuna kuti Hava asayamikire Yehova mpang’ono pomwe kotero kuti amupandukire, monga momwe Satana iyeyo anali atachitira. “Ea! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Anafunsa motero Satana. (Genesis 3:1) Mwachionekere zimene anali kutanthauza zinali zakuti Mulungu anali kubisira Hava chinthu chinachake chabwino kwambiri, chinthu chimene chikatsegula maso ake ndi kumupanga kukhala wofanana ndi Mulunguyo. M’malo moyamikira madalitso ochuluka amene Yehova anali atamupatsa, Hava anayamba kulakalaka chimene chinali choletsedwa.​—Genesis 3:5, 6.

Zotsatira zowonongazo zikudziŵika bwino. Ngakhale kuti anapatsidwa dzina lakuti Hava “chifukwa ndiye amake wa amoyo onse,” m’lingaliro lina iye anakhala mayi wa aliyense womafa. Anthu onse alandira uchimo umene umabweretsa imfa kuchokera kwa Adamu.​—Genesis 3:20; Aroma 5:12.

Tsanzirani Mulungu ndi Kristu

Taonani kusiyana kwa Satana ndi Yesu. Satana akufotokozedwa kukhala “wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.” (Chivumbulutso 12:10) Pamene Yesu “akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.”​—Ahebri 7:25.

Satana amaneneza atumiki a Mulungu. Yesu amawayamikira ndipo amawapembedzera. Monga otsanza Kristu, Akristu ayenera kuyesetsa kupeza zabwino mwa wina ndi mnzake, ndi kumayamikirana ndiponso kuonana kukhala ofunika. Mwa kuchita zimenezi, amasonyeza kuyamikira uyo amene amapereka chitsanzo chapamwamba kwambiri pa kukhala woyamikira, Yehova Mulungu.​—1 Akorinto 11:1.

[Chithunzi patsamba 17]

Yesu anayamikira ntchito yabwino ya Mariya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena