Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 5/1 tsamba 3-4
  • Aliyense Amafuna Ufulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aliyense Amafuna Ufulu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhalabe “Paukapolo”
  • Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Lolani Yehova Kukutsogolerani ku Ufulu Weniweni
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Musaphonye Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 5/1 tsamba 3-4

Aliyense Amafuna Ufulu

“Munthu anabadwa ndi ufulu, koma kulikonse ali paukapolo,” anatero Mfalansa wina wafilosofi JeanJacques Rousseau mu 1762. Kubadwa ndi ufulu. Limenelotu ndi lingaliro losangalatsadi! Koma monga mmene Rousseau anaonera, anthu mamiliyoni m’mbiri yonse sanakhalepo paufulu. M’malo mwake, akhala kwa moyo wawo wonse “paukapolo” chifukwa cha dongosolo limene lawachotsera chimwemwe ndi chikhutiro chawo chonse m’moyo.

ANTHU AMBIRI lerolino akupezabe kuti “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Pofunafuna ulamuliro, amuna ndi akazi ofuna kutchuka amamva pang’ono kapena samva n’komwe chisoni pamene akupondereza ufulu wa ena. Lipoti lina linati “magulu opha anthu anapha anthu 21.” Lipoti lina linanena za “kupha anthu mwachisawawa” pamene asilikali achitetezo ‘anali kupha amayi, ana ndi anthu achikulire opanda chitetezo, kuwadula makosi, kuwombera akaidi wamba m’mutu, ndi kuwononga midzi komanso kuphulitsa mabomba mwachisawawa.’

Ndithudi, n’chifukwa chake anthu akufunitsitsa komanso akumenyera ufulu wothetsa kuponderezedwa! Komabe, chomvetsa chisoni n’chakuti kumenyera ufulu wa anthu ena kumaponderezanso ufulu wa ena. Amuna, akazi, ndi ana osalakwa ndiwo amaphedwa pafupifupi nthaŵi zonse pazochitika zimenezi, ndipo imfa zawo zimaonedwa ngati “zoyenera” mwa kunena kuti anafera chinthu chofunika ndiponso choyenerera kuchifera. Mwachitsanzo, chaka chatha ku Ireland, “omenyera ufulu” anatchera bomba m’galimoto m’tauni yaing’ono ya Omagh ndipo bombalo linapha anthu osalakwa 29 omwe anali pafupi ndi kuvulaza anthu ambirimbiri.

Kukhalabe “Paukapolo”

Pamene kumenyana kwatha, kodi chimachitika n’chiyani? Pamene “omenyera ufulu” apambana nkhondoyo, angapezeko ufulu ndithu. Komano, kodi amakhaladi paufulu? Kodi si zoona kuti ngakhale m’mayiko aufulu kwambiri, anthu adakali “paukapolo” wopweteka kwambiri monga umphaŵi, kupanda ungwiro, kudwala ndi imfa? Kodi munthu anganene bwanji kuti ali paufulu weniweni pamene zinthu zimenezi zikumupatsabe ukapolo?

Mlembi wa Baibulo wakale Mose analongosola bwino moyo mofanana ndi mmene wakhalira kwa anthu ambiri m’mbiri yonse ya anthu ndi mmenenso ulili lerolino. Anati, tingakhale ndi moyo zaka 70 kapena 80, “koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake.” (Salmo 90:10) Kodi zimenezi zidzasintha? Kodi kudzatheka kuti tonsefe tidzakhale ndi moyo wokhutiritsa, opanda kumva zopweteka ndi mantha zimene zimavutitsa anthu ambiri lerolino?

Baibulo limanena kuti inde! Limanena za “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Tiyeni tipende mosamalitsa ufulu umenewu, wonenedwa ndi mtumwi Paulo m’zaka za zana loyamba m’kalata yomwe analembera Akristu a ku Roma. M’kalata imeneyi Paulo momveka bwino anafotokoza mmene aliyense wa ife angapezere “ufulu wa ulemerero” weniweni komanso wosatha.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Kuchokera m’buku lotchedwa Beacon Lights of History, Vol. XIII

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena