Khalani Atcheru Ndipo Chitani Khama!
“Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.”—MATEYU 25:13.
1. Kodi mtumwi Yohane anali kuyembekeza chiyani?
M’NKHANI yomaliza yokambirana m’Baibulo, Yesu analonjeza kuti: “Ndidza msanga.” Mtumwi wake Yohane anayankha kuti: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.” Mtumwiyo sanakayikire zoti Yesu akudza. Yohane anali mmodzi mwa atumwi amene anafunsa Yesu kuti: “Zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] [Chigiriki, pa·rou·siʹa] kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Inde, Yohane motsimikiza mtima anali kuyembekeza kukhalapo kwa Yesu kwam’tsogolo.—Chivumbulutso 22:20; Mateyu 24:3.
2. Ponena za kukhalapo kwa Yesu, kodi zinthu zili motani m’matchalitchi?
2 Kutsimikiza mtima koteroko n’kosoŵa masiku ano. Matchalitchi ambiri ali ndi chiphunzitso chonena za “kudza” kwa Yesu, koma m’matchalitchiwo anthu ochepa okha ndi amene amakuyembekezeradi. Moyo wawo amakhalanso mosonyeza zimenezo. Buku lakuti The Parousia in the New Testament (Parousia m’Chipangano Chatsopano) limati: “Pali kugwirizana kochepa kwambiri pakati pa chiyembekezo cha Parousia ndi moyo, maganizo ndi ntchito ya tchalitchi. . . . Changu chachikulu chimene tchalitchi chiyenera kukhala nacho pantchito yothandiza anthu kulapa ndi umishonale wolengeza uthenga wabwino, chikuchepa mwinanso chinatheratu.” Koma osati kwa aliyense!
3. (a) Kodi Akristu oona amamva bwanji ponena za pa·rou·siʹa? (b) N’chiyani kwenikweni chimene tidzakambirana tsopano?
3 Ophunzira oona a Yesu akudikira mwachidwi chimaliziro cha dongosolo loipa lilipoli. Pochita zimenezo mokhulupirika, tiyenera kukhala ndi malingaliro oyenera ponena za zonse zokhudzana ndi kukhalapo kwa Yesu ndi kuchita zinthu moyenerera. Zimenezo zidzatipangitsa ‘kulimbika chilimbikire kufikira chimaliziro ndi kupulumuka.’ (Mateyu 24:13) Popereka ulosi wopezeka pa Mateyu chaputala 24 ndi 25, Yesu anapereka uphungu wanzeru umene tingatsatire, ndi kupeza phindu lokhalitsa. Chaputala 25 chili ndi mafanizo amene muyenera kuti mumawadziŵa, kuphatikizapo lija la anamwali khumi (anamwali ochenjera ndi opusa) ndi fanizo la ndalama za matalente. (Mateyu 25:1-30) Kodi tingapindule nawo motani mafanizo ameneŵa?
Khalani Atcheru, Monga Analili Anamwali Asanu!
4. Kodi nkhani ya m’fanizo la anamwali n’njotani?
4 Mwina mungafune kuŵerenganso fanizo la anamwaliwo, lopezeka pa Mateyu 25:1-13. Nkhaniyo yazikidwa pa ukwati waukulu ndiponso wokongola wachiyuda umene mkwati amapita kunyumba ya mkwatibwi kuti apite naye kunyumba kwa mkwatiyo (kapena kunyumba kwa atate wake). Mwambo umenewu ungaphatikizepo oimba, ndipo nthaŵi ya kufika kwake ingakhale yosadziŵika kwenikweni. M’fanizolo, anamwali khumi anadikira mpaka usiku kuti mkwati afike. Asanu mopusa sanabwere ndi mafuta a nyali okwanira choncho anayenera kubwerera kukagula ena. Asanu enawo mwanzeru anabwera ndi mafuta ena m’zotengera kuti adzadzitse nyali zawo zikafuna mafuta ena podikira. Ndi asanu okhaŵa amene analipo komanso amene anali okonzeka mkwati atafika. Choncho okhaŵa ndiwo analoledwa kuloŵa m’phwandolo. Pamene anamwali asanu opusa anabwera sanaloŵe chifukwa anachedwa.
5. Kodi ndi malemba ati amene akumveketsa tanthauzo lophiphiritsira la fanizo la anamwali?
5 Mbali zambiri za fanizoli zingatengedwe kukhala zophiphiritsira. Mwachitsanzo, Malemba amatchula Yesu monga mkwati. (Yohane 3:28-30) Yesu anadziyerekezera ndi mwana wa mfumu amene wakonzedwera phwando laukwati. (Mateyu 22:1-14) Ndipo Baibulo limayerekezera Kristu ndi mwamuna wokwatira. (Aefeso 5:23) Chochititsa chidwi n’chakuti pamene kuli kwakuti Akristu odzozedwa penapake akunenedwa kukhala “mkwatibwi” wa Kristu, fanizolo silikutchulapo mkwatibwi. (Yohane 3:29; Chivumbulutso 19:7; 21:2, 9) Komano likutchula za anamwali khumi, ndipo penapake odzozedwa akuyerekezedwa ndi namwali wotomeredwa ndi Kristu.—2 Akorinto 11:2.a
6. Kodi Yesu anapereka chilimbikitso chotani pomaliza fanizo la anamwali?
6 Kuphatikiza pa mfundo zimenezi ndi matanthauzo alionse aulosi, ndithudi pali mfundo zabwino zimene tingaphunzire m’fanizo limeneli. Mwachitsanzo, onani kuti Yesu anamaliza fanizoli ndi mawu akuti: “Chifukwa chake dikirani [nthaŵi zonse, NW], pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.” Choncho fanizolo likusonyeza kufunika kwa aliyense wa ife kukhala tcheru, kudikira chimaliziro chikudzacho cha dongosolo loipali. Chimaliziro chimenechi chikudzadi mosakayikira, ngakhale kuti sitingadziŵe tsiku lake lenileni. Pamenepa, taonani maganizo amene magulu aŵiri a anamwali ameneŵa anasonyeza.
7. Chifukwa chiyani anamwali asanu a m’fanizolo anali opusa?
7 Yesu anati: “Asanu a iwo anali opusa.” Kodi chinali chifukwa chakuti sanali kukhulupirira kuti mkwatibwi akubwera? Kodi iwo anali kwina kokasangalala? Kapena kodi ananamizidwa? Iyayi. Yesu ananena kuti asanu ameneŵa ‘anatuluka kukakomana ndi mkwati.’ Iwo anadziŵa kuti akubwera, ndipo anafuna kukhalapo, ngakhale kutengamo mbali mu “phwando la ukwati.” Koma kodi anakonzekera mokwanira? Anam’dikira pang’ono, mpaka “pakati pa usiku,” koma anali osakonzeka kum’landira nthaŵi ina iliyonse—kaya mwamsanga kapena mochedwa mosiyana ndi mmene anaganizira poyamba.
8. Kodi anamwali asanu a m’fanizolo anasonyeza motani kuti anali ochenjera?
8 Asanu enawo—amene Yesu anawatcha ochenjera—nawonso anatuluka ndi nyali zoyaka, kudikira kufika kwa mkwati. Iwonso anayenera kudikira, koma anali “ochenjera.” Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “ochenjera” lingatanthauze kukhala “wanzeru, watcheru, waluntha.” Asanuŵa anasonyeza kuti ndi ochenjera mwa kubwera ndi mafuta ena m’zotengera oti adzadzitse nyali zawo ngati zingafunikire mafuta ena. Ndipo anasumika maganizo awo pa kulandira mkwati moti anakana kupatsako ena mafuta awo. Kukhala tcheru motero sikunali kopambanitsa, chifukwa pamene mkwati anafika, iwo analipo ndipo anali okonzeka mokwanira. “Okonzekawo analoŵa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.”
9, 10. Kodi mfundo ya fanizo la anamwali ndi yotani, ndipo ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa?
9 Yesu sanali kuphunzitsa za khalidwe labwino la paukwati, ndipo sanalinso kulangiza za kugaŵana zinthu ndi ena. Mfundo yake inali yakuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.” Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndilidi watcheru ndi kukhalapo kwa Yesu?’ Timakhulupirira kuti Yesu tsopano akulamulira kumwamba, koma kodi tikusumikadi malingaliro athu pa choonadi chakuti ‘Mwana wa munthu adzadza pamitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu’? (Mateyu 24:30) Podzafika “pakati pa usiku,” kufika kwa mkwati kunalidi pafupi kwambiri kuposa nthaŵi imene anamwaliwo anali atangopita kumene kukakomana naye. Momwemonso, kufika kwa Mwana wa munthu podzawononga dongosolo loipa lilipoli kuli pafupi kwambiri kuposa pamene tinayamba kudikira kubwera kwake. (Aroma 13:11-14) Kodi ndifebe atcheru nthaŵi zonse, atcheru kwambiri makamaka pamene nthaŵiyo ikuyandikira?
10 Kumvera lamulo lakuti “dikirani nthaŵi zonse” kumafuna kukhala tcheru nthaŵi zonse. Anamwali asanu anadikira mafuta awo kutha napita kukagulanso ena. Mofananamo Mkristu lerolino angadodometsedwe ndi zina n’kusakhala wokonzekera mokwanira kubwera kwa Yesu kumene kuli pafupiku. Akristu ena a m’zaka za zana loyamba zinawachitikira. Zingachitikirenso ena lerolino. Choncho tiyeni tidzifunse kuti, ‘Kodi zikundichitikira?’—1 Atesalonika 5:6-8; Ahebri 2:1; 3:12; 12:3; Chivumbulutso 16:15.
Chitani Khama Pamene Chimaliziro Chikuyandikira
11. Kodi fanizo la Yesu lotsatira linali lotani, ndipo linali lofanana ndi chiyani?
11 M’fanizo lake lotsatira, Yesu sanauze otsatira ake kungokhala atcheru basi. Atawauza za anamwali ochenjera ndi opusa, iye anasimba fanizo la ndalama za matalente. (Ŵerengani Mateyu 25:14-30) Mbali zambiri za fanizo limeneli zikufanana ndi za m’fanizo lake loyamba la ndalama, limene Yesu ananena chifukwa chakuti ambiri “anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.”—Luka 19:11-27.
12. Kodi nkhani ya m’fanizo la ndalama za matalente n’njotani?
12 M’fanizo la ndalama za matalente, Yesu ananena za mwamuna amene, asananyamuke kupita kudziko lakutali, anaitana akapolo atatu. Kapolo mmodzi anam’patsa ndalama zisanu za matalente, wina ziŵiri, ndi winanso ndalama imodzi yokha—“kwa iwo onse monga nzeru zawo.” Ndalama imeneyi iyenera kuti inali talente la siliva, malipiro ololedwa mwalamulo panthaŵiyo amene wantchito ankalandira pazaka 14—ndalama zambiri zedi! Mwamunayo atabwerako, anaitana akapolowo kuti anene zimene anachita pa “nthaŵi yaikulu” imene iye anali atachoka. Akapolo aŵiri oyambirira anaŵirikiza kaŵiri ndalama zimene anasungizidwa. Iye anawayamikira kuti “chabwino,” ndipo analonjeza aliyense wa iwo udindo wowojezereka, nati: ‘Loŵani m’chikondwero cha mbuye wanu.’ Kapolo wa ndalama imodzi ya matalente sanaigwiritse ntchito kuti apeze nayo phindu, akumati mbuye wake anali wovuta kwambiri. Iye anaibisa ndalamayo, osaiikiza ngakhale kwa okongola ndalama kuti ichuluke. Mbuye wake anamutcha “woipa ndi waulesi” chifukwa anachita zinthu motsutsana ndi zofuna zake. Chotero, analandidwa ndalamayo, naponyedwa kunja “kumene [kunali] kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
13. Kodi Yesu anakhala motani ngati mbuye wa m’fanizoli?
13 Pamenepanso, mfundo za fanizoli n’zophiphiritsira. Mwachitsanzo, Yesu, amene mwamuna wopita kudziko lakutaliyo akuimira, anali kudzasiya ophunzira ake, ndi kupita kumwamba, ndi kudikira nthaŵi yaitali kufikira atalandira mphamvu ya ufumu.b (Salmo 110:1-4; Machitidwe 2:34-36; Aroma 8:34; Ahebri 10:12, 13) Komanso, titha kuona phunziro lalikulu kapena pulinsipulo limene tonsefe tiyenera kugwiritsa ntchito m’miyoyo yathu. Kodi ndi pulinsipulo lotani limenelo?
14. Kodi fanizo la ndalama za matalente limagogomeza kuti chofunika kwambiri n’chiyani?
14 Kaya tili ndi chiyembekezo cha moyo wosakhoza kufa kumwamba kapena cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso, n’zoonekeratu m’fanizo la Yesu kuti tiyenera kulimbikira m’ntchito zachikristu. Ndiponso tanthauzo la fanizo limeneli lingafotokozedwe ndi liwu limodzi: khama. Atumwi anapereka chitsanzo kuyambira pa Pentekoste wa mu 33 C.E. kupita m’tsogolo. Timaŵerenga kuti: “Ndi mawu ena ambiri [Petro] anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.” (Machitidwe 2:40-42) Ndipo zotsatira za kuyesayesa kwake zinali zabwino bwanji! Pamene ena anatsatira atumwi m’ntchito yachikristu yolalikira, iwonso anakhala akhama, ndipo uthenga wabwino ‘unakula m’dziko lonse lapansi.’—Akolose 1:3-6, 23; 1 Akorinto 3:5-9.
15. Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito motani mfundo yaikulu ya fanizo la ndalama za matalente?
15 Kumbukirani nkhani yaikulu ya fanizo limeneli—ulosi wonena za kukhalapo kwa Yesu. Tili ndi umboni wochuluka wosonyeza kuti pa·rou·siʹa ya Yesu ikuchitika panopo ndipo idzafika pachimake posachedwapa. Kumbukirani mmene Yesu anagwirizanitsira “chimaliziro” ndi ntchito imene Akristu ayenera kuichita: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Poganizira zimenezi, kodi tikufanana ndi kapolo uti? Dzifunseni kuti: ‘Kodi pangakhale chifukwa chonenera kuti ndili ngati kapolo amene anabisa zimene zinaikizidwa kwa iye, mwina posamalira zinthu zaumwini? Kapena kodi n’zoonekeratu kuti ndili ngati aja amene anali abwino ndi okhulupirika? Kodi ndine wotsimikiza mtimadi kuŵirikiza zofuna za Ambuye panthaŵi iliyonse?’
Atcheru ndi Akhama pa Kukhalapo Kwake
16. Kodi mafanizo aŵiri amene takambirana ali ndi uthenga wanji kwa inu?
16 Inde, kuphatikiza pa matanthauzo ake ophiriphiritsira ndi aulosi, mafanizo aŵiri ameneŵa akutipatsa chilimbikitso chenicheni chochokera m’kamwa mwa Yesu. Uthenga wake ndi wakuti: Khalani atcheru; chitani khama, makamaka pamene chizindikiro cha pa·rou·siʹa ya Kristu chikuonekera. Nthaŵiyo ndiyo ino. Choncho kodi tikukhaladi tcheru ndi kuchita khama?
17, 18. Kodi wophunzira Yakobo anapereka uphungu wotani ponena za kukhalapo kwa Yesu?
17 Yakobo, mbale wom’peza wa Yesu, sanali nawo pa Phiri la Azitona pamene Yesu anali kunena ulosi wake; koma anamva za uwo pambuyo pake, ndipo anamvetsa lingaliro lake. Iye analemba kuti: ‘Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya myundo ndi masika. Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Ambuye kuyandikira.’—Yakobo 5:7, 8.
18 Atawatsimikizira kuti Mulungu adzaweruza ndi kulanga awo amene agwiritsa ntchito molakwa chuma chawo, Yakobo analimbikitsa Akristu kuti asataye mtima podikira kuti Yehova achitepo kanthu. Mkristu wosaleza mtima angayambe kumafuna kubwezera zolakwa, ngati kuti iyeyo ndiye amene ayenera kuwongolera zolakwa. Koma zimenezo siziyenera kukhala choncho chifukwa nthaŵi ya chiweruzo idzafikabe. Chitsanzo cha mlimi chimasonyeza zimenezo, monga momwe Yakobo akufotokozera.
19. Kodi mlimi wachiisrayeli anali kusonyeza kuleza mtima motani?
19 Mlimi wachiisrayeli amene anadzala mbewu anayenera, choyamba, kudikira kuti mmera uonekere, kenako kuti chomeracho chikhwime, ndiyeno pomalizira pake kuti akolole. (Luka 8:5-8; Yohane 4:35) M’miyezi imeneyo, panali nthaŵi, mwinanso zinthu zina zodetsadi nkhaŵa. Kodi mvula ya myundo idzagwa mokwanira? Nanga mvula ya masika? Kodi mbewu zingawonongeke ndi tizilombo kapena mphepo ya mkuntho? (Yerekezani ndi Yoweli 1:4; 2:23-25.) Ngakhale zikhale chonchi, mlimi wachiisrayeli anali kudalirabe Yehova ndi nyengo zimene anaika. (Deuteronomo 11:14; Yeremiya 5:24) Kuleza mtima kwa mlimiyo kunam’patsadi chiyembekezo chodalirika. Mwachikhulupiriro anali kudziŵa kuti chimene akudikira chidzachitikadi. Ndipo zinali kuchitikadi!
20. Potsatira uphungu wa Yakobo, kodi tingasonyeze motani kuleza mtima?
20 Pamene kuli kwakuti mlimi angadziŵe nthaŵi imene adzakolole, Akristu a m’zaka za zana loyamba sanaŵerengere masiku kuti adziŵe nthaŵi ya kukhalapo kwa Yesu. Koma nthaŵiyo inali kudzafikabe. Yakobo analemba kuti: “Kukhalapo [Chigiriki, pa·rou·siʹa] kwake kwa Ambuye kuyandikira.” Panthaŵi imene Yakobo analemba mawu ameneŵa, chizindikiro chachikulu, kapena kuti cha padziko lonse cha kukhalapo kwa Kristu chinali chisanaoneke. Koma lero chikuoneka! Chotero kodi tiyenera kumva bwanji m’nthaŵi ino? Chizindikiro chimenecho chilipo. Tikuchiona. Motsimikiza tinganene kuti ‘Ndikuona chizindikiro chikukwaniritsidwa.’ Motsimikiza mtima tinganene kuti, ‘Kukhalapo kwake kwa Ambuye kunayamba, ndipo kuli pafupi kufika pachimake.’
21. Kodi ndife otsimikiza mtima kuchita chiyani?
21 Popeza kuti zinthu zili choncho, tili ndi chifukwa chachikulu zedi chomvera ndi kutsatira maphunziro aakulu a m’mafanizo aŵiri a Yesu amene takambiranawo. Iye anati: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.” (Mateyu 25:13) Mosakayikira ino ndiyo nthaŵi yoti tikhale achangu mu utumiki wathu wachikristu. Masiku onse tiyeni tisonyeze m’moyo wathu kuti tikumvetsa mfundo ya Yesu. Tiyeni tikhale atcheru! Tiyeni tichite khama!
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mukufuna kudziŵa zambiri ponena za mfundo zophiphiritsira za fanizoli, onani buku lakuti God’s Kingdom of a Thousand Years Has Approached, masamba 169-211, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Onani buku lakuti God’s Kingdom of a Thousand Years Has Approached, masamba 212-56.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi mwatengapo mfundo yaikulu yotani pa fanizo la anamwali ochenjera ndi opusa?
◻ Mwa fanizo la ndalama za matalente, kodi ndi uphungu waukulu wotani umene Yesu akukupatsani?
◻ Kodi kuleza mtima kwanu ponena za pa·rou·siʹa kukufanana motani ndi kuleza mtima kwa mlimi wachiisrayeli?
◻ N’chifukwa chiyani ino ili nthaŵi yosangalatsa kwambiri komanso yovuta kukhalamo?
[Zithunzi patsamba 23]
Kodi mukuphunzirapo chiyani pa fanizo la anamwali ndi fanizo la ndalama za matalente?