Ndife Okondwa Kuti Yehova Amatisonyeza Njira Yake
“Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mawu a Yehova anayesedwa.”—2 SAMUELI 22:31.
1, 2. (a) Kodi anthu onse mwachibadwa amafuna chiyani? (b) Kodi tingachite bwino kutsanzira chitsanzo chayani?
ANTHU onse amafuna chitsogozo mwachibadwa. Ndithudi, timafuna kutsogozedwa m’moyo wonse. Zoonadi, Yehova anatipatsa nzeru ndi chikumbumtima pamlingo winawake kuti zitithandize kuzindikira chabwino ndi choipa. Koma kuti chikumbumtima chathu chikhale chitsogozo chodalirika, icho chiyenera kuphunzitsidwa. (Ahebri 5:14) Ndipo malingaliro athu amafunikira chidziŵitso cholondola—limodzinso ndi kuwaphunzitsa kupenda chidziŵitso chimenecho—kuti tithe kusankha zochita zabwino. (Miyambo 2:1-5) Ngakhale titatero, chifukwa cha kusinthasintha kwa zinthu m’moyo, zosankha zathu zingalephere kukhala mmene tinafunira. (Mlaliki 9:11) Mwa ife tokha, tilibe njira yotsimikizirika yodziŵira zimene zidzatichitikira m’tsogolo.
2 Pachifukwa chimenechi ndi zifukwanso zina zambiri, mneneri Yeremiya analemba kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Yesu Kristu, munthu wamkulu woposa onse amene akhalapo ndi moyo, analandira chitsogozo. Iye anati: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu payekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.” (Yohane 5:19) Choncho, n’kwanzerutu kwambiri kutsanzira Yesu ndi kuyang’ana kwa Yehova kuti atithandize kutsogoza mapazi athu! Mfumu Davide inaimba kuti: “Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mawu a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira iye.” (2 Samueli 22:31) Ngati tikufuna kuyenda m’njira ya Yehova m’malo motsatira nzeru zathu, tidzakhala ndi chitsogozo changwiro. Kukana njira ya Mulungu kumadzetsa tsoka.
Yehova Amasonyeza Njira
3. Kodi Yehova anatsogoza motani Adamu ndi Hava, kuwapatsa tsogolo lotani?
3 Lingalirani za Adamu ndi Hava. Ngakhale kuti iwo analibe uchimo uliwonse, anafunikira chitsogozo. Yehova sanam’siyirire Adamu kuti adziŵe yekha zonse zofunika kuchitidwa m’munda wokongolawo wa Edene. M’malo mwake, Mulungu anam’patsa ntchito yoti achite. Choyamba, Adamu anayenera kutcha zinyama mayina. Kenako, Yehova anapatsa Adamu ndi Hava ntchito zofunika kuchitidwa panthaŵi yaitali. Iwo anayenera kugonjetsa dziko lapansi, kulidzaza ndi mbadwa zawo, ndi kusamalira nyama za m’dziko. (Genesis 1:28) Imeneyitu inali ntchito yaikulu, koma pomalizira pake dziko lonse lapansi likanakhala paradaiso wodzaza anthu angwiro okhaokha okhala pamtendere ndi zinyama. Linalitu tsogolo labwino kwambiri! Komanso, pamene Adamu ndi Hava anali kuyenda mokhulupirika m’njira ya Yehova, iwo bwenzi akuyankhulana naye. (Yerekezani ndi Genesis 3:8.) Mwayi waukulu kwambiri umenewo—kukhala paunansi wosatha ndi Mlengi!
4. Kodi Adamu ndi Hava anasonyeza motani kuti si okhulupirika ndipo ndi opanda chikhulupiriro, ndipo zotsatirapo zake zoopsa zinali zotani?
4 Yehova analetsa anthu aŵiri oyamba amenewo kuti asadye za m’mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa umene unali mu Edene, ndipo nthaŵi yomweyo zimenezi zinawapatsa mpata wosonyeza kumvera kwawo—chikhumbo chawo choyenda m’njira ya Yehova. (Genesis 2:17) Komano posapita nthaŵi, kumvera kumeneko kunayesedwa. Pamene Satana anadza ndi mawu ake onyenga, Adamu ndi Hava anafunika kukhulupirika kwa Yehova ndi kukhulupirira malonjezo Ake ngati anafuna kukhalabe omvera. Koma n’zomvetsa chisoni kuti sanakhulupirike ndiponso analibe chikhulupiriro. Satana atauza Hava kuti adzapata ufulu naneneza Yehova kuti n’ngwonama, Hava ananyengedwa ndipo sanamvere Mulungu. Adamu anam’tsatira m’kuchita tchimo. (Genesis 3:1-6; 1 Timoteo 2:14) Zimene anataya chifukwa cha uchimowo zinali zambiri. Kuyenda m’njira ya Yehova kukanawapatsa chimwemwe chowonjezerekawonjezereka popitiriza kuchita chifuniro chake. M’malo mwake, anali kungokumana ndi zokhumudwitsa ndi zopweteka zokhazokha m’moyo wawo kufikira imfa yawo.—Genesis 3:16-19; 5:1-5.
5. Kodi cholinga cha Yehova chotenga nthaŵi yaitali n’chotani, ndipo amathandiza motani anthu okhulupirika kuona kukwaniritsidwa kwake?
5 Koma Yehova sanasinthebe cholinga chake chakuti tsiku lina dziko lapansi lidzakhale mudzi wa paradaiso wa anthu angwiro, opanda uchimo. (Salmo 37:11, 29) Ndipo sanalephere kupereka chitsogozo changwiro kwa awo amene akuyenda m’njira yake namayembekeza kuona lonjezo limenelo litakwaniritsidwa. Kwa ife amene tili ndi makutu akumva, liwu la Yehova lili kumbuyo kwathu, ndipo likuti: “Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo.”—Yesaya 30:21.
Ena Anayenda m’Njira ya Yehova
6. Ndi amuna aŵiri ati a m’nthaŵi zakale amene anayenda m’njira ya Yehova, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
6 Malinga ndi Baibulo, ndi ochepa okha mwa mbadwa za Adamu ndi Hava amene anayenda m’njira ya Yehova. Abele anali woyamba mwa ameneŵa. Ngakhale kuti anamwalira msanga, iye anamwalira ali woyanjidwa ndi Yehova, choncho ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika chodzaukitsidwa pa “kuuka kwa olungama” panthaŵi yoikika ya Mulungu. (Machitidwe 24:15) Iye adzaona cholinga chachikulu cha Yehova cha dziko lapansi ndi mtundu wa anthu chikukwaniritsidwa m’kupita kwa nthaŵi. (Ahebri 11:4) Winanso amene anayenda m’njira ya Yehova anali Enoke, amene ulosi wake wonena za chimaliziro cha dongosolo lino la zinthu ukupezeka m’buku la Yuda. (Yuda 14, 15) Nayenso Enoke sanakhale moyo kwautali womwe akanakhala. (Genesis 5:21-24) Komabe, “anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu.” (Ahebri 11:5) Atamwalira, iye, monga Abele, anali ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kuukitsidwa ndipo adzakhala mmodzi mwa amene adzaona zolinga za Yehova zikukwaniritsidwa.
7. Kodi Nowa ndi banja lake anasonyeza motani kukhulupirika kwa Yehova ndi kumukhulupirira?
7 Pamene dziko linali kuloŵerera m’zoipa Chigumula chisanachitike, kumvera Yehova mowonjezeka kunali kukhala chiyeso cha kukhulupirika. Dzikolo litatsala pang’ono kutha, ndi kagulu kamodzi kokha komwe kanapezeka kuti kakuyenda m’njira ya Yehova. Nowa ndi banja lake anali kumvetsera kwa Mulungu ndi kukhulupirira zonena zake. Mokhulupirika, anamaliza ntchito zimene anapatsidwa nakana kuloŵa m’zochitika zoipa za m’dziko la m’masikuwo. (Genesis 6:5-7, 13-16; Ahebri 11:7; 2 Petro 2:5) Tingathokoze kumvera kwawo kokhulupirika ndi kwachikhulupiriro. Chifukwa cha kumvera kumeneko, iwo anapulumuka Chigumula ndi kukhala makolo athu.—Genesis 6:22; 1 Petro 3:20.
8. Kwa mtundu wa Israyeli, kodi kuyenda m’njira ya Mulungu kunaphatikizapo chiyani?
8 M’kupita kwa nthaŵi, Yehova anachita pangano ndi mbadwa za Yakobo wokhulupirikayo, ndipo iwo anakhala mtundu wake wapadera. (Eksodo 19:5, 6) Kudzera mwa Chilamulo cholembedwa, unsembe, ndi maulosi otsogoza a nthaŵi ndi nthaŵi, Yehova anapereka chitsogozo kwa anthu ake a panganowo. Koma zinali kwa Aisrayeli kutsatira chitsogozo chimenecho. Yehova anauza mneneri wake kuti auze Aisrayeli kuti: “Taonani, ndili kuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero; dalitso ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lerolino; koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m’njira ndikuuzani lerolino, kutsata milungu ina imene simunaidziŵa.”—Deuteronomo 11:26-28.
Chifukwa Chimene Ena Anachokera Panjira ya Yehova
9, 10. Kodi Aisrayeli anafunikira kukulitsa kukhulupirira Yehova chifukwa cha mkhalidwe wotani?
9 Mofanana ndi Adamu ndi Hava, Aisrayeli anafunikira kukhulupirira Yehova ndi kukhala okhulupirika kwa iye ngati anafuna kukhalabe omvera. Israyeli unali mtundu waung’ono wozingidwa ndi anansi audani. Kummwera chakumadzulo kunali Igupto ndi Kusi [Ethiopia]. Kumpoto chakummaŵa kunali Aramu ndi Asuri. Chapafupi nawo panali Filistiya, Amoni, Moabu, ndi Edomu. Panthaŵi zosiyanasiyana, onseŵa anasonyeza udani kwa Israyeli. Ndiponso, onsewo anali ndi zipembedzo zonyenga, zodzaza ndi kulambira mafano, kupenda nyenyezi, ndipo nthaŵi zina madzoma achiwerewere chadzaoneni ndi kupereka ana nsembe mwankhanza. Mitundu yoyandikana ndi Israyeli inkayang’ana kwa milungu yawo kuti iwapatse mabanja aakulu, zokolola zochuluka, ndi chipambano pankhondo.
10 Israyeli yekha ndiye anali kulambira Mulungu mmodzi, Yehova. Iye anawalonjeza kuwadalitsa ndi mabanja aakulu, zokolola zochuluka, ndi chitetezo kwa adani awo ngati atamvera malamulo ake. (Deuteronomo 28:1-14) Mwachisoni, ambiri m’Israyeli analephera kuchita zimenezi. Mwa amene anayenda m’njira ya Yehova, ambiri anasautsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Ena mpaka anazunzidwa, kukwapulidwa, kutonzedwa, kuponyedwa m’ndende, kuponyedwa miyala, ndi kuphedwa ndi Aisrayeli anzawo. (Machitidwe 7:51, 52; Ahebri 11:35-38) Chimenechotu chinali chiyeso chachikulu kwambiri kwa okhulupirika! Koma n’chifukwa chiyani ambiri anachoka panjira ya Yehova? Zitsanzo ziŵiri za m’mbiri ya Israyeli zikutithandiza kuona maganizo awo olakwika.
Chitsanzo Choipa cha Ahazi
11, 12. (a) N’chiyani chimene Ahazi anakana kuchita Aramu atamuopseza? (b) Kodi Ahazi anayembekezera kupeza chitetezo kumagwero aŵiri ati?
11 Ahazi anali kulamulira ufumu wakummwera wa Yuda m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E. Ulamuliro wake sunali wamtendere. Nthaŵi inayake, Aramu ndi ufumu wakumpoto wa Israyeli anagwirizana kuti amenyane naye, ndipo “mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake.” (Yesaya 7:1, 2) Koma pamene Yehova anafuna kum’chirikiza napempha Ahazi kuti am’yese, Ahazi anakana kwamtu wa galu! (Yesaya 7:10-12) Chotsatirapo chake, Yuda anagonja m’nkhondoyo ndipo anthu ake ambiri anavulazidwa ndi kuphedwa.—2 Mbiri 28:1-8.
12 Pamene kuli kwakuti Ahazi anakana kuyesa Yehova, iye analephera kunyada moti anapempha thandizo kwa mfumu ya Asuri. Ngakhale zinali motero, Yuda anasautsidwabe ndi anansi ake. Pamene Asurinso anaukira Ahazi ndi ‘kum’sautsa,’ mfumuyo “[i]naphera nsembe milungu ya Damasiko yom’kantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso.”—2 Mbiri 28:20, 23.
13. Potembenukira kwa milungu ya Aramu, kodi Ahazi anasonyezanji?
13 Panthaŵi inayake, Yehova anadzanena kwa Israyeli kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Potembenukira kwa milungu ya Aramu, Ahazi anasonyeza kuti anali kutali kwambiri ndi ‘kuyenda m’njira yoyenera iye kupitamo.’ Iye anasokera kotheratu ndi maganizo a mitunduyo, kuyang’ana kumagwero awo onyenga a chitetezo m’malo moyang’ana kwa Yehova.
14. N’chifukwa chiyani Ahazi analibe chifukwa chomveka chotembenukira kwa milungu yonama?
14 Kuyambira kalekale, milungu ya mitunduyo, kuphatikizapo Aramu, inasonyezedwa kuti ndi “mafano.” (Yesaya 2:8) Kalelo, mu ulamuliro wa Mfumu Davide, ukulu wa Yehova pa milungu ya Aramu unaonekeratu pamene Aaramu anakhala otumikira Davide. (1 Mbiri 18:5, 6) Yehova yekha, “Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa,” ndiye angapereke chitetezo chenicheni. (Deuteronomo 10:17) Koma Ahazi anafulatira Yehova ndi kuyembekeza kuti milungu ya mitunduyo idzamuteteza. Chotsatirapo chake chinali choopsa kwa Yuda.—2 Mbiri 28:24, 25.
Ayuda ndi Yeremiya ku Igupto
15. Kodi Ayuda a m’tsiku la Yeremiya anachimwa motani ku Igupto?
15 Chifukwa cha kusakhulupirika kwakukulu kwa anthu ake, Yehova analola Ababulo kuwononga Yerusalemu ndi kachisi wake mu 607 B.C.E. Anthu ambiri a mtunduwo anatengedwa ukapolo ku Babulo. Koma ena anatsala, ndipo mmodzi wa iwo anali mneneri Yeremiya. Pamene Nduna Gedaliya inaphedwa, kagulu kameneka kanathaŵira ku Igupto ndipo anathaŵanso ndi Yeremiya yemwe. (2 Mafumu 25:22-26; Yeremiya 43:5-7) Kumeneko, iwo anayamba kupereka nsembe kwa milungu yonama. Yeremiya anawachonderera Ayuda osakhulupirikawo kuti asiye zimenezo, koma anachita mwano. Anakana kutembenukira kwa Yehova nalimbikira kunena kuti adzapitirizabe kufukizira nsembe “mfumu yaikazi ya kumwamba.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti n’zimene iwo ndi makolo awo anali kuchita ‘m’midzi ya Yuda, ndi m’misewu ya Yerusalemu, pamene anali ndi chakudya chokwanira, anali kukhala bwino, osaona choipa.’ (Yeremiya 44:16, 17) Ayudawo anatsutsanso kuti: “Chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kum’thirira iye nsembe zothira, tasoŵa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi chaola.”—Yeremiya 44:18.
16. N’chifukwa chiyani malingaliro a Ayuda ku Igupto anali olakwika kwambiri?
16 Mmene ubongonso ungasankhire zokumbukira! Kodi choonadi chinali choti bwanji? Ayuda anaperekadi nsembe kwa milungu yonama m’dziko limene Yehova anawapatsa. Nthaŵi zina, monga m’nthaŵi ya Ahazi, anazunzika chifukwa cha mpatuko umenewo. Komabe, Yehova anali “wosakwiya msanga” ndi anthu ake apanganowo. (Eksodo 34:6, NW; Salmo 86:15) Anatumiza aneneri ake kukawachonderera kuti alape. Nthaŵi zina, ngati mfumu inali yokhulupirika, Yehova ankaidalitsa, ndipo anthu ankapindula ndi dalitso limenelo, ngakhale kuti ambiri a iwo anali osakhulupirika. (2 Mbiri 20:29-33; 27:1-6) Ayudawo ku Igupto ananamatu kwambiri ponena kuti chuma chilichonse chimene anali nacho kalelo kudziko lawo chinachokera kwa milungu yonama!
17. N’chifukwa chiyani Yuda anataya dziko lake ndi kachisi wake?
17 Chaka cha 607 B.C.E. chisanakwane, Yehova analimbikitsa anthu a Yuda kuti: “Mverani mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m’njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.” (Yeremiya 7:23) Ayuda anataya kachisi wawo ndi dziko lawo kwenikweni chifukwa chakuti anakana kuyenda ‘m’njira yonse imene Yehova anawauza.’ Tiyeni tionetsetse kuti tikupeŵa kulakwa koopsa ngati kumeneko.
Yehova Amadalitsa Oyenda m’Njira Yake
18. Kodi oyenda m’njira ya Yehova ayenera kuchitanji?
18 Lerolino, monga kale, kuyenda m’njira ya Yehova kumafuna kukhulupirika—kutsimikiza mtima kuti tidzatumikira yekhayo basi. Zimafuna kum’khulupirira—chikhulupiriro chenicheni kuti malonjezo a Yehova n’ngodalirika ndipo adzachitikadi. Kuyenda m’njira ya Yehova kumafuna kumvera—kutsatira malamulo ake ndi kusawasiya ndiponso kusunga miyezo yake yapamwamba. “Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama.”—Salmo 11:7.
19. Kodi ambiri lerolino akulambira milungu iti, ndipo pali zotsatirapo zotani?
19 Ahazi anayembekezera kupeza chitetezo kwa milungu ya Aaramu. Aisrayeli ku Igupto ankati “mfumu yaikazi ya kumwamba,” mulungu wamkazi amene anthu ambiri anali kum’lambira kalelo ku Middle East, adzawalemeretsa. Lerolino, milungu yambiri si mafano enieni. Yesu anachenjeza za kutumikira “Chuma” m’malo motumikira Yehova. (Mateyu 6:24) Mtumwi Paulo ananena za “chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.” (Akolose 3:5) Ananenanso za awo amene “mulungu wawo ndiyo mimba yawo.” (Afilipi 3:19) Inde, ndalama ndi zinthu zakuthupi ndiyo ina mwa milungu yaikulu imene ikulambiridwa lerolino. Kwenikweni, anthu ochuluka—kuphatikizapo ambiri opembedza—‘akuyembekezera chuma chosadziŵika kukhala kwake.’ (1 Timoteo 6:17) Ambiri amagwira ntchito ndi mtima wonse potumikira milungu imeneyi, ndipo ena amapinduladi—amakhala m’nyumba zokongola koposa, kukhala ndi zinthu zamtengo wapamwamba, ndi kudya zakudya zapamwamba. Koma si onse amene akupeza bwino chonchi. Ndipo ngakhale awo amene amapeza bwinowo m’kupita kwa nthaŵi amaona kuti zinthu zimenezi sizikuwakhutiritsa mwa izo zokha. N’zosadziŵika kukhala kwake, zosakhalitsa, ndipo sizikhutiritsa zosoŵa zauzimu.—Mateyu 5:3.
20. Kodi tiyenera kukhala osamala pa chiyani?
20 Zoonadi, tiyenera kumachita zinthu zoti zitithandize pamene tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo ili la zinthu. Tiyenera kuchitapo kanthu kuti tizipezera mabanja athu zofunikira zakuthupi. Koma ngati timaona monga kuti kukhala ndi moyo wapamwamba, kupeza ndalama, kapena zinthu zina zofanana nazo ndizo zofunika kwambiri kuposa kutumikira Mulungu, ndiye kuti tayamba kulambira mafano kwa mtundu winawake ndipo sitikuyendanso m’njira ya Yehova. (1 Timoteo 6:9, 10) Komano bwanji ngati tayamba kudwala, tasoŵeratu ndalama, kapena takhala ndi mavuto ena? Tisakhaletu ngati Ayuda aja ku Igupto amene anaimba mlandu kutumikira Mulungu. M’malo mwake, tiyeni timuyese Yehova, zimene Ahazi analephera kuchita. Mokhulupirika yang’anani kwa Yehova Mulungu kuti akutsogozeni. Mwachikhulupiriro, tsatirani chitsogozo chake, ndipo pemphererani nyonga ndi nzeru kuti muchite ndi mkhalidwe wina uliwonse. Kenako, mwachidaliro dikirani dalitso la Yehova.
21. Kodi ndi madalitso otani amene amadza kwa awo amene amayenda m’njira ya Yehova?
21 M’mbiri yonse ya Israyeli, Yehova anadalitsa zedi awo amene anayenda m’njira yake. Mfumu Davide inaimba kuti: “Yehova, munditsogolere m’chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo.” (Salmo 5:8) Yehova anam’patsa chilakiko pankhondo zomenyana ndi mitundu yoyandikana nayo imene pambuyo pake inasautsa Ahazi. Mu ulamuliro wa Solomo, Israyeli anadalitsidwa ndi mtendere ndi kulemerera, zimene Ayuda analakalaka pambuyo pake ku Igupto. Kwa Hezekiya mwana wa Ahazi, Yehova anapereka chilakiko pa Asuri. (Yesaya 59:1) Inde, dzanja la Yehova silinafupike kwa okhulupirika ake amene sanaimirire “m’njira ya ochimwa” koma amene anakondwera ndi chilamulo cha Mulungu. (Salmo 1:1, 2) Izi sizinasinthe. Komano kodi tingatsimikizire bwanji lerolino kuti tikuyenda m’njira ya Yehova? Zimenezi zidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi mikhalidwe iti imene ili yofunika kwambiri ngati tikufuna kuyenda m’njira ya Yehova?
◻ N’chifukwa chiyani maganizo a Ahazi anali olakwika?
◻ Kodi n’chiyani chinali cholakwika ndi malingaliro a Ayuda ku Igupto?
◻ Kodi tingakulitse motani kutsimikiza mtima kwathu kuti tidzayenda m’njira ya Yehova?
[Chithunzi patsamba 13]
Ahazi anayang’ana kwa milungu ya Aramu m’malo moyang’ana kwa Yehova