Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 5/15 tsamba 15-20
  • Pitirizani Kuyenda M’njira ya Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kuyenda M’njira ya Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunika kwa Kukhulupirira ndi Kukhulupirika
  • Thandizo Poyenda m’Njira ya Mulungu
  • Chosankha
  • “Mulungu Ali ndi Ife”
  • Kodi Muyenda ndi Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kuyenda ndi Mulungu—Masitepe Oyambirira
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yendani mwa Chikhulupiriro Osati mwa Zooneka Ndi Maso
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Pitirizani Kuyenda ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 5/15 tsamba 15-20

Pitirizani Kuyenda M’njira ya Yehova

“Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.”​—SALMO 37:34.

1, 2. Kwa Mfumu Davide, kodi kuyenda m’njira ya Yehova kunaphatikizapo chiyani, ndipo kodi kumafunanji kwa ife lerolino?

“MUNDIDZIŴITSE njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.” (Salmo 143:8) Ndi mtima wonse, Akristu lerolino amabwereza mawu a Mfumu Davide amenewo. Iwo amafunitsitsa kukondweretsa Yehova ndi kuyenda m’njira yake. Kodi zimenezi zimafuna chiyani? Kwa Davide, zinatanthauza kusunga malamulo a Mulungu. Zinaphatikizapo kukhulupirira Yehova m’malo mokhulupirira zigwirizano ndi mitundu ina. Inde, zinatanthauzanso kutumikira Yehova mokhulupirika, osati kutumikira milungu ya anthu oyandikana nawo. Kwa Akristu, kuyenda m’njira ya Yehova kumafunanso zina zambiri.

2 Choyamba, kuyenda m’njira ya Yehova lerolino kumatanthauza kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, kumuonadi kuti ndiye “njira, ndi choonadi, ndi moyo.” (Yohane 3:16; 14:6; Ahebri 5:9) Kumatanthauzanso kukwaniritsa “chilamulo cha Kristu,” chimene chimaphatikizapo kusonyeza chikondi kwa wina ndi mnzake, makamaka kwa abale a Yesu odzozedwa. (Agalatiya 6:2; Mateyu 25:34-40) Amene amayenda m’njira ya Yehova amakonda mapulinsipulo ndi malamulo ake. (Salmo 119:97; Miyambo 4:5, 6) Amasangalaladi ndi mwayi wawo wa kuchita nawo utumiki wachikristu. (Akolose 4:17; 2 Timoteo 4:5) Pemphero ndi chinthu chachikhalire m’moyo wawo. (Aroma 12:12) Ndipo ‘amapenya bwino umo ayendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru.’ (Aefeso 5:15) Ndithudi sataya chuma chauzimu chifukwa cha chuma chakuthupi chosakhalitsa kapena zikhumbo zonyansa zakuthupi. (Mateyu 6:19, 20; 1 Yohane 2:15-17) Komanso, kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndi kum’khulupirira n’zofunika kwambiri. (2 Akorinto 1:9; 10:5; Aefeso 4:24) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kwa ife zinthu zili monga momwe zinalili kwa Israyeli wakale.

Kufunika kwa Kukhulupirira ndi Kukhulupirika

3. N’chifukwa chiyani kukhulupirika, chikhulupiriro, ndi kukhulupirira Yehova zidzatithandiza kuyendabe m’njira ya Yehova?

3 Israyeli unali mtundu waung’ono wozingidwa ndi anansi osakhala aubwenzi omwe ankachita miyambo yonyansa polambira mafano. (1 Mbiri 16:26) Israyeli yekha ndiye ankatumikira Mulungu yekha woona ndi wosaoneka ndi maso, Yehova, ndipo Iye anali kufuna kuti Aisrayeliwo azitsatira miyezo yapamwamba yakhalidwe. (Deuteronomo 6:4) Lerolinonso, anthu mamiliyoni ochepa okha ndi amene akulambira Yehova, ndipo akukhala m’dziko la anthu pafupifupi 6,000,000,000 amene miyezo yawo ndi malingaliro awo ponena za chipembedzo ali osiyana kwambiri ndi a anthu olambira Yehovawo. Ngati tili pakati pa mamiliyoni ochepawo, tiyenera kukhala tcheru kuti tisasonkhezeredwe m’njira yolakwika. Motani? Kukhulupirika kwa Yehova Mulungu, kum’khulupirira, ndiponso chikhulupiriro cholimba chakuti adzakwaniritsa malonjezo ake zidzatithandiza. (Ahebri 11:6) Zimenezi zidzatipangitsa kuti tisaike chikhulupiriro chathu pazinthu zimene dzikoli limaikapo chiyembekezo chake.​—Miyambo 20:22; 1 Timoteo 6:17.

4. N’chifukwa chiyani amitundu ali “odetsedwa m’nzeru zawo”?

4 Mtumwi Paulo anasonyeza mmene Akristu ayenera kukhalira osiyana ndi dziko pamene analemba kuti: “Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo.” (Aefeso 4:17, 18) Yesu ndiye “kuunika kwenikweni.” (Yohane 1:9) Aliyense wom’kana kapena amene amati amam’khulupirira koma satsatira “chilamulo cha Kristu” ali ‘wodetsedwa m’nzeru zake.’ Popeza sakuyeserera n’komwe kuyenda m’njira ya Yehova, iwo ali “oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu.” Ngakhale iwo atamaganiza kuti n’nganzeru motani m’zinthu zakudziko, iwo ali ndi ‘chipulukiro mkati mwawo’ ponena za chidziŵitso chokha chotsogolera ku moyo, chija chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu.​—Yohane 17:3; 1 Akorinto 3:19.

5. Ngakhale kuti kuunika kwa choonadi kukuwala m’dziko, n’chifukwa chiyani mitima yambiri ili youma?

5 Komabe, kuunika kwa choonadi kukuwala m’dzikoli! (Salmo 43:3; Afilipi 2:15) “Nzeru ifuula panja.” (Miyambo 1:20) Chaka chatha Mboni za Yehova zinathera maola oposa 1,000,000,000 zikuuza anansi awo za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Anthu zikwi mazanamazana anamvera. Koma kodi tiyenera kudabwa kuti enanso ambiri sanamvere? Iyayi. Paulo ananena za “kuumitsa kwa mitima yawo.” Ena ali ndi mitima youma chifukwa cha dyera kapena kukondetsa ndalama. Ena amasonkhezeredwa ndi chipembedzo chonyenga kapena malingaliro a dziko ofala kwambiri lerolino. Mavuto aakulu m’moyo apangitsa ambiri kufulatira Mulungu. Ena safuna kufitsa miyezo yapamwamba ya Yehova ya khalidwe. (Yohane 3:20) Kodi mtima wa munthu amene akuyenda m’njira ya Yehova ungaume pa zinthu zimenezi?

6, 7. Ngakhale kuti Aisrayeli anali olambira Yehova Mulungu, ndi pazochitika ziti pamene iwo anagwa, ndipo chifukwa chiyani?

6 Zimenezi zinawachitikira Aisrayeli akale, monga momwe Paulo anasonyezera. Iye analemba kuti: “Zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakelake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka. Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kuseŵera. Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.”​—1 Akorinto 10:6-8.

7 Choyamba Paulo akunena za nthaŵi pamene Aisrayeli analambira mwana wa ng’ombe wa golide m’munsi mwa Phiri la Sinai. (Eksodo 32:5, 6) Kumeneku kunali kusamvera lamulo la Mulungu limene anavomera kuti adzalimvera milungu yochepa poyambapo. (Eksodo 20:4-6; 24:3) Kenako, Paulo akunena za nthaŵi pamene Aisrayeli anagwadira Baala ndi ana aakazi a Moabu. (Numeri 25:1-9) Polambira mwana wang’ombe, anthuwo anali kukhutiritsa zilakolako zawo mopambanitsa, ‘kuseŵera.’a Polambira Baala anthuwo anali kuchita zachiwerewere zosaneneka. (Chivumbulutso 2:14) N’chifukwa chiyani Aisrayeli anachita machimo ameneŵa? Chifukwa analola mitima yawo ‘kulakalaka zoipa’​—kaya kulambira mafanoko kapena miyambo yonyansa imene anali kuichita polambira.

8. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene zinachitikira Aisrayeli?

8 Paulo anati tiyenera kuphunzirapo pa zochitika zimenezi. Kuphunzirapo chiyani? Mosakayikira Mkristu sangagwadire mwana wang’ombe wagolide kapena mulungu wakalekale wa Amoabu. Koma bwanji za chiwerewere kapena kukhutiritsa zilakolako mosadziletsa? Zimenezi n’zofala lerolino, ndipo ngati tilola chikhumbo cha kuchita zimenezi kukula m’mitima yathu, zidzakhala chopinga pakati pa ifeyo ndi Yehova. Chotsatira chake chidzakhala chofanana ndi kuti talambira mafano​—kupatutsidwa kwa Mulungu. (Yerekezani ndi Akolose 3:5; Afilipi 3:19.) Ndiye chifukwa chakedi Paulo anamaliza nkhani yake yofotokoza zochitikazo mwa kulimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Thaŵani kupembedza mafano.”​—1 Akorinto 10:14.

Thandizo Poyenda m’Njira ya Mulungu

9. (a) Kodi tikulandira thandizo lotani kuti tipitirize kuyenda m’njira ya Yehova? (b) Kodi ‘mawu kumbuyo kwathu’ timawamva m’njira yoyamba yotani?

9 Ngati tatsimikiza mtima kuyenda m’njira ya Yehova, sitimangokhala opanda thandizo. Yesaya analosera kuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Kodi ‘makutu athu’ amamva bwanji ‘mawuwo kumbuyo kwathu’? Inde, palibe munthu lerolino amene amamva liwu lenileni la Mulungu kapena kulandira uthenga kuchokera kwa iye mwachindunji. “Mawu” amene timamva amadza kwa tonsefe m’njira imodzimodzi. Choyamba ndiponso chofunika kwambiri, amadza kudzera mwa Malemba ouziridwa, Baibulo, limene limafotokoza malingaliro a Mulungu ndi kusimba mbiri ya zimene wachita ndi anthu. Popeza kuti masiku onse timamva manenanena a anthu “oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu,” tiyenera kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene taŵerenga nthaŵi zonse kuti tikhale athanzi mwauzimu. Zimenezi zidzatithandiza kupeŵa “zinthu zachabe” ndi kukhala “woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (Machitidwe 14:14, 15; 2 Timoteo 3:16, 17) Zidzatipatsa mphamvu ndi kutilimbikitsa, ndi kutithandiza ‘kukometsa njira yathu.’ (Yoswa 1:7, 8) Ndiye chifukwa chake Mawu a Yehova amatilimbikitsa kuti: “Tsopano, ananga, mundimvere ine, n’ngodala akusunga njira zanga. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.”​—Miyambo 8:32, 33.

10. Kodi ‘mawu kumbuyo kwathu’ timawamvanso m’njira yachiŵiri iti?

10 ‘Mawuwo kumbuyo kwathu’ amadzanso kwa ife kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” amene amapereka “zakudya panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45-47) Njira imodzi imene amaperekera chakudyachi ndiyo kudzera m’zofalitsa zothandiza kuphunzira Baibulo, ndipo m’zaka zingapo zapitazi chakudya chimenechi chakhalapo chochuluka kwambiri. Mwachitsanzo, kudzera m’magazini ya Nsanja ya Olonda, kamvedwe kathu ka maulosi kawongoleredwa. M’magazini imeneyi, talimbikitsidwa kulimbikirabe pantchito yolalikira ndi kupanga ophunzira ngakhale kuti anthu ambiri alibe chidwi, tathandizidwa kupeŵa misampha, ndipo talimbikitsidwa kukulitsa mikhalidwe yabwino yachikristu. Chakudya cha panthaŵi yake chimenechi n’chamtengo wapatali kwambiri kwa ife!

11. Fotokozani njira yachitatu imene tingamvere ‘mawu kumbuyo kwathu.’

11 Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsanso chakudya kudzera m’misonkhano yathu yanthaŵi zonse. Imeneyi imaphatikizapo misonkhano yampingo, misonkhano yadera yochitika kaŵiri pachaka, ndi misonkhano yaikulu yochitika kamodzi pachaka. Ndi Mkristu wokhulupirika wotani amene sangaone misonkhanoyi kukhala yofunika? Iyo imatithandiza kwambiri potichirikiza kuyenda m’njira ya Yehova. Popeza kuti ambiri amathera nthaŵi yochuluka kuntchito kapena kusukulu pakati pa anthu osiyana nawo chikhulupiriro, mayanjano achikristu a nthaŵi zonse n’ngopulumutsa moyo m’lingaliro lenileni. Misonkhano imatipatsa mpata wabwino ‘wofulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ (Ahebri 10:24) Abale athu timawakonda, ndipo timakonda kuyanjana nawo.​—Salmo 133:1.

12. Kodi Mboni za Yehova n’zotsimikiza mtima kuchitanji, ndipo zinasonyeza motani zimenezo posachedwapa?

12 Polimbikitsidwa ndi chakudya chauzimu chimenechi, anthu pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi lerolino akuyenda m’njira ya Yehova, ndipo anthu enanso mamiliyoni ambiri akuphunzira Baibulo kuti adziŵe kayendedwe ka m’njirayo. Kodi akugwa ulesi kapena kulefuka poona kuti chiŵerengero chawo n’chaching’ono pochiyerekezera ndi anthu mabiliyoni amene ali padziko lapansi? Kutalitali! Iwo n’ngotsimikiza mtima kupitirizabe kumvera ‘mawu kumbuyo kwawo,’ kuchita chifuniro cha Yehova mokhulupirika. Posonyeza poyera kutsimikiza mtima kumeneku, pa Misonkhano Yachigawo ndi Yamitundu Yonse ya “Njira ya Moyo ya Mulungu” mu 1998/99, osonkhanawo anavomereza chosankha kusonyeza kaimidwe kawo kochokera pansi pa mtima. Otsatiraŵa ndi mawu a chosankha chimenecho.

Chosankha

13, 14. Kodi Mboni za Yehova zimaona dziko m’njira yoyenera yotani?

13 “Ifeyo, monga Mboni za Yehova amene tasonkhana pano pa Msonkhano Wachigawo wa ‘Njira ya Moyo ya Mulungu,’ tikuvomereza ndi mtima wonse kuti njira ya Mulungu ndiyo njira yabwino koposa ya moyo. Komabe, tikudziŵa kuti si mmene anthu ambiri lerolino amaonera. Anthu ayesa njira zambiri, mafilosofi, ndi malingaliro achipembedzo kuti apeze njira yabwino koposa ya moyo. Kusanthula moona mtima mbiri ya anthu ndiponso mikhalidwe yapadziko lapansi lerolino kukusonyeza kulondola kwa chilengezo cha Mulungu cholembedwa pa Yeremiya 10:23 kuti: ‘Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’

14 “Masiku onse timaona umboni wowonjezeka wakuti mawuwo n’ngoonadi. Nkhani yaikulu n’njakuti anthu akunyalanyaza njira ya moyo ya Mulungu. Anthu amangolondola zimene zikuoneka kukhala zoyenera m’maso mwawo. Zotsatirapo zake n’zoopsa​—kuwonongeka kwa mabanja, ana n’kumakhala opanda chitsogozo; kutsata chuma kwa padziko lonse, kosaphula kanthu ndiponso kokhumudwitsa pomalizira pake; upandu ndi chiwawa popanda chifukwa chake chenicheni, zomwe zavutitsa anthu osaŵerengeka; udani ndi nkhondo zaufuko, zimene zapha anthu ochuluka koopsa; makhalidwe onyansa ofala, osonkhezera mliri wa matenda opatsirana mwakugonana. Zimenezi zangokhala zitsanzo zoŵerengeka za mavuto ambirimbiri osamvetsetseka amene akusokoneza ofuna kupeza chimwemwe, mtendere, ndi chisungiko.

15, 16. Ponena za njira ya moyo ya Mulungu, kodi ndi kutsimikiza mtima kotani kumene kunasonyezedwa m’chosankhacho?

15 “Chifukwa cha mkhalidwe womvetsa chisoni wa anthu ndiponso kuyandikira kwa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,’ yotchedwa Armagedo (Chivumbulutso 16:14, 16), ife monga Mboni za Yehova tasankha:

16 “Choyamba: Kudziona kukhala anthu a Yehova Mulungu, popeza aliyense wa ife, ndi mtima wonse popanda zina zowonjezapo, anadzipatulira kwa iye modzifunira payekha, ndipo tidzakhalabe ndi chikhulupiriro chosagwedera mwa makonzedwe a Yehova a nsembe kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu. Ndife otsimikiza mtima kuti tidzayenda m’njira ya moyo ya Mulungu, kutumikira monga Mboni zake ndi kulemekeza uchifumu wake wochitidwa kudzera mwa ulamuliro wa Yesu Kristu.

17, 18. Kodi Mboni za Yehova zidzapitirizabe ndi kaimidwe kotani ponena za miyezo ya khalidwe ndi ubale wachikristu?

17 “Chachiŵiri: Kupitirizabe kutsatira mosamalitsa malamulo apamwamba a m’Baibulo a khalidwe labwino ndiponso auzimu. Ndife otsimikiza mtima kuti sitidzayenda monga amayendera amitundu mu uchitsiru wa mtima wawo. (Aefeso 4:17-19) Tasankha kukhalabe oyera pamaso pa Yehova osachitidwa maŵanga ndi dzikoli.​—Yakobo 1:27.

18 “Chachitatu: Kusasintha konse kaimidwe kathu ka m’Malemba monga abale achikristu apadziko lonse. Tidzasungabe uchete wachikristu pakati pa amitundu, osadziloŵetsa m’magaŵano kapena udani waufuko kapena wautundu.

19, 20. (a) Kodi makolo achikristu adzachitanji? (b) Kodi Akristu onse oona adzapitiriza kuchita chiyani pofuna kupereka chizindikiro chakuti ndi ophunzira a Kristu?

19 “Chachinayi: Kuti ife amene tili makolo tidzaphunzitsa ana athu njira ya Mulungu. Tidzapereka chitsanzo cha moyo wachikristu, umene umaphatikizapo kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse, phunziro la banja, ndi kutengamo mbali ndi mtima wonse m’zochitika za mumpingo wachikristu ndi mu utumiki wakumunda.

20 “Chachisanu: Kuti tonsefe tidzayesetsa kukulitsa mikhalidwe yaumulungu imene Mlengi wathu amatisonyeza, ndipo tidzayesetsa kutsanzira umunthu wake ndi njira zake, monga momwe Yesu anachitira. (Aefeso 5:1) Tasankha kuchita zinthu zonse mwachikondi, tikumapereka chizindikiro chakuti ndife ophunzira a Kristu.​—Yohane 13:35.

21-23. Kodi Mboni za Yehova zidzapitiriza kuchita chiyani, ndipo kodi zimakhulupirira chiyani?

21 “Chachisanu ndi chimodzi: Kupitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mosaleka, kupanga ophunzira, ndipo tidzawalangiza za njira ya moyo ya Mulungu ndi kuwalimbikitsa kukaphunzira zambiri pamisonkhano yampingo.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20; Ahebri 10:24, 25.

22 “Chachisanu ndi chiŵiri: Kuti aliyense payekha ndiponso monga gulu lachipembedzo, tidzapitirizabe kuona chifuniro cha Mulungu monga chinthu chofunika koposa pamoyo wathu. Mwa kugwiritsa ntchito Mawu ake, Baibulo, monga chitsogozo chathu, sitidzapambukira kulamanja kapena kulamanzere, tikumasonyezadi kuti njira ya Mulungu n’njopambana zedi pa njira za dzikoli. Tatsimikiza mtima kulondola njira ya Mulungu ya moyo​—molimba ndiponso mokhulupirika, tsopano ndiponso kosatha!

23 “Tapanga chosankha chimenechi chifukwa chakuti timakhulupirira zedi lonjezo lachikondi la Yehova lakuti iye amene achita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha. Tapanga chosankhachi chifukwa chakuti timakhulupirira kuti kukhala motsatira mapulinsipulo, malangizo, ndi uphungu wa m’Malemba ndiyo njira yabwino koposa ya moyo lerolino ndipo kumayala maziko abwino a m’tsogolo, kuti tigwiritsitse moyo weniweniwo. (1 Timoteo 6:19; 2 Timoteo 4:7b, 8) Komanso chachikulu n’chakuti, tapanga chosankha chimenechi chifukwa chakuti timakonda Yehova Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, nzeru zathu zonse, ndi mphamvu zathu zonse!

24, 25. Kodi panali yankho lotani ponena za chosankha chimene chinafotokozedwacho, ndipo awo amene akuyenda m’njira ya Yehova n’ngotsimikiza mtima kuchita chiyani?

24 “Tonsefe amene tili pamsonkhano uno amene tikuvomereza chosankhachi, tiyeni tinene kuti TIKUVOMEREZA!”

25 Mabwalo osiyanasiyana mazana ambiri padziko lonse lapansi ananjenjemera pamene onse amene analipo anayankha ndi mkokomo kuti “TIKUVOMEREZA!” Mboni za Yehova sizikayikira kuti zidzapitirizabe kuyenda m’njira ya Yehova. Zimam’khulupirira zedi Yehova ndipo zili ndi chikhulupiriro chakuti adzakwaniritsa malonjezo ake. Zikhalabe zokhulupirika kwa iye, zivute zitani. Ndipo n’zotsimikiza mtima kuchita chifuniro chake.

“Mulungu Ali ndi Ife”

26. Kodi oyenda m’njira ya Yehova ali mumkhalidwe wotani wokondweretsa?

26 Mboni za Yehova zimakumbukira chilimbikitso cha wamasalmo chakuti: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.” (Salmo 37:34) Siziiŵala mawu olimbikitsa a Paulo akuti: “Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani? Iye amene sanatimana Mwana wake wa iye yekha, koma anam’pereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?” (Aroma 8:31, 32) Inde, ngati tiyendabe m’njira ya Yehova, adzatipatsa “zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” (1 Timoteo 6:17) Kwinanso n’kuti kwabwino kwambiri kuposa malo amene tilipo kale​—kuyenda m’njira ya Yehova, pamodzi ndi abale ndi alongo athu okondedwa. Pokhala Yehova ali kumbali yathu, tiyeni motsimikiza mtima tikhalebe pamalowo ndi kupirira mpaka mapeto, tili otsimikizira zedi kuti panthaŵi yake yoikika, tidzamuona akukwaniritsa malonjezo ake onse.​—Tito 1:2.

[Mawu a M’munsi]

a Ponena za mawu achigiriki otembenuzidwa panopo kuti “kuseŵera,” womasulira mawu wina ananena kuti mawuwo amatanthauza magule amene anali kuchitika pamapwando achikunja ndipo anawonjezera kuti: “Ambiri mwa magule ameneŵa, monga momwe timadziŵira bwino lomwe, anakonzedwa kwenikweni kuti azinyanyula anthu kuti akhale ndi zilakolako zonyansa kotheratu.”

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi Mkristu afunikira chiyani kuti ayende m’njira ya Yehova?

◻ N’chifukwa chiyani tifunikira kukulitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi kukhala wokhulupirika kwa iye?

◻ Kodi pali chithandizo chotani pamene tikuyenda m’njira ya Yehova?

◻ Tchulani mfundo zina zazikulu za chosankha chimene chinavomerezedwa pa Misonkhano ya “Njira ya Moyo ya Mulungu.”

[Zithunzi patsamba 18]

Chosankha chofunika chinavomerezedwa pa Misonkhano Yachigawo ndi Yamitundu Yonse ya “Njira ya Moyo ya Mulungu”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena