Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 6/15 tsamba 14-19
  • Mlengi Angawonjezere Tanthauzo la Moyo Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mlengi Angawonjezere Tanthauzo la Moyo Wanu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupeza Mayankho ndi Tanthauzo
  • Zifukwa Zotipangitsa Kukhulupirira
  • Lolani Kuti Mlengi Awonjezere Tanthauzo
  • Dziŵani Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Chilengedwe Chonsechi Ndiponso Zamoyozi Zinakhalako Bwanji?
    Galamukani!—2002
  • ‘Pakusoŵeka Chinthu China’—Chiyani?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Mungafufuze Bwanji?
    Galamukani!—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 6/15 tsamba 14-19

Mlengi Angawonjezere Tanthauzo la Moyo Wanu

“Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.”​—SALMO 148:5.

1, 2. (a) Kodi ndi funso liti limene tiyenera kuliganizapo? (b) Kodi chilengedwe chikuphatikizidwa motani m’funso la Yesaya?

“KODI iwe sunadziŵe?” Limenelo lingamveke ngati funso wamba, limene lingapangitse ambiri kufunsa kuti ‘Kudziŵa chiyani?’ Koma ndi funso lalikulu zedi. Ndipo yankho lake tingalimvetse bwino mwa kudziŵa kumene linafunsidwa​—m’chaputala 40 cha buku la m’Baibulo la Yesaya. M’Hebri wakale, Yesaya, ndi amene analilemba, choncho funsolo ndi lamakedzana. Komanso ndi lamakono kwambiri. Limakhudzana ndi tanthauzo lenileni la moyo wanu.

2 Pokhala ndi lofunika chotero, funso la pa Yesaya 40:28 limeneli tiyenera kuliganizapo kwambiri: “Kodi iwe sunadziŵe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, [ndi] Mlengi wa malekezero a dziko lapansi.” (Tapendeketsa mawu ndife.) Choncho ‘kudziŵa’ kumeneko kukukhudza Mlengi wa dziko lapansi, ndipo nkhani yakeyo ikusonyeza kuti si dziko lokha limene likuphatikizidwapo. Mavesi aŵiri pamwamba Yesaya analemba za nyenyezi kuti: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga . . . ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.”

3. Ngakhale kuti mukudziŵa zambiri ponena za Mlengi, n’chifukwa chiyani muyenera kudziŵabe zowonjezera?

3 Inde, funso lakuti “Kodi iwe sunadziŵe?” kwenikweni likunena za Mlengi wa chilengedwe cha ponseponse. Mwina inuyo mumakhulupirira kuti Yehova Mulungu ndiye “Mlengi wa malekezero a dziko lapansi.” Mwinanso mumadziŵa zambiri ponena za umunthu wake ndi njira zake. Koma bwanji ngati mwakumana ndi mwamuna kapena mkazi amene amakayikira zonena kuti kuli Mlengi, amenenso sadziŵa kuti ndi wotani? Simuyenera kudabwa mutakumana ndi munthu woteroyo chifukwa chakuti pali anthu miyandamiyanda amene sadziŵa kapena kukhulupirira kuti kuli Mlengi.​—Salmo 14:1; 53:1.

4. (a) N’chifukwa chiyani kuganiza za Mlengi kuli koyenera panthaŵi ino? (b) Kodi ndi mafunso otani amene sayansi singayankhe?

4 Masukulu atulutsa anthu ambiri okonda kukayikira amene amaganiza kuti sayansi ili ndi mayankho (kapena idzapeza mayankho) a mafunso onena za chiyambi cha thambo ndi moyo. M’buku lakuti The Origin of Life (Chiyambi cha Moyo) (mutu wake m’Chifalansa: Aux Origines de la Vie) olemba bukulo Hagene ndi Lenay anati: “Ngakhale pamene zaka za zana la 21 zikuyamba, anthu akutsutsanabe ponena za chiyambi cha moyo. Nkhani imeneyi, yovuta kwambiri kuipezera mayankho, n’njofunika kuifufuza mbali zonse, kuyambira ku zinthu zazikulu modabwitsa zakuthambo mpaka ku tinthu tochepetsetsa tosaoneka ndi maso wamba.” Komabe, mutu wake womaliza wakuti, “Funsolo Silinayankhidwebe,” ukuvomereza kuti: “Taona mayankho ena asayansi pafunso lakuti, Kodi moyo unakhalako motani padziko lapansi? Koma n’chifukwa chiyani moyo unakhalako? Kodi moyo uli ndi cholinga? Sayansi singayankhe mafunso ameneŵa. Imangofufuza kuti zinthu zinachitika ‘motani.’ ‘Motani’ ndi ‘chifukwa chiyani’ ndi mafunso aŵiri osiyana kotheratu. . . . Ponena za funso lakuti ‘n’chifukwa chiyani,’ filosofi, chipembedzo, ndiponso​—makamaka​—aliyense wa ife ayenera kufufuza yankho lake.”

Kupeza Mayankho ndi Tanthauzo

5. Kodi ndi anthu otani makamaka amene angapindule mwa kuphunzira zambiri ponena za Mlengi?

5 Inde, tikufuna kumvetsa chifukwa chimene moyo unakhalirako​—makamakanso chifukwa chimene ifeyo tiliri pano. Ndiponso, tiyenera kusonyeza chidwi kwa anthu amene sanafikebe potsimikiza kuti Mlengi aliko, amenenso sadziŵa zambiri ponena za njira zake. Kapenanso talingalirani za awo amene amadziŵa Mulungu m’njira yosiyana kwambiri ndi imene Baibulo limafotokoza, chifukwa cha kumene amachokera. Anthu mabiliyoni akulira Kum’maŵa kapena kumalo ena kumene anthu ambiri saganiza kuti Mulungu ali ndi umunthu wake weniweni, umunthu wabwino. Kwa iwo, mawu akuti “mulungu” mwina amawapangitsa kuganiza za mphamvu inayake yosadziŵika bwino imene imatheketsa zinthu kuchitika. ‘Sanam’dziŵe Mlengi’ kapena njira zake. Anthu ameneŵa, kapena enanso miyandamiyanda amene amalingalira zimenezi, atati akhulupirire kuti Mlengi aliko, angalandire mapindu abwino bwanji! Angakhalenso ndi chiyembekezo cha tsogolo losatha! Angapezenso chinthu chosoŵa kwambiri​—tanthauzo lenileni, cholinga chenicheni ndi mtendere wa maganizo, m’moyo.

6. Kodi moyo wa anthu ambiri lerolino umafanana motani ndi zimene Paul Gauguin anakumana nazo komanso ndi chimodzi mwa zojambula zake?

6 Mwachitsanzo: Mu 1891, mmisiri wachifalansa wojambula zithunzi Paul Gauguin anakafunafuna moyo wokhutiritsa ku French Polynesia, kumalo ooneka ngati paradaiso. Koma chifukwa cha moyo wake wakale wosadziletsa, iyeyo ndi ena anayamba kudwala. Ataona kuti anali pafupi kufa, iye anajambula chithunzi pachinsalu chachikulu ndipo anaoneka kuti ‘akumasulira moyo kukhala chinthu chozizwitsa kwambiri.’ Kodi mukudziŵa dzina limene Gauguin anatcha chithunzicho? Anachitcha kuti: “Kodi Tinachokera Kuti? Kodi Ndife Chiyani? Kodi Tikupita Kuti?” Mwina mwamvapo ena akufunsa mafunso oterowo. Anthu ambiri amawafunsa. Koma akalephera kupeza mayankho okhutiritsa​—tanthauzo lenileni la moyo​—kodi iwo angatani? Angangonena kuti moyo wawo n’ngwosasiyana kwenikweni ndi moyo wa nyama.​—2 Petro 2:12.a

7, 8. N’chifukwa chiyani zofufuza za sayansi sizili zokwanira mwa izo zokha?

7 Chotero mutha kumvetsa chifukwa chimene munthu monga polofesa wa maphunziro a physics Freeman Dyson analembera kuti: “Ndimagwirizana ndi anthu ambiri olemekezeka pamene ndifunsanso mafunso amene Yobu anafunsa. N’chifukwa chiyani timavutika? N’chifukwa chiyani pali chisalungamo chotere padziko lapansi? Kodi n’chifukwa chiyani pali mavuto ndi masoka?” (Yobu 3:20, 21; 10:2, 18; 21:7) Monga tatchulapo kale, anthu ambiri amayembekezera kuti sayansi idzawapatsa mayankho m’malo moyembekezera Mulungu. Akatswiri odziŵa za zinthu zamoyo, akatswiri a zam’nyanja, ndi ena akuwonjezera chidziŵitso chokhudza dziko lathuli ndi zamoyo zimene zilipo. Kwinaku, akatswiri a zakuthambo ndi akatswiri a maphunziro a physics akutulukirabe zinthu zowonjezeka zokhudza zakuthambo zimene zimazungulira dzuŵa, nyenyezi, ngakhale milalang’amba yakutali. (Yerekezani ndi Genesis 11:6.) Kodi zinthu zimene apezazo zingatifikitse pamfundo zomveka zotani?

8 Asayansi ena amanena za “malingaliro” a Mulungu kapena “dzanja” lake zimene zimaonekera m’thambo. Koma kodi amaphonyanso mfundo yofunika? Magazini yotchedwa Science inati: “Ofufuza akamanena kuti sayansi ya chilengedwe imavumbula ‘malingaliro’ kapena ‘dzanja’ la Mulungu, iwo amangoganiza za zinthu zooneka ndi maso zokha kuti mphamvu yaumulungu ndiyodi inazipanga.” Kwenikweni, katswiri wa maphunziro a physics yemwenso anapata mphoto ya Nobel Steven Weinberg analemba kuti: “Pamene tiphunzira zambiri ponena za thambo, m’pamenenso limaoneka kuti lilibe tanthauzo.”

9. Ndi umboni wotani umene ungatithandize ifeyo ndi enanso kuphunzira za Mlengi?

9 Komabe, mwina ndinu mmodzi mwa anthu mamiliyoni angapo amene afufuza nkhaniyi mosamala amenenso amazindikira kuti tanthauzo lenileni m’moyo limaphatikizapo kudziŵa Mlengi. Kumbukirani zimene mtumwi Paulo analemba kuti: “Anthu sanganene kuti sakudziŵa Mulungu. Kuyambira pachiyambi cha dziko, anthu aona mmene Mulungu alili kudzera m’zinthu zimene Iye wapanga. Zimenezi zimasonyeza mphamvu Yake yosatha. Zimasonyeza kuti Iye ndi Mulungu.” (Aroma 1:20, Holy Bible, New Life Version) Inde, pali mfundo zina zokhudza dziko lathu lapansi ndiponso zokhudza ifeyo zimene zingathandize anthu kuzindikira Mlengi ndi kupeza tanthauzo mwa iye. Talingalirani mbali zitatu za mfundozi: thambo lotizinga, chiyambi cha moyo, ndi nzeru zathu.

Zifukwa Zotipangitsa Kukhulupirira

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganiza za “chiyambi”? (Genesis 1:1; Salmo 111:10)

10 Kodi thambo linakhalapo motani? Mwina mwamvapo m’nkhani zonena za zipangizo zoonera ndi zofufuzira zinthu za kuthambo kuti asayansi ambiri amadziŵa kuti nthaŵi inayake kunalibe thambo. Linachita kuyamba, ndipo likufutukuka. Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Mverani zimene katswiri wina wa zakuthambo Bwana Bernard Lovell ananena: “Ngati panthaŵi inayake kalelo, Thambo linali kanthu kakang’onong’ono kokhala ndi kulemera kwakukulu kosadziŵika, tiyenera kufunsa kuti nanga poyamba kunali chiyani . . . Tiyenera kuyang’anizana ndi nkhani ya Chiyambi.”

11. (a) Kodi thambo ndi lalikulu motani? (b) Kodi kulinganizika kwa zinthu zakuthambo kumapereka lingaliro lotani?

11 Kapangidwe ka thambo, kuphatikizapo dziko lathu lapansili, kamasonyeza kulinganiza kodabwitsa. Mwachitsanzo, mikhalidwe iŵiri ya dzuŵa lathu ndi nyenyezi zina ndiyo kugwira bwino ntchito kwa nthaŵi yaitali komanso kusasintha. Ziŵerengero zimene akuziganizira tsopano za milalang’amba m’thambo limene amatha kuona zimayambira pa 50,000,000,000 mpaka 125,000,000,000. Ndipo mlalang’amba umene tilimowu wotchedwa Milky Way uli ndi nyenyezi mabiliyoni, mabiliyoni. Tsopano talingalirani: Tikudziŵa kuti injini ya galimoto imafuna mlingo wolinganiza bwino kwambiri wa mafuta ndi mpweya. Ngati muli ndi galimoto, mwina mungapemphe wokonza galimoto waluso kuti alinganize mlingo wofunika mu injini yake, kuti galimoto yanu iziyenda bwino popanda zovuta. Ngati kulinganiza kotereku n’kofunika mu injini wamba, bwanji ponena za dzuŵa lathuli “loyaka moto,” limene limagwira bwino ntchito popanda zovuta? Ndithudi, mphamvu zimene zimapangitsa zimenezo n’zolinganizika bwino kwambiri kuti dziko lapansi lithe kukhala ndi zamoyo. Kodi zimenezo zinangochitika zokha? Yobu wakaleyo anafunsidwa kuti: “Kodi ndiwe unalengeza malamulo amene amatsogoza zakuthambo, kapena kukhazikitsa malamulo achilengedwe padziko lapansi?” (Yobu 38:33, The New English Bible) Palibe munthu amene anachita zimenezo. Nangano kulinganiza kumeneko kunachokera kuti?​—Salmo 19:1.

12. N’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kulingalira kuti Nzeru yamphamvu ndi imene inalenga zinthu?

12 Kodi mwina kunachokera kwa chinachake kapena Winawake wosaoneka ndi maso aumunthu? Lingalirani funso limeneli malinga ndi sayansi yamakono. Akatswiri a zakuthambo ambiri tsopano amavomereza kuti kumwambaku kuli zinthu zina zamphamvu kwambiri​—ma black hole. Ma black hole ameneŵa saoneka, koma akatswiriwo amakhulupirira kuti aliko. Mofananamo, Baibulo limanena kuti kwinakwake kuli zolengedwa zamphamvu zosaoneka​—zolengedwa zauzimu. Ngati zolengedwa zamphamvu, zosaoneka zimenezo ziliko, kodi sikungakhale kwanzeru kunena kuti kulinganiza koonekera m’thambo lonse kunachokera ku Nzeru inayake yamphamvu kwambiri?​—Nehemiya 9:6.

13, 14. (a) Kodi kwenikweni sayansi imati chiyani ponena za chiyambi cha moyo? (b) Kodi moyo padziko lapansi umasonyeza kuti unachokera kuti?

13 Umboni wina umene ungathandize anthu kuzindikira kuti kuli Mlengi ukukhudza chiyambi cha moyo. Kuchokera panthaŵi ya kufufuza kwa Louis Pasteur, anthu amavomereza kuti moyo sumangokhalapo wokha popanda china chouyambitsa. Chotero kodi moyo padziko lapansi unayamba motani? Cha m’ma 1950, asayansi anayesa kupereka umboni wakuti moyo uyenera kuti unayambira m’nyanja inayake yoyambirira pamene mlengalenga woyambirirawo unali kuombedwa mosalekeza ndi mphezi. Koma umboni watsopano kwambiri ukusonyeza kuti moyo padziko lapansi sukanayamba m’njira imeneyo chifukwa chakuti kunalibe mlengalenga ngati umenewo. Chotero, asayansi akufunafuna mafotokozedwe abwinopo. Koma kodi iwonso akuphonya mfundo yake?

14 Atatha zaka makumi, makumi akuphunzira chilengedwe chonse ndi zamoyo zake, wasayansi wa ku Britain Bwana Fred Hoyle anati: “M’malo movomereza nkhani yosathekayo yakuti moyo unangoyamba wokha mwa mphamvu zachilengedwe, zinaoneka kuti ndi bwino kuganiza kuti chinthu china chanzeru n’chimene chinauyambitsa.” Inde, pamene tidziŵa zodabwitsa zowonjezeka za moyo, mpamenenso kumaoneka kuti n’kwanzeru kwambiri kunena kuti unachokera ku Gwero lina lanzeru.​—Yobu 33:4; Salmo 8:3, 4; 36:9; Machitidwe 17:28.

15. N’chifukwa chiyani kunganenedwe kuti ndinu wapadera?

15 Chotero umboni woyamba ukukhudza thambo, ndipo wachiŵiri, chiyambi cha moyo padziko lapansi. Taonani wachitatu​—kusiyana kwathu ndi zolengedwa zina zonse. Anthu onse n’ngapadera m’njira zambiri, choncho zikutanthauza kuti inunso ndinu wapadera. Motani? Muyenera kuti munamvapo zonena kuti ubongo uli ngati kompyuta yamphamvu kwambiri. Komatu, zimene apeza posachedwapa zikusonyeza kuti kompyuta imachepa kutalitali. Wasayansi wina pa Massachusetts Institute of Technology anati: “Makompyuta amakono sangafanane mpang’ono pomwe ndi munthu wa zaka zinayi zakubadwa m’mphamvu zawo za kuona, kuyankhula, kuyenda, kapena kuganiza. . . . Kwayerekezedwa kuti ngakhale mphamvu yolongosola chidziŵitso ya kompyuta yaikulu, yamphamvu koposa, ikulingana ndi mphamvu ya m’minyewa yonyamula mauthenga ya nkhono​—komwe kali kachigawo kochepa zedi pokayerekeza ndi mphamvu ya mu kompyuta yaikulu imene ili m’mutu [mwanu].”

16. Kodi luso lanu la kuyankhula limasonyeza chiyani?

16 Mumatha kuyankhula chifukwa cha ubongo wanu. Anthu ena amayankhula zinenero ziŵiri, zitatu, kapena zambiri, komabe ngakhale kungoyankhula chinenero chimodzi kumasonyeza kuti ndife apadera. (Yesaya 36:11; Machitidwe 21:37-40) Mapolofesa aŵiri R. S. ndi D. H. Fouts anafunsa kuti: “Kodi anthu . . . amangotha kuyankhulana pogwiritsa ntchito zinenero? . . . Nyama zonse zanzeru zimayankhulana pogwiritsira ntchito . . . magesichala, fungo, kuitana, kulira ndi kuimba nyimbo, ndipo ngakhale kuvina kwa njuchi. Komatu mwa nyama zonse ndi munthu yekha amene ali ndi chinenero chokhala ndi galamala yolongosoka. Ndipo n’zodziŵikiratu kuti nyama sizingathe kujambula zithunzi zatanthauzo. Zitati zitero ndiye kuti zingathe kungojambula zinthu zopanda tanthauzo.” Ndithudi, ndi anthu okha amene ubongo wawo umawatheketsa kuyankhula chinenero ndi kujambula zithunzi zatanthauzo.​—Yerekezani ndi Yesaya 8:1; 30:8; Luka 1:3.

17. Kodi pali kusiyana kwakukulu kotani pamene nyama iyang’ana m’galasi ndi pamene munthu atero?

17 Komanso, inuyo mumadzizindikira; mumadzidziŵa kuti ndinu. (Miyambo 14:10) Kodi munaonapo mbalame, galu, kapena mphaka akuyang’ana m’galasi n’kumajompha, kuyamba kulusa, kapena kufuna kumenyana ndi chithunzicho? Zimayesa kuti zikuona nyama ina, sizitha kudzizindikira. Mosiyana ndi zimenezo, mukayang’ana m’galasi, mumadzidziŵa kuti ndinu. (Yakobo 1:23, 24) Mungaone mmene mukuonekera kapena kuganizira mmene mudzaonekera patapita zaka zingapo. Nyama sizingachite zimenezo. Inde, ubongo wanu umakupangitsani kukhala wapadera. Kodi tingati ndani anapanga zimenezo? Kodi ubongo wanu unakhalapo motani, ngati sunachokere kwa Mulungu?

18. Kodi ndi maganizo otani amene amakusiyanitsani ndi nyama?

18 Ubongo wanu umakutheketsaninso kusangalala ndi zinthu zokonzedwa mwaluso ndi nyimbo komanso kudziŵa khalidwe labwino. (Eksodo 15:20; Oweruza 11:34; 1 Mafumu 6:1, 29-35; Mateyu 11:16, 17) Chifukwa chiyani inuyo osati nyama? Ubongo wa nyama umazitheketsa makamaka kuchita zinthu zofunikira panthaŵiyo​—kupeza chakudya, kupeza inzake yoti iswe nayo ana, kapena kumanga chisa. Ndi anthu okha amene amaganizira zam’tsogolo. Ena amaganiza ngakhale mmene zochita zawo zidzakhudzira malo okhala kapena mbadwa zawo kalekale m’tsogolo. Chifukwa chiyani? Mlaliki 3:11 amanena za anthu kuti: “Ndipo [Mlengi] waika zamuyaya m’mitima yawo.” Inde, kuganiza kwanu za tanthauzo la nthaŵi yosatha kapena kuganizira za moyo wosatha n’kwapadera.

Lolani Kuti Mlengi Awonjezere Tanthauzo

19. Kodi ndi njira ya mbali zitatu iti imene mungagwiritse ntchito pothandiza ena kuganiza za Mlengi?

19 Tatchula mbali zitatu zokha: kulinganiza kwabwino kwambiri kumene kumaonekera m’thambo lalikululi, chiyambi cha moyo padziko lapansi, ndi kusiyana koonekeratu kwa ubongo wa munthu, ndi mphamvu zake zosiyanasiyana pouyerekeza ndi ubongo wa nyama. Kodi zinthu zitatu zimenezi zikusonyeza chiyani? Nayi njira imene mungagwiritse ntchito kuti muthandize ena kupeza yankho. Choyamba mungafunse kuti: Kodi thambo linali ndi chiyambi? Ambiri angavomereze kuti inde. Kenako funsani kuti: Kodi pali chimene chinapangitsa chiyambicho kapena chinangoyamba chokha? Anthu ambiri amaona kuti chinachake chinayambitsa thambo kuti likhalepo. Zimene zidzakufikitsani pa funso lomaliza lakuti: Kodi chiyambicho chinapangitsidwa ndi chinachake chosatha kapena ndi Winawake wosatha? Ndiyeno mfundo zonse zitafotokozedwa bwino momveka, ambiri angafike ponena kuti: Kuyenera kuti kuli Mlengi! Ngati zili choncho, kodi sikotheka kupeza tanthauzo m’moyo?

20, 21. N’chifukwa chiyani kudziŵa Mlengi kuli kofunika kuti moyo wathu ukhale watanthauzo?

20 Kukhalapo kwathu konse, kuphatikizapo kukhumba kwathu khalidwe labwino komanso khalidwe labwinolo ziyenera kukhala zokhudzana ndi Mlengi. Panthaŵi inayake Dr. Rollo May analemba kuti: “Malongosoledwe okha okhutiritsa a khalidwe labwino amachokera pa tanthauzo lofunika la moyo.” Kodi tingawapeze kuti? Iye anapitiriza kuti: “Malongosoledwe ofunika ali umunthu wa Mulungu. Mapulinsipulo a Mulungu ndiwo mapulinsipulo amene moyo wazikidwapo kuchokera pachiyambi cha kulenga mpaka mapeto ake.”

21 Chotero, tikumvetsa chifukwa chimene wamasalmo anasonyezera zonse ziŵiri kudzichepetsa ndi nzeru pamene anapempha Mlengi kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.” (Salmo 25:4, 5) Pamene anapitiriza kum’dziŵa bwino Mlengi, ndithudi moyo wa wamasalmo unayenera kukhala watanthauzo kwambiri, wokhala ndi chifuno, ndi cholinga. Zingakhalenso chimodzimodzi ndi aliyense wa ife.​—Eksodo 33:13.

22. Kodi kudziŵa njira za Mlengi kumaphatikizapo chiyani?

22 Kufika pakudziŵa ‘njira zake’ za Mlengi kumaphatikizapo kufika pakudziŵa bwino kwambiri mmene alili, zonse ziŵiri umunthu wake ndi njira zake. Koma popeza kuti Mlengi saoneka komanso n’ngwamphamvu koopsa, kodi tingam’dziŵe bwino motani? Nkhani yotsatira idzafotokoza zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

a Poona zimene zinachitika m’misasa yachibalo ya Nazi, Dr. Viktor E. Frankl anati: “Kupeza tanthauzo la moyo ndiko nkhani yaikulu m’moyo wa munthu ndipo chimenecho ‘sichibadwa wamba,’” ngati cha nyama. Anawonjezera kuti zaka zambiri kuchokera pamene nkhondo yadziko yachiŵiri inatha, kafukufuku wina ku France “anasonyeza kuti 89 peresenti ya anthu amene anafunsidwa anavomera kuti munthu akufuna ‘chifukwa’ chokhalira ndi moyo.”

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ N’chifukwa chiyani tiyenera kupeza chidziŵitso chowonjezeka ndipo osati chasayansi chokha ponena za thambo lathu?

◻ Pothandiza ena kuti aganize za Mlengi, kodi mungasonye ku chiyani?

◻ N’chifukwa chiyani kudziŵa Mlengi kuli chinsinsi chopezera tanthauzo lokhutiritsa m’moyo?

[Chithunzi patsamba  18]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kodi Maganizo Anu ndi Otani?

Thambo lathu

↓ ↓

Linalibe Linali ndi

Chiyambi Chiyambi

↓ ↓

Popanda Choliyambitsa Linayambitsidwa

↓ ↓

Ndi Chinachake Ndi Winawake

Chamuyaya Wamuyaya

[Chithunzi patsamba 15]

Ukulu ndi kulinganiza kwabwino kwambiri koonekera m’thambo zapangitsa ambiri kuganizira za Mlengi

[Mawu a Chithunzi]

Masamba 15 ndi 18: Jeff Hester (Arizona State University) and NASA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena