Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 7/1 tsamba 8-12
  • Makolo, Kodi Chitsanzo Chanu Chimaphunzitsa Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo, Kodi Chitsanzo Chanu Chimaphunzitsa Chiyani?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Chitsanzo Chimachita
  • Zimene Chitsanzo Chathu Chingaphunzitse
  • Kupereka Chitsanzo pa Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Makolo, Pezerani A M’banja Lanu Zosowa Zawo
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 7/1 tsamba 8-12

Makolo, Kodi Chitsanzo Chanu Chimaphunzitsa Chiyani?

“Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.”​—AEFESO 5:1, 2.

1. Kodi Yehova anapereka malangizo otani ku banja loyambirira?

YEHOVA ndiye Woyambitsa makonzedwe a banja. Banja lililonse lilipo chifukwa cha iye popeza kuti iye ndiye amene anakhazikitsa banja loyambirira napatsa anthu aŵiri oyambawo mphamvu za kubala. (Aefeso 3:14, 15) Anapatsa Adamu ndi Hava malangizo ofunika pa ntchito yawo ndiponso anawapatsa mpata wokwanira woti iwo aone wokha mmene angamachitire ntchitoyo. (Genesis 1:28-30; 2:15-22) Adamu ndi Hava atachimwa, mikhalidwe imene mabanja anafunika kulimbana nayo inakhala yovuta kwambiri. Komabe, mwachikondi Yehova anapereka zitsogozo zimene zikathandiza atumiki ake kulimbana ndi mikhalidwe imeneyo.

2. (a)  Ndi m’njira ziti zimene Yehova wachirikizira malangizo olembedwa ndi apakamwa? (b) Kodi makolo afunika kudzifunsa funso lotani?

2 Monga Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova wachita zinthu zambiri kuposa kungopereka malangizo olembedwa onena za zimene tiyenera kuchita ndi zimene tiyenera kupeŵa. M’nthaŵi zakale ankaphatikiza malangizo olembedwa ndi apakamwa kudzera mwa ansembe ndi aneneri ndiponso mitu ya mabanja. Kodi iye akugwiritsa ntchito ndani kupereka malango apakamwa amenewo m’masiku athu ano? Akulu achikristu ndiponso makolo. Ngati ndinu kholo, kodi mukuchita mbali yanu kuti mulangize banja lanu m’njira za Yehova?​—Miyambo 6:20-23.

3. Kodi mitu ya mabanja ingaphunzire chiyani kwa Yehova ponena za kuphunzitsa kogwira mtima?

3 Kodi malangizo otero ayenera kuperekedwa motani m’banja? Yehova akutipatsa chitsanzo. Iye amanena momveka bwino chimene chili chabwino ndi chimene chili choipa, ndipo mokoma mtima amabwerezabwereza. (Eksodo 20:4, 5; Deuteronomo 4:23, 24; 5:8, 9; 6:14, 15; Yoswa 24:19, 20) Amagwiritsa ntchito mafunso opangitsa kuganiza. (Yobu 38:4, 8, 31) Mwa mafanizo ndi zitsanzo za zochitika zenizeni m’moyo, amasonkhezera malingaliro athu ndi kuumba mitima yathu. (Genesis 15:5; Danieli 3:1-29) Makolo, pamene mukuphunzitsa ana anu, kodi mumayesa kutsatira chitsanzo chimenechi?

4. Kodi timaphunziranji kwa Yehova ponena za kupereka chilango, ndipo kodi n’chifukwa chiyani chilango chili chofunika?

4 Yehova amamamatira pa chimene chili cholondola, komanso amamvetsa bwino zotsatira za kupanda ungwiro. Motero asanapereke chilango, iye amaphunzitsa ndipo amachenjeza ndi kukumbutsa anthu opanda ungwiro mobwerezabwereza. (Genesis 19:15, 16; Yeremiya 7:23-26) Popereka chilango, amalanga moyenera, salanga mopitirira muyeso. (Salmo 103:10, 11; Yesaya 28:26-29) Ngati mmenemu ndi mmene timachitira ndi ana athu, zimapereka umboni wakuti Yehova timamudziŵa, ndipo kudzakhala kosavuta kwa iwonso kuti amudziŵe.​—Yeremiya 22:16; 1 Yohane 4:8.

5. Kodi makolo angaphunzirenji kwa Yehova pankhani ya kumvetsera?

5 Modabwitsa kwambiri, Yehova amamvetsera monga Atate wachikondi wa kumwamba. Iye sangopereka malamulo. Amatilimbikitsa kuti tizimukhuthulira zamumtima mwathu. (Salmo 62:8) Ndipo ngati malingaliro amene timamuuza sali olondola kwenikweni, satidzudzula ndi mawu ozaza kuchokera kumwamba. Iye amatiphunzitsa moleza mtima. Motero, uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Khalani akutsanza a Mulungu,” ulidi woyenerera kwambiri! (Aefeso 4:31–5:1) Yehova amaperekadi chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo pamene akuyesa kulangiza ana awo! Chili chitsanzo chimene chimatifika pamtima ndi kutipangitsa kufuna kuyenda m’njira yake ya moyo.

Zimene Chitsanzo Chimachita

6. Kodi kaonedwe ka zinthu ndi chitsanzo cha makolo zimasonkhezera ana awo motani?

6 Kuwonjezera pa malango apakamwa, ana amasonkhezeredwa kwambiri ndi chitsanzo. Kaya makolo akufuna kapena sakufuna, ana awo adzatengera iwo basi. Zingawasangalatse makolo​—nthaŵi zina zingawadabwitse​—pamene amva ana awo akunena zinthu zimene iwowo ananena. Pamene khalidwe ndi kaonedwe ka zinthu ka makolo kasonyeza kuyamikira kwambiri zinthu zauzimu, zimenezi zimasonkhezera ana kuchita zinthu bwino.​—Miyambo 20:7.

7. Kodi Yefita monga kholo anaonetsa chitsanzo chotani kwa mwana wake wamkazi, ndipo panali zotsatira zotani?

7 Zimene chitsanzo cha makolo chimachita zikusonyezedwa bwino m’Baibulo. Yefita, amene Yehova anamugwiritsa ntchito kutsogolera Aisrayeli kuti apambane polimbana ndi a Amoni, analinso kholo. Nkhani yonena za yankho lake kwa mfumu ya a Amoni imasonyeza kuti Yefita anali kuŵerenga kaŵirikaŵiri mbiri ya zochita za Yehova ndi Aisrayeli. Iye anatchula bwino lomwe zochitika za m’mbiri imeneyo, ndipo anasonyeza chikhulupiriro cholimba mwa Yehova. Mosakayikira, chitsanzo chake chinathandiza mwana wake wamkazi kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso mzimu wodzimana umene anaonetsa mwa kukhala mu utumiki wodzipereka kwa Yehova kwa moyo wake wonse ali wosakwatiwa.​—Oweruza 11:14-27, 34-40; yerekezerani ndi Yoswa 1:8.

8. (a) Kodi ndi malingaliro abwino otani amene makolo ake a Samueli anasonyeza? (b) Kodi zimenezo zinamupindulitsa motani Samueli?

8 Samueli anali mwana wa chitsanzo chabwino ndiponso anali mneneri wokhulupirika kwa Mulungu pa moyo wake wonse. Kodi mukufuna kuti ana anu adzakhale monga mmene iye analili? Lingalirani chitsanzo chimene makolo ake a Samueli, Elikana ndi Hana, anapereka. Ngakhale kuti zinthu m’nyumba mwawo sizinali bwino, iwo nthaŵi zonse anali kupita ku Silo kukalambira, kumalo amene chihema chopatulika chinalili. (1 Samueli 1:3-8, 21) Taonani malingaliro akuya amene Hana anali nawo pamene anali kupemphera. (1 Samueli 1:9-13) Onani mmene onse aŵiri anaonera kufunika kwa kukwaniritsa chilichonse chimene analonjeza kwa Mulungu. (1 Samueli 1:22-28) Mosakayikira chitsanzo chawo chabwino chinathandiza Samueli kukhala ndi mikhalidwe imene inamuthandiza kulondola njira yoyenera​—ngakhale pamene anthu amene anali kukhala nawo amene ankaoneka kuti anali kutumikira Yehova sanasonyeze ulemu uliwonse ku njira za Mulungu. M’kupita kwa nthaŵi, Yehova anapatsa Samueli udindo wokhala mneneri Wake.​—1 Samueli 2:11, 12; 3:1-21.

9. (a) Ndi zochitika za panyumba zotani zimene zinamusonkhezera Timoteo? (b) Kodi Timoteo anadzakhala munthu wotani?

9 Kodi mukufuna kuti mwana wanu adzakhale ngati Timoteo, amene pamene anali mnyamata anakhala mnzake wa mtumwi Paulo wogwira naye ntchito? Abambo ake a Timoteo anali wosakhulupirira, koma amayi ake ndi agogo ake anapereka chitsanzo chabwino cha kuyamikira zinthu zauzimu. Mosakayikira zimenezi zinathandiza kuyala maziko abwino a moyo wa Timoteo monga Mkristu. Timauzidwa kuti amayi ake, a Yunike, ndi agogo ake a Loisi anali ndi “chikhulupiriro chosanyenga.” Moyo wawo monga Akristu sunali wachinyengo; anakhaladi mogwirizana ndi zimene ankati anali kukhulupirira, ndipo anamuphunzitsanso mwanayo Timoteo kuchita chimodzimodzi. Timoteo anasonyeza kuti anali munthu wodalirika ndi kuti analidi kusamala za ubwino wa ena.​—2 Timoteo 1:5; Afilipi 2:20-22.

10. (a) Kodi ndi zitsanzo zotani zimene sizili za panyumba zimene zingakhudze ana athu? (b) Kodi tiyenera kuchitanji pamene zinthu zimenezi zionekera m’kalankhulidwe ndi zochita za ana athu?

10 Zitsanzo zimene zimakhudza ana athu si zapanyumba zokha. Pali ana ena amene amakhala nawo kusukulu, aphunzitsi amene ntchito yawo ndi kuumba maganizo athete, anthu amene amakhulupirira zolimba kuti aliyense ayenera kuchita mogwirizana ndi miyambo yachikhalire ya mtunduwo kapena ya m’deralo, anthu otchuka a zamaseŵera amene zochita zawo zimatamandidwa ponseponse, ndi akuluakulu aboma amene khalidwe lawo limasimbidwa m’nkhani. Ana ena miyandamiyanda aonaponso nkhanza za nkhondo. Kodi tiyenera kudabwa ngati zinthu zimenezi zionekera m’kalankhulidwe kapena zochita za ana athu? Kodi timachita motani iwo akatero? Kodi kudzudzula kapena kulangiza mwaukali kungathetse vutolo? M’malo mokamba ndi ana athu mwamsanga, kodi sikungakhale bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali chilichonse m’njira imene Yehova amachitira nafe zinthu chimene chingathandize kuzindikira mmene ndingachitire ndi mkhalidwewu?’​—Yerekezerani ndi Aroma 2:4.

11. Pamene makolo achita zolakwa, kodi zimenezi zingakhudze motani khalidwe la ana awo?

11 Zoonadi, makolo opanda ungwiro sadzachita zinthu m’njira yabwino kwambiri nthaŵi zonse. Iwo adzakhala ndi zolakwitsa ndithu. Pamene ana azindikira zimenezi, kodi zidzawachititsa kusapereka ulemu kwa makolo awo? Zingatero, makamaka ngati makolo amayesa kupeputsa zolakwa zawo mwa kusonyeza ulamuliro wawo mwaukali. Koma pangachitike zosiyana kwambiri ngati makolo ali odzichepetsa ndiponso ngati avomereza zolakwa zawo mosavuta. Mwakutero, iwo angapereke chitsanzo chabwino kwambiri kwa ana awo, amene afunika kuphunzira kuchita zofananazo.​—Yakobo 4:6.

Zimene Chitsanzo Chathu Chingaphunzitse

12, 13. (a) Kodi ana ayenera kuphunziranji pankhani ya chikondi, ndipo kodi ndi motani mmene zimenezi zingaphunzitsidwire bwino kwambiri? (b) Kodi ndi chifukwa chiyani kuli kofunika kuti ana aphunzire za chikondi?

12 Pali maphunziro amtengo wapatali ambirimbiri amene angaphunzitsidwe bwino kwambiri pamene malango apakamwa aphatikizidwa ndi chitsanzo chabwino. Talingaliraniko ochepa.

13 Kusonyeza chikondi chopanda dyera: Phunziro limodzi mwa maphunziro ofunika kwambiri oyenera kuchirikizidwa ndi chitsanzo ndilo tanthauzo la chikondi. “Tikonda ife, chifukwa anayamba [Mulungu] kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Iye ndiye Gwero ndi chitsanzo chapamwamba kwambiri cha chikondi. Chikondi cha lamulo chimenechi, a·gaʹpe, chikutchulidwa m’Baibulo nthaŵi zoposa 100. Ndiwo mkhalidwe umene umadziŵikitsa Akristu oona. (Yohane 13:35) Chikondi choterechi chifunika kusonyezedwa kwa Mulungu ndi Yesu Kristu ndiponso ndi anthu kwa wina ndi mnzake​—ngakhalenso kwa anthu amene satisangalatsa. (Mateyu 5:44, 45; 1 Yohane 5:3) Chikondi chimenechi poyamba chiyenera kukhala m’mitima mwathu ndi kumaoneka m’miyoyo yathu kuti tichiphunzitse mogwira mtima kwa ana athu. Zochita zimanena zambiri kusiyana ndi mawu. M’banja ana ayenera kuona chikondi ndi mikhalidwe ina yofanana nacho, monga kuyanjana, komanso ayenera kumamva kuti amakondedwa. Popanda zinthu zimenezi, mwana amakwinimbira m’kakulidwe kake kakuthupi, kamaganizo, ndi kamalingaliro. Ana ayeneranso kuona mmene chikondi ndi kuyanjana zimasonyezedwera bwino kwa Akristu anzawo amene sali a m’banjamo.​—Aroma 12:10; 1 Petro 3:8.

14. (a) Kodi ana angaphunzitsidwe motani kugwira bwino ntchito yokhutiritsa? (b) Kodi zimenezi zingachitidwe motani m’mikhalidwe ya banja lanu?

14 Kuphunzira kugwira ntchito: Ntchito ndi mbali yofunika kwambiri ya moyo. Kuti munthu azidzimva kuti ndi wofunika, iye ayenera kuphunzira kugwira bwino ntchito. (Mlaliki 2:24; 2 Atesalonika 3:10) Ngati mwana apatsidwa ntchito zimene analangizidwa pang’ono chabe mmene angazigwirire ndiyeno kenaka ndi kukalipidwa chifukwa chosazigwira bwino, ndi zokayikitsa kuti adzaphunzira kugwira bwino ntchito. Koma pamene ana aphunzira mwa kugwira ntchito pamodzi ndi makolo awo ndiponso ndi kumawayamikira moyenerera, iwo angathedi kuphunzira mmene angamagwirire ntchito yokhutiritsa. Pamene chitsanzo cha makolo chiphatikizapo kulongosola mmene zikuchitikira, ana angaphunzire osati kokha kugwira ntchito komanso kugonjetsa mavuto, kulimbikira kugwira ntchito mpaka itatha, ndiponso kuganiza ndi kusankha zochita. M’kuchita kotereku iwo angathandizidwe kuzindikira kuti Yehovanso amagwira ntchito, kuti iye amagwira bwino ntchito, ndi kuti Yesu amatsanzira Atate ake. (Genesis 1:31; Miyambo 8:27-31; Yohane 5:17) Ngati ndinu alimi pabanja lanu kapena ngati mumagulitsa malonda, ena a m’banja lanu angamagwirire ntchito pamodzi. Kapena mwina amayi angaphunzitse mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi kuphika ndi kutsuka ziwiya mukatha kudya. Atate amene amagwirira ntchito kutali ndi nyumba yawo angakonze kugwira ntchito za pakhomopo pamodzi ndi ana awo. Zilidi zothandiza kwambiri pamene makolo akumbukira kuti sangofunika kuonetsetsa kuti ntchito za mwamsanga zili kugwiridwa komanso kuti akukonzekeretsa ana za moyo wawo!

15. Kodi maphunziro okhudza chikhulupiriro angaperekedwe motani? Perekani chitsanzo.

15 Kukhalabe ndi chikhulupiriro pokumana ndi mavuto: Chikhulupiriro chilinso mbali yofunika kwambiri ya moyo wathu. Pamene mukambirana za chikhulupiriro pa phunziro labanja, ana angaphunzire kuchifotokoza. Iwo angazindikirenso umboni umene umapangitsa chikhulupiriro kuyamba kukula m’mitima yawo. Koma pamene aona makolo awo akusonyeza chikhulupiriro chosagwedera pokumana ndi mayesero aakulu, zotsatira zake zingakhale kwa moyo wonse. Wophunzira Baibulo wina ku Panama anaopsezedwa ndi mwamuna wake kuti adzamuthamangitsa panyumba ngati sasiya kutumikira Yehova. Komabe, ndi ana ake ang’ono anayi, iye nthaŵi zonse anali kuyenda pansi ulendo wa makilomita 16 ndiyeno ndi kukwera basi n’kuyenda makilomita 30 kuti akafike pa Nyumba ya Ufumu yapafupi ndi kwawo. Polimbikitsidwa ndi chitsanzo chimenecho, achibale ake ena okwana ngati 20 atsatira njira ya choonadi.

Kupereka Chitsanzo pa Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku

16. Kodi ndi chifukwa chiyani kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kuli koyenera?

16 Chimodzi mwa zizoloŵezi zabwino koposa zimene banja lililonse lingapange​—chizoloŵezi chimene chidzapindulitsa makolo ndi kukhala chitsanzo chakuti ana atsanzire​—ndicho kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. Ngati kuli kotheka, ŵerengani Baibulo tsiku lililonse. Si kuchuluka kwa zimene mwaŵerenga kumene kuli kofunika kwambiri. Chimene chili chofunika kwambiri ndi chakuti kodi mumaŵerenga kaŵirikaŵiri motani ndiponso m’njira yotani. Kwa ana, mungawonjezere pa kuŵerenga Baibulo kumvetsera makaseti a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ngati alipo m’chinenero chanu. Kuŵerenga m’Mawu a Mulungu tsiku lililonse kumatithandiza kuika patsogolo malingaliro a Mulungu. Ndipo ngati kuŵerenga Baibulo koteroko kuchitidwa osati kokha ndi anthu ena chabe koma ndi mabanja, izi zingathandize mabanja athunthu kuyenda m’njira za Yehova. Ndi m’khalidwe umenewu umene seŵero lakuti Mabanja​—Pangani Kuŵerenga Baibulo kwa Tsiku ndi Tsiku Kukhala Chizoloŵezi Chanu! linalimbikitsa pa Misonkhano Yachigawo yaposachedwapa ya “Njira ya Moyo ya Mulungu.”​—Salmo 1:1-3.

17. Kodi kuŵerenga Baibulo kwa banja ndi kuloweza malemba akuluakulu kumathandiza motani kugwiritsa ntchito uphungu wopezeka pa Aefeso 6:4?

17 Kuŵerenga Baibulo monga banja kukugwirizana ndi zimene mtumwi Paulo analemba m’kalata yake youziridwa yopita kwa Akristu a ku Efeso, kuti: “Atate . . . musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Kwenikweni “chilangizo” chimatanthauza “kuikapo maganizo”; motero atate achikristu akulimbikitsidwa kuika maganizo a Yehova Mulungu mwa ana awo​—kuthandiza ana kudziŵa malingaliro a Mulungu. Kulimbikitsa ana kuloweza malemba akuluakulu kungathandize kukwaniritsa zimenezi. Cholinga ndi chakuti malingaliro a Yehova azitsogolera maganizo a ana kotero kuti zikhumbo zawo ndi zochita zawo mwapang’onopang’ono zidzafika posonyeza miyezo ya Mulungu kaya akhale ndi makolo awo kapena ayi. Baibulo ndilo maziko a maganizo ameneŵa.​—Deuteronomo 6:6, 7.

18. Poŵerenga Baibulo, kodi ndi chiyani chimene chingafunike kuti (a) mulimvetse bwinobwino? (b) mupindule ndi uphungu umene lili nalo? (c) muchite mogwirizana ndi zimene limavumbula ponena za chifuno cha Yehova? (d) mupindule ndi zimene limanena pa maganizo ndi zochita za anthu?

18 Zoonadi, ngati Baibulo liti likhudze miyoyo yathu, tifunika kumvetsa zimene limanena. Kwa anthu ambiri, izi zingafune kuti aŵerenge mbali zina maulendo angapo. Kuti timvetsetsedi mawu ena, tingafunike kuyang’ana matanthauzo a mawuwo mu dikishonale kapena mu Insight on the Scriptures. Ngati lemba lili ndi uphungu kapena lamulo, khalani ndi nthaŵi yokwanira yokamba za mikhalidwe m’masiku athu ano imene imapangitsa lembalo kukhala loyenerera. Ndiyeno mungafunse kuti, ‘Kodi kugwiritsa ntchito uphungu umenewu kungatithandize bwanji?’ (Yesaya 48:17, 18) Ngati lembalo likunena za mbali ina ya chifuno cha Yehova, funsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikukhudza bwanji moyo wathu?’ Mwina mukuŵerenga nkhani imene ikunena za khalidwe la anthu ndi zochita zawo. Kodi pamoyo wawo iwo anali kukumana ndi mavuto otani? Kodi iwo anachita nawo motani mavutowo? Kodi tingapindule motani ndi chitsanzo chawo? Nthaŵi zonse khalani ndi nthaŵi yokwanira yokambirana kufunika kwa nkhaniyo m’moyo wathu lerolino.​—Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11.

19. Mwa kukhala otsanza a Mulungu, kodi tidzakhala tikupereka chiyani kwa ana athu?

19 Ndi njiratu yabwino kwambiri yochititsira malingaliro a Mulungu kukhazikika m’maganizo ndi m’mitima yathu! Motero tidzathandizidwadi kukhala “akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Ndipo tidzapereka chitsanzo chimene chidzakhaladi chofunika kuti ana athu atsanzire.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi makolo angapindule motani ndi chitsanzo cha Yehova?

◻ Kodi ndi chifukwa chiyani kupereka malango apakamwa kwa ana kuyenera kuphatikizidwa ndi chitsanzo chabwino cha makolo?

◻ Kodi ndi maphunziro ena ati amene amaphunzitsidwa bwino kwambiri ndi chitsanzo cha makolo?

◻ Kodi ndi motani mmene tingapindulire mokwanira ndi kuŵerenga Baibulo kwa banja?

[Zithunzi patsamba 10]

Ambiri amasangalala kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku monga banja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena